Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 36

Nyamulani Zinthu Zofunika Ndipo Tayani Zina Zonse

Nyamulani Zinthu Zofunika Ndipo Tayani Zina Zonse

“Tiyeninso tivule cholemera chilichonse . . . , ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.”​—AHEB. 12:1.

NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Mogwirizana ndi Aheberi 12:1, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikafike kumapeto kwa mpikisano wokalandira moyo?

 BAIBULO limayerekezera moyo wa Akhristu ndi mpikisano wothamanga. Amene apambana amapatsidwa mphoto ya moyo wosatha. (2 Tim. 4:7, 8) Tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tipitirize kuthamanga chifukwa kuposa ndi kale lonse, panopa tili kumapeto kwa mpikisanowu. Mtumwi Paulo, yemwe anapambana pampikisano wokalandira moyo anafotokoza chomwe chingatithandize kuti tipambane. Iye anatiuza kuti “tivule cholemera chilichonse . . . ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.”​—Werengani Aheberi 12:1.

2. Kodi mawu akuti “tivule cholemera chilichonse” amatanthauza chiyani?

2 Pamene Paulo analemba kuti “tivule cholemera chilichonse,” kodi ankatanthauza kuti palibe chilichonse chimene Mkhristu ayenera kunyamula? Ayi, sankatanthauza zimenezo. M’malomwake ankatanthauza kuti tiyenera kutaya chilichonse chosafunika. Zinthu zimenezi zingatilepheretse kuthamanga bwino komanso kutichititsa kuti titope. Kuti tipirire, tiyenera kumazindikira komanso kutaya mwamsanga chilichonse chomwe chingachititse kuti tilemedwe. Koma pamene tikuchita zimenezo, sitiyenera kutaya zinthu zomwe timafunika kunyamula chifukwa ngati titatero tikhoza kukhala osayenera mpikisanowu. (2 Tim. 2:5) Ndiye kodi tiyenera kunyamula zinthu ziti?

3. (a) Mogwirizana ndi Agalatiya 6:5, kodi tiyenera kunyamula chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Werengani Agalatiya 6:5. Paulo anatchula chinthu china chimene tiyenera kunyamula. Iye analemba kuti “aliyense ayenera kunyamula katundu wake.” Apatu Paulo ankanena zinthu zimene Yehova amayembekezera kuti aliyense azichita monga mtumiki wake, zomwe munthu wina sangatichitire. Munkhaniyi tikambirana kuti “katundu wathu” akuphatikizapo zinthu ziti komanso mmene tingamunyamulire. Tionanso zinthu zina zosafunika zomwe n’kutheka kuti tanyamula komanso mmene tingazitayire. Kunyamula katundu wathu komanso kutaya zinthu zosafunika, kungatithandize kuti tipambane pampikisano wokalandira moyo.

KATUNDU YEMWE TIYENERA KUNYAMULA

Kunyamula katundu wathu kukuphatikizapo kuchita zinthu mogwirizana ndi lonjezo lathu lakuti tidzatumikira Yehova mpaka kalekale, kukwaniritsa udindo wathu m’banja ndiponso kuvomereza zotsatirapo za zimene timasankha (Onani ndime 4-9)

4. N’chifukwa chiyani tingati zimene tinalonjeza kuti tidzatumikira Yehova mpaka kalekale si zolemetsa? (Onaninso chithunzi.)

4 Lonjezo lakuti tidzatumikira Yehova mpaka kalekale. Pamene tinadzipereka kwa Yehova, tinalonjeza kuti tizidzamulambira komanso kuchita chifuniro chake. Tiyenera kumakwaniritsa lonjezo lathuli. Kuchita zinthu mogwirizana ndi zomwe tinalonjeza kuti tidzatumikira Yehova, ndi udindo waukulu. Koma si wolemetsa. Ndipotu Yehova anatilenga kuti tizichita chifuniro chake. (Chiv. 4:11) Iye anatilenga m’chifaniziro chake komanso ndi mtima woti tizifuna kumulambira. Zotsatira zake n’zakuti timakhala naye pa ubwenzi komanso timasangalala kuchita chifuniro chake. (Sal. 40:8) Koposa zonse, tikamachita chifuniro cha Mulungu komanso kutsanzira Mwana wake, ‘timatsitsimulidwa.’​—Mat. 11:28-30.

(Onani ndime 4-5)

5. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa lonjezo lanu lakuti mudzatumikira Yehova mpaka kalekale? (1 Yohane 5:3)

5 Kodi munganyamule bwanji katunduyu? Pali zinthu ziwiri zomwe zingakuthandizeni. Choyamba, pitirizani kuyesetsa kuti muzikonda kwambiri Yehova. Mungachite zimenezo poganizira zabwino zimene wakhala akukuchitirani komanso madalitso omwe adzakupatseni m’tsogolo. Mukamakonda kwambiri Mulungu, m’pamenenso zimakhala zosavuta kuti muzimumvera. (Werengani 1 Yohane 5:3.) Chachiwiri, muzitsanzira Yesu. Iye anakwanitsa kuchita chifuniro cha Mulungu chifukwa ankapempha Yehova kuti amuthandize komanso ankaganizira kwambiri madalitso omwe adzapeze m’tsogolo. (Aheb. 5:7; 12:2) Mofanana ndi Yesu, muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu ndipo nthawi zonse muziganizira chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Pamene mukukonda kwambiri Mulungu komanso kutsanzira Mwana wake, mudzatha kukwaniritsa lonjezo lanu lakuti mudzamutumikira mpaka kalekale.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kumakwaniritsa maudindo athu m’banja? (Onaninso chithunzi.)

6 Maudindo athu m’banja. Pampikisano wathu wokalandira moyo, tiyenera kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu kuposa mmene timakondera achibale athu. (Mat. 10:37) Komabe zimenezi sizitanthauza kuti tizinyalanyaza maudindo athu m’banja ngati kuti ndi amene akutichititsa kuti tisamasangalatse Mulungu ndi Khristu. M’malomwake, kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu ndi Khristu, tiyenera kukwaniritsa udindo wathu m’banja. (1 Tim. 5:4, 8) Tikamachita zimenezi tidzakhala osangalala. Ndipotu Yehova anakonza zoti banja lizikhala losangalala ngati mwamuna ndi mkazi wake amakondana komanso kulemekezana, ngati makolo amakonda ana awo komanso kuwaphunzitsa ndiponso ngati ana amamvera makolo awo.​—Aef. 5:33; 6:1, 4.

(Onani ndime 6-7)

7. Kodi mungakwaniritse bwanji udindo wanu m’banja?

7 Kodi munganyamule bwanji katunduyu? Kaya udindo wanu ndi wotani m’banja, muzidalira nzeru zopezeka m’Baibulo m’malo mochita zinthu pongotengera mmene mukumvera, chikhalidwe kapena zimene anthu omwe amati ndi akatswiri amanena. (Miy. 24:3, 4) Muzigwiritsanso ntchito bwino mabuku athu. Mabukuwa amafotokoza zomwe mungachite kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, munkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” muli mfundo zomwe zingathandize mabanja, makolo komanso ana pamavuto omwe amakumana nawo masiku ano. b Muzikhala otsimikiza kutsatira mfundo za m’Baibulo, ngakhale pamene anthu ena m’banja lanu sakuzitsatira. Zimenezi zidzathandiza banjalo ndiponso Yehova adzakudalitsani.​—1 Pet. 3:1, 2.

8. Kodi zosankha zathu zingatikhudze bwanji?

8 Kukumana ndi zotsatira za zosankha zathu. Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita, ndipo amafuna tizisangalala ndi zotsatirapo zabwino zobwera chifukwa chosankha zinthu moyenera. Koma sikuti amatiteteza ku mavuto obwera chifukwa chakuti sitinasankhe bwino. (Agal. 6:7, 8) Choncho timavomereza zinthu zomwe timakumana nazo chifukwa chakuti sitinasankhe moyenera, talankhula mosaganiza bwino komanso tachita zinthu mwaphuma. Potengera zimene tachita, chikumbumtima chathu chikhoza kumativutitsa. Komabe kudziwa kuti timafunika kukumana ndi zotsatira za zimene tasankha, kungatilimbikitse kuti tiulule machimo athu, tikonze zimene talakwitsazo komanso tisadzazibwerezenso. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tipitirize kuthamanga pampikisano wokalandira moyo.

(Onani ndime 8-9)

9. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni ngati munasankha zinthu molakwika? (Onaninso chithunzi.)

9 Kodi munganyamule bwanji katunduyu? Ngati simungathe kusintha zomwe munasankha molakwika, muzivomereza mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa. Dziwani kuti simungasinthe zimene zinachitika m’mbuyo. Musamataye nthawi ndi mphamvu zanu poyesa kudzilungamitsa, kudziimba mlandu kapenanso kumaimba ena mlandu pa zomwe simunasankhe bwino. M’malomwake, muzivomereza zimene munalakwitsa n’kumayesetsa kuchita zimene mungathe kuti zinthu zikhale bwino panopa. Ngati mukudziimba mlandu chifukwa cha zimene munalakwitsa, modzichepetsa muzipemphera kwa Yehova, kuvomereza zimene munalakwitsazo komanso kupempha kuti akukhululukireni. (Sal. 25:11; 51:3, 4) Muzipepesa kwa amene munawalakwira. Muzipemphanso kuti akulu akuthandizeni ngati pakufunika kutero. (Yak. 5:14, 15) Muziphunzira pa zimene munalakwitsa ndipo muziyesetsa kuti musazibwerezenso. Mukamachita zimenezi, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakuchitirani chifundo komanso adzakuthandizani.​—Sal. 103:8-13.

ZOLEMERA ZOMWE TIYENERA KUTAYA

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuyembekezera zinthu zomwe n’zosatheka ndi katundu wolemetsa? (Agalatiya 6:4)

10 Kuyembekezera zinthu zosatheka. Tikamayembekezera zosatheka, podziyerekezera ndi ena tikhoza kudzilemetsa. (Werengani Agalatiya 6:4.) Ngati nthawi zonse timadziyerekezera ndi ena, tikhoza kuyamba mtima wansanje komanso wampikisano. (Agal. 5:26) Poyesetsa kuti tikwanitse zomwe ena achita, tikhoza kumadzikakamiza kuti tichite zimene sitingathe potengera luso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Komanso “chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.” Ndiye tingamve bwanji ngati titamafuna kuchita zinthu zomwe sitingazikwanitse n’komwe? (Miy. 13:12) Kuchita zimenezo kungatiwonongere mphamvu zathu komanso kungachititse kuti tizivutika kuthamanga pampikisano wokalandira moyo.​—Miy. 24:10.

11. N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamayembekezere zinthu zosatheka?

11 Kodi mungataye bwanji cholemera chimenechi? Musamayembekezere kuti muchita zoposa zimene Yehova amayembekezera kuti mungachite. Iye sayembekezera kuti muzimupatsa zimene mulibe. (2 Akor. 8:12) Dziwani kuti Yehova sayerekezera zomwe mumachita ndi zimene ena amachita. (Mat. 25:20-23) Zimene iye amaona kuti ndi zamtengo wapatali ndi zoti mumamutumikira ndi mtima wonse, ndinu wokhulupirika komanso ndinu wopirira. Modzichepetsa, muzivomereza kuti simungathe kuchita zinthu zina panopa chifukwa cha msinkhu wanu, thanzi lanu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Mofanana ndi Barizilai, muzikhala wokonzeka kukana mautumiki ena ngati thanzi lanu silili bwino. (2 Sam. 19:35, 36) Mofanana ndi Mose, muzivomera kuthandizidwa komanso muzipatsa ena zochita ngati pakufunikira kutero. (Eks. 18:21, 22) Kudzichepetsa kumeneku kungakuthandizeni kuti musamakonze zochita zinthu zosatheka, zomwe zikhoza kungokutopetsani pampikisano wokalandira moyo.

12. Kodi vuto limakhala ifeyo ena akasankha zinthu molakwika? Fotokozani.

12 Kudziimba mlandu chifukwa chakuti ena sanasankhe bwino. Sitingasankhire ena zochita komanso si nthawi zonse pamene tingawateteze kuti asakumane ndi mavuto obwera chifukwa chosankha zinthu molakwika. Mwachitsanzo, mwana angasankhe kusiya kutumikira Yehova. Zimenezi zingachititse kuti makolo ake amve chisoni kwambiri. Komabe makolo akamadziimba mlandu chifukwa chakuti mwana wawo wasankha zinthu molakwika, amakhala akunyamula katundu wolemera. Ameneyu si katundu amene Yehova amafuna kuti iwo anyamule.​—Aroma 14:12.

13. Kodi makolo angatani ngati mwana wawo sanasankhe zinthu moyenera?

13 Kodi mungataye bwanji cholemera chimenechi? Muzikumbukira kuti Yehova anapatsa tonsefe ufulu wosankha ndipo amalola kuti aliyense azisankha yekha zochita. Zimenezi zikuphatikizapo kusankha kumutumikira kapena ayi. Yehova amadziwa kuti si inu kholo langwiro ndipo amangofuna kuti muzichita zonse zomwe mungathe. Ndi udindo wa mwana wanuyo kusankha zochita, osati inuyo. Koma mwina mukhoza kumadandaula pa zimene munalakwitsa monga kholo. Ngati ndi choncho, muziuza Yehova mmene mukumvera ndipo muzimupempha kuti akukhululukireni. Iye amadziwa kuti simungathe kusintha zomwe zinachitikazo. Pa nthawi imodzimodziyo, sayembekezera kuti muteteze mwana wanuyo kuti asakolole zimene anafesa. Muzikumbukira kuti ngati mwana wanuyo atayesetsa kuti abwerere kwa Yehova, iye adzamulandira mofunitsitsa.​—Luka 15:18-20.

14. N’chifukwa chiyani kudziimba mlandu kwambiri ndi katundu yemwe tiyenera kutaya?

14 Kudziimba mlandu kwambiri. N’zomveka kuti tikachimwa timadziimba mlandu. Komabe kudziimba mlandu kwambiri si katundu yemwe Yehova amafuna kuti tinyamule. Kudziimba mlandu ndi cholemera chimene tiyenera kutaya. Koma kodi tingadziwe bwanji ngati tikudziimba mlandu kwambiri? Ngati taulula tchimo lathu, kulapa komanso kuchita zonse zofunika kuti tisalibwerezenso, tingakhale otsimikiza kuti Yehova watikhululukira. (Mac. 3:19) Tikachita zimenezi, Yehova samafuna kuti tizipitiriza kudziimba mlandu. Iye amadziwa kuti kumangokhalira kudziimba mlandu n’koopsa. (Sal. 31:10) Ngati titakhala ndi chisoni chopitirira malire, tikhoza kusiya kuthamanga pampikisano wokalandira moyo.​—2 Akor. 2:7.

Pambuyo poti mwalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sapitiriza kuganizira machimo anu, ndipo inunso simuyenera kutero (Onani ndime 15)

15. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musamadziimbe mlandu kwambiri? (1 Yohane 3:19, 20) (Onaninso chithunzi.)

15 Kodi mungataye bwanji cholemera chimenechi? Mukamadziimba mlandu kwambiri, muziganizira mfundo yakuti Mulungu ‘amakhululukiradi.’ (Sal. 130:4) Iye akakhululukira amene alapa mochokera pansi pa mtima amalonjeza kuti: “Machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sangadzakuimbeninso mlandu chifukwa cha machimo omwe munachita m’mbuyomu. Choncho musamaganize kuti mavuto omwe mukukumana nawo chifukwa chakuti munachimwa, ndi umboni wakuti sanakukhululukireni. Ndipo musamadzikwiyire kapena kudzilanga chifukwa chakuti zimene munalakwitsa m’mbuyo mwina zikuchititsa kuti musamachite zambiri potumikira Yehova panopa. Yehova samangokhalira kuganizira machimo anu, ndipo inunso simuyenera kutero.​—Werengani 1 Yohane 3:19, 20.

MUZITHAMANGA KUTI MUPAMBANE

16. Monga anthu omwe tili pampikisano wothamanga, kodi tiyenera kuzindikira chiyani?

16 Pamene tikuthamanga pampikisano wokalandira moyo, tiyenera ‘kuthamanga m’njira yoti tikalandire mphotoyo.’ (1 Akor. 9:24) Tingachite zimenezi ngati titazindikira katundu amene tiyenera kunyamula komanso zolemera zomwe tiyenera kutaya. Munkhaniyi, takambirana zitsanzo zochepa chabe za zinthu zomwe tiyenera kunyamula komanso zimene tiyenera kutaya. Koma pali zinanso zambiri. Yesu ananena kuti tikhoza ‘kulemedwa ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.’ (Luka 21:34) Zimenezi komanso malemba ena zingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene mungafunike kusintha pamene mukuthamanga pampikisano wokalandira moyo.

17. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti tidzapambana pampikisano wokalandira moyo?

17 Tingakhale otsimikiza kuti tidzapambana mpikisano wokalandira moyo, chifukwa Yehova adzatipatsa mphamvu zimene tikufunikira. (Yes. 40:29-31) Choncho musachepetse liwiro lanu. Muzitsanzira mtumwi Paulo, yemwe anathamanga mwakhama kuti akapeze mphoto yomwe anamuikira patsogolo pake. (Afil. 3:13, 14) Palibe yemwe angakuthamangireni mpikisanowu, komabe Yehova angakuthandizeni kuti mupambane. Iye angakuthandizeninso kunyamula katundu wanu komanso kutaya zolemera zosafunika. (Sal. 68:19) Popeza Yehova ali kumbali yanu, mungakwanitse kuthamanga mopirira komanso kupambana.

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

a Nkhaniyi itithandiza kuti tikwanitse kuthamanga mpikisano wokalandira moyo. Monga anthu amene tikuthamanga nawo, pali zinthu zina zimene tiyenera kunyamula. Izi zikuphatikizapo zomwe tinalonjeza kuti tidzatumikira Yehova, udindo wathu m’banja komanso kukumana ndi zotsatirapo za zimene tasankha. Komabe tiyenera kutaya cholemera chilichonse chomwe chingatilepheretse kuti tizithamanga bwino. Kodi zimenezi zikuphatikizapo chiyani? Munkhaniyi tipeza yankho la funso limeneli.

b Mungapeze nkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” pa jw.org. Nkhani zina zimene zingathandize mwamuna ndi mkazi wake zomwe zilipo ndi zakuti: “Kodi Mungasonyezane Bwanji Ulemu?” komanso “Kodi Mungasonyeze Bwanji kuti Mumayamikira Zimene Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amachita?” Zomwe zingathandize makolo: “Phunzitsani Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Foni Mosamala” komanso “Zimene Mungachite Kuti Muzimasukirana ndi Mwana Wanu.” Zimene zingathandize achinyamata: “Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?” komanso “Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye?