Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Baibo imatiululila ciyani za mphamvu za Yehova zokwanitsa kunenelatu zamtsogolo?

Baibo imafotokoza momveka bwino kuti Yehova amakwanitsa kunenelatu zamtsogolo. (Yes. 45:21) Koma sitiuza mfundo zonse za mmene amacitila zimenezi, kapena kuculuka kwa zinthu zimene angasankhe kudziŵa pa zamtsogolo. Conco, ngakhale kuti sitingakhale otsimikiza za nkhaniyi, onankoni mfundo zotsatilazi.

Yehova angacite ciliconse cimene akufuna, koma amadziikila malile. Cifukwa cakuti ali na nzelu zopanda malile, iye angalosele za ciliconse cimene wasankha. (Aroma 11:33) Komabe, popeza kuti iye amakwanitsa kudziletsa, angasankhe kuti asadziŵiletu zimene zidzacitika kutsogolo.—Yelekezelani na Yesaya 42:14.

Yehova amapangitsa cifunilo cake kucitika. Kodi mfundo imeneyi igwilizana bwanji na mphamvu zake zokwanitsa kulosela zamtsogolo? Yesaya 46:10 imati: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi. kuyambila kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinacitike. Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalila zanga zidzacitikadi, ndipo ndidzacita ciliconse cimene ndikufuna.’”

Cotelo cifukwa cimodzi cimene cimapangitsa Yehova kunenelatu zamtsogolo n’cakuti, iye ali na mphamvu zopangitsa zinthu kucitika. Iye safunika kucita kuthamangitsa nthawi titelo kunena kwake kuti aone zomwe zili m’tsogolo—monga kuti zinthu zamtsogolozo zinacitika kale, ndiye Yehova akuzionelatu pasadakhale. M’malo mwake, iye angasankhe kuti cina cake cicitike pa nthawi ina yake, na kupangitsa cinthuco kucitika nthawiyo ikakwana.—Eks. 9:​5, 6; Mat. 24:36; Mac. 17:31.

Ndiye cifukwa cake Baibo imaseŵenzetsa mawu monga akuti “ndinakoza,” komanso “ndakonza,” pofotokoza zimene Yehova amacita ponena za zinthu zinazake zamtsogolo. (2 Maf. 19:25; Yes. 46:11) Mawu amenewa anawamasulila kucokela ku mawu amene m’cilankhulo coyambilila ni ogwilizana na mawu omwe amatanthauza “woumba.” (Yer. 18:4) Woumba mbiya waluso ali na mphamvu yopanga ciwiya cokongola poseŵenzetsa dongo. Yehova nayenso ali na mphamvu yopangitsa zinthu kucitika m’njila yakuti colinga cake cikwanilitsike.—Aef. 1:11.

Yehova amalemekeza ufulu wa aliyense wodzipangila zisankho. Iye sakonzelatu zimene zidzacitikila munthu aliyense mu umoyo wake. Ndipo sapangitsanso anthu abwino kucita zinthu zinazake zomwe zingawononge moyo wawo. Iye amalola aliyense kudzisankhila yekha zocita, ndipo amalimbikitsa anthu kusankha moyo waphindu.

Onankoni zitsanzo ziŵili izi. Citsanzo coyamba cikhudza anthu a ku Nineve. Yehova ananenelatu kuti mzinda umenewu udzaonongedwa cifukwa ca zoipa zimene anali kucita. Koma anthuwo atalapa, Yehova “anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweletsela, moti sanawabweletsele.” (Yona 3:​1-10) Yehova anasintha maganizo ake pa zimene ananenelatu zokhudza Anineve. Anatelo cifukwa anthuwo anaseŵenzetsa ufulu wawo wodzisankhila zocita kulapa atalandila uthenga wa ciweluzo.

Citsanzo caciŵili ni ulosi wonena za Koresi, yemwe anali kudzamasula Ayuda kucoka ku ukapolo, komanso kupeleka lamulo lomanganso kacisi wa Yehova. (Yes. 44:26–45:4) Mfumu Koresi ya ku Perisiya inakwanilitsa ulosi umenewu. (Ezara 1:​1-4) Komabe, Koresi sanali kulambila Mulungu woona. Yehova anaseŵenzetsa Koresi kukwanilitsa ulosiwu popanda kumuphela ufulu wodzisankhila zocita pa amene ayenela kumulambila ayi.—Miy. 21:1.

Komabe, izi si mfundo zonse zimene Yehova amayendela akafuna kunenelatu zamtsogolo. Kukamba zoona, kulibe munthu angamvetse njila za Yehova. (Yes. 55:​8, 9) Komabe, zimene Yehova watiululila zimalimbikitsa cikhulupililo cathu cakuti iye nthawi zonse amacita zoyenela—kuphatikizapo akasankha kunenelatu zamtsogolo.