Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Baibulo limafotokoza zotani zokhudza Yehova pa nkhani yoneneratu zam’tsogolo?

Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova amatha kuneneratu zam’tsogolo. (Yes. 45:21) Komabe silimafotokoza zonse zokhudza mmene iye amachitira izi, nthawi yomwe amasankha kuti adziwe zinthuzo kapenanso kuchuluka kwa zimene amasankha kudziwiratu. Choncho sitidziwa zonse zokhudza Yehova pa nkhaniyi. Komabe pali zinthu zochepa zomwe tikudziwa.

Yehova angathe kuchita chilichonse chomwe akufuna koma nthawi zina amasankha kuti asachite zinthu zina. Popeza kuti ali ndi nzeru zopanda malire, akhoza kuneneratu chilichonse chimene akufuna. (Aroma 11:33) Komanso popeza ndi wodziletsa, angathe kusankha kuti asadziwiretu zimene zichitike.​—Yerekezerani ndi Yesaya 42:14.

Yehova amachititsa kuti chifuniro chake chichitike. Ndiye kodi zimenezi zikutithandiza kumvetsa chiyani pa nkhani yakuti iye amatha kudziwiratu zam’tsogolo? Lemba la Yesaya 46:10 limafotokoza kuti: “Kutatsala nthawi yaitali, ndimaneneratu zimene zidzachitike, ndipo kale kwambiri ndinaneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Ine ndimanena kuti, ‘Zolinga zanga zidzachitikadi, ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.ʼ”

Choncho chifukwa chimodzi chomwe chingachititse Yehova kuneneratu zam’tsogolo ndi chakuti ali ndi mphamvu yochititsa zinazake kuti zichitike. Sikuti iye ali ngati munthu amene akuonera vidiyo, yemwe amatha kuifulumizitsa kuti aoneretu zimene zili kumapeto, ngati kuti zimene zidzachitike m’tsogolo zinachitika kale. M’malomwake, Yehova angasankhe kuti chinachake chichitike pa nthawi inayake kenako n’kuchichititsa kuti chichitike nthawiyo ikafika.​—Eks. 9:5, 6; Mat. 24:36; Mac. 17:31.

Pa chifukwa chimenechi, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti ‘kukonza’ pofotokoza zimene Yehova amachita pa nkhani yokhudza zinthu zina zam’tsogolo. (2 Maf. 19:25; Yes. 46:11) Mawuwa anamasuliridwa ku mawu a chilankhulo choyambirira omwe amagwirizana ndi tanthauzo la mawu akuti “woumba.” (Yer. 18:4) Mofanana ndi woumba waluso yemwe akhoza kugwiritsa ntchito dongo kuumba mphika wokongola, nayenso Yehova akhoza kupanga kapena kusintha zinthu kuti akwaniritse chifuniro chake.​—Aef. 1:11.

Yehova amalola kuti anthu azisankha okha zimene akufuna. Iye samakonzeratu zimene zidzachitike pa moyo wa munthu aliyense. Komanso samachititsa kuti anthu abwino azichita zinthu zimene pamapeto pake zingawaonongetse. Iye amalola kuti aliyense azisankha yekha zimene akufuna kuchita koma amalimbikitsa anthu kuti azisankha zoyenera.

Tiyeni tione zitsanzo ziwiri. Chitsanzo choyamba ndi chokhudza anthu a ku Nineve. Yehova anali ataneneratu kuti mzindawo udzawonongedwa chifukwa anthu ankachita zoipa. Koma anthu a mumzindawo atalapa, Yehova “anasintha maganizo ake ndipo sanawabweretsere tsoka limene ananena kuti awabweretsera.” (Yona 3:1-10) Yehova anasintha maganizo ake pa zimene ananeneratu chifukwa anthu a ku Nineve anagwiritsa ntchito ufulu wawo wosankha polapa, atamva uthenga wochenjeza wochokera kwa Yehova.

Chitsanzo chachiwiri ndi ulosi wokhudza Koresi, yemwe anamasula Ayuda ku ukapolo n’kulamula kuti akamangenso kachisi wa Yehova. (Yes. 44:26–45:4) Mfumu Koresi ya ku Perisiya inakwaniritsa ulosi umenewu. (Ezara 1:1-4) Komatu Koresi sankalambira Mulungu woona. Yehova anagwiritsa ntchito Koresi pokwaniritsa ulosiwu koma anamulola kugwiritsa ntchito ufulu wake wosankha yemwe akufuna kumulambira.​—Miy. 21:1.

Izi ndi mfundo zochepa chabe zomwe Yehova amaziganizira akafuna kuneneratu zomwe zidzachitike m’tsogolo. Kunena zoona, palibe munthu yemwe angamvetse zonse zokhudza mmene Yehova amachitira zinthu. (Yes. 55:8, 9) Komabe zimene tikudziwa zokhudza Yehova zimatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti iye nthawi zonse amachita zoyenera, kuphatikizapo nkhani yoneneratu zomwe zidzachitike m’tsogolo.