Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumacita Zinthu na Akazi Mmene Yehova Amacitila Nawo?

Kodi Mumacita Zinthu na Akazi Mmene Yehova Amacitila Nawo?

TILI na mwayi wotumikila Yehova pamodzi na akazi ambili okhulupilika. Ndipo timawakonda na kuyamikila aliyense wa alongo akhama amenewa! a Cotelo, inu abale, yesetsani kumacita nawo mokoma mtima, mwacilungamo, komanso mwaulemu. Koma pokhala opanda ungwilo, nthawi zina timalephela kucita zimenezi. Ndipo abale ena amapezanso vuto lina kuwonjezela pa zimenezi.

Amuna ambili anakulila ku madela kumene amaona akazi osafunika kwenikweni. Mwacitsanzo, m’bale Hans, woyang’anila dela ku Bolivia, anati: “Kumene tikhala, amuna ena analeledwa m’cikhalidwe cimene cimaphunzitsa kuti amuna ayenela kucita zinthu modzikuza na kuona akazi kuti ni otsika powayelekezela na amuna.” b M’bale Shengxian, mkulu mu mpingo ku Taiwan, anati: “Kumene nikhala, akazi sayenela kupeleka lingalilo kwa mwamuna. Ngati mwamuna wachula lingalilo la mkazi pa nkhani inayake, anzake amamuona kuti saganiza bwino.” Amuna ena amaonetsa tsankho kwa akazi m’njila zinanso. Mwacitsanzo, iwo amakamba nthabwala zoseleula akazi ni otsika kapena osafunika.

Bwino lake n’lakuti mwamuna aliyense ali na ufulu wosankha kuganiza mosiyana na cikhalidwe ca kwawo. Ndipo akhoza kusiya maganizo akuti amuna ni ofunika kwambili kuposa akazi. (Aef. 4:​22-24) Izi zingatheke potengela citsanzo ca Yehova. M’nkhani ino tiona mmene Yehova amacitila nawo akazi na kuona mmene abale angatengele citsanzo cake. Tionenso mmene akulu angakhalile patsogolo poonetsa ulemu kwa alongo.

MMENE YEHOVA AMACITILA NAWO AKAZI

Yehova anapeleka citsanzo cabwino ngako ca mocitila nawo akazi. Monga Tate wacifundo, iye amakonda anthu onse. (Yoh. 3:16) Ndipo alongo okhulupilika ali monga ana akazi a mtengo wapatali kwa iye. Onani njila zotsatilazi zimene Yehova amaonetsela kuti amalemekeza akazi.

Sawasala. Yehova analenga amuna na akazi m’cifanizilo cake. (Gen. 1:27) Sikuti analenga amuna kukhala na nzelu komanso maluso kuposa akazi. Ndipo sakondela amuna. (2 Mbiri 19:7) Analenga amuna na akazi na nzelu zofanana kuti azitha kumvetsa coonadi ca m’Baibo, komanso kuti azitha kuonetsa makhalidwe ake abwino. Ndiponso Yehova amaona kuti amuna na akazi amakhala okhulupilika mofanana—kaya ciyembekezo cawo n’codzakhala na moyo kwamuyaya m’paradaiso pa dziko lapansi kapena n’cokatumikila monga mafumu komanso ansembe kumwamba. (2 Pet. 1:1) Conco, n’zoonekelatu kuti Yehova sasala akazi.

Amawamvetsela. Yehova amasamala za mmene akazi amamvela, komanso za zofunikila zawo. Mwacitsanzo, iye anamvetsela mapemphelo a Rakele na Hana ndipo anacitapo kanthu. (Gen. 30:22; 1 Sam. 1:​10, 11, 19, 20) Cina, Yehova anauzila olemba Baibo kuphatikizamo nkhani za amuna omwe anamvela akazi. Mwacitsanzo, Abulahamu anatsatila malangizo a Yehova omuuza kuti amvele mkazi wake, Sara. (Gen. 21:​12-14) Nayenso Mfumu Davide anamvela malangizo ya Abigayeli. Ndipo iye anazindikila kuti ni Yehova amene anatuma Abigayeli kuti abwele kudzalankhula naye. (1 Sam. 25:​32-35) Ndiponso Yesu, amene amaonetsa bwino kwambili makhalidwe ya Atate wake, anamvela kwa amayi ake, Mariya. (Yoh. 2:​3-10) Zitsanzo izi zionetsa kuti njila imodzi imene Yehova amaonetsela ulemu kwa akazi ni kuwamvetsela.

Amawadalila. Mwacitsanzo, Yehova anadalila Hava kuti athandizile pa nchito yosamalila dziko lonse lapansi. (Gen. 1:28) Mwakutelo, anaonetsa kuti sanali kuona Hava kukhala wotsika kwa mwamuna wake, Adamu, koma anali kumuona ngati mthandizi wake womuyenelela. Yehova anadalilanso aneneli aakazi Debora na Hulida kuti azilangiza anthu ake, kuphatikizapo mfumu komanso wansembe. (Ower. 4:​4-9; 2 Maf. 22:​14-20) Masiku anonso Yehova wapatsa akazi a Cikhristu mwayi wogwila nchito yake. Alongo okhulupilika amenewo amatumikila monga ofalitsa, apainiya, komanso amishonale. Amathandizilanso pa nchito yopanga mapulani, kumanga, komanso kukonzanso Nyumba za Ufumu, na maofesi a nthambi. Ena amatumikila pa Beteli, ena m’maofesi omasulila. Alongo amenewa ali ngati khamu lalikulu limene Yehova akusonkhanitsa kuti akwanilitse cifunilo cake. (Sal. 68:11) N’zoonekelatu kuti Yehova saona akazi kukhala ofooka, kapena otsika.

ZIMENE ABALE ANGACITE KUTI AZIONA AKAZI MMENE YEHOVA AMAWAONELA

Kuti ife abale tidziŵe ngati timacita na alongo mmene Yehova amacitila nawo, tiyenela kusanthula maganizo athu na zocita zathu moona mtima. Koma tifunikila thandizo kuti ticite zimenezi. Monga mmene makina ounikila ziwalo angatithandizile kuona vuto la mtima wa munthu, nalonso bwenzi labwino, komanso Mawu a Mulungu, angatithandize kuzindikila maganizo alionse olakwika amene tingakhale nawo mkati mwathu. Tingatani kuti tilandile thandizo limeneli?

Funsani bwenzi labwino. (Miy. 18:17) Tingacite bwino kufunsa bwenzi lodalilika limene ni lokoma mtima, komanso loganiza bwino mafunso ngati awa: “Muona kuti nimacita motani kwa alongo? Kodi amaona kuti nimawalemekeza? Kodi pali zimene niyenela kuwongolela pambali imeneyi?” Ngati mnzanuyo wachula zinthu zina zimene muyenela kuwongolela musapeleke zifukwa zodzikhululukila, koma khalani wofunitsitsa kupanga masinthidwe oyenela.

Muziŵelenga Mawu a Mulungu. Njila yabwino koposa imene tingadziŵile ngati timacita moyenela na alongo, ni kuunika maganizo na zocita zathu ngati zigwilizana na zimene Mawu a Mulungu amanena. (Aheb. 4:12) Poŵelenga Baibo, timapeza amuna omwe anacita zinthu moyenela kwa akazi, komanso amene sanatelo. Tingayelekezele zocita zawo. Kuwonjezela apo, kuyelekezela mavesi a m’Baibo kungatithandize kupewa kuseŵenzetsa Malemba m’njila yolakwika pofuna kupeleka cifukwa codzikhululukila na mmene timacitila nawo zinthu. Mwacitsanzo, malinga na 1 Petulo 3:​7, mkazi ayenela kupatsidwa “ulemu monga ciwiya cosalimba”. c Kodi izi zitanthauza kuti iye ni wofooka—wopeleŵela m’kaganizidwe—pomuyelekezela na mwamuna? Kutalitali! Yelekezelani mawu a Petulo na zimene zili pa Agalatiya 3:​26-29. Imati, Yehova anasankha amuna na akazi kuti akalamulile na Yesu kumwamba. Tikamaŵelenga Mawu a Mulungu na kufunsila maganizo kwa mnzathu za mmene timacitila nawo akazi, tidzaphunzila kupeleka ulemu woyenela kwa alongo athu.

MMENE AKULU AMAWACITILA ULEMU ALONGO

Abale mu mpingo angayambe kucitila ulemu alongo potengela citsanzo ca akulu acikondi. Kodi akulu amakhala angakhale bwanji citsanzo cabwino polemekeza alongo? Onani njila zotsatilazi.

Amawayamikila. Mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino coyenela kutengela. Anayamikila alongo angapo m’kalata imene analembela mpingo wa ku Roma. (Aroma 16:12) Mosakaikila, alongo anakondwela ngako pomwe kalatayo inali kuŵelengedwa mu mpingo. Mofananamo, akulu mwacikondi amayamikila alongo pa makhalidwe awo abwino, komanso cifukwa ca nchito zimene amagwila mu utumiki wa Yehova. Izi zimapangitsa alongo kumva kuti amayamikilidwa komanso kulemekezedwa kwambili. Mawu olimbikitsa a mkulu angakhale mawu oyenela a pa nthawi yake amene alongo angafunike kumva pomwe apitilizabe kutumikila Yehova mokhulupilika.—Miy. 15:23.

Ayamikileni

Poyamikila alongo, akulu amakamba moona mtima komanso kuchula zimene akuyamikilazo. Cifukwa ciyani? Mlongo wina dzina lake Jessica anati: “Zimamveka bwino m’bale akauza mlongo kuti ‘mwagwila nchito.’ Koma timamva bwino zedi m’bale akachula cimene akuyamikila monga, kuphunzitsa ana athu kukhala cete pa misonkhano kapena kupita kukatenga wophunzila Baibo kuti abwela ku misonkhano.” Ngati mkulu ayamikila alongo pa zimene iwo acita, zimawapangitsa kumva kuti ni ofunika komanso a mtengo wapatali mumpingo.

Amawamvetsela. Akulu odzicepetsa amadziŵa kuti sindiwo okha amakhala na malingalilo abwino. Akulu otelo amapempha alongo kuti anenepo maganizo awo, ndipo amawamvetsela mwachelu. Mwakutelo, akulu amalimbikitsa alongo, ndipo iwonso amapindula. Motani? Mkulu wina amene akutumikila pa Beteli, dzina lake Gerardo, anati: “Napeza kuti kufunsila maganizo ya alongo kumanithandiza kugwila bwino nchito yanga. Kambili, ena agwila nchito inayake kwa nthawi yaitali kuposa abale ambili.” M’mipingo yambili, alongo oculuka amatumikila monga apainiya. Conco adziŵa bwino anthu komanso gawo la mpingo. Mkulu wina dzina lake Bryan anati: “Alongo athu ali na zambili zimene angacite m’gulu lathu. Conco pindulani na kudziŵa kwawo zinthu!”

Amvetseleni

Akulu ozindikila safulumila kusuliza maganizo ya alongo. Cifukwa ciyani? Mkulu wina dzina lake Edward anati, “Maganizo ya mlongo, komanso zimene wakumana nazo, zingathandize m’bale kumvetsa bwino nkhani inayake na nkhawa za ena.” (Miy. 1:5) Ngakhale pamene mkulu sanaseŵenzetse maganizo ya mlongo, angafunikebe kumuyamikila mlongoyo pa maganizo ake komanso kuzindikila kwake.

Amawaphunzitsa. Akulu ozindikila amapeza mipata yophunzitsa alongo. Mwacitsanzo, angaphunzitse alongo motsogozela makambilano a utumiki, kucitila nthawi pamene m’bale wobatizika sangapezeke ku makambilano. Angawaphunzitse moseŵenzetsela zipangizo kapena makina ena ake, kuti azithandiza pomanga kapena posamalila malo olambilila. Ku Beteli, oyang’anila amaphunzitsa alongo mocitila maudindo ena kuphatikizapo kukonza na kugula zinthu, kusamalila ndalama, nchito za pa kompyuta na zina zotelo. Ngati akulu aphunzitsa alongo, amaonetsa kuti amawadalila komanso kuti ni aluso.

Aphunzitseni

Alongo ambili amaseŵenzetsa zimene aphunzila kwa akulu kuti apindulitse ena. Mwacitsanzo, alongo ena amaseŵenzetsa zimene aphunzila pomanga zimango za gulu kuthandiza ena kumanganso nyumba zawo zikaonongedwa na tsoka lacilengedwe. Alongo ena amaseŵenzetsa zomwe aphunzila pa ulaliki wapoyela kuphunzitsa alongo anzawo mocitila ulalikiwu. Kodi alongo amamva bwanji akulu akawaphunzitsa zinazake? Mlongo wina dzina lake Jennifer anati: “Pogwila nchito pa Nyumba ya Ufumu inayake, woyang’anila anapatula nthawi kuti aniphunzitse nchito inayake. Pambuyo pake, iye anaona nchito imene ninagwila ndipo ananiyamikila pa nchitoyo. N’nasangalala kugwila nchito na m’baleyu cifukwa anali kunidalila komanso kunipangitsa kumva kuti ndine wofunika.”

MAPINDU OONA AKAZI MONGA A M’BANJA LATHU

Timawakonda kwambili alongo athu mmenenso Yehova amacitila! Conco timawatenga monga azilongosi a m’banja lathu. (1 Tim. 5:​1, 2) Timanyadila kwambili kutumikila nawo limodzi. Ndipo timasangalala kwambili ngati iwo aona kuti timawakonda komanso timawathandiza .Mlongo wina dzina lake Vanessa anati: “Nimayamikila kwambili Yehova cifukwa cokhala m’gulu lake, lodzala na abale otsitsimula moyo wanga.” Mlongo wina wa ku Taiwan anati: “Nimayamikila kwambili kuti Yehova, komanso gulu lake, amalemekeza kwambili akazi, komanso amamvetsa mmene timamvela. Izi zimalimbikitsa cikhulupililo canga, ndipo zimanipangitsa kuyamikila kwambili mwayi umene nili nawo wokhala m’gulu la Yehova.”

Mosakaikila, Yehova amanyadila kwambili poona amuna okhulupilika acikhristu akuyesetsa kutengela citsanzo cake pocita zinthu na akazi! (Miy. 27:11) Mkulu wina wa ku Scotland dzina lake Benjamin anati, “Dziko limaona akazi kukhala otsika kwambili. Conco ngati akazi aloŵa m’Nyumba ya Ufumu, timafuna kuti aziona zosiyana na mmene dziko limacitila.” Tiyeni tonse tiziyesetsa kutengela Yehova pocita zinthu na alongo athu mwacikondi, komanso kuwapatsa ulemu wowayenelala.—Aroma 12:10.

a M’nkhani ino, mawu akuti “alongo” akutanthauza alongo a mumpingo osati cibale ca kuthupi.

b Amuna ena amaseŵenzetsa molakwika mawu akuti “camuna” poutamanda mokokomeza. Anthu otelo amaona kuti amuna amaganiza bwino, komanso amacita bwino zinthu kuposa akazi. Iwo amaonanso kuti akazi ni anthu otsikilapo.

c Kuti mudziŵe zambili pa mawu akuti “ciwiya cosalimba,” onani nkhani yakuti “Mtengo wa ‘Cotengela Cocepa Mphamvu’” mu Nsanja ya Mlonda ya May 15, 2006, komanso yakuti “Malangizo Anzelu kwa Okwatilana” mu Nsanja ya Mlonda ya March 1, 2005.