Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 44

Muzichita Khama Kuti Muzimvetsa Bwino Mawu a Mulungu

Muzichita Khama Kuti Muzimvetsa Bwino Mawu a Mulungu

‘Muzidziwa bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama.’—AEF. 3:18.

NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Kodi njira yabwino yowerengera komanso kuphunzirira Baibulo ndi iti? Perekani chitsanzo.

 TAYEREKEZERANI kuti mukufuna kugula nyumba. Kodi kungoona chithunzi chosonyeza kutsogolo kwa nyumbayo kungakhale kokwanira kuti muigule? Mosakayikira, mungafune kuti mupite kukaiona, kuizungulira, kulowa m’zipinda zake komanso kuona chilichonse chokhudza nyumbayo. Mwinanso mungafune kuona pulani ya nyumbayo kuti mudziwe mmene inamangidwira. N’zodziwikiratu kuti mungafune kudziwa kalikonse kokhudza nyumba yomwe mukufuna kugulayo.

2 Tingachitenso zofanana ndi zimenezi pamene tikuwerenga komanso kuphunzira Baibulo. Katswiri wina anayerekezera uthenga wa m’Baibulo ndi “nyumba yaikulu yomwe ili ndi zipilala zazitali komanso maziko olimba.” Ndiye tingatani kuti tidziwe bwino zonse zimene zili m’Baibulo? Ngati mutaliwerenga mofulumira, mukhoza kungodziwa “mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) Koma mofanana ndi zimene mungachite ndi nyumba ija, muyenera kulowa “mkati” kapena kuti kuliphunzira mosamala kuti mulimvetse. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo ndi kuona mmene mbali zosiyanasiyana za uthenga wake zilili zogwirizana. Muziyesetsa kuti mumvetse, osati mfundo za choonadi zomwe mumakhulupirira zokha, koma chifukwa chakenso mumazikhulupirira.

3. Kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Aefeso 3:​14-19)

3 Kuti tizimvetsa bwino Mawu a Mulungu, tiyenera kumaphunzira mosamala mfundo zozama za choonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti aziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama n’cholinga choti ‘adziwe bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi. Iwo akanachita zimenezi, ‘akanazika mizu ndi kukhala okhazikika’ m’chikhulupiriro chawo. (Werengani Aefeso 3:​14-19.) Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Tiyeni tione zimene tingachite kuti tiziphunzira Mawu a Mulungu mosamala kuti tiziwamvetsa bwino.

MUZIPHUNZIRA MOSAMALA MFUNDO ZOZAMA ZA CHOONADI

4. Kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova? Perekani zitsanzo.

4 Monga Akhristu, sitimangokhutira ndi kumvetsa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timafunitsitsanso kudziwa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:​9, 10) Bwanji osakonza zoti mufufuze mozama zinthu zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mwachitsanzo, mungafufuze mmene anasonyezera kuti ankakonda atumiki ake akale komanso mmene zimenezo zimasonyezera kuti inunso amakukondani. Mungaphunzirenso zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azichita pomulambira n’kuziyerekezera ndi zimene amafuna kuti ifenso tizichita pomulambira masiku ano. Kapenanso mungaphunzire mozama zokhudza maulosi amene Yesu anakwaniritsa pa utumiki wake padziko lapansi.

5. Kodi ndi nkhani iti imene mukufuna kuifufuza mosamala pophunzira Baibulo panokha?

5 Anthu ena omwe amakonda kuphunzira Baibulo mwakhama anafunsidwa kuti afotokoze zinthu zozama zimene angafune kuti azifufuze m’Mawu a Mulungu. Zimene ena anayankha zili mubokosi lakuti “ Nkhani Zoti Ndifufuze Ndikamaphunzira Pandekha.” Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lingakuthandizeni kuti muzisangalala pophunzira nkhani ngati zimenezi. Kuphunzira Baibulo mozama kungalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kungakuthandizeni kuti ‘mumudziwedi Mulungu.’ (Miy. 2:​4, 5) Tsopano tiyeni tione mfundo zina zozama za choonadi zomwe tingafufuze.

MUZIGANIZIRA KWAMBIRI CHOLINGA CHA MULUNGU

6. (a) Kodi pulani imasiyana bwanji ndi cholinga? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti cholinga cha Yehova chokhudza anthu komanso dzikoli ndi “chamuyaya”? (Aefeso 3:11)

6 Tsopano tiyeni tikambirane zomwe Baibulo limanena zokhudza cholinga cha Mulungu. Kukhala ndi pulani n’kosiyana kwambiri ndi kukhala ndi cholinga. Kukhala ndi pulani tingakuyerekezere ndi kusankha msewu woti mudutse popita kwinakwake. Koma pulani ikhoza kulephereka ngati msewu watsekedwa. Pomwe cholinga tingachiyerekezere ndi malo omwe mukufuna kupita. Tikhoza kudziwa malo enieni omwe tikupita koma sitisankhiratu msewu woti tidutse. Ngati msewu wina watsekedwa tikhoza kudutsa msewu wina. Timayamikira kwambiri kuti mwapang’onopang’ono, Yehova wakhala akuulula za “cholinga [chake] chamuyaya” m’Baibulo. (Aef. 3:11) Yehova angagwiritse ntchito njira zosiyanasiyana pofuna kukwaniritsa cholinga chake ndipo nthawi zonse amapangitsa kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. (Miy. 16:4) Komanso zotsatira za zimene amachita zimakhalapo mpaka kalekale. Kodi cholinga cha Yehova n’chiyani, nanga wasintha zinthu ziti kuti achikwaniritse?

7. Anthu oyambirira atachimwa, kodi Yehova anasintha bwanji njira yokwaniritsira cholinga chake? (Mateyu 25:34)

7 Mulungu anauza anthu oyambirira za cholinga chomwe anali nacho. Iye ankafuna kuti iwo ‘aberekane, achuluke, adzaze dziko lapansi, ndipo aliyang’anire, ayang’anirenso . . . cholengedwa chilichonse . . . padziko lapansi.’ (Gen. 1:28) Adamu ndi Hava atachimwira Yehova komanso kuchititsa anthu onse kuti akhale ochimwa, cholinga chake sichinalephereke. Anangosintha njira yokwaniritsira cholingacho. Nthawi yomweyo, iye anakhazikitsa Ufumu kumwamba kuti ukwaniritse cholinga chake chokhudza dzikoli komanso anthu. (Werengani Mateyu 25:34.) Pa nthawi yake, Yehova anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa padzikoli kuti adzaphunzitse anthu zokhudza Ufumuwu komanso kudzapereka moyo wake monga dipo kuti atiwombole ku uchimo ndi imfa. Kenako Yesu anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba kuti akakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Komabe pali zambiri zofunika kuphunzira zokhudza cholinga cha Mulungu.

Ganizirani mmene zidzakhalire onse kumwamba ndi padziko lapansi akadzakhala ogwirizana komanso okhulupirika kwa Yehova (Onani ndime 8)

8. (a) Kodi nkhani yaikulu ya m’Baibulo ndi yotani? (b) Mogwirizana ndi Aefeso 1:​8-11, kodi cholinga chachikulu cha Yehova n’chiyani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

8 Nkhani yaikulu m’Baibulo ndi yakuti dzina la Yehova lidzayeretsedwa akamadzakwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi pogwiritsa ntchito Ufumu wolamulidwa ndi Khristu. Cholinga cha Yehova sichingasinthidwe. Iye adzakwaniritsa chilichonse chomwe walonjeza ndipo sizidzalephereka. (Yes. 46:​10, 11; Aheb. 6:​17, 18) Kenako dzikoli lidzasinthidwa kukhala Paradaiso ndipo ana a Adamu ndi Hava angwiro komanso olungama ‘adzakhala ndi moyo kosatha m’dzikolo.’ (Sal. 22:26) Kuwonjezera pamenepo, pali zinthu zinanso zimene Yehova akufuna kuchita. Cholinga chake chachikulu ndi chakuti onse kumwamba ndi padziko lapansi akhale ogwirizana. Ndipo onse omwe adzakhale ndi moyo azidzagonjera Mulungu monga Wolamulira wawo. (Werengani Aefeso 1:​8-11.) Kunena zoona, Yehova akukwaniritsa cholinga chake m’njira yochititsa chidwi.

MUZIGANIZIRA KWAMBIRI ZA TSOGOLO LANU

9. Kodi kuwerenga Baibulo kungatithandize kudziwa zinthu ziti zam’tsogolo?

9 Taganizirani ulosi wa pa Genesis 3:15 womwe Yehova anaufotokoza m’munda wa Edeni. b Ulosiwo unkanena za zinthu zomwe zidzakwaniritse cholinga chake koma patapita zaka masauzande angapo. Izi zinkaphatikizapo kubadwa kwa ana a Abulahamu omwe anadzakhala mzera wobadwira wa Khristu. (Gen. 22:​15-18) Ndiyeno mogwirizana ndi ulosiwo, Yesu anavulazidwa chidendene mu 33 C.E. (Mac. 3:​13-15) Ndipo mbali yomalizira ya ulosiwu, yomwe ndi kuphwanya mutu wa Satana, idzachitika zaka zoposa 1,000 kutsogoloku. (Chiv. 20:​7-10) Ndipo Baibulo limafotokoza zambiri zomwe zidzachitike udani wa pakati pa dziko la Satanali ndi gulu la Yehova ukadzafika pachimake.

10. (a) Kodi ndi zinthu ziti zomwe zichitike posachedwapa? (b) Kodi tingakonzekeretse bwanji maganizo ndi mtima wathu? (Onani mawu a m’munsi.)

10 Taganizirani zinthu zina zapadera izi zomwe Baibulo linaneneratu. Choyamba, mayiko adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:​2, 3) “Nthawi yomweyo” chisautso chachikulu chidzayamba pomwe mayiko adzaukire zipembedzo zonse zabodza. (Chiv. 17:16) Kenako pambuyo pake padzaoneka zinthu zodabwitsa pamene “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mat. 24:30) Yesu adzaweruza anthu onse ndipo adzalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:​31-33, 46) Koma sikuti Satana adzangokhala. Chifukwa chokwiya, iye adzalimbikitsa mgwirizano wa mayiko, womwe Baibulo limautchula kuti Gogi wa kudziko la Magogi, kuti aukire anthu a Yehova. (Ezek. 38:​2, 10, 11) Pa nthawi ina chisautso chachikulu chitayamba, odzozedwa omwe adzakhale ali padzikoli adzatengedwa kuti akakhale limodzi ndi Khristu ndi gulu lankhondo la kumwamba kuti adzamenye nkhondo ya Aramagedo, ndipo chimenechi chidzakhala chimake cha chisautso chachikulu. c (Mat. 24:31; Chiv. 16:​14, 16) Kenako Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu udzayamba kulamulira dzikoli.—Chiv. 20:6.

Kodi ubwenzi wanu ndi Yehova udzafika pati mukadzaphunzira za iye kwa zaka mabiliyoni? (Onani ndime 11))

11. Kodi chiyembekezo cha moyo wosatha chingakuthandizeni bwanji? (Onaninso chithunzi.)

11 Tsopano taganizirani zomwe zidzachitike pambuyo pa zaka 1,000 zimenezo. Baibulo limati Mlengi wathu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlal. 3:11) Kodi mfundo imeneyi imakukhudzani bwanji inuyo komanso ubwenzi wanu ndi Yehova? Patsamba 319 m’buku la Yandikirani kwa Yehova, pali mfundo yochititsa chidwi yakuti: “Pambuyo pokhala ndi moyo kwa zaka mahandiredi ambirimbiri, masauzande, mamiliyoni, ngakhale mabiliyoni ambirimbiri, tidzadziwa zinthu zochuluka zokhudza Yehova Mulungu kuposa mmene tikudziwira panopa. Koma tidzaonabe kuti pali zinthu zodabwitsa zosawerengeka zoti tiziphunzire. . . . Moyo wamuyaya udzakhala watanthauzo kwambiri ndi wa zochita zosiyanasiyana, ndipo nthawi zonse kuyandikana ndi Yehova kudzakhala mbali yopindulitsa kwambiri ya moyo umenewo.” Koma kodi ndi zinthu zina ziti zomwe tingaphunzire m’Mawu a Mulungu panopa?

MUZIGANIZIRA ZINTHU ZAKUMWAMBA

12. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziganizira zinthu zakumwamba? Perekani chitsanzo.

12 Mawu a Mulungu amatithandiza kudziwako zina zokhudza ‘malo apamwamba’ omwe Yehova amakhala. (Yes. 33:5) Amatithandizanso kudziwa zinthu zochititsa chidwi zokhudza Yehova komanso mbali ya kumwamba ya gulu lake. (Yes. 6:​1-4; Dan. 7:​9, 10; Chiv. 4:​1-6) Mwachitsanzo, timatha kuwerenga zinthu zochititsa mantha zomwe Ezekieli anaona pamene ‘kumwamba kunatseguka ndipo anayamba kuona masomphenya a Mulungu.’—Ezek. 1:1.

13. Mogwirizana ndi Aheberi 4:​14-16, kodi mumamva bwanji mukaganizira udindo umene Yesu ali nawo kumwamba?

13 Taganiziraninso za udindo wa Yesu monga Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wachifundo. Kudzera mwa iye tikhoza kufika ku “mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu” popemphera kwa Mulungu kuti atichitire chifundo komanso kuti atithandize pa nthawi yoyenera. (Werengani Aheberi 4:​14-16.) Choncho tisamalole kuti tsiku lidutse tisanaganizire zimene Yehova ndi Yesu atichitira komanso zimene akutichitira panopa ali kumwamba. Chikondi chawo chizitifika pamtima ndipo chizitichititsa kukhala akhama potumikira Mulungu komanso kumulambira.—2 Akor. 5:​14, 15.

Taganizirani mmene mudzasangalalire m’dziko latsopano podziwa kuti munathandiza anthu ena kukhala a Mboni za Yehova komanso ophunzira a Yesu (Onani ndime 14)

14. Fotokozani chinthu chofunika kwambiri chomwe tingachite posonyeza kuti timayamikira Yehova ndi Yesu. (Onaninso zithunzi.)

14 Njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti timayamikira Mulungu ndi Mwana wake ndi kuyesetsa kuthandiza ena kuti akhale a Mboni za Yehova komanso ophunzira a Yesu. (Mat. 28:​19, 20) Izi ndi zimene mtumwi Paulo anachita chifukwa choyamikira Mulungu ndi Khristu. Iye ankadziwa kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:​3, 4) Paulo ankachita utumiki wake mwakhama kwambiri kuti athandize anthu ambiri mmene angathere n’cholinga choti ‘mulimonse mmene zingakhalire apulumutseko ena.’—1 Akor. 9:​22, 23.

MUZIKONDA KWAMBIRI KUPHUNZIRA MAWU A MULUNGU

15. Mogwirizana ndi Salimo 1:​2, kodi n’chiyani chingatithandize kukhala osangalala?

15 Wolemba masalimo ananena kuti munthu wodala kapena kuti wosangalala ndi amene “amakondwera ndi chilamulo cha Yehova” ndipo ‘amachisinkhasinkha usana ndi usiku.’ (Sal. 1:​1-3) Womasulira Baibulo wina dzina lake Joseph Rotherham anafotokoza lembali m’buku lake lina (Studies in the Psalms) kuti munthu amafunika “azisangalala kwambiri ndi malangizo a Mulungu, aziyesetsa kuwafufuza, kuwaphunzira ndiponso kuwaganizira.” Iye ananenanso kuti “ngati tsiku ladutsa asanawerenge Baibulo kuti apezemo nzeru aziona kuti tsiku limenelo langowonongeka.” Munthu angasonyeze kuti amasangalala ndi kuphunzira Baibulo akamachita chidwi ndi mfundo zake zozama komanso akamaona kugwirizana kwake. Zimakhala zosangalatsa kwambiri munthu akamayesetsa kuti amvetse bwino Mawu a Mulungu.

16. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

16 Mfundo za choonadi zosangalatsa zimene Yehova amatiphunzitsa m’Mawu ake si zovuta kuzimvetsa. Munkhani yotsatira tikambirana mfundo ina yozama ya choonadi yokhudza kachisi wamkulu wauzimu amene Paulo anamufotokoza m’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi. Tikukhulupirira kuti musangalala kwambiri mukamaphunzira nkhani imeneyi.

NYIMBO NA. 94 Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

a Kuphunzira Baibulo kungatithandize kuti tikhale osangalala kwa moyo wathu wonse ndipo kungatithandize kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tizimvetsa bwino m’lifupi, m’litali, kukwera ndi kuzama kwa Mawu a Mulungu.

b Onani nkhani yakuti “Ulosi Wakalekale Umene Umakukhudzani,” mu Nsanja ya Olonda ya July 2022.

c Kuti mudziwe zimene mungachite pokonzekera zinthu zoopsa zimene zichitike posachedwapa, onani buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira tsamba 230.