Muzisangalala Pamene Mukuyembekezera Yehova Moleza Mtima

Muzisangalala Pamene Mukuyembekezera Yehova Moleza Mtima

KODI mukuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova adzachotse zoipa zonse, n’kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano? (Chiv. 21:1-5) N’zosachita kufunsa. Komabe si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuyembekezera Yehova moleza mtima, makamaka pamene tikukumana ndi mavuto. Zinthu zimene timayembekezera zikamachedwa kuchitika, mtima umadwala.​—Miy. 13:12.

Komabe Yehova amafuna kuti tiziyembekezera moleza mtima mpaka nthawi yoti adzachite kanthu itakwana. N’chifukwa chiyani amafuna tizichita zimenezo? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala pamene tikuyembekezera?

N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA AMAFUNA KUTI TIZIYEMBEKEZERA?

Baibulo limati: “Yehova akuyembekezera moleza mtima kuti akukomereni mtima, ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo. Osangalala ndi anthu onse amene akumuyembekezera.” (Yes. 30:18) Yehova ankalankhula mawu amenewa kwa Ayuda osamvera. (Yes. 30:1) Koma panali Ayuda ena omwe anali okhulupirika ndipo mawuwa anawapatsa chiyembekezo. Masiku anonso mawu amenewa amapereka chiyembekezo kwa atumiki a Yehova okhulupirika.

Choncho tiyenera kuyembekezera moleza mtima chifukwa Yehova nayenso akuyembekezera moleza mtima. Iye anakhazikitsa nthawi yomwe adzawononge dziko loipali ndipo akuyembekezera kuti tsikulo komanso ola lake zifike. (Mat. 24:36) Pa nthawiyo zidzakhala zoonekeratu kuti zonse zimene Mdyerekezi wakhala akunenera Yehova komanso anthu omwe amamutumikira, n’zabodza. Kenako adzawononga Satana ndi onse omwe ali kumbali yake, koma ifeyo ‘adzatichitira chifundo.’

Panopa Yehova sangathetse mavuto athu onse, komabe akutitsimikizira kuti tingathe kumasangalala pamene tikuyembekezera. Choncho monga mmene Yesaya ananenera, tingamasangalale pamene tikuyembekezera zinthu zabwino. (Yes. 30:18) a Ndiye kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kuti tizisangalala? Tiyeni tione zinthu 4 zomwe zingatithandize.

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TIZISANGALALA PAMENE TIKUYEMBEKEZERA

Tiziganizira zabwino zomwe zikuchitika pa moyo wathu. Mfumu Davide anakumana ndi zoipa zambiri pa moyo wake. (Sal. 37:35) Koma iye analemba kuti: “Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umuyembekezere moleza mtima. Usakhumudwe ndi munthu amene amakonza ziwembu n’kuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.” (Sal. 37:7) Davide anatsatira malangizo amenewa poika maganizo ake onse pa chiyembekezo chake chakuti Yehova amupulumutsa. Ankayamikiranso zabwino zonse zomwe Yehova ankamuchitira. (Sal. 40:5) Ngati ifenso titamaganizira zinthu zabwino zomwe zikutichitikira, osati zoipa, zingakhale zosavuta kuti tiziyembekezera Yehova.

Muzigwiritsa ntchito mpata uliwonse kutamanda Yehova. Wolemba Salimo 71, amene n’kutheka kuti ndi Davide, anauza Yehova kuti: “Ndipitiriza kuyembekezera. Ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale.” (Sal. 71:14) Kodi iye ankatamanda bwanji Yehova? Ankauza ena zokhudza Yehova komanso kuimba nyimbo zomutamanda. (Sal. 71:16, 23) Mofanana ndi Davide, ifenso tingamasangalale poyembekezera Yehova. Timamutamanda tikamalalikira, tikamacheza ndi ena komanso tikamaimba nyimbo zathu. Nthawi ina mukamadzaimba nyimbo ya Ufumu, mudzaganizire mawu ake mosamala kuti mudzaone mmene angakulimbikitsireni.

Muzilola kuti abale ndi alongo anu azikulimbikitsani. Davide atakumana ndi mavuto anauza Yehova kuti: “Pamaso pa okhulupirika anu, ndidzayembekezera dzina lanu, chifukwa ndi labwino.” (Sal. 52:9) Ifenso Akhristu anzathu angatilimbikitse, osati pamisonkhano pokha kapena tikamalalikira, komanso tikamacheza.​—Aroma 1:11, 12.

Muzikhala ndi chiyembekezo champhamvu. Lemba la Salimo 62:5 limati: “Ndikuyembekezera Mulungu modekha chifukwa chiyembekezo changa chimachokera kwa iye.” Chiyembekezo champhamvu ndi chofunika kwambiri makamaka ngati mapeto sakufika pa nthawi imene timayembekezera. Tizikhulupirira kwambiri kuti malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa ngakhale patatenga nthawi yaitali. Tingakhale ndi chiyembekezo champhamvu ngati timaphunzira Mawu a Mulungu, zomwe zikuphatikizapo maulosi, kugwirizana kwa nkhani zake komanso mfundo zomwe Yehova amatiuza zokhudza iye. (Sal. 1:2, 3) Tiyeneranso kupitiriza kupemphera “mogwirizana ndi mzimu woyera” kuti tipitirizebe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo lake la moyo wosatha.​—Yuda 20, 21.

Mofanana ndi Mfumu Davide, mungakhale otsimikiza kuti Yehova amayang’anira onse omwe amamuyembekezera ndipo amawasonyeza chikondi chake chokhulupirika. (Sal. 33:18, 22) Pitirizani kuyembekezera Yehova molimba mtima poganizira zabwino zimene zikuchitika pa moyo wanu, kumutamanda, kulola Akhristu anzanu kuti azikulimbikitsani komanso popitiriza kukhala ndi chiyembekezo cholimba.

a M’chilankhulo choyambirira, mawu amene anawamasulira kuti “kuyembekezera” angatanthauzenso “kudikira kuti chinachake chichitike.” Izi zikusonyeza kuti si kulakwa kumafuna kuti Yehova athetse mavuto athu.