NKHANI YOPHUNZIRA 45

Muziyamikira Mwayi Wanu Wolambira M’kachisi Wauzimu wa Yehova

Muziyamikira Mwayi Wanu Wolambira M’kachisi Wauzimu wa Yehova

“Lambirani iye amene anapanga kumwamba [ndi] dziko lapansi.”—CHIV. 14:7.

NYIMBO NA. 93 Mudalitse Msonkhano Wathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi mngelo akunena kuti chiyani, nanga zimene akunenazo zikutikhudza bwanji?

 KODI mngelo akanabwera kudzalankhula nanu, mukanamvetsera zimene akanakuuzani? Masiku ano mngelo akulankhula “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” Kodi iye akunena kuti chiyani? Iye akuti, “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero . . . lambirani iye amene anapanga kumwamba [ndi] dziko lapansi.” (Chiv. 14:​6, 7) Yehova ndi Mulungu woona amene aliyense ayenera kumulambira. Timayamikira kuti watipatsa mwayi wamtengo wapatali womulambira m’kachisi wake wamkulu wauzimu.

2. Kodi kachisi wauzimu wa Yehova ndi chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “ Kodi Kachisi Wamkulu Wauzimu Si Chiyani?”)

2 Kodi kachisi wauzimu ndi chiyani, nanga tingapeze kuti mfundo zofotokoza kachisiyu? Kachisi wauzimu si nyumba yeniyeni koma ndi njira yolambirira Yehova movomerezeka kudzera mu nsembe ya Yesu. Mtumwi Paulo anafotokoza za kachisiyu m’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi omwe ankakhala ku Yudeya. b

3-4. Kodi Paulo ankadera nkhawa chiyani zokhudza Akhristu a Chiheberi a ku Yudeya, nanga anawathandiza bwanji?

3 N’chifukwa chiyani Paulo analembera kalata Akhristu a Chiheberi omwe ankakhala ku Yudeya? N’kutheka kuti anachita zimenezi pa zifukwa ziwiri. Choyamba, kuti awalimbikitse. Ambiri mwa Akhristuwa anakulira m’chipembedzo cha Chiyuda, choncho atsogoleri a chipembedzo chawo chakale ayenera kuti ankawanyoza chifukwa chokhala Akhristu. N’chifukwa chiyani ankawanyoza? Chifukwa choti Akhristuwo analibe kachisi wochititsa chidwi woti azipitako kukalambira. Analibe guwa la nsembe looneka loti aziperekapo nsembe komanso analibe wansembe woti aziwatumikira. Zimenezi zikanatha kufooketsa ophunzira a Khristu ndiponso kuchititsa kuti chikhulupiriro chawo chiyambe kuchepa. (Aheb. 2:1; 3:​12, 14) Mwina ena akanatha kukopeka kuti abwererenso ku Chiyuda.

4 Chachiwiri, Paulo ananena kuti Akhristu a Chiheberiwa sankachita khama kuti azimvetsa mfundo zatsopano kapena mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi “chakudya chotafuna” chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:​11-14) Zikuoneka kuti ena mwa Akhristuwo ankatsatirabe Chilamulo cha Mose. Koma Paulo anafotokoza kuti nsembe zomwe zinkaperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo sizikanachotseratu machimo. Chifukwa cha zimenezi, Chilamulo ‘chinachotsedwa.’ Choncho Paulo anayamba kuwaphunzitsa mfundo zozama za choonadi. Iye anakumbutsa Akhristu anzakewo za “chiyembekezo chabwino” kudzera mu nsembe ya Yesu, chomwe chikanawathandiza ‘kuyandikira kwa Mulungu.’—Aheb. 7:​18, 19.

5. Kodi tiyenera kumvetsa mfundo ziti za m’buku la Aheberi, nanga n’chifukwa chiyani?

5 Paulo anafotokozera abale ake a Chiheberi kuti njira imene Akhristu ankaitsatira polambira inali yapamwamba kwambiri kusiyana ndi yomwe ankatsatira m’mbuyomo. Zimene Ayuda ankachita polambira zinali chabe “mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.” (Akol. 2:17) Mthunzi wa chinthu umangosonyeza mmene chinthu chenicheni chimaonekera. Choncho zimene Ayuda akale ankachita polambira zinali mthunzi wa zinthu zenizeni zimene zinkabwera. Tiyenera kumvetsa njira imene Yehova wapereka yotithandiza kuti machimo athu akhululukidwe ndipo tizimulambira m’njira yovomerezeka. Tiyeni tione zimene zafotokozedwa m’buku la Aheberi kuti tiyerekezere “mthunzi” (womwe ndi njira yolambirira ya Ayuda) ndi “zenizeni” (zomwe ndi njira yolambirira ya Akhristu). Kuchita zimenezi kutithandiza kumvetsa zokhudza kachisi wauzimu komanso mmene amatikhudzira.

CHIHEMA

6. Kodi chihema chinkagwiritsidwa ntchito bwanji?

6 Njira yolambirira ya Ayuda. Paulo anafotokoza mfundo zake pogwiritsa ntchito chihema chimene Mose anapanga mu 1512 B.C.E. (Onani tchati chakuti “Njira Yolambirira ya Ayuda—Njira Yolambirira ya Akhristu.”) Chihema chinali chitenti chimene Aisiraeli ankanyamula akamachoka malo ena kupita ena. Iwo anachigwiritsa ntchito kwa zaka pafupifupi 500, mpaka pamene kachisi weniweni anamangidwa ku Yerusalemu. (Eks. 25:​8, 9; Num. 9:22) ‘Chihema chokumanakochi’ ndi malo amene Aisiraeli ankakumana kuti alambire Mulungu komanso kupereka nsembe. (Eks. 29:​43-46) Koma chihemacho chinkaimiranso zinthu zina zazikulu zimene zinkabwera.

7. Kodi kachisi wauzimu anayamba liti kugwira ntchito?

7 Njira yolambirira ya Akhristu. Chihema chinali “mthunzi wa zinthu zakumwamba” ndipo chinkaimira kachisi wamkulu wa Yehova. Paulo ananena kuti “chihema chimenecho chinali chifaniziro cha nthawi yoikidwiratu imene tsopano yafika.” (Aheb. 8:5; 9:9) Choncho pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a Chiheberiwa, kachisi wauzimuyu anali alipo kale. Kachisiyu anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E. M’chaka chimenechi Yesu anabatizidwa, anadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kutumikira ngati “mkulu wa ansembe wapamwamba” m’kachisi wauzimu wa Yehova. cAheb. 4:14; Mac. 10:​37, 38.

MKULU WA ANSEMBE

8-9. Mogwirizana ndi Aheberi 7:​23-27, kodi pali kusiyana kotani pakati pa akulu a ansembe a ku Isiraeli ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba?

8 Njira yolambirira ya Ayuda. Mkulu wa ansembe anali ndi udindo woimira anthu kwa Mulungu. Mkulu wa ansembe woyamba wa Aisiraeli anali Aroni ndipo anasankhidwa ndi Yehova pamene chihema chinayamba kugwira ntchito. Koma mogwirizana ndi zimene Paulo anafotokoza, “panayenera kukhala ansembe ambiri olowana m’malo chifukwa imfa inali kuwaletsa kupitiriza unsembe wawo.” d (Werengani Aheberi 7:​23-27.) Popeza sanali angwiro, akulu a ansembewo ankafunikanso kumapereka nsembe za machimo awo. Apa m’pamene akulu a ansembe a Aisiraeli akusiyana kwambiri ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba, yemwe ndi Yesu Khristu.

9 Njira yolambirira ya Akhristu. Monga Mkulu wa Ansembe, Yesu Khristu ndi “wantchito wotumikira ena . . . m’chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova, osati munthu.” (Aheb. 8:​1, 2) Paulo anafotokoza kuti “chifukwa chokhala ndi moyo kosatha, palibe womulowa m’malo [Yesu] pa unsembe wake.” Paulo anapitiriza kuti mosiyana ndi ansembe a Chiisiraeli, Yesu ndi “wosaipitsidwa, wosiyana ndi anthu ochimwa,” choncho “safunikira kupereka tsiku ndi tsiku nsembe za machimo ake.” Tsopano tiyeni tikambirane kusiyana kwa njira yolambirira ya Ayuda ndi njira yolambirira ya Akhristu pa nkhani ya maguwa ndi nsembe.

MAGUWA NDI NSEMBE

10. Kodi nsembe zimene zinkaperekedwa pa guwa lamkuwa zinkaimira chiyani?

10 Njira yolambirira ya Ayuda. Pafupi ndi khomo la chihema panali guwa lamkuwa lomwe ankaperekerapo nsembe za nyama kwa Yehova. (Eks. 27:​1, 2; 40:29) Koma nsembe zimenezi sizinkathandiza kuti machimo onse a anthu akhululukidwe. (Aheb. 10:​1-4) Nsembe za nyama, zomwe zinkaperekedwa mobwerezabwereza pachihema zinkaimira nsembe imodzi imene idzayeretseretu machimo a anthu.

11. Kodi Yesu anadzipereka ngati nsembe paguwa liti? (Aheberi 10:​5-7, 10)

11 Njira yolambirira ya Akhristu. Yesu ankadziwa kuti Yehova anamutumiza padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake ngati dipo n’cholinga choti awombole anthu. (Mat. 20:28) Choncho pa ubatizo wake, Yesu anadzipereka kuti azichita zimene Yehova amafuna. (Yoh. 6:38; Agal. 1:4) Yesu anadzipereka paguwa la nsembe lophiphiritsa, lomwe limaimira “chifuniro” cha Mulungu choti Mwana wakeyu apereke nsembe moyo wake wangwiro. Moyo wa Yesu unaperekedwa “kamodzi kokha” kuti uphimbiretu machimo a munthu aliyense amene amakhulupirira Khristu. (Werengani Aheberi 10:​5-7, 10.) Tsopano tiyeni tikambirane tanthauzo la zinthu zomwe zinali mkati mwa chihema.

MALO OYERA NDI MALO OYERA KOPOSA

12. Kodi ndi ndani amene ankaloledwa kulowa m’chipinda chilichonse chapachihema?

12 Njira yolambirira ya Ayuda. Zinthu zimene zinkapezeka m’kati mwa chihema zinali zofanana ndi zimene zinkapezeka mu akachisi omwe anadzamangidwa ku Yerusalemu. Mkati mwake munali zipinda ziwiri: “Malo Oyera” ndi “Malo Oyera Koposa.” Zipindazi zinasiyanitsidwa ndi nsalu yopetedwa. (Aheb. 9:​2-5; Eks. 26:​31-33) Mkati mwa Malo Oyera munali choikapo nyale chagolide, guwa la nsembe la zofukiza ndi tebulo la mkate wachionetsero. “Ansembe odzozedwa” okha ndi amene ankaloledwa kulowa mkati mwa Malo Oyera kukagwira ntchito zawo. (Num. 3:​3, 7, 10) M’malo Oyera Koposa munkakhala likasa la pangano lagolide, lomwe linkaimira kukhalapo kwa Yehova. (Eks. 25:​21, 22) Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kudutsa nsalu yotchinga kupita ku Malo Oyera Koposa pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. (Lev. 16:​2, 17) Chaka chilichonse, iye ankalowa ndi magazi a nyama kuti akaphimbe machimo ake komanso a Aisiraeli onse. Kenako Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera pofotokoza tanthauzo la zinthu zomwe zinkapezeka muchihema.—Aheb. 9:​6-8. e

13. Kodi Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa amaimira chiyani pa kulambira kwa Akhristu?

13 Njira yolambirira ya Akhristu. Ophunzira ochepa a Khristu adzozedwa ndi mzimu woyera ndipo ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Anthu 144,000 amenewa adzatumikira ngati ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyera a chihema amaimira kuti iwowa atengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu pa nthawi imene ali padziko lapansi. (Aroma 8:​15-17) Malo Oyera Koposa amaimira kumwamba, komwe Yehova amakhala. “Nsalu,” imene inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa imaimira thupi la Yesu limene linali ngati chotchinga chomulepheretsa kupita kumwamba kukatumikira ngati Mkulu wa Ansembe wapamwamba m’kachisi wauzimu. Yesu atapereka thupi lake ngati nsembe yopulumitsira anthu, anatsegula njira yoti Akhristu onse odzozedwa akakhale ndi moyo kumwamba. Iwonso amafunika kusiya thupi lomwe ali nalo padzikoli kuti akalandire mphoto yawo kumwamba (Aheb. 10:​19, 20; 1 Akor. 15:50) Yesu ataukitsidwa analowa m’Malo Oyera Koposa a kachisi wauzimu, kumene odzozedwa onse adzakakhale naye limodzi.

14. Mogwirizana ndi Aheberi 9:​12, 24-26, n’chifukwa chiyani tinganene kuti kulambira Yehova m’kachisi wake wamkulu wauzimu n’kwapamwamba kwambiri?

14 Apa titha kuona kuti njira imene Yehova anakonza yoti pakhale kulambira koyera kudzera mu nsembe ya dipo ndiponso udindo wa Yesu Khristu monga Mkulu wa Ansembe, ndi yapamwamba kwambiri. Mkulu wa ansembe ku Isiraeli ankalowa m’Malo Oyera Koposa opangidwa ndi anthu atatenga magazi a nyama koma Yesu “analowa kumwamba kwenikweniko,” komwe ndi malo oyera kuposa ena alionse, kukaonekera pamaso pa Yehova. Kumwambako anakapereka kwa Mulungu ufulu umene anali nawo wokhala ndi moyo monga munthu wangwiro padziko lapansi ndipo anachita zimenezi m’malo mwa ifeyo “kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.” (Werengani Aheberi 9:​12, 24-26.) Nsembe ya Yesu imathandiza kuti machimo athu akhululukidwe mpaka kalekale. Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padzikoli, tonsefe tikhoza kulambira Yehova m’kachisi wake wauzimu, ndipo tikambirana zimenezi m’ndime zotsatira.

MABWALO

15. Kodi ndi ndani ankatumikira m’bwalo la chihema?

15 Njira yolambirira ya Ayuda. Chihema chinali ndi bwalo lomwe linali malo otchingidwa ndi mpanda kumene ansembe ankagwira ntchito zawo. M’bwaloli munali guwa la nsembe lalikulu lamkuwa ndiponso beseni lamkuwa la madzi limene ansembe ankaligwiritsa ntchito podziyeretsa asanayambe utumiki wawo wopatulika. (Eks. 30:​17-20; 40:​6-8) Akachisi amene anamangidwa pambuyo pake ankakhala ndi bwalo lakunja, kumene anthu omwe si ansembe ankaimako n’kumalambira Mulungu.

16. M’kachisi wauzimu, kodi ndi ndani amatumikira m’bwalo lamkati, nanga ndi ndani amatumikira m’bwalo lakunja?

16 Njira yolambirira ya Akhristu. Abale a Yesu odzozedwa asanapite kukatumikira ndi Yesu kumwamba monga ansembe amatumikira mokhulupirika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kachisi wauzimu. Beseni lalikulu la madzi limakumbutsa odzozedwawo komanso Akhristu ena onse kuti ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino komanso oyera mwauzimu. Koma kodi a “khamu lalikulu,” omwe amathandiza mokhulupirika abale a Khristu odzozedwa, amatumikira Yehova ali kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu,” zimene zikusonyeza kuti ali m’bwalo lakunja lomwe ndi padziko lapansi kumene ‘akuchitira [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake.” (Chiv. 7:​9, 13-15) Timayamikira kwambiri kuti Yehova watipatsa mwayi wamtengo wapatali womulambira m’kachisi wake wamkulu wauzimu.

MWAYI WOMWE TILI NAWO WOLAMBIRA YEHOVA

17. Kodi ifeyo tili ndi mwayi wopereka nsembe ziti kwa Yehova?

17 Masiku ano Akhristu onse ali ndi mwayi wopereka nsembe kwa Yehova pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso zinthu zawo pomutumikira. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo anauza Akhristu a Chiheberi, ‘nthawi zonse tikhoza kutamanda Mulungu, ndipo tingachite zimenezi ngati nsembe imene tikupereka kwa iye pogwiritsa ntchito milomo yathu kuti tilengeze dzina lake.’ (Aheb. 13:15) Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wathu wolambira Yehova poyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira.

18. Mogwirizana ndi Aheberi 10:​22-25, ndi zinthu ziti zimene sitiyenera kuzinyalanyaza, nanga ndi zinthu ziti zomwe tiyenera kukumbukira nthawi zonse?

18 Werengani Aheberi 10:​22-25. Chakumapeto kwa kalata imene analembera Aheberi, Paulo anatchula zinthu zosiyanasiyana zokhudza kulambira kwathu zimene sitiyenera kuzinyalanyaza. Zinthu zake zikuphatikizapo kupemphera kwa Yehova, kulengeza poyera chiyembekezo chathu, kusonkhana pamodzi ngati mpingo ndiponso kulimbikitsana, ‘makamaka pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikira.’ Pofuna kutsindika, chakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova ananena kawiri kuti: “Lambirani Mulungu.” (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mfundo zozama za choonadi zokhudza kachisi wamkulu wauzimu zimene taphunzira, ndipo tiziyamikira mwayi wolambira Mulungu wathu wamkulu, Yehova.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

a Mfundo imodzi yozama yopezeka m’Mawu a Mulungu ndi yokhudza kachisi wamkulu wauzimu. Kodi kachisi ameneyu ndi chiyani? Munkhaniyi tikambirana mfundo zopezeka m’buku la Aheberi zokhudza kachisiyu. Tikukhulupirira kuti kuphunzira nkhaniyi kukuthandizani kuti muziyamikira kwambiri mwayi wanu wolambira Yehova.

b Kuti muone mwachidule nkhani zopezeka m’buku la Aheberi, onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Aheberi pa jw.org.

c M’malemba a Chigiriki a Chikhristu, buku la Aheberi lokha ndi limene limanena za Yesu kuti ndi Mkulu wa Ansembe.

d Buku lina limafotokoza kuti pamene Yerusalemu ankawonongedwa mu 70 C.E., ku Isiraeli kunali kutakhala akulu a ansembe okwana 84.

f Onani buku la Chingelezi lakuti Pure Worship of Jehovah—Restored At Last! tsamba 240.

g Onani bokosi lakuti “Mmene Mzimu Woyera Unaululira Tanthauzo la Kachisi Wauzimu,” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2010, tsamba 22.