Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1923​—Zaka 100 Zapitazo

1923​—Zaka 100 Zapitazo

NSANJA ya Mlonda ya January 1, 1923 inati: “Zioneka kuti caka ca 1923 cidzakhala cosangalatsa kwa anthu a Mulungu. Ni mwayi waukulu kulengeza kwa anthu opendelezedwa m’dzikoli, kuti posacedwapa zinthu zidzakhala bwino. Caka cimeneci ophunzila Baibo adzalimbikitsidwa kuona kuti nchito yawo yolalikila komanso kulambila kwawo zikulimbikitsa mgwilizano, umene ni cizindikilo ca kulambila koona masiku ano.”

KULAMBILA KUNALIMBIKITSA MGWILIZANO

Kalenda yokhala na m’ndandanda wa malemba na ma nambala a nyimbo

M’caka cimeneci gulu lathu linapanga masinthidwe amene anathandiza Ophunzila Baibo kukhala ogwilizana pa kulambila kwawo. Mu Nsanja ya Mlonda munayamba kupezeka mbali ina imene inali kufotokoza lemba imene anali kukambilana mlungu uliwonse pa Msonkhano wawo wa Kupemphela, Kutamanda, na Kufotokoza Zokumana Nazo. Kuwonjezela apo, Ophunzila Baibo anapanga kalenda imene inali na m’ndandanda wa malemba a mlungu wonse, komanso nyimbo zoimba pa phunzilo la munthu mwina na pa kulambila kwa pa banja.

Pa misonkhano imeneyi, Ophunzila Baibo anali kufotokoza “zokumana nazo” zimene ziphatikizapo za mu utumiki, zifukwa zoyamikila Yehova, nyimbo, kapena pemphelo. Mlongo Eva Barney amene anabatizika mu 1923 ali na zaka 15, anafotokoza zimene zinali kucitika pa nthawiyo kuti: “Ngati munthu afuna kufotokoza cokumana naco, anali kuima na kunena mawu ngati ‘nifuna kuyamikila Ambuye, cifukwa ca zabwino zimene anicitila.’” Abale ena anali kukonda kufotokoza zokumana nazo. Mlongo Barney anapitiliza kuti: “M’bale wina wacikulile dzina lake Godwin anali na zifukwa zambili zoyamikila ambuye. Koma akazi awo akaona kuti wotsogoza watopa kuyembekeza kuti iwo atsilize kufotokoza, anali kuwakoka covala, ndiyeno iwo anali kuleka kulankhula na kukhala pansi.”

Kamodzi pa mwezi, mpingo uliwonse unali kukhala na msonkhano wapadela wa Kupemphela, Kutamanda, na Kufotokoza Zokumana Nazo. Pofotokoza za msonkhanowu, Nsanja ya Mlonda ya April 1, 1923 inati: “Theka la msonkhanowu, liyenela kukhala lofotokoza zokumana nazo polalikila, na kulimbikitsa ofalitsa. . . . Ndife otsimikiza kuti misonkhano imeneyi, idzalimbikitsa mgwilizano pakati pathu.”

M’bale Charles Martin wofalitsa wa zaka 19 wa mu mzinda wa Vancouver ku Canada anapindula kwambili na misonkhano imeneyi. Pokumbukila zimene zinali kucitika pa misonkhanoyi, iye anati: “Pa misonkhano imeneyi, m’pamene n’naphunzila zimene ningakambe pocita ulaliki wa khomo na khomo. Nthawi zambili, wina anali kufotokoza zimene anakumana nazo pocita ulaliki wa khomo na khomo. Izi zinanithandiza kudziŵa zimene ninganene, kapena kuyankha nikakumana na otsutsa.”

NCHITO YOLALIKILA INALIMBIKITSA MGWILIZANO

Bulletin ya May 1, 1923

“Masiku a utumiki” anathandizanso kuti gulu lathu likhale logwilizana. Mu Nsanja ya Mlonda ya April 1 1923, munali cilengezo cakuti: “Kuti tiziseŵenza mogwilizana pa nchito yathu, pa Ciŵili May 1, 1923, idzakhala tsiku la utumiki kwa tonsefe. Ndiyeno zidzikhalabe conco pa Ciŵili coyamba ca mwezi uliwonse. Conco, wofalitsa aliyense m’mipingo yonse, akulimbikitsidwa kuti ayenela kutengamo mbali.”

Ngakhale Ophunzila Baibo acicepele anali kugwila nawo nchito imeneyi. Hazel Burford, yemwe anali na zaka 16 pa nthawiyi anati: “Mu Bulletin munali kupezeka makambilano (omwe timati maulaliki acitsanzo masiku ano) amene tinali kuloŵeza pa mtima. a Ine na Agogo tinali kutengamo mbali mokwanila mu nchito imeneyi.” Komabe, mlongo Burford anakumana na citsutso kucokela kumene sanali kuyembekezela. Iye anati: “M’bale wina wacikulile, sanagwilizane nazo zakuti nizilalikila kwa anthu ena. Pa nthawi imeneyo, ena sanamvetse kuti Ophunzila Baibo onse, kuphatikizapo ‘anyamata na atsikana’ ayenela kutengako mbali pa nchito yotamanda Mlengi wathu wamkulu.” (Sal. 148:​12, 13) Ngakhale n’telo, mlongo Burford anapitilizabe kulalikila, mpaka analoŵa Sukulu ya Giliyadi, na kukhala mmishonale ku Panama. M’kupita kwa nthawi, abalewo anamvetsa kuti acicepele nawonso ayenela kutengamo mbali mu nchito yolalikila.

MISONKHANO IKULU-IKULU INALIMBITSA MGWILIZANO

Nayonso misonkhano yadela komanso yacigawo, inathandiza kuti abale akhale ogwilizana. Yambili mwa misonkhano imeneyi, inali kukhala na masiku a ulaliki. Citsanzo cimodzi ni msonkhano umene unacitikila mu mzinda wa Winnipeg ku Canada. Pa March 31 msonkhano Wacigawo, unali na “Kampeni Yapadela Yolalikila mu Mzinda wa Winnipeg.” Ndipo osonkhana onse analimbikitsidwa kuti atengemo mbali. Masiku a ulaliki amenewa, anathandiza kuti gulu lathu liziwonjezeka. Pa August 5 anthu pafupi-fupi 7,000 anapezekapo pa msonkhano wina ku Winnipeg. Pa nthawi imeneyo, ici ndiye cinali ciŵelengelo cacikulu ca opezeka pa misonkhano yonse ku Canada.

Msonkhano wofunika kwambili kwa anthu a Mulungu mu 1923, unacitika kuyambila pa August 18-26, mu mzinda wa Los Angeles ku California. Kutatsala milungu yocepa kuti msonkhanowo ucitike, m’manyuzipepala anaikamo ciitanilo ca msonkhanowu ndipo Ophunzila Baibo anagaŵila makope oposa 500,000 a tumapepala twaciitanilo. Mapepalawo anamatidwanso ngakhale pa magalimoto.   

Msonkhano wa Cigawo wa Ophunzila Baibo mu 1923 ku Los Angeles

Pa Ciŵelu August 25, M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Nkhosa na Mbuzi,”mmene anafotokoza momveka bwino kuti “nkhosa” ni anthu olungama amene adzakhala m’paradaiso pa dziko la pansi. Iye anaŵelenganso kalata, ya mutu wakuti: “Cenjezo.” Kalata imeneyo, inatsutsa zakuti zipembedzo zonse ziyenela kucitila zinthu pamodzi, ndipo inalimbikitsa anthu oona mtima kuti atulukemo mu “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 18:​2, 4) Pambuyo pake, Ophunzila Baibo akhama kuzungulila dziko lonse la pansi, anaseŵenzela pamodzi kuti agaŵile makope ofika m’mamiliyoni a tumathilakiti tokhala na kalata imeneyi.

“Zocitika zimenezi, zidzalimbikitsa mgwilizano pakati pathu”

Patsiku lothela la msonkhanowo, anthu oposa 30,000 anamvetsela nkhani ya M’bale Rutherford ya mutu wakuti, “Mitundu Yonse ya Anthu Ikupita ku Aramagedo, Koma Anthu Mamiliyoni Amene Ali na Moyo Sadzafa.” Popeza anali kuyembekezela anthu ambili, Ophunzila Baibo anacita lendi sitediyamu imene inali itangomangidwa kumene mu mzinda wa Los Angeles. Pofuna kuonetsetsa kuti onse apindule, abale anagwilitsa nchito ma sipika aakulu a sitediyamuyo, amene anali amakono pa nthawiyo. Anthu ena ambili anamvetsela msonkhanowu pa wailesi.

KUWONJEZEKA KWA CIŴELENGELO PA DZIKO LONSE

M’caka ca 1923, nchito yolengeza uthenga wabwino inapita patsogolo kwambili ku Africa, Europe, India, na South America. Ku India, m’bale A J Joseph anali kuyang’anila nchito yopulinta mabuku m’Cihindi, Citamil, Citelugu na Ciurdu. Pa nthawi imodzi-modziyo, anali kusamalilanso mkazi wake na ana ake 6.

M’bale William R. Brown na banja lake

Alfred Joseph na Leonard Blackman omwe anali Ophunzila Baibo ku Sierra Leone, analemba kalata yopempha thandizo ku likulu lathu ku Brooklyn, New York. Pa April 14, 1923, pempho lawo linayankhidwa. M’bale Alfred anati, “Pa Ciŵelu m’madzulo, n’nalandila foni imene sin’nali kuyembekezela.” Iye anamva munthu wa mawu aakulu akum’funsa kuti, “kodi ndinu munalemba kalata ku Watch Tower Society yopempha thandizo la olalikila?” Alfred anayankha kuti, “Inde,” ndiyeno munthuyo anati, “Cabwino atumiza ine.” Munthuyo anali m’bale William R Brown amene anali atangofika kumene kucokela ku Caribbean na mkazi wake Antonia pamodzi na ana awo aakazi aŵili, Louise na Lucy. Abale anali ofunitsitsa kuonana na m’bale Brown komanso banja lake.

M’bale Alfred anapitiliza kunena kuti: “Tsiku lotsatila m’maŵa ine na m’bale Leonard tikucita phunzilo la Baibo la mlungu uliwonse, tinangoona munthu wamtali pa khomo. Anali M’bale Brown. Iye anali wacangu pa coonadi, moti anali wofunitsitsa kupeleka nkhani tsiku lotsatila.” Asanathe ngakhale mwezi umodzi, anagaŵila zofalitsa zonse zimene anabwela nazo. Conco analandila makope a mabuku 5,000, koma posakhalitsa panafunikilanso ena. Koma sanali kudziŵika monga wogulitsa mabuku. Pa umoyo wake wonse, monga mtumiki wacangu wa Yehova, m’baleyu anali kuseŵenzetsa kwambili malemba m’nkhani zake. Conco, anali kudziŵika na dzina lakuti Baibo Brown.

Beteli ya ku Magdeburg ca m’ma 1920

Abale anaganiza zosamutsa ofesi ya nthambi kuicotsa mu mzinda wa Barmen ku Germany, cifukwa malowo anali aang’ono. Komanso cifukwa cakuti panali mphekesela zakuti dziko la France lifuna kulanda mzindawo. Ophunzila Baibo anapeza malo amene anali na nyumba yoyenela kugwililamo nchito yosindikiza mabuku mu mzinda wa Magdeburg. Conco, pa June 19 abale anamaliza kulongeza makina opulintila komanso katundu wina na kusamukila ku Beteli yatsopano mu mzinda wa Magdeburg. Tsiku limenelo, atangodziŵitsa likulu lathu kuti nchito yosamuka yatha, mu nyuzipepala munapelekedwa cilengezo cakuti dziko la France yalanda mzinda wa Barmen. Cocitika cimeneci, cinatsimikizila abale za dalitso na citetezo ca Yehova.

George Young na Sarah Ferguson, komanso mlongo wake

Ku Brazil, m’bale George Young amene anayenda maulendo atali-atali kulengeza uthenga wabwino, anakhadzikitsa nthambi yatsopano na kuyamba kutsindikidza magazini a Nsanja ya Mlonda mu Ciportuguese. M’miyezi yocepa cabe, anagaŵila zofalitsa zoposa 7,000. Kufika kwa m’baleyu ku Brazil, kunapatsa Sarah Ferguson mwayi wapadela. Iye anali kuŵelenga magazini a Nsanja ya Mlonda kuyambila mu 1899, koma anali asanaonetse kudzipatulila kwake mwa kubatizika m’madzi. Patapita miyezi yocepa cabe, mlongo Ferguson komanso ana ake anayi anatenga sitepe yofunika imeneyi.

KUPEZA CIMWEMWE POTUMIKILA YEHOVA

Cakumapeto kwa cakaci, Nsanja ya Mlonda ya December 15, 1923 inafotokoza mmene masinthidwe amene anapanga polimbikitsa mgwilizano anakhudzila Ophunzila Baibo. Inati: “N’zoonekelatu kuti mipingo yonse ni yolimba mwauzimu . . . tiyeni tikhalebe okonzeka kugwila nchito zowonjezeleka na kupitiliza kupeza cimwemwe mu utumiki wathu.”

Caka cotsatila cinalinso caka cokondweletsa kwa Ophunzila Baibo. Abale a pa Beteli anali kugwila nchito ya cimango pa cilumba ca Staten cimene cinali pafupi na likulu lathu ku Brooklyn. Zimango zimenezo, zinamalizidwa kumayambililo kwa 1924. Ndipo zinathandiza kulimbikitsa mgwilizano pakati pa abale, komanso kufalitsa uthenga wabwino m’njila zimene sanali kuyembekezela.

Kagulu ka omanga pa cilumba ca Staten

a Kamene masiku ano timati—Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wacikhristu.