Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Mmene Mungapezele Masinthidwe pa Kamvedwe Kathu Katsopano

Ni mwayi wapadela kukhala m’nthawi imene Yehova akumveketsa bwino coonadi ca m’Baibo kuposa n’kale lonse. (Dan. 12:⁠4) Ngakhale n’telo, zingakhalebe zovuta kwa ife kuti tiziyendela pamodzi na kamvedwe katsopano ka m’Baibo. Kodi tingapeze kuti kamvedwe katsopano kameneka na kafotokozedwe kake?

• Mu Watch Tower Publications Index pansi pa ka mutu kakuti “Beliefs Clarified” pamafotokoza kamvedwe katsopano motsatila caka. Kuti mupeza nkhanizo, lembani mawu akuti “understanding clarified” m’danga lofufuzila la pa Watchtower Library kapena pa Laibulale ya pa Intaneti ya Watchtower

Buku Lofufuzila la Mboni za Yehova ili na nkhani zocepa, ndipo imazindandalika motsatila mitu yake. Pitani pa kamutu kakuti “Mboni za Yehova,” kenako “Zikhulupililo za Akhristu na Mmene Amaonela Nkhani Zina,” ndiyeno pitani pa kamutu kakuti “Kamvedwe Katsopano ka Zimene Timakhulupilila.”

Pa phunzilo la inu mwini, mungasankhe nkhani ya kamvedwe kathu katsopano ya posacedwa. Fufuzani pamene panasintha na kuona zifukwa za m’Malemba zimene zinacititsa kuti pakhale kusinthako.