Tonsefe Tili Ndi Udindo Wosankha Choyenera Ndi Chosayenera

Tonsefe Tili Ndi Udindo Wosankha Choyenera Ndi Chosayenera

Ngati mukufuna kupita kudera lina lomwe simunapiteko, kodi mungachite chiyani?

  1. 1. Kudzera njira yomwe mukungoiganizira.

  2. 2. Kutsatira anthu ena poganiza kuti akudziwa bwino njira ya kumene mukupita.

  3. 3. Kufufuza njira yolondola pogwiritsa ntchito mapu kapena kufunsa mnzanu wodalirika amene akudziwa bwino njira ya kumene mukufuna kupita.

Ngati tingayendere maganizo oyamba ndi achiwiriwo titha kufika kwinakwake koma osati kumene timafunadi kupita. Koma ngati tingayendere maganizo achitatuwo, n’zosakayikitsa kuti tikafika bwinobwino kumene tikufuna kupitako.

Moyo wathu uli ngati ulendo ndipo timayembekezera kuti tsogolo lathu lidzakhala losangalatsa kwambiri. Koma tingakafike kumene tikupita kapena ayi potengera kumene timafufuza malangizo otithandiza kusankha zochita.

Zinthu zambiri zimene timafunika kusankha zochita, zimakhala zing’onozing’ono pomwe zina zimakhala zofunika kwambiri. Zimene timasankha zimasonyeza mfundo za makhalidwe abwino zimene timayendera, komanso mmene timaonera zoyenera ndi zosayenera. Kwa nthawi yaitali, zimenezi zimakhudza ifeyo ndiponso anthu ena omwe timawakonda ndipo zingawabweretsere mavuto kapena ayi. Zosankha zimenezi zimakhudza nkhani monga izi:

  • Kugonana ndiponso ukwati

  • Kuchita zinthu moona mtima, ntchito ndi ndalama

  • Kulera ana

  • Mmene tingachitire zinthu ndi ena

Kodi mungatsimikizire bwanji kuti zosankha zanu pa nkhani zimenezi zidzathandiza kuti inuyo limodzi ndi banja lanu mukhale moyo wosangalala?

Aliyense ayenera kumadzifunsa funso ili: Kodi n’chiyani chimene chingandithandize kusankha zinthu mwanzeru pa nkhani zokhudza zoyenera ndi zosayenera?

Magaziniyi ifotokoza chifukwa chake Baibulo lili buku lodalirika posankha zoyenera ndi zosayenera komanso mmene lingachitire zimenezi.