Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 7

NYIMBO 51 Tinadzipeleka kwa Mulungu

Zimene Tikuphunzilapo kwa Anazili

Zimene Tikuphunzilapo kwa Anazili

“Iye ndi woyela kwa Yehova masiku onse a unazili wake.”NUM. 6:8.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuona mmene citsanzo ca Anazili cimatithandizila kutumikila Yehova molimba mtima, komanso na mzimu wodzimana.

1. Ni mzimu wabwino uti umene olambila Yehova aonetsa kuyambila kalekale?

 KODI mumaona ubwenzi wanu na Yehova kukhala wa mtengo wapatali? N’zosacita kufunsa! Ndipo sindinu nokha. Kuyambila nthawi zamakedzana, anthu ankhani-nkhani amaona ubwenzi wawo na Mulungu kukhala wofunika zedi. (Sal. 104:​33, 34) Anthu ambili adzimanapo zina zake kuti alambile Yehova. Umu ni mmenenso zinalili na anthu ena a mu Isiraeli wakale odziŵika kuti Anazili. Kodi iwo anali ndani? Ndipo tingaphunzile ciyani ku citsanzo cawo?

2. (a) Kodi Anazili anali ndani? (Numeri 6:​1, 2) (b) N’ciyani cinapangitsa Aisiraeli ena kusankha kukhala Anazili?

2 Mawu a Ciheberi omwe anawamasulila kuti “Mnazili” amacokela ku mawu otanthauza “Wosankhidwa,” “Wopatulidwa,” kapena “Wodzipeleka Mwapadela.” Mawu amenewa amafotokoza bwino cangu ca Aisiraeli amene anadzimana zina zake pa umoyo kuti atumikile Yehova m’njila yapadela. Cilamulo ca Mose cinalola mwamuna kapena mkazi kupanga lumbilo lina lake lapadela kwa Yehova losankha kukhala Mnazili kwa nthawi imene wadziikila. a (Ŵelengani Numeri 6:​1, 2.) Lumbilo limenelo, kapena kuti lonjezo ya lamulo linaphatikizapo kutsatila mfundo zina zake pa umoyo zomwe Aisiraeli ena onse sanali kudzitsatila. Ndiye, n’ciyani cinali cinalimbikitsa Mwisiraeli kupanga lumbilo lokhala Mnazili? Mwacionekele, cinali cikondi cake cacikulu pa Yehova, komanso mtima woyamikila madalitso Ake.—Deut. 6:5; 16:17.

3. Kodi anthu a Mulungu afanana bwanji na Anazili?

3 Makonzedwe a Unazili anatha pomwe Cilamulo ca Mose cinaloŵedwa m’malo na “cilamulo ca Khristu.” (Agal. 6:2; Aroma 10:4) Ngakhale n’telo, monga zinalili kwa Anazili, anthu a Yehova masiku ano amaonetsa cifuno com’tumikila na mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, maganizo awo onse, komanso mphamvu zawo zonse. (Maliko 12:30) Timapanga lumbilo limeneli mofunitsitsa pamene tidzipatulila kwa Yehova. Kuti tikwanilitse lumbilo limeneli, timagonjela ku cifunilo ca Yehova na kuonetsa mzimu wodzimana. Pamene tikambilana zimene Anazili anali kucita kuti akwanilitse lumbilo lawo, tiphunzile mfundo zofunika zotithandiza nafenso kusunga lumbilo lathu. b (Mat. 16:24) Tiyeni tikambitsilaneko zitsanzo zotsatila.

ONETSANI MZIMU WODZIMANA

4. Malinga na Numeri 6:​3, 4, n’ciyani cinali kuwayesa Anazili pa kudzipeleka kwawo?

4 Ŵelengani Numeri 6:​3, 4. Anazili sanali kuyenela kumwa vinyo kapena kudya mphesa zongokolola kumene kapena zouma. Anthu omwe anali kukhala moyandikana nawo anali kudya na kusangalala na zakudya zimenezi popeza sikunali kolakwika kucita zimenezo. Baibo imafotokoza kuti “vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu” ni mphatso yocokela kwa Mulungu. (Sal. 104:​14, 15) Ngakhale n’telo, Anazili mofunitsitsa anali kudzimana mwayi wawo wosangalala na zinthu zimenezi. c

Kodi ndinu wokonzeka kudzimana zinthu zina monga anacitila Anazili? (Onani ndime 4-6)


5. Kodi Madián na Marcela anacita zotani poonetsa mzimu wodzimana? Ndipo cifukwa ciyani?

5 Monga zinalili kwa Anazili, nafenso timaonetsa mzimu wodzimana kuti tilambile Yehova mofikapo. Ganizilani citsanzo ca Madián na Marcela. d Banja la Cikhristu limeneli linali kukhala umoyo wa wofu-wofu. Madián anali pa nchito yabwino yowalola kukhala m’nyumba yabwino kwambili. Komabe, iwo anali kufuna kucita zoculuka mu utumiki wa Yehova. Kuti akwanilitse colingaco, anasinthako zinthu zina pa umoyo wawo. Iwo anati: “Tinayamba kucepetsa zinthu zogula. Kenako tinasamukila m’nyumba yaing’ono na kugulitsa motoka yathu.” Anapanga masinthidwe amenewa kuti akhale na mpata wowonjezela utumiki wawo. Iwo ni okhutila, komanso osangalala kuti anapanga masinthidwe amenewa.

6. N’ciyani cimacititsa Akhristu kudzimana zina zake? (Onaninso cithunzi.)

6 Akhristu masiku ano amapeza cimwemwe podzimana zina zake zaumwini kuti aseŵenzetse nthawi yawo yoculuka mu utumiki. (1 Akor. 9:​3-6) Pa nkhani ya kudzimana Yehova satikakamiza ayi. Ndipo ngakhale zinthu zimene timadzimanazo sikuti n’zolakwika. Mwacitsanzo, ena amasankha kusakhala na nyumba yawo-yawo, kusasunga ciweto, kapena kusaloŵa nchito imene amaifuna. Enanso ambili asankha kukhalabe mbeta kwa kanthawi, kapena kusakhala na ŵana akaloŵa m’banja. Ena amakatumikila kumalo osoŵa ngakhale kuti azikhala kutali na acibale awo, komanso mabwenzi awo. Ambili a ife tadzimana zinthu zimenezi pofuna kupatsa Yehova zabwino koposa. Dziŵani kuti Yehova amayamikila ngako kudzimana kwanu pom’tumikila, kaya kwakukulu kapena kwakung’ono.—Aheb. 6:10.

KHALANI WOKOZEKA KUKHALA WOSIYANA NA ENA

7. N’cifukwa ciyani kunali kovuta kwa Anazili kusunga lumbilo lawo? (Numeri 6:5) (Onaninso cithunzi.)

7 Ŵelengani Numeri 6:5. Anazili anali kulumbila kuti sadzameta tsitsi lawo. Iyi inali njila imene anali kuonetsela kuti anali odzipeleka kothelatu kwa Yehova. Malinga na kutalika kwa nthawi imene Mwisiraeli anakhala Mnazili, zinali zosavuta kwa Aisiraeli ena kum’zindikila cifukwa cosameta tsitsi lake. Kukanakhala kuti Aisiraeli ena anali kuwalimbikitsa Anazili kusunga lumbilo lawo, akanatha kutumikila mosavuta. Koma n’zomvetsa cisoni kuti nthawi zina Aisiraeli sanali kuwayamikila Anazili kapena kulemekeza cisankho cawo. M’nthawi ya mneneli Amosi, Aisiraeli opanduka anali “kupatsa Anazili vinyo kuti amwe,” n’colinga coti awapwanyitse lumbilo lawo lopewa vinyo. (Amosi 2:12) Nthawi zina, zinafuna kulimba mtima kuti Mnazili asunge lumbilo lake na kukhala wosiyana na ena.

Mnazili wosunga lumbilo lake mokhulupilika, sanali kuopa kuoneka wosiyana na ena (Onani ndime 7)


8. N’ciyani cakulimbikitsani pa cocitika ca wacinyamata Benjamin?

8 Na thandizo la Yehova, nafenso molimba mtima tingakhale osiyana na ena ngakhale kuti mwacibadwa ndife amanyazi kapena amantha. Ganizilani citsanzo ca Benjamin, mnyamata wa zaka 10 amene ni Mboni ku Norway. Cifukwa ca nkhondo ya ku Ukraine, kusukulu kwawo anakonza cocitika coonetsa kukhalila kumbuyo anthu a ku Ukraine. Ana a sukulu anauzidwa kuti aimbe nyimbo atavala zovala za mitundu ya mbendela ya dziko la Ukraine. Benjamini anapanga nzelu yopewela cocitika cokondela dziko cimeneci. Conco, iye anaima capatali na malo a cocitikaco. Komabe, mphunzitsi wina anamuona, ndipo mokuwa anamuuza kuti: “Bwela kuno, uyenela kucita nawo cocitika cimeneci. Tonse tiyembekeza iwe!” Benjamin molimba mtima anayandikila mphunzitsiyo na kumuuza kuti: “Sinitengako mbali mu zionetselo zandale. Ndipo Mboni za Yehova zambili zili m’ndende kaamba kokana kutengako mbali m’nkhondo.” Mphunzitsiyo anamvela zimene Benjamin ananena moti anamulola kusatengako mbali pa cocitikaco. Ngakhale n’telo, anzake a m’kalasi anayamba kumufunsa cifukwa cake sanatengeko mbali. Benjamin anacita mantha kwambili moti anasala pang’ono kulila, koma molimba mtima anabwelezanso zimene anauza mphunzitsi wake kwa onse m’kalasi. Pambuyo pake, Benjamin anauza makolo ake kuti anamva kuti Yehova anam’thandiza kuteteza cikhulupililo cake.

9. Tingakondweletse mtima wa Yehova m’njila ziti?

9 Timakhala osiyana na anthu ena cifukwa tinasankha kumvela Yehova. Timafunika kulimba mtima kuti anthu atidziŵe kuti ndife Mboni ku nchito, kapena kusukulu. Pamene mikhalidwe na zocita za anthu zikuipila-ipila m’dzikoli, zingakhale zovuta kwa ife kukhala na umoyo woyendela mfundo za m’Baibo, komanso kuti tilalikile uthenga wabwino kwa ena. (2 Tim. 1:8; 3:13) Komabe, nthawi zonse tizikumbukila kuti, ‘timakondweletsa mtima wa Yehova’ ngati molimba mtima timasankha kukhala osiyana na anthu amene sam’tumikila.—Miy. 27:11; Mal. 3:18.

IKANI YEHOVA PATSOGOLO MU UMOYO WANU

10. Kodi kutsatila lamulo la pa Numeri 6:​6, 7 kunali kukhala bwanji ciyeso kwa Mnazili?

10 Ŵelengani Numeri 6:​6, 7. Anazili sanali kuyandikila mtembo wa munthu aliyense. Iyi ingaoneke monga nkhani yosavuta. Koma m’nthawi za anthu ochulidwa m’Baibo, zinali kukhala zovuta kwa Mnazili kutsatila lamulo limeneli ngati yemwe wamwalila ni wacibale wake wapafupi. Miyambo ya malilo pa nthawiyo inali kufuna kukhala pafupi na mtembo. (Yoh. 19:​39, 40; Mac. 9:​36-40) Cifukwa ca lumbilo la Unazili, cinali covuta kwa Mnazili kutsatila miyambo imeneyi. Ngakhale pocita zinthu na acibale awo pa nthawi ya cisoni cacikulu imeneyi, Anazili anali kusungabe lumbilo lawo mokhulupilika. Mosakaikila, Yehova analimbikitsa alambili ake odzipeleka amenewa polimbana na zokhoma zimene anali kukumana nazo.

11. Kodi Akhristu ayenela kutsimikiza mtima kucita ciyani akamacita zinthu zokhudza banja lawo? (Onaninso cithunzi.)

11 Ife Akhristu, sititenga mopepuka lumbilo lathu lodzipatulila kwa Yehova. Izi zimakhudza zisankho zathu na zocita zathu pa nkhani za m’banja. Timasamalila bwino maudindo athu a m’banja ofotokozedwa m’Malemba, koma sititsogoza zofuna za banja lathu m’malo mwa zofuna za Yehova. (Mat. 10:​35-37; 1 Tim. 5:8) Nthawi zina tingafunikile kupanga zisankho zosakomela acibale athu kuti tikondweletse Yehova.

Kodi ndinu wofunitsitsa kutsogoza cifunilo ca Yehova pa umoyo wanu ngakhale zinthu zivute bwanji? (Onani ndime 11) e


12. Posamalila vuto la banja, kodi Alexandru anacita ciyani, m’malo mocita ciyani?

12 Ganizilani za Alexandru na mkazi wake Dorina. Ataphunzila Baibo kwa caka cimodzi, Dorina analeka kuphunzila, ndipo anali kufuna kuti nayenso Alexandru asiye. Komabe, modekha komanso mwaluso, iye anamuuza kuti adzapitiliza. Dorina sanakondwele nazo, ndipo anayesa kum’kakamiza kuti aleke kuphunzila. Alexandru ananena kuti anayesa kumumvetsa mkazi wake, koma sicinali copepuka kwa iye. Nthawi zina Dorina akamamunyodola na kumuyankha mwaukali, iye anali kuganiza kuti mwina zingakhale bwino kungosiya kuphunzila Baibo. Ngakhale n’telo, Alexandru anapitilizabe kuika Yehova patsogolo, ndipo anali kuonetsa mkazi wake cikondi cacikulu na kumulemekeza. Pamapeto pake, citsanzo cake cabwino cinasonkhezela mkazi wake kuphunzila Baibo, ndipo pothela pake anabatizika.—Onani vidiyo yakuti Alexandru na Dorina Văcar: “Cikondi n’Coleza Mtima Ndiponso n’Cokoma Mtima” pa jw.org pansi pa nkhani zakuti “Coonadi Cimasintha Miyoyo.”

13. Kodi tingaonetse bwanji kuti Yehova timamukonda, komanso timakonda a m’banja lathu?

13 Yehova ndiye anakhazikitsa makonzedwe a banja, ndipo amafuna kuti tikhale na banja lacimwemwe. (Aef. 3:​14, 15) Ngati tifuna kukhaladi acimwemwe, tiyenela kucita zinthu mogwilizana na cifunilo cake. Musamakaikile zakuti Yehova amayamikila kudzipeleka kwanu pom’tumikila pamene mukusamalila a m’banja lanu na kuwaonetsa cikondi, komanso ulemu.—Aroma 12:10.

LIMBIKITSANI AMENE ALI NA MZIMU NGATI WA ANAZILI

14. Kodi ndani makamaka amene tiyenela kuyesetsa kulimbikitsa na mawu athu?

14 Onse amene asankha kutumikila Yehova masiku ano ayenela kukhala ofunitsitsa kudzimana zina zake cifukwa ca cikondi. Koma nthawi zina kucita zimenezi sikopepuka. Kodi tingathandizane bwanji wina na mnzake kuonetsa mzimu umenewu? Mwa kukhala wolimbikitsa m’mawu athu. (Yobu 16:5) Kodi pali ena mu mpingo wanu amene akuyesetsa kukhala umoyo wosalila zambili kuti awonjezele utumiki wawo? Kodi mudziŵako acicepele amene amakhala umoyo wosiyanako na anzawo kusukulu, ngakhale kuti si copepuka kutelo? Nanga bwanji za maphunzilo a Baibo, komanso okhulupilila anzathu amene akuvutika kukhalabe okhulupilika cifukwa cotsutsidwa na a m’banja lawo? Tiyeni tiseŵenzetse mpata ulionse umene tapeza kuti tilimbikitse alambili anzathu amenewa. Ndipo tiziwayamikila pa mzimu wawo wodzipeleka umenewo na kulimba mtima kwawo.—Filim. 4, 5, 7.

15. Kodi ena awacilikiza motani omwe ali mu utumiki wa nthawi zonse?

15 Nthawi zina, tingapeleke thandizo lofunikila kwa Akhristu anzathu omwe ali mu utumiki wa nthawi zonse. (Miy. 19:17; Aheb. 13:16) Ici ndiye cinali cikhumbo ca mlongo wokhulupilika wacikulile amene akhala m’dziko la Sri Lanka. Atamuwonjezela malipilo ake a penshoni, anafuna kuthandiza apainiya aŵili acitsikana kuti apitilize utumiki wawo mosasamala za mavuto a zacuma. Conco, iye anadzipeleka kuwapatsa ndalama mwezi ulionse zoti aziseŵenzetsa pogula tokotaimu. Mlongoyu anaonetsa mzimu wabwino zedi!

16. Tingaphunzile ciyani kwa Anazili a m’nthawi zakale?

16 Tingaphunzile zambili pa citsanzo ca Anazili odzipeleka akale! Komabe, makonzedwe amenewa amaonetsa cinthu cina cake cokhudza Atate wathu wa kumwamba. Amadziŵa bwino lomwe kuti timafuna kum’kondweletsa, komanso kuti ndife ofunitsitsa kudzimana zina zake kuti tisunge lumbilo lathu la kudzipatulila. Iye amatilemekeza potilola kuonetsa cikondi cathu pa iye mmene tingathele. (Miy. 23:​15, 16; Maliko 10:​28-30; 1 Yoh. 4:19) Makonzedwe a Unazili amasonyeza kuti Yehova amaona na kuyamikila kudzimana kwathu kuti tim’tumikile. Conco tisaleke kutumikila Yehova, na kukhala ofunitsitsa kumupatsa zabwino koposa.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Anazili anaonetsa motani kudzimana komanso kulimba mtima?

  • Nanga tingaulimbikitse motani mzimu wa Unazili masiku ano?

  • Kodi makonzedwe a Unazili anaonetsa bwanji kuti Yehova amawadalila alambili ake?

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

a Anazili ena anacita kusankhidwa mwacindunji na Yehova, koma ambili a iwo anali Aisiraeli odzipeleka mwa kufuna kwawo kuti akhale Anazili kwa kanthawi.—Onani mbali yakuti “ Anazili Osankhidwa na Yehova.”

b Nthawi zina, zofalitsa zathu zimayelekezela Anazili na amene ali mu utumiki wa nthawi zonse. Komabe, nkhani ino idzafotokoza mmene atumiki onse odzipatulila a Yehova angaonetsele mzimu wa Unazili.

c Zioneka kuti Anazili analibe maudindo a nchito zinanso zoti azicita kuti akwanilitse lumbilo lawo.

d Onani nkhani yakuti “Tinasankha Kukhala Moyo Wosalila Zambili” pansi pa kamutu kakuti “Zocitika pa Moyo wa a Mboni za Yehova” pa jw.org.

e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mnazili ali pa mtenje, ndipo akuonelela mwambo wa malilo a wacibale wake. Cifukwa ca lumbilo lake sakanatha kutengako mbali pa mwambo umenewo.