Abale Awiri Atsopano M’Bungwe Lolamulira

Abale Awiri Atsopano M’Bungwe Lolamulira

LACHITATU pa 18 January 2023, pa jw.org panaikidwa chilengezo chapadera chonena kuti M’bale Gage Fleegle ndi M’bale Jeffrey Winder aikidwa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Abale awiri onsewa atumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali.

Gage Fleegle ndi mkazi wake Nadia

M’bale Fleegle anakulira m’banja la Mboni kumadzulo kwa mzinda wa Pennsylvania, U.S.A. Ali wachinyamata, banja lawo linasamukira ku tauni ina yaing’ono komwe kunkafunika olalikira ambiri. Pasanapite nthawi yaitali, anabatizidwa pa 20 November 1988.

Nthawi zonse makolo a M’bale Fleegle ankamulimbikitsa kuti adzachite utumiki wanthawi zonse. Iwo ankakonda kulandira oyang’anira dera komanso atumiki a pa Beteli kunyumba kwawo ndipo M’bale Fleegle ankatha kuona mmene abale ndi alongowa ankasangalalira. Pasanapite nthawi yaitali atabatizidwa, anayamba upainiya wokhazikika pa 1 September 1989. Patapita zaka ziwiri, anakwaniritsa cholinga chomwe anadziikira ali ndi zaka 12, choti adzakatumikire ku Beteli. Anayamba kutumikira ku Beteli ya ku Brooklyn mu October 1991.

Ku Beteli, M’bale Fleegle anatumikira m’dipatimenti yosindikiza mabuku kwa zaka 8 ndipo pambuyo pake anayamba kutumikira mu Dipatimenti ya Utumiki. Pa nthawiyo anatumikira mu mpingo wa chinenero cha Chirasha kwa zaka zingapo. Mu 2006, anakwatirana ndi mkazi wake Nadia ndipo nayenso anayamba kutumikira pa Beteli. Iwo anatumikira limodzi m’gawo la Chipwitikizi ndiponso kwa zaka zoposa 10 m’gawo la Chisipanishi. Atatumikira kwa zaka zambiri m’Dipatimenti ya Utumiki, M’bale Fleegle anayamba kutumikira mu Ofesi ya Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ndipo pambuyo pake anatumikira mu Ofesi ya Komiti ya Utumiki. Mu March 2022, anaikidwa kukhala wothandiza Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira.

Jeffrey Winder ndi mkazi wake Angela

M’bale Winder anakulira ku Murrieta mumzinda wa California ku U.S.A. Iye anaphunzitsidwa choonadi ndi makolo ake ndipo anabatizidwa pa 29 March 1986. M’mwezi wotsatira anayamba upainiya wothandiza. Anasangalala kwambiri ndi utumikiwu ndipo anaganiza zongopitiriza ndipo atachita upainiya wothandiza kwa miyezi ingapo, anayamba upainiya wokhazikika pa 1 October 1986.

Ali mnyamata, M’bale Winder anapita kukaona azichimwene ake awiri omwe pa nthawiyo ankatumikira ku Beteli. Ulendowu unachititsa kuti m’baleyu azifunitsitsa kukatumikira pa Beteli akadzakula. Ndipo mu May 1990, anaitanidwa kuti akatumikire ku Beteli ya ku Wallkill.

Ku Beteli, M’bale Winder anatumikira m’madipatimenti osiyanasiyana kuphatikizapo dipatimenti yoyeretsa, kufamu komanso mu Ofesi ya Osamalira Banja la Beteli. Mu 1997, anakwatirana ndi mkazi wake Angela ndipo akhala akutumikira limodzi pa Beteli kuchokera nthawi imeneyo. Mu 2014, iwo anasamukira ku Warwick komwe M’bale Winder anathandiza pa ntchito yomanga maofesi kulikulu lathu. Mu 2016, anasamukira ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson komwe ankatumikira m’Dipatimenti Yojambula Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera. Patapita zaka 4 iwo anabwereranso ku Warwick komwe M’bale Winder anayamba kutumikira mu Ofesi ya Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli. Mu March 2022, anaikidwa kukhala wothandiza m’Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli ya Bungwe Lolamulira.

Ndi pemphero lathu kuti Yehova apitirize kudalitsa ‘amunawa omwe ndi mphatso’ pamene akupitiriza kugwira mwakhama ntchito za Ufumu.​—Aef. 4:8.