Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Timalambila Yehova pamodzi na gulu lalikulu pa misonkhano ya mpingo, ya dela, komanso ya cigawo. Timamulambilanso monga banja komanso aliyense payekha-payekha. Pansipa pali zina mwa zinthu zimene mungacite pa phunzilo la munthu mwini komanso pa kulambila kwa pabanja:

  • Konzekelani misonkhano yampingo. Mungaphatikizepo kuimba nyimbo komanso kuthandiza aliyense m’banja kukonzekela ndemanga.

  • Ŵelengani nkhani ya m’Baibo. Kenako, onani mmene nkhaniyo yakukhudzilani kapena lembani zimene mwaphunzilapo.

  • Ŵelengani pemphelo lopezeka m’Baibo na kuona mmene lingakuthandizileni kuwongolela mapemphelo anu.

  • Onelelani vidiyo ya pa jw.org. Kenako kambilanani na ena kapena kulemba mfundo zimene mwaphunzilapo.

  • Konzekelani utumiki, mwina mungayeseze mmene muzalalikilila.

  • Onani zacilengedwe na kusinkhasinkha kapena kukambilana zimene cakuphunzitsani za Yehova. a

a Onani nkhani yakuti “Phunzilani Zambili za Yehova Poyang’ana Cilengedwe Cake” mu Nsanja ya Mlonda ya March 2023.