Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza Yokhudza Webusaiti Yathu

Mfundo Yothandiza Yokhudza Webusaiti Yathu

Kupeza Nkhani Zimene Zinaikidwapo pa Webusaiti

Abale na alongo athu ambili amagwilitsa nchito nkhani zimene zimaikidwa patsamba loyamba pa webusaiti ya jw.org mu ulaliki. Iwo amatumikilako ena nkhanizo mosavuta kupitila pa zipangizo. Ndipo nthawi zambili, nkhanizo zimafotokoza mmene zocitika padzikoli zimakwanilitsila ulosi wa m’Baibo. M’bale wina analemba kuti: “Nkhani zoikidwa patsamba loyamba pa webusaiti yathu n’zimene zatithandiza kwambili pocita ulaliki m’njila imene tikucita palipano.”

Komabe, nkhani zimenezi zimasintha-sintha. Kodi mungazipeze kuti nkhani zimene sizikuonekelanso patsamba loyamba pa webusaiti yathu?

  • Pitani pa jw.org patsamba loyamba polemba kuti “Laibulale.” Kenako, dinizani link yakuti “Mpambo wa Nkhani.” Kenako, dinizani polemba kuti “Nkhani Zinanso.” Pamenepo mudzapeza nkhani zosiyanasiyana zimene zinaikidwa pa tsamba loyamba pa webusaiti yathu m’mbuyomu.

  • Pitani pa jw.org patsamba loyamba polemba kuti Laibulale. Kenako, dinizani link yakuti Mpambo wa Nkhani. Kenako, dinizani polemba kuti Nkhani Zinanso. Pamenepo mudzapeza nkhani zosiyanasiyana zimene zinaikidwa pa tsamba loyamba pa webusaiti yathu mbuyomu.