Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Mmene Tingapezere Zinthu Zimene Zasintha Kamvedwe

Ndi mwayi waukulu kukhala pa nthawi imene mwapang’onopang’ono, Yehova akutithandiza kumvetsa mfundo za m’Baibulo kuposa kale. (Dan. 12:4) Ngakhale zili choncho, nthawi zina zikhoza kumativuta kudziwa mfundo za choonadi za m’Baibulo zimene zasintha. Kodi tingapeze kuti zinthu zimene zasintha komanso kafotokozedwe kake?

• Mu Watch Tower Publications Index pa mutu wakuti Beliefs Clarified,” pali mndandanda wa zinthu zomwe zinasintha potengera chaka. Kuti mupeze mitu ya nkhani zimene zasintha, lembani “Understanding Clarified” (n’kuika m’mikodolero) pamalo ofufuzira pa Watchtower Library kapena pa LAIBULALE YA PA INTANETI.

Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lili ndi mndandanda wochepa potsatira mitu ya nkhani. Pitani pa mutu wakuti “Mboni za Yehova” kenako “Zikhulupiriro za Akhristu Komanso Mmene Amaonera Nkhani Zosiyanasiyana” ndipo kenako pitani pa kamutu kakuti “Kumveketsa Zikhulupiriro Zathu.”

Pophunzira panokha, mukhoza kusankha nkhani yomwe yasintha kamvedwe posachedwapa n’kufufuza kamvedwe katsopano komanso mfundo za m’Malemba zomwe zachititsa kuti tisinthe.