Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 4

Yehova Amadalitsa Kuyesetsa Kwathu Kuti Ticite Cikumbutso

Yehova Amadalitsa Kuyesetsa Kwathu Kuti Ticite Cikumbutso

“Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—LUKA 22:19.

NYIMBO 19 Mgonelo wa Ambuye

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. N’cifukwa ciyani timapezeka ku Cikumbutso caka ciliconse?

 ZAKA pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka ife. Izi zinatsegula mwayi wokalandila moyo wosatha. Usiku wakuti Yesu maŵa lake aphedwa, analamula otsatila ake kuti azikumbukila cikondi cimene iye anaonetsa, pocita mwambo wosalila zambili pogwilitsa nchito mkate na vinyo.—1 Akor. 11:23-26.

2 Timamvela lamulo la Yesu limeneli cifukwa timam’konda kwambili. (Yoh. 14:15) Ndipo caka ciliconse pa nyengo ya Cikumbutso, timaonetsa ciyamikilo cathu pa zimene iye anaticitila, mwa kusinkhasinkha mmene imfa yake imatipindulila. Cinanso, timawonjezela utumiki wathu poitanila anthu ambili mmene tingathele kuti adzakhale nafe pa cocitika capadela cimeneci. Ndipo timaonetsetsa kuti sitikulola ciliconse kutilepheletsa kukapezeka ku Cikumbutso.

3. M’nkhani ino tikambilane ciyani?

3 M’nkhani ino, tikambilane njila zitatu zoonetsa mmene anthu a Yehova amacitila zonse zotheka kuti akumbukile imfa ya Yesu: (1) mwa kucita Cikumbutso m’njila imene Yesu anacitila, (2) mwa kuitanilako ena, komanso (3) mwa kucita Cikumbutso mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta.

KUCITA CIKUMBUTSO M’NJILA IMENE YESU ANACITILA

4. Ni mfundo ziti za coonadi zimene timamvetsela pa Cikumbutso caka ciliconse? Nanga n’cifukwa ciyani sitiyenela kuzitenga mopepuka mfundozo? (Luka 22:19, 20)

4 Caka ciliconse pa Cikumbutso, timamvetsela nkhani yozikika m’Baibo, yofotokoza mfundo zingapo za coonadi momveka bwino. Timaphunzila cifukwa cake anthufe tifunikila dipo, komanso mmene imfa ya munthu mmodzi inaombolela macimo a anthu ambili. Cina, timakumbutsidwa zimene mkate na vinyo ziimila, komanso amene ayenela kudya ziphiphilitso zimenezi. (Ŵelengani Luka 22:19, 20.) Kuwonjezela apo, timasinkhasinkha madalitso amene Mulungu wasungila anthu ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi. (Yes. 35:5, 6; 65:17, 21-23) Mfundo za coonadi zimenezi sitimazitenga mopepuka, cifukwa anthu mabiliyoni sazidziŵa. Cinanso, samvetsa phindu la nsembe ya Yesu. Komanso, sacita Cikumbutso ca imfa yake potengela mmene Yesu iye mwiniyo anacitila. Cifukwa ciyani?

5. Atumwi onse atatha kumwalila, kodi anthu anayamba kuucita m’njila yotani mwambo umene Yesu anayambitsa?

5 Atumwi a Yesu atatha kumwalila, Akhristu onyenga analoŵa mu mpingo wacikhristu. (Mat. 13:24-27, 37-39) Iwo anali kukamba “zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzila aziwatsatila.” (Mac. 20:29, 30) Cimodzi mwa “zinthu zopotoka” zimene Akhristu onyenga amenewo anali kuphunzitsa, n’cakuti Yesu sanapeleke thupi lake “nsembe kamodzi kokha kuti anyamule macimo a anthu ambili,” malinga na zimene Baibo imakamba. Koma kuti nsembe yake iyenela kupelekedwa mobweleza-bweleza. (Aheb. 9:27, 28) Masiku ano, anthu ambili amakhulupilila ciphunzitso cabodza cimeneci. Iwo amasonkhana m’machalichi mwawo mlungu uliwonse—nthawi zina tsiku lililonse—kuti acite mwambo umene amaucha kuti “Nsembe ya Misa.” b Zipembedzo zina si kambili kucita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu, koma anthu ambili m’zipembedzo zimenezo samvetsa phindu lenileni la nsembe ya Yesu. Ena amafunsa kuti, ‘Kodi n’zoonadi kuti imfa ya Yesu ingapangitse kuti macimo anga akhululukidwe?’ N’cifukwa ciyani amafunsa funsoli? Cifukwa amakhulupilila zokamba za anthu ena amene amati n’zosatheka kukhululukidwa macimo pamaziko a nsembe ya Yesu. Kodi otsatila oona a Yesu awathandiza bwanji anthu amene amakayikila zimenezi?

6. Mu 1872, kodi ophunzila Baibo anafika podziŵa mfundo yotani?

6 Mu 1870, kagulu ka ophunzila Baibo motsogozedwa na M’bale Charles Taze Russell, kanayamba kuphunzila Malemba mozama. Iwo anali kufuna kudziŵa zoona zake zokhudza tanthauzo la imfa ya Yesu, komanso mmene imfa yake iyenela kukumbukilidwa. Mu 1872, iwo anafika podziŵa mfundo ya m’Baibo yakuti Yesu anapelekadi dipo lowombola mtundu wa anthu. Zimene anaphunzilazo sanangozisunga osauzako ena ayi. M’malo mwake, anazifalitsa kwa anthu kupyolela m’mabuku, manyuzipepala, na m’magazini. Ndipo posakhalitsa, anayamba kusonkhana kamodzi pacaka kuti acite Cikumbutso, potengela citsanzo ca Akhristu a m’zaka za zana loyamba.

7. Kodi timapindula nako motani kufufuza kumene ophunzila Baibo anacita kalelo?

7 Masiku ano, timapindula na mfundo zimene Akhristu oona mtima amenewo anafufuza kalelo. Motani? Yehova watithandiza kudziŵa zimene nsembe ya Yesu imatanthauza, komanso mmene imapindulila anthu onse. (1 Yoh. 2:1, 2) Taphunzilanso kuti Baibo imachula ziyembekezo ziŵili za anthu amene amakondweletsa Mulungu—ciyembekezo codzakhala na moyo wosakhoza kufa kumwamba, komanso ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi. Timamuyandikila kwambili Yehova tikamaganizila mmene iye amatikondela, komanso mmene timapindulila na nsembe ya Yesu. (1 Pet. 3:18; 1 Yoh. 4:9) Conco, monga mmene abale athu okhulupilika akale anacitila, ifenso timaitanila ena kuti adzacite nafe Cikumbutso, m’njila imene Yesu anacitila.

KUMEMEZA ANTHU KU CIKUMBUTSO

Kodi mungacite ciyani kuti mukatengeko mbali mokwanila pa kampeni yoitanila anthu ku Cikumbutso? (Onani ndime 8-10) e

8. Kodi anthu a Yehova acita zotani poitanila ena ku Cikumbutso? (Onani cithunzi.)

8 Kwa zaka zambili, anthu a Yehova akhala akuitanila anthu ku Cikumbutso. Kungoyambila mu 1881, abale na alongo ku United States anaitanidwa ku cocitika capadela cimeneci, cimene cinacitikila m’nyumba ya m’bale ku Allegheny, Pennsylvania. Patapita nthawi, mpingo uliwonse unayamba kucita paokha Cikumbutso. Mu March 1940, ofalitsa anauzidwa kuti aitanile aliyense amene waonetsa cidwi m’gawo lawo. Ndipo mu 1960, kwa nthawi yoyamba ofesi ya nthambi inapatsa mipingo tumapepala topulinta toitanila anthu. Kucokela nthawiyo, tumapepela tomemeza anthu ku Cikumbutso tofika m’mabiliyoni twafalitsidwa. N’cifukwa ciyani timataila nthawi na mphamvu zathu kuitanila anthu ku Cikumbutso?

9-10. Ndani amapindula tikamayesetsa kuitanila anthu ku Cikumbutso? (Yohane 3:16)

9 Cifukwa cimodzi cimene timaitanila ena ku Cikumbutso, n’cakuti timafuna kuti anthu omwe apezekapo kwa nthawi yoyamba aphunzile coonadi pa zimene Yehova na Yesu anaticitila tonsefe. (Ŵelengani Yohane 3:16.) Timakhalanso na ciyembekezo cakuti zimene adzamva na kuona ku Cikumbutso zidzawalimbikitsa kuphunzila zambili, komanso kukhala atumiki a Yehova. Koma palinso ena amene amapindula.

10 Timaitanilanso anthu amene analeka kutumikila Yehova. Timacita zimenezi pofuna kuwakumbutsa kuti Mulungu akali kuwakonda. Ambili amalabadila ciitano cathu, ndipo timakondwela kuwaona kuti apezekapo. Kupezeka ku Cikumbutso kumawakumbutsa cimwemwe cimene anali naco pamene anali kutumikila Yehova. Ganizilani citsanzo ici ca Monica. c Iye anautsidwanso monga wofalitsa panthawi ya mlili wa COVID-19. Atapezeka pa Cikumbutso mu 2021, anati: “Cikumbutso ici cakhala capadela kwa ine. Pambuyo pa zaka 20, n’nayamba kulalikila na kuitanilako anthu ku Cikumbutso. N’naikilapo mtima pa nchitoyi cifukwa nimayamikila kwambili pa zimene Yehova na Yesu ananicitila.” (Sal. 103:1-4) Kaya anthu alandile ciitano cathu kapena ayi, timapitilizabe kuwaitanila podziŵa kuti Yehova amayamikila kuyesetsa kwathu.

11. Kodi Yehova amadalitsa bwanji khama lathu poitanila anthu ku Cikumbutso? (Hagai 2:7)

11 Yehova amadalitsa kuyesetsa kwathu poitanila anthu ku Cikumbutso. Mwacitsanzo, mu 2021 ngakhale kuti panali ziletso cifukwa ca mlili wa COVID-19, amene anapezeka pa Cikumbutso anali 21,367,603, kuwilikiza pafupifupi kaŵili na theka ciŵelengelo ca Mboni za Yehova padziko lonse. Koma Yehova samangoyang’ana ciŵelengelo ca anthu opezeka pa Cikumbutso. Cidwi cake cimakhala pa munthu aliyense amene wapezekapo. (Luka 15:7; 1 Tim. 2:3, 4) Sitikayika zakuti Yehova amatithandiza kupeza anthu a mitima yabwino kupyolela m’nchito yoitanila anthu.—Ŵelengani Hagai 2:7.

KUCITA CIKUMBUTSO NGAKHALE PA NTHAWI YOVUTA

Yehova amadalitsa kuyesetsa kwathu kuti ticite Cikumbutso (Onani ndime 12) f

12. Ni mavuto ati amene angapangitse kuti cikhale covuta kupezeka ku Cikumbutso? (Onani cithunzi.)

12 Yesu anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, tidzakumana na mavuto osiyana-siyana, monga kutsutsidwa na acibale, mazunzo, nkhondo, milili, na zina zotelo. (Mat. 10:36; Maliko 13:9; Luka 21:10, 11) Nthawi zina, mavuto amenewa amapangitsa kuti cikhale covuta kupezeka ku mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Kodi abale na alongo amacita ciyani kuti agonjetse zopinga zimenezi? Nanga Yehova amawathandiza bwanji?

13. Kodi Yehova anadalitsa bwanji kulimba mtima kwa m’bale Artem, komanso kuyesetsa kwake kuti acite Cikumbutso ngakhale kuti anali m’ndende?

13 Tikakhala m’ndende. Abale athu amene ali m’ndende amacita zonse zimene angathe kuti akumbukile imfa ya Yesu. Ganizilani citsanzo ici ca m’bale Artem. Mu 2020, kutatsala milungu ingapo kuti Cikumbutso cicitike, iye anaponyedwa m’citolokosi cokwana anthu asanu okha. Ngakhale kuti anali m’ndende, iye anakwanitsa kupeza ziphiphilitso zogwilitsa nchito, ndipo anakonza zakuti adzikambile yekha nkhani ya Cikumbutso. Koma akaidi anzake m’citolokosi cimeneco anali kukoka fodya na kutukwana kwambili. Kodi iye anacita ciyani? Iye anawapempha kuti asakoke fodya na kutukwana kwa ola limodzi cabe. M’bale Artem anadabwa kwambili kuona kuti akaidiwo avomela kuti sadzacita zimenezo. Iye anati: “N’nawapempha kuti niwafotokozele za Cikumbutso.” Iwo anakana kumvetsela zokhudza cocitika cimeneci. Koma pambuyo pomvetsela na kuona m’bale Artem akucita Cikumbutso, anam’pempha kuti awafotokozele zambili.

14. Kodi anthu a Yehova anayesetsa kucita ciyani kuti acite Cikumbutso mosasamala kanthu za mlili wa COVID-19?

14 Mlili wa COVID-19. Pamene mliliwu unabuka, cinali cosatheka anthu a Yehova kucita Cikumbutso pamaso-m’pamaso. Koma zimenezi sizinawalepheletse kucita Cikumbutso. d Mipingo imene inali kukwanitsa kuloŵa pa Intaneti, inacita Cikumbutso pa Zoom. Nanga bwanji anthu mamiliyoni amene analibe mwayi woloŵa pa Intaneti? M’maiko ena, anapanga makonzedwe akuti aulutse nkhani ya Cikumbutso pa TV kapena pa wailesi. Kuwonjezela apo, maofesi a nthambi anajambula nkhani ya Cikumbutso m’zinenelo zopitilila 500, kuti anthu okhala m’madela akutali acite Cikumbutso. Ndipo abale okhulupilika anakonza zakuti nkhani yojambulidwa imeneyo itumizidwe kwa ofalitsa a ku madela akutali amenewo.

15. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca wophunzila Baibo dzina lake Sue?

15 Kutsutsidwa m’banja. Kwa ena, vuto lalikulu limene amakumana nalo kuti acite Cikumbutso, ni kutsutsidwa m’banja. Ganizilani citsanzo ici ca wophunzila Baibo wina dzina lake Sue. Mu 2021, tsiku lakuti maŵa ni Cikumbutso, Sue anauza wom’phunzitsa Baibo kuti cifukwa cotsutsidwa na a m’banja lake, sadzapezeka ku Cikumbutso. Mphunzitsi wakeyo anamuŵelengela Luka 22:44. Ndiyeno anamufotokozela kuti tikakumana na mavuto, tiyenela kutsatila citsanzo ca Yesu mwa kupemphela kwa Yehova, komanso kuika cidalilo cathu conse mwa iye. Pa tsiku la Cikumbutso, Sue anakonza ziphiphilitso, na kumvetsela pulogilamu ya Kulambila kwa M’maŵa kwa pa Cikumbutso pa jw.org. Ndiyeno m’madzulo, ali yekha m’cipinda analumikiza ku pulogilamu ya Cikumbutso pa foni. Pambuyo pake, Sue analembela mphunzitsi wake wa Baibo kuti: “Munanilimbikitsa kwambili dzulo. N’nacita zonse zotheka kuti nipezeke pa Cikumbutso, ndipo Yehova ananithandiza. Pano nisoŵa na cokamba poonetsa kuyamikila na cimwemwe cimene nili naco!” Kodi muona kuti inunso Yehova angakuthandizeni mukakumana na vuto ngati limeneli?

16. N’cifukwa ciyani sitikayika olo pang’ono kuti Yehova adzadalitsa kuyesetsa kwathu kuti tikapezeke pa Cikumbutso? (Aroma 8:31, 32)

16 Yehova amayamikila kwambili kuyesetsa kwathu kuti tikumbukile imfa ya Yesu. Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa tikamaonetsa kuti timayamikila zimene iye anaticitila. (Ŵelengani Aroma 8:31, 32.) Conco, tiyeni ticite zotheka kuti tikapezeke pa Cikumbutso caka cino, komanso kuwonjezela utumiki wathu pa nyengo ya Cikumbutso.

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

a Pa Ciŵili, April 4, 2023, anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi adzasonkhana kuti acite Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Ena kudzakhala kuyamba kupezekapo. Ndipo ena amene akhala Mboni zozilala kwa zaka zambili nawonso adzapezekapo. Ena adzakhala atagonjetsa zopinga zina kuti akapezeke pa Cikumbutso. Kaya zinthu zili motani pa umoyo wanu, dziŵani kuti Yehova adzakondwela kwambili poona kuti mwayesetsa kuti mupezekepo.

b Anthu a zipembedzo zimenezo amakhulupilila kuti pa nthawi ya mwambo umenewu, mkate na vinyo zimasandulika n’kukhala thupi lenileni, komanso magazi enieni a Khristu. Iwo amaona kuti thupi la Yesu na magazi ake zimapelekedwa nsembe nthawi iliyonse mwambowu ukamacitika.

c Maina ena asinthidwa.

d Onani nkhani zakuti, “Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2021.” Nkhanizi zipezeka pa jw.org ku Chichewa.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kuyambila m’ma 1960, tumapepala tomemeza anthu ku Cikumbutso twakhala tukukonzedwanso, ndipo tumapezeka topulinta komanso twa pa zipangizo.

f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Citsanzo—Abale na alongo akucita Cikumbutso pa nthawi yaciwawa.