Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

Gonjetsani Mantha Mwa Kudalila Yehova

Gonjetsani Mantha Mwa Kudalila Yehova

LEMBA LA CAKA CA 2024: “Ine ndidzadalila inu, tsiku lililonse limene ndingacite mantha.”SAL. 56:3.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tiphunzile mmene tingalimbikitsile cidalilo cathu mwa Yehova na kugonjetsa mantha athu.

1. N’cifukwa ninji tingacite mantha nthawi zina?

 MUNTHU aliyense amacita mantha nthawi zina. Koma cifukwa cophunzila Baibo, sitiopanso akufa, ziŵanda, kapena za m’tsogolo. Ngakhale n’telo, tikukhalabe m’nthawi imene zinthu “zoopsa zikuonekela,” monga nkhondo, zaciwawa, komanso matenda. (Luka 21:11) Tingamaopenso anthu, kuphatikizapo maboma amene amatipondeleza, kapena a m’banja lathu omwe amatsutsa kulambila koona. Ndiponso anthu ena amada nkhawa akaona kuti sangathe kupilila mayeso amene akukumana nawo, kapena amene angadzakumane nawo m’tsogolo.

2. Fotokozani mmene zinthu zinalili kwa Davide ali ku Gati.

2 Davide nayenso anacitapomantha. Mwacitsanzo, pamene Mfumu Sauli anali kumusakasaka kuti amuphe, Davide anathaŵila ku mzinda wa Afilisiti wochedwa Gati. Posakhalitsa, Akisi Mfumu ya ku Gati, anatulukila kuti Davide anali msilikali wamphamvu yemwe anthu anali kumuimbila nyimbo yakuti wakantha Afilisiti “masauzande makumimakumi.” Davide “anacita mantha kwambili.” (1 Sam. 21:​10-12) Iye anada nkhawa na zimene Akisi adzamucita. Kodi Davide anagonjetsa bwanji mantha ake?

3. Malinga na Salimo 56:​1-3, 11, kodi Davide anagonjetsa bwanji mantha ake?

3 Mu Salimo 56, Davide anafotokoza mmene anali kumvela ali ku Gati. Salimo limeneli lifotokoza cifukwa cake Davide anacita mantha, komanso cimene cinam’thandiza kuwagonjetsa. Iye anaika cidalilo cake mwa Yehova. (Ŵelengani Salimo 56:​1-3, 11.) Davide anali na zifukwa zabwino zodalila Yehova. Na thandizo la Yehova, Davide anapanga nzelu ina yake yom’thandiza: Anadzipanga kukhala wamisala! Akisi anayamba kuona Davide kukhala munthu wacabe-cabe womunyansa, m’malo momuona monga munthu woopsa. Basi Davide anakwanitsa kuthawa.—1 Sam. 21:13–22:1.

4. Kodi tingalimbikitse bwanji cidalilo cathu mwa Yehova? Fotokozani citsanzo.

4 Nafenso tingagonjetse mantha athu podalila Yehova. Koma kodi tingalimbikitse bwanji cidalilo cathu mwa Yehova, maka-maka tikacita mantha? Ganizilani citsanzo ici. Mukadziŵa kuti muli na matenda ena ake, poyamba mungacite mantha. Koma ngati dokotala mumamudalila mantha anu angacepeko. Iye angakhale na mbili yakuti anacilitsapo anthu ena matenda amene muli nawo. Angakumvetseleni mwachelu, ndipo mungaone kuti akumvetsa mmene mukumvela. Kenako angakupatseni mankhwala amene anaseŵenzapo kwa ena. Mofananamo, ifenso tingalimbikitse cidalilo cathu mwa Yehova poganizila zimene iye anaticitila kumbuyoku, zimene akuticitila pali pano komanso zimene adzaticitile m’tsogolo. Izi n’zimene Davide anacita. Pamene tikambilana mawu ake ena ouzilidwa opezeka mu Salimo 56, ganizilani mmene inunso mungalimbikitsile cidalilo canu mwa Yehova na kugonjetsa mantha anu.

KODI YEHOVA WACITAPO KALE CIYANI?

5. Kodi Davide anali kusinkhasinkha za ciyani kuti agonjetse mantha ake? (Salimo 56:​12, 13)

5 Ngakhale kuti umoyo wa Davide unali paciopsezo, iye anaika maganizo pa zimene Yehova anacitapo kale. (Ŵelengani Salimo 56:​12, 13.) Izi n’zimene Davide anali kucita pa umoyo wake wonse. Mwacitsanzo, iye anali kuganizila nchito zodabwitsa za Yehova, zimene zinali kumukumbutsa kuti Yehova ni wamphamvu kwambili, komanso kuti ali na cidwi pa anthu. (Sal. 65:​6-9) Anali kuganizilanso zimene Yehova anacitila anthu ena. (Sal. 31:19; 37:​25, 26) Ndipo anali kuganizilanso maka-maka zimene Yehova anamucitila iye mwini. Yehova anamuthandiza Davide na kum’teteza kucokela ali mwana. (Sal. 22:​9, 10) Ndipo mosakaikila kusinkhasinkha mwa njila imeneyi kunalimbikitsa cidalilo cake mwa Yehova!

Davide analimbikitsa cidalilo cake mwa Yehova poiika maganizo ake pa zinthu zimene Yehova anali atacita kale, zimene anali kucita, komanso zimene anali kudzacita (Onani ndime 5, 8, 12)) d


6. N’ciyani cingatithandize kudalila Yehova tikacita mantha?

6 Ngati mwacita mantha, dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova wanicitilapo kale ciyani?’ Ganizilani zimene iye analenga. Mwacitsanzo, ‘tikaonetsetsa’ mmene Yehova amasamalila mbalame komanso maluŵa—zomwe sizinalengedwe m’cifanizilo cake, ndiponso sizimulambila—nafenso timalimbikitsa cidalilo cakuti adzatisamalila. (Mat. 6:​25-32) Ganizilaninso zimene Yehova wacitila alambili ake. Mungaŵelenge za munthu wa m’Baibo amene anaonetsa cikhulupililo colimba, kapena kuŵelenga cocitika ca mtumiki wa Yehova wa masiku ano. a Kuwonjezela apo, sinkhasinkhani mmene Yehova akusamalilani inuyo panokha. Kodi iye anakukokelani bwanji m’coonadi? (Yoh. 6:44) Ndipo kodi wayankha motani mapemphelo anu? (1 Yoh. 5:14) Nanga mumapindula motani tsiku na tsiku cifukwa ca nsembe ya Mwana wake wokondedwa?—Aef. 1:7; Aheb. 4:​14-16.

Timalimbikitsa cidalilo cathu mwa Yehova mwa kuika maganizo athu pa zinthu zimene anacita kale, zimene akucita, ndiponso zimene adzacita m’tsogolo (Onani ndime 6, 9-10, 13-14)) e


7. Kodi citsanzo ca mneneli Danieli cinam’thandiza bwanji mlongo Vanessa kugonjetsa mantha ake?

7 Mlongo wina wa ku Haiti, dzina lake Vanessa, b anakumana na vuto lalikulu. Mwamuna wina m’dela lawo anali kum’tumila foni tsiku lililonse na kumulembela mameseji omukakamiza kuti akhale naye pa cibwenzi. Vanessa anakanilatu zimenezo. Koma mwamunayo anakwiya kwambili ndipo anaopseza Vanessa kuti adzamuonetsa zakuda. Vanessa anati, “N’nacita mantha kwambili.” Kodi Vanessa anawagonjetsa motani mantha amenewa? Anacita zonse zotheka kuti adziteteze. Mkulu wina mu mpingo anamuthandiza kudziŵitsa apolisi. Koma anayambanso kuganizila mmene Yehova anatetezela atumiki ake akale. Iye anati “Munthu woyamba amene n’naganizila ni mneneli Danieli. Iye anaponyedwa m’dzenje la mikango ya njala ngakhale kuti sanalakwe ciliconse. Ngakhale n’telo, Yehova anamuteteza. N’nasiya nkhani yonse m’manja mwa Yehova. N’tacita zimenezi, mantha anga anathelatu.”—Dan. 6:​12-22.

KODI YEHOVA AKUCITA CIYANI PALI PANO?

8. Kodi Davide anali wotsimikiza mtima za ciyani? (Salimo 56:8)

8 Ngakhale kuti moyo wa Davide unali pa ciwopsezo ali ku Gati, sanalole mantha kumukhwethemula. M’malo mwake, anaika maganizo ake pa zimene Yehova anali kumucitila pa nthawiyo. Davide anali kudziŵa kuti Yehova anali kum’tsogolela na kumuteteza, komanso kuti anali kumvetsa mmene iye anali kumvela. (Ŵelengani Salimo 56:8.) Davide analinso na mabwenzi okhulupilika amene anali kum’thandiza, monga Yonatani, na Mkulu wa Ansembe Ahimeleki. (1 Sam. 20:​41, 42; 21:​6, 8, 9) Ngakhale kuti Mfumu Sauli anafuna kupha Davide, iye anakwanitsa kuthaŵa. Anali wotsimikiza kuti Yehova anali kudziŵa bwino masautso omwe anali kukumana nawo, komanso mmene anali kumvela.

9. Kodi Yehova amadziŵa ciyani za aliyense wa ife?

9 Mukakumana na vuto lokucititsani mantha, kumbukilani kuti Yehova amadziŵa za vutolo komanso mmene lakukhudzilani. Mwacitsanzo, Yehova anali kudziŵa bwino mazunzo amene Aisiraeli anali kukumana nawo ku Iguputo komanso “zowawa zawo.” (Eks. 3:7) Davide anaimba kuti Yehova anali kudziŵa bwino “kusautsika” kwake, komanso “zowawa” zake. (Sal. 31:7) Ndipo pamene anthu a Mulungu anali kukumana na mavuto—ngakhale cifukwa copanga zisankho mosaganiza bwino —“Iyenso anali kuvutika.” (Yes. 63:9) Mukacita mantha, Yehova amamvetsa mmene mukumvela, ndipo amakhala wofunitsitsa kukuthandizani kuti mugonjetse manthawo.

10. N’cifukwa ciyani muli otsimikiza kuti Yehova amakusamalilani, komanso kuti adzakuthandizani kupilila mavuto alionse?

10 Mwina mungakaikile za kuti Yehova akukuthandizani pokumana na vuto loopsa. Zikatelo, m’pempheni kuti akuthandizeni kuona thandizo lake. (2 Maf. 6:​15-17) Ndiyeno ganizilani izi: Kodi munalimbikitsidwapo na nkhani kapena ndemanga pa msonkhano wa mpingo? Kodi munalimbikitsidwapo na cofalitsa, vidiyo, kapena nyimbo yopekedwa koyamba? Kodi munthu wina anakugaŵilam’poni mfundo yolimbikitsa kapena lemba? Tingaiŵale mwamsanga mmene timapindulila na cikondi ca abale na alongo komanso cakudya cauzimu cimene timalandila. Zimenezi ni mphatso za mtengo wapatali zocokela kwa Yehova. (Yes. 65:13; Maliko 10:​29, 30) Zimaonetsa kuti Yehova amasamala za ife. (Yes. 49:​14-16) Ndipo zimatipatsanso cifukwa comudalila.

11. N’ciyani cinathandiza mlongo Aida kugonjetsa mantha ake?

11 Mlongo Aida wa ku Senegal, anaona mmene Yehova anamuthandizila panthawi ya mavuto. Pokhala mwana woyamba, makolo ake anali kumuyembekezela kukhala na ndalama zambili kuti azidzisamalila yekha na kuwasamalila. Koma atapeputsa moyo wake kuti ayambe upainiya, mlongo Aida anayamba kupezana na mavuto a zacuma. A m’banja lake anakhumudwa naye ndipo anayamba kumunenela zoipa. Iye anati: “N’naopa kuti nidzalephela kuthandiza makolo anga, komanso kuti onse adzanikana, n’nafika ngakhale poimba Yehova mlandu polola zinthu kuipa mpaka pamenepo.” Ndiyeno atamvetsela nkhani pa msonkhano, anakamba kuti, “mkambi anatikumbutsa kuti Yehova amadziŵa mavuto onse omwe timakumana nawo. Kupitila mu upangili wocokela kwa akulu komanso ena, pang’ono-m’pang’ono n’nafika potsimikiza cakuti Yehova amanikonda. N’nayamba kupemphela kwa Yehova nili na cidalilo, ndipo n’nali kupeza mtendele wa mu mtima nikaona mapemphelo anga akuyankhidwa.” M’kupita kwa nthawi, mlongo Aida anapeza nchito imene inam’thandiza kudzisamalila pocita upainiya, komanso kuthandiza makolo ake na anthu ena. Pamapeto pake anati, “naphunzila kudalila Yehova kwatunthu. Tsopano nikapemphela, nkhawa zanga zonse zimathelatu.”

KODI YEHOVA ADZACITA CIYANI M’TSOGOLO?

12. Malinga na Salimo 56:​9, kodi Davide anali wotsimikiza mtima za ciyani?

12 Ŵelengani Salimo 56:9. Vesili lionetsa njila ina imene Davide anagonjetsela mantha ake. Ngakhale kuti moyo wa Davide unali ukali pa ciopsezo, iye anali kusinkhasinkha pa zinthu zimene Yehova anali kudzamucitila. Anali kudziŵa kuti Yehova adzamupulumutsa pa nthawi yoyenela. Ndi iko komwe, Yehova anali atanena kuti Davide adzakhala mfumu yotsatila ya Isiraeli. (1 Sam. 16:​1, 13) Kwa Davide, zimene Yehova analonjeza zinali ngati zakwanilitsika kale.

13. Kodi tingakhale na cidalilo cotani mwa Yehova?

13 Kodi Yehova walonjeza kuti adzakucitilani ciyani? Sitiyembekezela Yehova kutiikila chinga ku mavuto onse. c Ngakhale n’telo, mavuto alionse omwe amatigwela pali pano, Yehova adzawathetsa m’dziko latsopano likubwelalo. (Yes. 25:​7-9) Ndife otsimikiza kuti Mlengi wathu ali nazo mphamvu zoukitsa akufa, kuticilitsa, komanso kucotsa anthu onse otsutsa.—1 Yoh. 4:4.

14. Kodi tingasinkhesinkhe pa zinthu ziti?

14 Mukakhala na mantha, muzisinkhasinkha zimene Yehova adzacita m’tsogolo. Ganizilani mmene mudzamvele Satana akadzacotsedwapo, anthu oipa akadzaloŵedwa m’malo na anthu olungama, komanso pamene kupanda ungwilo kuzikazimililika tsiku lililonse. Msonkhano wa cigawo wa mu 2014 unali na citsanzo coonetsa zimene tingacite posinkhasinkha za ciyembekezo cathu ca za m’tsogolo. Tate anakambilana na banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:​1-5 likanalembedwela cikanakhala kuti linali kulosela mmene Paradaiso adzakhalile. Analiŵelenga motele: “Masiku a m’dziko latsopano adzakhala nthawi yapadela komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambila Mulungu, odzicepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvela makolo, oyamika, okhulupilika, okonda acibale awo, ofuna kugwilizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalilika, oganizila ena, osadzitukumula, ndiponso osanyada, okonda Mulungu m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odzipelekadi kwa Mulungu, anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambilana nawo a m’banja lanu kapena alambili anzanu za mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano?

15. Ngakhale kuti mlongo Tanja anali na mantha, n’ciyani cinam’thandiza kuwagonjetsa?

15 Mlongo wina wa kumpoto kwa Macedonia, dzina lake Tanja, anagonjetsa mantha ake mwa kusinkhasinkha pa madalitso a m’tsogolo. Makolo ake sanali kufuna olo pang’ono kuti aziphunzila Baibo. Iye anati: “Zinthu zina zimene n’nali kuopa kuti zingacitike, zinacitikadi. Amayi anali kunimenya nthawi zonse nikapita ku misonkhano. Makolo anga ananiopseza kuti adzanipha nikakhala wa Mboni za Yehova.” Pothela pake, makolo ake anamupitikitsa pa khomo. Ndiyeno anatani? Iye anati: “Ninaika maganizo anga pa cimwemwe cimene nidzakhala naco kwamuyaya nikakhalabe wokhulupilika. N’naganizilanso mmene Yehova anganifupile m’dziko latsopano pa cinthu ciliconse cimene ningataye pa nthawi ino, komanso mmene tidzaiŵalile zinthu zonse zoipa.” Mlongo Tanja anakhalabe wokhulupilika. Ndipo mwa thandizo la Yehova, anapeza malo okhala. Pano tikamba, iye anakwatiwa kwa m’bale wokhulupilika, ndipo akutumikila pamodzi mosangalala mu utumiki wa nthawi zonse.

LIMBIKITSANI CIKHULUPILO CANU PALI PANO

16. N’ciyani cingatithandize kukhalabe olimba mtima pamene tiona kukwanilitsika kwa zinthu zoloseledwa pa Luka 21:​26-28?

16 Pa cisautso cacikulu, anthu ambili “adzakomoka cifukwa ca mantha.” Koma anthu a Yehova adzaimabe nji, ndipo adzakhalabe olimba mtima. (Ŵelengani Luka 21:​26-28.) Sitidzacita mantha cifukwa ciyani? Cifukwa tidzakhala titaphunzila kale kudalila Yehova. Mlongo Tanja, amene tamuchula uja anati, zinthu zimene anakumana nazo m’mbuyomo, zikum’thandiza kuyang’anizana na mikhalidwe yovuta pali pano. Anakamba kuti: “Nadziŵa kuti Yehova angathetse mavuto alionse amene tingakumane nawo na kutidalitsa. Nthawi zina zingaoneke monga anthu ali na mphamvu zonse pa ife. Koma zenizeni n’zakuti Yehova ndiye walolela zimenezo, ndipo ali na mphamvu kuposa iwo. Conco olo mavuto akule bwanji, iwo adzatha.”

17. Kodi lemba la caka ca 2024 lidzatithandiza bwanji? (Onani cithunzi pacikuto.)

17 Masiku ano pali zinthu zambili zimene zingaticititse mantha. Monga anacitila Davide, nafenso tisalole mantha kutifooketsa. Lemba la caka ca 2024 ni pemphelo la Davide kwa Yehova lakuti: “Ine ndidzadalila inu, tsiku lililonse limene ndingacite mantha.” (Sal. 56:3) Buku lina lofotokozela Baibo linati, Davide “sanali kungoganizila zinthu zimene zikanamucititsa mantha kapena za mavuto ake. M’malo mwake, anali kuika maganizo ake pa amene akanamupulumutsa.” Muziganizila lemba lathu la caka miyezi ikubwelayi, maka-maka pokumana na zinthu zocititsa mantha. Muzipatula nthawi yosinkha-sinkha zimene Yehova anacita kumbuyo, zimene akucita pali pano, komanso zimene adzacita m’tsogolo. Mukatelo, inunso mofanana na Davide, mudzanena kuti: “Ine ndimadalila Mulungu, sindidzaopa.”—Sal. 56:4.

Mlongo akusinkhasinkha lemba la caka atagwedwa tsoka la cilengedwe (Onani ndime 17)

KODI MUNGAWAGONJETSE BWANJI MANTHA POGANIZILA . . .

  • zimene Yehova anacita kumbuyoku?

  • zimene akucita pali pano?

  • zimene adzacita m’tsogolo?

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

a Mungapeze mfundo zolimbikitsa cikhulupililo pa jw.org mwa kulemba mu danga lofufuzila mawu akuti “tsanzirani cikhulupiriro cawo” kapena “zocitika”. Mu JW Library®, mungapeze nkhanizi pansi pa kamutu kakuti article series zolembedwa kuti “Mbiri ya Mboni za Yehova Zosiyanasiyana” kapena “Tsanzirani Cikhulupirilo Cawo” m’Chichewa.

b Maina ena asinthidwa.

d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Davide anaganizila mmene Yehova anam’patsila mphamvu kuti aphe cimbalangondo, mmene anam’patsila ulangizi wothandiza kupitila mwa Ahimeleki, komanso mmene anali kudzamuikila kukhala mfumu.

e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale amene anamangidwa cifukwa ca cikhulupililo cake akusinkhasinkha mmene Yehova anamuthandizila kuleka kukoka fodya, mmene akumulimbikitsila kupitila m’makalata ocokela kwa okondeka ake, komanso mmene adzamupatsile moyo wosatha m’Paradaiso.