Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

NYIMBO 10 Tamandani Yehova, Mulungu Wathu!

“Tamandani Dzina la Yehova”

“Tamandani Dzina la Yehova”

“Inu atumiki a Yehova, mutamandeni, tamandani dzina la Yehova.”SAL. 113:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mfundo zomwe zimatilimbikitsa kutamanda dzina loyela la Yehova pa mpata ulionse umene takhala nawo.

1-2. N’ciyani cingatithandize kumvetsa mmene Yehova amamvelela pa kunenezedwa kwa dzina lake?

 YELEKEZANI kuti munthu amene mumadalila wanena zinthu zoipa zokhudza inu. Inu mudziŵa kuti nkhaniyo ni yabodza; koma ena akuikhulupilila. Coposa pamenepa, iwo akuifalitsa, ndipo anthu ambili akuikhulupilila. Kodi mungamve bwanji? Ngati mumasamala za anthu, komanso za mbili yanu, bodza limenelo lingakupangitseni kumva kuipa kwambili, si conco?—Miy. 22:1.

2 Citsanzoci, citithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvela pomwe dzina lake linaipitsidwa. Mmodzi wa ana ake auzimu ananena bodza lokhudza iye kwa mkazi woyamba, Hava. Ndipo iye analikhulupilila. Bodzalo linacititsa kuti makolo athu oyambilila apandukile Yehova. Zotsatila zake n’zakuti ucimo na imfa zinaloŵa m’banja la anthu. (Gen. 3:​1-6; Aroma 5:12) Mavuto onse amene timaona m’dzikoli—imfa, nkhondo, kuvutika—anabwela cifukwa ca bodza limene Satana anayambitsa mu Edeni. Ndipo mosapeneka konse, bodzalo linamuŵaŵa ngako Yehova, komanso zotulukapo zake. Ngakhale n’telo, Yehova sanasunge msunamo kapena kusunga cakukhosi. M’malo mwake, iye akupitilizabe kukhala “Mulungu wacimwemwe.”—1 Tim. 1:11.

3. Kodi tili na mwayi wocita ciyani?

3 Tili na mwayi wothandizila kuyeletsa dzina la Yehova mwa kutsatila lamulo ili lakuti: “Tamandani dzina la Yehova.” (Sal. 113:1) Tingatelo mwa kukamba zabwino za amene dzina loyelalo limaimila. Kodi inunso mudzatamanda dzinalo? Tiyeni tikambilane zifukwa zitatu zamphamvu zotilimbikitsa kutamanda dzina la Mulungu wathu na mtima wathu wonse.

TIMAKONDWELETSA YEHOVA TIKAMATAMANDA DZINA LAKE

4. N’cifukwa ciyani Yehova amakondwela tikamatamanda dzina lake? Fotokozani citsanzo. (Onaninso cithunzi.)

4 Timakondweletsa Atate wathu wa kumwamba ngati titamanda dzina lake. (Sal. 119:108) Kodi izi zitanthauza kuti Mulungu wamphamvu zonse ali monga anthu opanda ungwilo omwe amafunitsitsa citamando cifukwa cofuna kulimbikitsidwa? Ayi. Ganizilani citsanzo ici. Mwana wamng’ono akukumbatila atate ake mwacikondi, n’kuwauza kuti, “Nimwe atate abwino kwambili mu dziko lonse!” Tateyo wakondwela ngako ndipo wakhudzika mtima kumva zimenezi. Cifukwa ciyani? Kodi tinganene kuti tate ameneyu amadalila citamando ca mwana wake kuti amveko bwino? Ayi. Iye ni tate wolimba, ndipo amamva bwino kuona mwana wake akumuonetsa cikondi na kumuyamikila. Adziŵanso kuti makhalidwe amenewo angathandize mwanayo kukhala wacimwemwe pomwe akukula. Pa zifukwa zofananazo, Yehova amene ndiye Tate wamkulu koposa, amakondwela tikamamutamanda.

Monga mmene tate waumunthu amakondwelela mwana wake akamuonetsa cikondi na ciyamikilo, nayenso Yehova amakondwela tikatamanda dzina lake (Onani ndime 4)


5. Ni mabodza ati omwe timathandiza kutsutsa tikamatamanda dzina la Mulungu?

5 Tikamatamanda Atate wathu wa kumwamba, timathandiza kutsutsa bodza limene limatikhudza aliyense payekha-payekha. Satana amanena kuti palibe munthu angakhalile kumbuyo dzina la Mulungu mokhulupilika. Amatinso palibe munthu angakhalebe wokhulupilika poyesedwa. Amakambanso kuti tonsefe tikhoza kum’pandukila Mulungu tikaona kuti tingapindulepo kenakake tikatelo. (Yobu 1:​9-11; 2:4) Koma munthu wokhulupilika Yobu, anaonetsa kuti Satana ni wabodza. Nanga bwanji inuyo? Aliyense wa ife ali na mwayi wokhalila kumbuyo dzina la Atate wathu na kum’kondweletsa pom’tumikila mokhulupilika. (Miy. 27:11) Ni mwayi wapadela zedi kucita zimenezi!

6. Tingatengele motani citsanzo ca Mfumu Davide, komanso Alevi? (Nehemiya 9:5)

6 Kukonda Mulungu kumasonkhezela anthu okhulupilika kulemekeza dzina lake na mtima wonse. Mfumu Davide analemba kuti: “Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Ciliconse mkati mwanga, citamande dzina lake loyela.” (Sal. 103:1) Davide anadziŵa kuti kutamanda dzina la Yehova kunali kutamanda Yehova iye mwini. Dzina la Yehova limaphatikizapo mbili yake. Limatikumbutsa za makhalidwe ake abwino, komanso zocita zake zocititsa cidwi. Davide anaona dzina la Atate wake kukhala loyela, ndipo analitamanda. Anacita zimenezi na ‘ciliconse ca mkati mwake’—kutanthauza kuti na mtima wake wonse. Mofananamo, Alevi anatsogolela pa nchito yotamanda Yehova. Iwo anavomeleza modzicepetsa kuti mawu awo sakanakwanitsa kupeleka citamando coyenela kupatulika kwa dzinalo. (Ŵelengani Nehemiya 9:5.) Mosakaikila, mawu odzicepetsa acitamando amenewa, anakondweletsa mtima wa Yehova.

7. Tingamutamande motani Yehova mu utumiki, komanso m’zocita zathu za tsiku na tsiku?

7 Masiku ano, tingamukondweletse Yehova pokamba za iye mwaubwenzi, moyamikila, komanso mwacikondi. Tikakhala mu utumiki timakumbukila kuti colinga cathu cacikulu ni kukokela anthu kwa Yehova, na kuwathandiza kumuona monga Tate wacikondi mmene ifeyo timamuonela. (Yak. 4:8) Timakondwela kusonyeza anthu mmene Baibo imamufotokozela Yehova, mmene imaonetsela cikondi cake, cilungamo cake, nzelu zake, mphamvu zake, komanso makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova na kumukondweletsa pamene tiyesetsa kutengela citsanzo cake. (Aef. 5:1) Tikatelo, timakhala osiyana nawo anthu oipa a m’dzikoli. Anthu angaone kuti ndife osiyana nawo, ndipo angafune kudziŵa cifukwa cake. (Mat. 5:​14-16) Pocita nawo zinthu za tsiku na tsiku, tingawafotokozele cifukwa cake timacita zinthu zina mosiyana. Zotsatila zake n’zakuti, timakokela anthu a mitima yabwino kwa Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njila zimenezi, timakondweletsa mtima wake.—1 Tim. 2:​3, 4.

TIMAKONDWELETSA YESU TIKAMATAMANDA DZINA LA YEHOVA

8. Kodi Yesu wakhala bwanji citsanzo copambana pa kutamanda dzina la Yehova?

8 Pa zolengedwa zonse za kumwamba komanso padziko lapansi, palibe amene amadziŵa bwino Atate kuposa Yesu. (Mat. 11:27) Yesu amakonda Atate wake, ndipo n’citsanzo copambana pa kutamanda dzina la Yehova. (Yoh. 14:31) M’pemphelo limene anapeleka kwa Atate wake usiku wakuti maŵa lake adzaphedwa, iye anafotokoza utumiki wake wa padziko lapansi motele: “Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.” (Yoh. 17:26) Kodi anacita motani zimenezi?

9. Kodi Yesu anaseŵenzetsa ciyani pofotokoza momveka bwino mmene Atate wake alili?

9 Yesu anacita zambili kuposa kungouza anthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Ayuda omwe Yesu anali kuphunzitsa anali kulidziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anakhala patsogolo ‘kuwafotokozela za Mulungu.’ (Yoh. 1:​17, 18) Mwacitsanzo, Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo, komanso wacisomo. (Eks. 34:​5-7) Yesu anafotokoza coonadi cimeneci momveka bwino pomwe anakamba za fanizo la mwana woloŵelela. Bambo wa m’fanizoli ataona mwana wake wolapa “ali capatali ndithu,” anathamangila mwanayo, kumukumbatila na kum’khululukila na mtima wonse. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino cifundo ca Yehova na cisomo cake. (Luka 15:​11-32) Yesu anathandiza ena kumvetsa kuti Yehova ni Tate wotani kwenikweni.

10. (a) Tidziŵa bwanji kuti Yesu anali kuseŵenzetsa dzina lenileni la Atate wake, komanso anali kufuna kuti ena azicita cimodzimodzi? (Maliko 5:19) (Onaninso cithunzi.) (b) Kodi Yesu amafuna kuti tizicita ciyani masiku ano?

10 Mosakayikila, Yesu anafunanso kuti ena aziseŵenzetsa dzina lenileni la Atate wake. Atsogoleli ena a cipembedzo a m’nthawi imeneyo anali kunena kuti dzina la Mulungu ni lolemekezeka kwambili moti siliyenela kuchulidwa. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosazikika m’Malemba imeneyo imulepheletse kulemekeza dzina la Atate wake. Ganizilani zimene zinacitika atacilitsa munthu wogwidwa na ziŵanda m’cigawo ca Agerasa. Anthu anacita mantha kwambili, ndipo anacondelela Yesu kuti acoke. Conco, iye sanakhalise m’cigawo cimeneco. (Maliko 5:​16, 17) Ngakhale n’telo, iye anafunabe kuti anthu adziŵe dzina la Yehova m’cigawo cimeneci. Conco, anauza wocilitsidwayo kuti aziuza anthu zimene Yehova anam’citila, osati zimene Yesu anacita. (Ŵelengani Maliko 5:19.) a N’zimenenso amafuna masiku ano—kuti tidziŵikitse dzina la Atate ake pa dziko lonse lapansi! (Mat. 24:14; 28:​19, 20) Tikacita zimenezi, timakondweletsa Mfumu yathu, Yesu.

Yesu anauza munthu yemwe anamutulutsa ziŵanda kuti aziuza ena za mmene Yehova anamuthandizila (Onani ndime 10)


11. Kodi Yesu anauza otsatila ake kuti azipemphelela ciyani? Nanga n‘cifukwa ciyani mfundo imeneyi ni yofunika? (Ezekieli 36:23)

11 Yesu anali kudziŵa kuti colinga ca Yehova ni kuyeletsa dzina Lake, kucotsa citonzo ciliconse pa dzinalo. Ndiye cifukwa cake Ambuye wathu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu anadziŵa kuti iyi ndiyo nkhani yaikulu imene ikhudza cilengedwe conse. (Ŵelengani Ezekieli 36:23.) Pa zolengedwa zonse zanzelu, palibe amene wacita zambili poyeletsa dzina la Yehova kuposa Yesu. Ngakhale n’telo, adani ake atamugwila, anamuimba mlandu wakuti ananyoza Mulungu! Yesu anadziŵa bwino kuti kunyoza dzina loyela la Atate wake, kapena kulineneza linali chimo lalikulu zedi. Iye anasokonezeka maganizo kwambili poona kuti akumugwila na kumupeza na mlandu pa nkhani imeneyi. Ici ciyenela kuti ndico cinali cifukwa cacikulu comwe cinacititsa Yesu ‘kuzunzika koopsa mumtima mwake’ kutatsala maola ocepa kuti amugwile.—Luka 22:​41-44.

12. Kodi Yesu anayeletsa motani dzina la Atate wake m’njila yabwino koposa?

12 Kuti ayeletse dzina la Atate wake, Yesu anapilila mazunzo, manyozo, komanso mabodza amene anamuneneza. Iye anadziŵa kuti anamvela Atate ake m’zinthu zonse; ndipo analibe cifukwa cocitila manyazi. (Aheb. 12:2) Anadziŵanso kuti Satana anali kum’tsutsa m’nthawi zovuta zimenezo. (Luka 22:​2-4; 23:​33, 34) Satana anali wofunitsitsa kucititsa Yesu kuti ataye cikhulupililo cake mwa Mulungu. Koma iye analemba m’madzi! Yesu anaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza wankhalwe, ndiponso kuti Yehova ali na atumiki omwe amakhulupilikabe, ngakhale mayeso akhale ovuta bwanji!

13. Kodi mungaikondweletse motani Mfumu yanu imene ikulamulila?

13 Kodi mukufuna kukondweletsa Mfumu yanu imene ikulamulila? Pitilizani kutamanda dzina la Yehova, pothandiza ena kudziŵa mmene Mulungu wathu alilidi. Mukatelo, mudzakhala mukutsatila mapazi a Yesu. (1 Pet. 2:21) Mofanana ni Yesu, mumakondweletsa mtima wa Yehova na kuonetsa poyela kuti mdani wake, Satana, ni wabodza lamkunkhuniza!

TIMATHANDIZA KUPULUMUTSA MIYOYO TIKAMATAMANDA DZINA LA YEHOVA

14-15. N’zotulukapo zabwino ziti zimene zingakhalepo tikaphunzitsa anthu za Yehova?

14 Timathandiza kupulumutsa miyoyo tikatamanda dzina la Yehova. Cifukwa ciyani? Cifukwa Satana “wacititsa khungu maganizo a anthu osakhulupilila.” (2 Akor. 4:4) Zotsatila zake n’zakuti iwo amakhulupilila mabodza a Satana monga awa: kulibe Mulungu, Mulungu ali kutali kwambili na anthu, ndipo sasamala za iwo, Mulungu ni wankhanza, ndipo amazunza anthu ocita zoipa kwamuyaya. Colinga ca mabodza onsewa ni kuphimba anthu pamaso, kapena kuwononga dzina la Yehova na mbili yake, kuti anthu asakhale na cifuno comuyandikila. Koma nchito yathu imalepheletsa colinga ca Satana cimeneci. Timaphunzitsa anthu coonadi ponena za Atate wathu, kutamanda dzina la Mulungu wathu loyela. Kodi pamakhala zotulukapo zotani?

15 Coonadi ca mawu a Mulungu cili na mphamvu yaikulu. Pophunzitsa anthu za Yehova, komanso mmene iye alilidi, zotulukapo zimakhala zokondweletsa ngako! Cidima ca mabodza a Satana cimacoka m’maso mwawo pang’ono-pang’ono, ndipo amayamba kuona Atate wathu mmene ifeyo timamuonela. Amakhala na mantha aulemu akadziŵa za mphamvu zake zopanda malile. (Yes. 40:26) Amayamba kumukhulupilila poona mmene amacitila zinthu mwacilungamo. (Deut. 32:4) Amaphunzila zambili ku nzelu zake zakuya. (Yes. 55:9; Aroma 11:33) Ndipo amalimbikitsidwa akadziŵa kuti iye ndiye gwelo la cikondi. (1 Yoh. 4:8) Pamene akumuyandikila Yehova, ciyembekezo cawo codzakhala na moyo kwamuyaya monga ana ake cimakhala cotsimikizilika. Ni mwayi waukulu zedi umene tili nawo wothandiza anthu kuyandikila Atate wawo! Tikamatelo, Yehova amatitenga kukhala “anchito anzake.”—1 Akor. 3:​5, 9.

16. Kodi ena amamva bwanji akadziŵa dzina la Mulungu? Fotokozani zitsanzo.

16 Poyamba, tingangophunzitsa munthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Mfundo imeneyi ingasinthe kwambili umoyo wake. Mwacitsanzo, mayi wina dzina lake Aaliyah b anakulila m’cipembedzo comwe si ca Cikhristu. Koma iye sanali wokhutila na cipembedzo cake, ndipo anaona kuti sanali woyandikana naye Mulungu. Zimenezi zinasintha atayamba kuphunzila na Mboni. Anayamba kuona Mulungu kukhala bwenzi lake. Ndipo anadabwa kudziŵa kuti dzina la Mulungu analicotsamo m’ma Baibo ambili na kuikamo maina audindo monga Ambuye. Kudziŵa dzina la Yehova kunasintha kwambili moyo wake. Anafuula kuti: “Ha, bwenzi langa la pamtima lili na dzina!” Pamapeto pake iye anati: “Tsopano nili na mtendele woculuka mumtima mwanga, nimaona kuti ni mwayi waukulu kudziŵa dzinali.” Mwamuna wina dzina lake Steve anali woimba wodzipeleka kwambili m’cipembedzo ca Ciyuda. Sanafune kuloŵa cipembedzo ciliconse cifukwa anaona zambili zopanda cilungamo. Koma amayi ake atamwalila, ndiponso ali na cisoni, anavomela kuyamba kuphunzila Baibo na Mboni ya Yehova. Anakhudzika mtima kwambili atadziŵa dzina la Mulungu. Iye anati “N’nali n’sanamvepo dzina la Mulungu.” Anapitiliza kuti “Kwa nthawi yoyamba n’namvetsa kuti Mulungu ni weniweni, n’nayamba kumuona ngati Munthu weniweni. Pa nthawiyo n’nadziŵa kuti napezadi Bwenzi.”

17. N’cifukwa ciyani ndinu otsimikiza kupitilizabe kutamanda dzina la Yehova? (Onaninso cithunzi.)

17 Pogwila nchito yanu yolalikila na kuphunzitsa anthu, kodi mumawauzako za dzina lopatulika la Yehova? Kodi mumawathandiza kumuona mmene Iye alilidi? Mukamacita zimenezi, mumatamanda dzina la Mulungu. Pitilizani kutamanda dzina loyela la Yehova pothandiza anthu kudziŵa mtundu wa Mulungu amene iye ali. Mwa njila imeneyi mudzapulumutsa miyoyo, komanso mudzatsatila citsanzo ca Mfumu yanu, Khristu Yesu. Koposa zonse, mudzakondweletsa Atate wanu wacikondi, Yehova. Conco pitilizani ‘kutamanda dzina lake mpaka kale-kale, ndithu mpaka muyaya’!—Sal. 145:2.

Timatamanda dzina la Yehova poliphunzitsa kwa anthu, komanso powaonetsa mmene Yehova alili (Onani ndime 17)

KODI KUTAMANDA DZINA LA YEHOVA . . .

  • kumam’kondweletsa motani Yehova?

  • kumam’kondweletsa bwanji Yesu Khristu?

  • kumapulumutsa motani miyoyo?

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

a Pali umboni wamphamvu woonetsa kuti polemba vesili, Maliko anaseŵenzetsa dzina la Mulungu pogwila mawu a Yesu amenewa. Dzinali linabwezeletsedwa m’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.

b Maina ena asinthidwa.