Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pezani Cimwemwe Poyembekezela Yehova Moleza Mtima

Pezani Cimwemwe Poyembekezela Yehova Moleza Mtima

MOSAPENEKA konse, mukuyembekezela mwacidwi nthawi pomwe Yehova adzacotselatu zoipa zonse pa dzikoli na kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano. (Chiv. 21:​1-5) Komabe, si copepuka kuyembekezela Yehova moleza mtima maka-maka ngati tikukumana na mavuto. Ndipo cinthu cimene tikuyembekezela cikacedwa kucitika cimadwalitsa mtima.—Miy. 13:12.

Ngakhale n’telo, Yehova amafuna kuti tizimuyembekezela moleza mtima kuti iye acitepo kanthu pa nthawi yake yoikika. N’cifukwa ciyani amacita zimenezo? N’ciyani cingatithandize kukhalabe acimwemwe pomuyembekezela?

CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAFUNA KUTI TIZIMUYEMBEKEZELA

Baibo imati: “Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima ndipo adzanyamuka kuti akucitileni cifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweluza mwacilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.” (Yes. 30:18) Mawu a Yesaya amenewa anali kupita kwa Ayuda osamvela. (Yes. 30:1) Koma pakati pa Ayudawo panalinso anthu ena okhulupilika, ndipo mawuwa anawapatsa ciyembekezo. Ndipo amapelekanso ciyembekezo kwa atumiki okhulupilika a Yehova masiku ano.

Conco, tiyenela kuyembekezela moleza mtima cifukwa Yehova nayenso akuyembekezela moleza mtima. Iye anaikilatu nthawi yoononga dongosolo loipali la zinthu, ndipo akuyembekezela tsikulo na ola lake kuti ikwane. (Mat. 24:36) Panthawiyo, zidzaonekelatu poyela kuti zinenezo za Mdyelekezi zokhudza Yehova, komanso atumiki Ake n’zabodza. Iye adzacotsa Satana na onse amene ali kumbali yake, koma ife ‘adzaticitila cifundo.’

Pali pano, Yehova sangaticotsele mavuto athu onse, koma amatitsimikizila kuti tingakhale acimwemwe pomuyembekezela. Mogwilizana na mawu a Yesaya, tingakhale acimwemwe poyembekezela mwacidwi kuti cina cake cicitike. (Yes. 30:18) a Tiyeni tikambilane njila zinayi zimene zingatithandize kukhala na cimwemwe cimeneci.

MMENE TINGAKHALILE ACIMWEMWE POYEMBEKEZA

Ikani maganizo anu pa zinthu za zabwino. Mfumu Davide anaona zinthu zambili zoipa mu umoyo wake. (Sal. 37:35) Ngakhale n’telo, iye analemba kuti: “Khala cete pamaso pa Yehova, ndipo umuyembekezele ndi mtima wako wonse. Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendela bwino, munthu amene akukwanilitsa zolinga zake zoipa.” (Sal. 37:7) Davide iye mwini anaseŵenzetsa uphungu umenewu mwa kuika maganizo ake pa ciyembekezo cakuti Yehova adzamupulumutsa. Anayamikilanso dalitso lililonse limene Yehova anam’patsa. (Sal. 40:5) Nafenso cidzakhala copepuka kuyembekezela Yehova ngati tiika maganizo athu pa zinthu zabwino, m’malo moganizila kwambili zinthu zoipa zimene zikuticitikila.

Seŵenzetsani mpata uliwonse kutamanda Yehova. Wolemba Salimo 71, amene zioneka kuti ni Davide, ananena izi ponena za Yehova: “Ine ndidzayembekezela inu nthawi zonse. Ndipo ndidzakutamandani mowilikiza kuposa kale.” (Sal. 71:14) Kodi anali kum’tamanda bwanji Yehova? Anali kuuza ena za Yehova, komanso kumuimbila zitamando. (Sal. 71:​16, 23) Mofanana na Davide, nafenso tingapeze cimwemwe poyembekezela Yehova. Timam’tamanda polalikila, poceza na ena, komanso poimba nyimbo zom’tamanda. Cotelo, ulendo wotsatila pomwe mudzaimba nyimbo ya Ufumu, mukaike maganizo anu pa uthenga wake na kuona mmene ungakupatsileni cimwemwe.

Pezani cilimbikitso kucokela kwa apaubale wanu. Pamene Davide anali kuyang’anizana na mavuto, anauza Yehova kuti: “Ndidzayembekezela dzina lanu pamaso pa okhulupilika anu, cifukwa ndi labwino.” (Sal. 52:9) Nafenso tingapeze cilimbikitso kucokela kwa alambili anzathu okhulupilika. Tingatelo tikakhala pa misonkhano, mu utumiki, komanso pa maceza.—Aroma. 1:​11, 12.

Limbikitsani ciyembekezo canu. Salimo 62:5 imati: “Yembekezela Mulungu modekha, iwe moyo wanga, cifukwa ciyembekezo canga cicokela kwa iye.” Ciyembekezo colimba ni cofunika kwambili, maka-maka ngati mapeto a dzikoli sanabwele pomwe tinali kuwayembekezela. Tiyenela kukhala otsimikiza kuti malonjezo a Yehova adzacitikadi ngakhale kuti zingaoneke monga akucedwa. Tingalimbikitse ciyembekezo cathu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu. Tingaŵelengemo maulosi, kuona mmene nkhani zake zimagwilizanila, komanso zimene Yehova anavumbula za iye mwini. (Sal. 1:​2, 3) Komanso, tiyenela kupitilizabe “kupemphela mu mphamvu ya mzimu woyela” kuti tisungebe ubwenzi wathu na Yehova uli wolimba, poyembekezela kukwanilitsidwa kwa lonjezo la moyo wosatha.—Yuda 20, 21.

Mofanana na Davide, inunso khalani otsimikiza kuti Yehova amawaona amene amamuyembekezela, ndipo amawaonetsa kukoma mtima Kwake kosatha. (Sal. 33:​18, 22) Pitilizani kuyembekezela Yehova moleza mtima mwa kuika maganizo anu pa zinthu zabwino mu umoyo wanu, komanso mwa kum’tamanda. Cina, pezani cilimbikitso kwa alambili anzanu, na kupitilizabe kusunga ciyembekezo canu ca mtengo wapatali cili colimba.

a Mawu amene anawamasulila kuti “amamuyembekezela” angatanthauzenso “kuyembekezela mwacidwi, kapena kulakalaka kuti cina cake cicitike.” Izi zionetsa kuti sikulakwa kulakalaka cipulumutso cathu.