Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 2

NYIMBO 19 Mgonelo wa Ambuye

Kodi Mwalikonzekela Tsiku Lofunika Kwambili M’caka?

Kodi Mwalikonzekela Tsiku Lofunika Kwambili M’caka?

“Muzicita izi pondikumbukila.”LUKA 22:19.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuona cifukwa cake cikumbutso ni cocitika capadela, mmene tingacikonzekelele, komanso mmene tingathandizile ena kupezekapo.

1. N’cifukwa ninji tsiku la Cikumbutso ndilo tsiku lapadela m’caka? (Luka 22:​19, 20)

 KWA anthu a Yehova, tsiku lokumbukila imfa ya Khristu ndilo tsiku lofunika kwambili m’caka. Ni cocitika cokhaco cimene Yesu mwacindunji analamula otsatila ake kuti azicita. (Ŵelengani Luka 22:​19, 20.) Timaciyembekezela mwacidwi Cikumbutso pa zifukwa zingapo. Tiyeni tikambilaneko zina za izo.

2. N’cifukwa ciyani timayembekezela mwacidwi tsiku la Cikumbutso?

2 Cikumbutso cimatithandiza kuganizila kufunika kwa dipo. Cimatikumbutsa njila zoonetsela kuti timayamikila nsembe ya Yesu. (2 Akor. 5:​14, 15) Cimapelekanso mwayi wakuti ‘tilimbikitsane’ na abale na alongo athu. (Aroma 1:12) Caka ciliconse, anthu ena ozilala amapezekapo. Ena amalimbikitsidwa kubwelela kwa Yehova cifukwa colandilidwa mwacikondi. Cifukwa ca zimene amaona na kumva, anthu ambili acidwi amasonkhezeledwa kuyamba kuyenda pa njila ya ku moyo. Ndiye cifukwa cake Cikumbutso cili capadela kwa ife!

3. Kodi Cikumbutso cimaligwilizanitsa motani pa ubale wathu wa pa dziko lonse? (Onaninso cithunzi)

3 Ganizilaninso mmene Cikumbutso cimatigwilizanitsila pa ubale wathu wa pa dziko lonse. Mboni za Yehova zimasonkhana pa dziko lonse lapansi pamene dzuŵa likukaloŵa. Tonsefe timamvetsela nkhani yogogomeza kufunika kwa dipo. Timaimba nyimbo ziŵili zotamanda Mulungu, kupatsilana ziphiphilitso, komanso kukamba “ameni” wocokela pansi pa mtima ku mapemphelo anayi. M’maola 24, mipingo yonse imakhala itatsatila ndondomeko imeneyi. Tangoganizilani cimwemwe cimene Yehova na Yesu amakhala naco potiona tikuwalemekeza mwa njila imeneyi!

Cikumbutso cimatigwilizanitsa pa ubale wathu wa pa dziko lonse (Onani ndime 3) f


4. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane mafunso aya: Tingakonzekeletse bwanji mitima yathu poyembekezela Cikumbutso? Tingathandizile bwanji ena kupindula naco Cikumbutso? Nanga ozilala tingawathandize bwanji? Mayankho pa mafunso amenewa adzatithandiza kukonzekela cocitika copatulika cimeneci.

KUKONZEKELETSA MITIMA YATHU KAAMBA KA CIKUMBUTSO

5. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kusinkhasinkha za dipo? (Salimo 49:​7, 8) (b) Munaphunzila ciyani mu vidiyo yakuti N’cifukwa Ciyani Yesu Anafa?

5 Imodzi mwa njila zofunika kwambili imene tingakonzekeletsele mitima yathu poyembekezela Cikumbutso, ni kuganizila kufunika kwa nsembe ya Yesu Khristu. Sizikanatheka mwa ife tokha kudzipulumutsa ku ucimo na imfa. (Ŵelengani Salimo 49:​7, 8; onaninso vidiyo yakuti N’cifukwa Ciyani Yesu Anafa?) a Yehova na Yesu anatayilapo zambili kuti apange makonzedwe akuti Yesu abwele pa dziko lapansi kudzapeleka moyo wake nsembe kaamba ka ife. (Aroma 6:23) Kuganizila kwambili zimene Yehova na Yesu anadzimana kaamba ka ife, kudzatithandiza kuyamikila kwambili mphatso ya dipo. Tidzakambilanako zocepa cabe mwa zinthu zambili zimene Yehova na Yesu anadzimana. Koma coyamba, kodi panafunikila ciyani kuti dipo lipelekedwe?

6. Kodi kupeleka dipo kunalowetsamo ciyani?

6 Dipo ni malipilo amene amapelekedwa kuti munthu awombole cinacake. Munthu woyamba, Adamu, anali wangwilo atalengedwa. Koma iye atacimwa, anadzitayila mwai wokhala na moyo kwamuyaya komanso wa ana ake. Kuti awombole zimene Adamu anataya, Yesu anapeleka moyo wake wangwilo monga nsembe. Yesu ali pa dziko lapansi, “sanacite chimo, ndipo m’kamwa mwake simunapezeke cinyengo” ciliconse. (1 Pet. 2:22) Panthawi ya imfa yake, moyo wake wangwilo unafanana ndendende na umene Adamu anataya.—1 Akor. 15:45; 1 Tim. 2:6.

7. Ni mayeselo otani amene Yesu anakumana nawo ali padziko lapansi?

7 Ali pano pa dziko lapansi, Yesu anakhalabe womvela kwa Atate wake wa kumwamba m’zinthu zonse. Anatelo mosasamala kanthu za kuculuka kwa mavuto amene anakumana nawo. Yesu ali mwana, anali kumvela makolo ake aumunthu opanda ungwilo ngakhale kuti iye anali wangwilo. (Luka 2:51) Atafika pa unyamata, anafunika kugonjetsa zisonkhezelo zilizonse zimene zikanamupangitsa kukhala wosamvela makolo kapena wosakhulupilika kwa Yehova. Yesu atakula, analimbana na mayeselo osiyanasiyana ocokela kwa Satana, kuphatikizapo ciyeso comuuza mwacindunji kuti aleke kukhala wokhulupilika kwa Mulungu. (Mat. 4:​1-11) Satana anali wotsimikiza mtima kucimwitsa Yesu kuti asathe kupeleka dipo.

8. Ni mavuto ena ati amene Yesu anapilila?

8 Yesu anakumananso na mayeso ena pocita utumiki wake pa dziko lapansi. Anazunzidwa, ndipo moyo wake unali paciopsezo. (Luka 4:​28, 29; 13:31) Anali kupililanso zophophonya za otsatila ake. (Maliko 9:​33, 34) Pozengedwa mlandu kuti aphedwe, anazunzidwa na kunyozedwa. Ndipo anaphedwa m’njila yoŵaŵa komanso yonyanzitsa kwambili. (Aheb. 12:​1-3) Anapilila yekha mavuto othela popanda Yehova kum’tetezo. bMat. 27:46.

9. Timamva bwanji tikaganizila nsembe ya Yesu? (1 Petulo 1:8)

9 Kunena zoona, Yesu anavutika zedi kuti apeleke dipo. Ndipo tikaganizila zinthu zimene Yesu anapitamo modzipeleka kaamba ka ife, cikondi cathu pa iye cimakula.—Ŵelengani 1 Petulo 1:8.

10. Kodi imfa ya Yesu inamukhudza bwanji Yehova?

10 Nanga kodi Yehova anadzimana ciyani kuti Yesu apeleke dipo? Ubale uli pakati pa Yehova na Yesu ni wolimba ngako kuposa umene uli pakati pa tate na mwana wake. (Miy. 8:30) Ndiye ganizilani mmene cinamuŵaŵila Yehova, kuona Yesu akupilila mavuto ambili pa dziko lapansi. Mosakaikila, cinamuŵaŵa ngako Yehova kuona Mwana wake akuzunzidwa, kukanidwa, na kuvutitsidwa.

11. Pelekani citsanzo coonetsa mmene Yehova anamvela poona Yesu akuphedwa.

11 Kholo lililonse limene linataikilidwapo mwana mu imfa limadziŵa bwino cisoni cimene imfa ya mwana imabweletsa. Ngakhale kuti tili na ciyembekezo camphamvu pa nkhani ya ciukitso, cimatiŵaŵabe kwambili wokondedwa wathu akamwalila. Citsanzoci citithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvela poona Mwana wake wokondeka akuzunzidwa na kuphedwa mu 33 C.E. cMat. 3:17.

12. Kodi tingacite ciyani poyembekezela Cikumbutso?

12 Poyembekezela Cikumbutso, khazikitsani pulogalamu kuti muphunzile zambili zokhudza dipo pa phunzilo la inu mwini kapena pa Kulambila kwa Pabanja. Seŵenzetsani buku Lofufuzila la Mboni za Yehova kapena zida zina zophunzilila Baibo kuti muimvetse bwino kwambili nkhaniyo. d Cina, muzitsatila ndandanda ya kuŵelenga Baibo ya pa Cikumbutso imene ili mu Kabuku ka Misonkhano ka Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu. Ndipo pa tsiku la Cikumbutso osaiŵala kutamba pulogalamu yapadela ya Kulambila kwa M’maŵa. Tikakonzekeletsa maganizo athu kaamba ka Cikumbutso, tidzakhala pa malo abwino othandiza ena kuti akapindule naco.—Ezara 7:10.

THANDIZANI ENA KUPINDULA

13. N’cinthu coyamba citi cimene tingacite kuti tithandize ena kupindula na Cikumbutso?

13 Kodi tingathandize bwanji ena kupindula naco Cikumbutso? Njila yoyamba, ni kuwaitanila. Kuwonjezela pa aja amene timakambilana nawo nthawi zonse mu utumiki, tingalembe maina ya anthu ena amene tidziŵa kuti tiwaitanile. Tingaphatikizepo acibale athu, anzathu a ku nchito, a kusukulu, na ena. Ngakhale tilibe tumapepala twambili toitanila ku Cikumbutso, tingawatumizile linki pa cipangizo. Mungadabwe na kuculuka kwa anthu omwe angapezekepo.—Mlal. 11:6.

14. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti kuitanila munthu mwacindunji kuli na cikoka.

14 Kuitanila munthu mwacindunji kuli na cikoka. Tsiku lina, mlongo wa m’banja la zipembedzo zosiyana, anadabwa pamene mwamuna wake anamuuza mosangalala kuti akufuna kupita ku Cikumbutso. Anadabwa cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zambili m’mbuyomo, mlongoyo anali kulimbikitsa mwamuna wake kuti apezeke ku Cikumbutso koma sizinaphule kanthu. N’cifukwa ciyani anafuna kupita ulendo uno? Mwamunayo anati, “ninaitanidwa mwacindunji.” Anafotokoza kuti mkulu wina m’delalo amene anali kudziŵana naye anamupatsa kapepala ka ciitanilo. Mwamunayo anapezeka pa Cikumbutso caka cimeneco, komanso zaka zambili zotsatila.

15. Tizikumbukila ciyani poitanila anthu ku Cikumbutso?

15 Kumbukilani kuti anthu omwe tawaitanila angakhale na mafunso—maka-maka ngati n’kuyamba kupezekapo pa misonkhano yathu. Tingacite bwino kuganizila mafunso amene angafunse na kukonzekela kuwayankha. (Akol. 4:6) Mwacitsanzo, ena angafunse kuti: ‘Kodi Cikumbutso cimacitika motani?’ ‘Kodi cidzatenga utali wotani?’ ‘Kodi ni kuvala motani?’ ‘Kodi n’kulipila poloŵa?’ ‘Kodi kudzakhala mbale ya pelekani-pelekani?’ Tikaitanila munthu ku Cikumbutso, tizimufunsa kuti, “Kodi muliko na mafunso alionse?” Ndiyeno yankhani mafunso onse amene munthuyo ali nawo. Tingamutambitsenso mavidiyo akuti Kumbukilani Imfa ya Yesu komanso N’ciyani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? kuti timuthandize kumvetsa mmene misonkhano yathu imacitikila. Tingapeze mfundo zingapo zabwino zimene tingakambilane nawo m’phunzilo 28 la buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

16. Ni mafunso ena ati amene anthu opezeka pa Cikumbutso angakhale nawo?

16 Anthu acidwi akapezeka ku Cikumbutso, amakhalanso na mafunso ena. Angadzifunse kuti n’cifukwa ciyani anthu ocepa cabe (ngati analipo) ni amene anadya ziphiphilitso. Angafunsenso kuti timacita kangati Cikumbutso pa caka. Komanso angafune kudziŵa ngati misonkhano yonse ya Mboni za Yehova imacitika mwa njila imeneyi. Ngakhale kuti nkhani ya Cikumbutso imafotokozako zina mwa mfundozi, anthu amene n’kuyamba kupezekapo angafunike kuwafotokozela mwatsatanetsatane. Nkhani ya pa jw.org yakuti “N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?” ingakuthandizeni kuyankha ena mwa mafunso amenewa. Tidzacita zonse zotheka—Cikumbutso cisanacitike, cili mkati, komanso cikatha—kuti tithandize anthu a “maganizo abwino” kupindula na cocitika cimeneci.—Mac. 13:48.

KUTHANDIZA OZILALA

17. Kodi akulu angawathandize bwanji ozilala? (Ezekieli 34:​12, 16)

17 Kodi akulu angawathandize motani anthu ozilala pa nyengo ya Cikumbutso? Mwa kuwaonetsa cikondi. (Ŵelengani Ezekieli 34:​12, 16.) Cikumbutso cisanacitike, onetsetsani kuti mwafikila ozilala ambili mmene mungathele. Aonetseni kuti mumawakonda, komanso kuti ndinu wofunitsitsa kuwathandiza m’njila iliyonse. Aitanileni ku Cikumbutso. Ndipo akabwela, alandileni na manja aŵili. Pambuyo pa Cikumbutso, pitilizani kukambilana na abale na alongo okondedwa amenewa, komanso kupeleka thandizo lililonse lauzimu limene angafunikile kuti abwelele kwa Yehova.—1 Pet. 2:25.

18. Kodi tonsefe tingawathandize motani ozilala? (Aroma 12:10)

18 Onse mu mpingo angathandize ozilala amene apezeka pa Cikumbutso. Motani? Mwa kucita nawo mwacikondi, mokoma mtima, komanso mwaulemu. (Ŵelengani Aroma 12:10.) Kumbukilani kuti mwina sicinali capafupi kwa nkhosa zokondedwa zimenezi kubwelanso ku Cikumbutso. Mwina anali na mantha akuti sadzalandilidwa bwino. e Conco pewani kuwafunsa mafunso ocititsa manyazi, kapena kukamba zinthu zimene zingawakhumudwitse. (1 Ates. 5:11) Abale na alongo athu amenewa ni okhulupilila anzathu. Ndipo timakondwela kulambilanso nawo capamodzi!—Sal. 119:176; Mac. 20:35.

19. Timapeza mapindu anji cifukwa cokumbukila imfa ya Yesu?

19 N’zosadabwitsa kuti Yesu anapanga makonzedwe akuti tizicita Cikumbutso caka ciliconse. Tikapezekapo, timapindula ife eni komanso kupindulitsa ena. (Yes. 48:​17, 18) Cikondi cathu pa Yehova na Yesu cimakula. Timaonetsa kuti timayamikila zimene iwo aticitila. Timalimbikitsa mgwilizano na alambili anzathu. Cina, tingathandizenso ena mmene angapindulile na madalitso obwela cifukwa ca dipo. Conco, tiyeni ticite zonse zotheka kuti tikhale ocikonzekela bwino Cikumbutso ca caka cino—cocitika capadela m’caka!

MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi mungakonzekeletse bwanji mtima wanu kaamba ka Cikumbutso?

  • Tingathandize bwanji ena kupindula naco Cikumbutso?

  • Kodi tingawathandize bwanji ozilala?

NYIMBO 18 Tiyamikila Cifukwa ca Dipo

a Kuti mupeze nkhani na mavidiyo ochulidwa m’nkhani ino pitani pa jw.org na kulemba mutu wake m’danga lofufuzila.

b Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Mlonda ya April 2021.

d Onani danga lakuti “ Zimene Mungafufuze.”

e Onani zithunzi komanso danga lakuti “ Kodi Mpingo Unawalandila Motani?” M’bale wozilala akuopa kuloŵa m’Nyumba ya Ufumu, koma wagonjetsa mantha amenewo. Walandilidwa bwino, ndipo akusangalala na mayanjano.

f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pomwe anthu a Yehova akucita Cikumbutso m’dela lina, abale na alongo awo m’mbali zina za dzikoli akukonzekela cocitika cimeneci.