Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 12

Phunzilani Zambili za Yehova Poyang’ana Cilengedwe Cake

Phunzilani Zambili za Yehova Poyang’ana Cilengedwe Cake

“Cilengedwele dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.”—AROMA 1:20.

NYIMBO 6 Zakumwamba Zilengeza Ulemelelo wa Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Ni njila iti imene inathandiza Yobu kum’dziŵa bwino Yehova?

 PA UMOYO wake wonse Yobu, makambilano ake na Yehova Mulungu ndiwo anali ofunika kwambili kuposa ena alionse. Pa makambilano amenewo, Yehova anauza Yobu kuti ayang’ane mwacidwi zinthu zimene iye analenga. Izi zinali kudzathandiza Yobu kudziŵa kuti Yehova ni wanzelu. Zinam’thandizanso kulimbitsa cidalilo cake cakuti Yehova amasamalila zosoŵa za atumiki ake. Mwacitsanzo, Yobu anakumbutsidwa kuti Mulungu amasamalila nyama. Conco, sakanalephela kum’samalila Yobu. (Yobu 38:39-41; 39:1, 5, 13-16) Mwa kuyang’ana mwacidwi zinthu zacilengedwe, Yobu anadziŵa zambili zokhudza makhalidwe a Mulungu.

2. N’cifukwa ciyani cingakhale covuta kusinkhasinkha zimene Yehova analenga?

2 Nafenso tingaphunzile zambili za Mulungu tikamayang’ana mwacidwi zinthu zimene analenga. Komabe, nthawi zina cingakhale covutilapo kucita zimenezo. Ngati tikhala m’tauni, sitingaone zambili zimene Mulungu analenga. Koma ngakhale kumadela akumidzi, kumene zacilengedwe zili paliponse, tingamaone kuti tilibe nthawi yokwanila yosinkhasinkha zinthuzo. Conco, tiyeni tikambilane cifukwa cake n’kopindulitsa kupatula nthawi yoyang’ana zacilengedwe. Tionenso mmene Yehova na Yesu anaseŵenzetsela zacilengedwe pophunzitsa, na zimene tingacite kuti tiphunzile zambili ku zacilengedwe.

N’CIFUKWA CIYANI TIYENELA KUYANG’ANITSITSA ZACILENGEDWE?

Yehova anali kufuna kuti Adamu azisangalala naco cilengedwe cake, komanso kuti apatse maina nyama (Onani ndime 3)

3. Cikuonetsa n’ciyani kuti Yehova anafuna kuti Adamu azisangalala nazo zacilengedwe?

3 Yehova anali kufuna kuti munthu woyamba azikondwela na zimene iye analenga. Mulungu atalenga Adamu, anam’patsa paradaiso wokongola kuti audziŵe bwino, kuusamalila, komanso kufutukula malile ake. (Gen. 2:8, 9, 15) Tangoganizilani cimwemwe cimene Adamu anali kukhala naco akaona mbewu zikumela, komanso maluŵa akuphukila. Ha! unali mwayi wapadela cotani nanga kwa Adamu kusamalila munda wa Edeni. Yehova anapatsanso Adamu nchito yopatsa nyama maina. (Gen. 2:19, 20) Yehova akanafuna, akanapatsa yekha nyama zonse maina. Koma anapeleka mwayi umenewo kwa Adamu. Mosakayikila, Adamu asanazipatse maina nyama, anali kuyang’anitsitsa mwacidwi makhalidwe na zocita za nyamazo. Iye ayenela kuti anakondwela nayo kwambili nchito imeneyi. Izi zinam’thandiza kuyamikila nzelu na luso la kulenga zinthu la Atate wake.

4. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kucita cidwi na zimene Mulungu analenga? (b) Ni zinthu ziti zacilengedwe zimene mumacita nazo cidwi kwambili?

4 Cifukwa cimodzi cimene tiyenela kucitila cidwi na zacilengedwe, n’cakuti n’zimene Yehova amafuna. Iye akutipempha kuti: “Kwezani maso anu kumwamba muone.” Kenako akutifunsa kuti: “Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?” Yankho n’lacidziŵikile. (Yes. 40:26) Yehova anadzaza kumwamba, dziko lapansi, komanso nyanja na zinthu zambili zopatsa cidwi, zimene zimatiphunzitsa za iye. (Sal. 104:24, 25) Ndipo tangoganizilani mmene Mulungu anatilengela. Anatilenga m’njila yakuti tizikopeka na zinthu zokongola zacilengedwe. Komanso, anapangitsa kuti tizikwanitsa kusangalala na zinthu zosiyanasiyana zimene iye analenga, potilenga m’njila yakuti tizitha kuona, kumva, kukhudza, kulaŵa, na kununkhiza.

5. Malinga na Aroma 1:20, kodi timapindula bwanji tikamaphunzila zinthu zimene Yehova analenga?

5 Baibo imatiuza cifukwa cina cofunika kwambili cimene tiyenela kucitila cidwi na zacilengedwe. Zinthu zacilengedwe zimatiphunzitsa makhalidwe a Yehova. (Ŵelengani Aroma 1:20.) Mwacitsanzo, ganizilani zinthu zimene Mulungu analenga, ndipo onani mmene anazilengela mopatsa cidwi. Kodi simukuonapo nzelu za Mulungu? Ndipo ganizilani za mitundu yolekana-lekana ya zakudya zimene timasangalala nazo. Umenewu ni umboni wosatsutsika wa cikondi cake kwa ife anthu. Tikamaona makhalidwe abwino a Yehova kudzela m’zinthu zimene analenga, timafika pom’dziŵa bwino kwambili, ndipo timalimbikitsidwa kumuyandikila. Lomba tiyeni tione mmene Yehova anagwilitsila nchito cilengedwe pophunzitsa anthu mfundo zofunika kwambili.

MULUNGU AMAGWILITSA NCHITO ZACILENGEDWE POTIPHUNZITSA ZA IYE

6. Kodi kuyang’ana mbalame zikusamuka kungatiphunzitse ciyani?

6 Yehova ali na nthawi imene amacitila zinthu. Caka ciliconse kumapeto kwa mwezi wa February na pakati pa mwezi wa May, Aisiraeli anali kuona adokowe akuuluka kusamukila cakumpoto. Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziŵa bwino nthawi yake yoikidwilatu.” (Yer. 8:7) Yehova anaikilatu nthawi pamene mbalamezi zimasamuka. Mofananamo, anaikilatu nthawi imene adzapeleke ciweluzo cake. Masiku ano tikamaona mbalamezi zikusamukila kwina, timakhulupililadi kuti Yehova ‘anaikilatu nthawi’ yakuti adzawononge dziko loipali.—Hab. 2:3.

7. Kodi kuyang’ana mbalame ikuuluka kungatitsimikizile za ciyani? (Yesaya 40:31)

7 Yehova amapeleka mphamvu kwa atumiki ake. Kudzela mwa Yesaya, Yehova analonjeza kuti adzalimbitsa atumiki ake akafooka kapena akalefuka. Ponena za iwo, Mulungu anati: “Adzaulukila m’mwamba ngati ali ndi mapiko a ciwombankhanga.” (Ŵelengani Yesaya 40:31.) Aisiraeli anali atazolowela kuona ziwombankhanga zikuulukila m’mwamba mosavuta, mothandizidwa na mpempho yocokela pansi kukwela m’mwamba. Izi zitikumbutsa kuti monga mmene Yehova amapelekela mphamvu kwa mbalamezi, angapelekenso mphamvu kwa atumiki ake. Conco, mukaona mbalame yaikulu ikuuluka mosavuta kupita m’mwamba kwambili, muzikumbukila kuti Yehova angakupatseni mphamvu zolimbana na mavuto anu.

8. Kodi Yobu anaphunzilapo ciyani pa nchito zodabwitsa za Mulungu? Nanga ife tiphunzilapo ciyani?

8 Yehova ni woyenela kumukhulupilila. Yehova anathandiza Yobu kuti akulitse cidalilo cake mwa iye. (Yobu 32:2; 40:6-8) Pamene Mulungu anali kukamba na Yobu anachula zinthu zambili zacilengedwe, monga nyenyezi, mitambo, komanso mphenzi. Yehova anakambanso za nyama monga ng’ombe yamphongo ya kuchile na hachi. (Yobu 38:32-35; 39:9, 19, 20) Zinthu zonsezi zinapeleka umboni wakuti Mulungu ali na mphamvu zazikulu, cikondi, na nzelu zakuya. Cifukwa ca makambilano amenewa, Yobu anayamba kum’khulupilila kwambili Yehova kuposa kale lonse. (Yobu 42:1-6) Mofananamo, tikamaphunzila zacilengedwe timakumbutsidwa kuti Yehova ali na nzelu zakuya komanso ni wamphamvu kupambana ife. Ndipo mosapeneka konse, iye adzathetsanso mavuto onse amene timakumana nawo. Mfundo imeneyi ingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye.

YESU ANAGWILITSA NCHITO ZACILENGEDWE POPHUNZITSA ZA ATATE WAKE

9-10. Kodi dzuŵa na mvula zimatiphunzitsa ciyani za Yehova?

9 Yesu anali kucidziŵa bwino kwambili cilengedwe. Monga “mmisili waluso,” anali na mwayi wothandizila Atate wake polenga zinthu zonse. (Miy. 8:30) Pambuyo pake, Yesu atabwela padziko lapansi, anagwilitsa nchito zacilengedwe pophunzitsa za Atate wake. Tiyeni tioneko zina mwa mfundo zimene anaphunzitsa.

10 Yehova amakonda anthu onse. Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anakamba za dzuŵa na mvula, zinthu zimene anthu ambili saziganizila kwenikweni. Koma zinthuzi n’zofunika kwambili kuti tikhalebe na moyo. Yehova akanafuna, akanapatsa zinthuzo anthu okhawo amene amam’tumikila. Koma iye mwacikondi amapeleka dzuŵa na mvula kwa anthu onse. (Mat. 5:43-45) Yesu anagwilitsa nchito mfundo imeneyi pophunzitsa ophunzila ake kuti, Yehova amafuna kuti tizionetsa cikondi kwa munthu aliyense. Nthawi zonse tikamaona kuloŵa kwa dzuŵa kokongola, na kamvula kowaza kotsitsimula, tizikumbukila cikondi ca Yehova copanda tsankho. Citsanzo cake cingatilimbikitse kuonetsa cikondi cofananaco mwa kulalikila kwa anthu onse.

11. Kodi tingalimbikitsidwe bwanji tikamaona mbalame?

11 Yehova amatipatsa zosoŵa zathu zakuthupi. Pa ulaliki wa pa phili umenewo, Yesu anatinso: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga cakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa.” N’kutheka kuti anthu amene Yesu anali kulankhula nawo anali kuona mbalame zikuuluka m’mwamba, pomwe anawafunsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mat. 6:26) Imeneyi ni njila yacikondi yotitsimikizila kuti Yehova adzatisamalila kuthupi. (Mat. 6:31, 32) Phunzilo locokela ku zacilengedwe limeneli likupitilizabe kulimbikitsa atumiki a Mulungu okhulupilika. Mpainiya wina wacitsikana ku Spain analefuka atalephela kupeza nyumba yabwino yokhalamo. Koma ataona mbalame zikudya mbewu na tuzipatso analimbikitsidwa. Iye anati: “Mbalamezo zinanikumbutsa kuti Yehova ndiye amazisamalila, komanso kuti inenso adzanisamalila.” Posakhalitsa, mlongoyo anapeza nyumba yabwinopo.

12. Malinga na Mateyu 10:29-31, kodi mpheta zimatiphunzitsanji za Yehova?

12 Yehova amaona munthu aliyense kukhala wofunika. Asanatumize atumwi ake kukalalikila, Yesu anawalimbikitsa kuti asamaope anthu otsutsa. (Ŵelengani Mateyu 10:29-31.) Anacita zimenezi powafotokozela za mpheta, mbalame zodziŵika kwambili ku Isiraeli. Mbalame zimenezi zinali zotsika mtengo m’nthawi ya Yesu. Koma iye anauza ophunzila ake kuti: “Palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziŵa.” Kenako anawonjezela kuti: “Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zoculuka.” Apa Yesu anatsimikizila ophunzila ake kuti Yehova amaona aliyense wa iwo kukhala wofunika kwambili. Conco, panalibe cifukwa coopela mazunzo. Mosayikila, ophunzilawo anali kukumbukila mawu a Yesu nthawi zonse akaona mpheta akamalalikila m’matauni na m’midzi. Inunso mukaona mbalame yaing’ono, muzikumbukila kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Ngakhale inu ‘ndinu wofunika kwambili kuposa mpheta zoculuka.’ Inde, iye adzakuthandizani kuti musamacite mantha anthu akamakutsutsani.—Sal. 118:6.

MMENE TINGAPHUNZILILE ZAMBILI ZOKHUDZA MULUNGU KU ZACILENGEDWE

13. Kodi tingacite ciyani kuti tiphunzile za Mulungu ku zacilengedwe?

13 Tingaphunzile zambili za Yehova ku zacilengedwe. Motani? Coyamba, tizipatula nthawi yoyang’anitsitsa zacilengedwe. Cotsatila, tizisinkhasinkha zimene tiphunzilapo ponena za Yehova. Nthawi zina, cingakhale covuta kucita zimenezi. Géraldine, mlongo wa ku Cameroon anati: “Popeza n’nakulila m’tauni, n’nazindikila kuti niyenela kucita khama kuti niziyang’anitsitsa zacilengedwe.” M’bale Alfonso, amene ni mkulu mumpingo, nayenso anati: “Naphunzila kuti niyenela kupatula nthawi yoyang’anitsitsa zimene Yehova analenga, komanso kusinkhasinkha zimene zinthuzo zimaniphunzitsa za iye.”

Davide amati akayang’ana zacilengedwe, anali kusinkhasinkha zimene akuphunzilapo za Yehova (Onani ndime 14)

14. Kodi Davide anadziŵa ciyani atasinkhasinkha zimene Mulungu analenga?

14 Davide anali kuganizila mozama zimene Mulungu analenga. Iye anauza Yehova kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, nchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: munthu ndani kuti muzimuganizila?” (Sal. 8:3, 4) Inde, Davide amati akayang’ana kumwamba usiku, anali kuyamikila ulemelelo wa cilengedwe ca Mulungu. Koma anacita zoposa pamenepo. Anali kusinkhasinkha za nyenyezi kuti aphunzile za Mulungu. Iye anadziŵa ukulu wa Yehova. Nthawi zina, Davide anali kusinkhasinkha mmene thupi lake linapangidwila m’mimba mwa amayi ake. Akamasinkhasinkha zinthu zocititsa cidwi zimenezi, ciyamikilo cake pa nzelu za Yehova cinali kukulilako.—Sal. 139:14-17.

15. Kodi inu pacanu, ni zinthu ziti zacilengedwe zimene zakuphunzitsani makhalidwe a Yehova? (Salimo 148:7-10)

15 Mofanana na Davide, simufunikila kucita kupita kutali kuti mukapeze zinthu zacilengedwe zimene mungasinkhesinkhepo. Mukamayang’ana zacilengedwe zimene muli nazo pafupi, mudzadziŵa makhalidwe ambili a Yehova. Mwacitsanzo, mukamamva kuthuma kwa dzuŵa, muziganizila za mphamvu za Yehova. (Yer. 31:35) Muziganizilanso za nzelu za Mulungu mukamaona mbalame ikupanga cisa. Komanso, muziganizila khalidwe lacimwemwe la Yehova mukamaona mwana wagalu akuthamangitsa m’cila wake. Ndipo muziyamika Yehova kaamba ka cikondi cake nthawi zonse mukamaona mayi akuseŵela na mwana wake wakhanda. Tili na mipata yambili yophunzila za Yehova, cifukwa zonse zimene analenga kaya zazikulu, zazing’ono, kapena zili nafe pafupi, olo zakutali, zimam’tamanda.—Ŵelengani Salimo 148:7-10.

16. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani?

16 Mulungu wathu ni wanzelu zakuya, wacikondi, waluso, komanso wamphamvu. Makhalidwe amenewa na enanso ambili amaonekela m’zinthu zimene analenga. Conco, tiyeni nthawi zonse tizipatulako nthawi yosangalala nazo zacilengedwe, komanso tizisinkhasinkha zimene tiphunzilapo za Yehova. Mwakutelo, tidzamuyandikila kwambili Mlengi wathu. (Yak. 4:8) M’nkhani yotsatila, tidzakambilane mmene makolo angagwilitsile nchito zacilengedwe pothandiza ana awo kumuyandikila Yehova.

NYIMBO 5 Nchito Zodabwitsa za Mulungu

a Cilengedwe ca Yehova ni cocititsa cidwi kwambili. Kungoyambila pa zinthu zamphamvu monga dzuŵa mpaka ku zinthu zofewa monga maluŵa, nchito zake zonse timacita nazo cidwi. Cilengedwe cimatiphunzitsanso makhalidwe a Yehova. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tiyenela kupatula nthawi yoyang’ana zacilengedwe mwacidwi, komanso mmene kucita zimenezi kungatithandizile kumuyandikila Mulungu wathu.