Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani mawu ena m’Baibulo amanenedwa mobwerezabwereza?

NTHAWI zina olemba Baibulo ankabwereza ndendende mawu omweomwewo. Tiyeni tione mfundo zitatu zomwe ziyenera kuti zinkawachititsa kuchita zimenezi.

Nthawi yomwe zinthuzo zinalembedwa. M’nthawi ya Aisiraeli, anthu ambiri analibe mabuku awoawo a Chilamulo. Ankangomvetsera Chilamulo chikamawerengedwa akasonkhana kuchihema. (Deut. 31:10-12) N’zoonekeratu kuti pankakhala zosokoneza akamamvetsera ataimirira kwa maola angapo pagulu lalikulu. (Neh. 8:2, 3, 7) Pa nthawi ngati zimenezi, kubwereza mawu kunali kofunika kwambiri chifukwa kukanathandiza anthuwo kuti azikumbukira mosavuta malemba n’kumawagwiritsa ntchito. Komanso kubwerezako kukanawathandiza kuti azikumbukira mfundo zonse zokhudza malamulo omwe Mulungu anawapatsa.​—Lev. 18:4-22; Deut. 5:1.

Mmene zinalembedwera. Mabuku ena m’Baibulo analembedwa ngati nyimbo, mwachitsanzo buku la Masalimo, Nyimbo ya Solomo komanso la Maliro. Nthawi zina mawu a nyimbo ankabwerezedwa pofuna kutsindika mutu wa nyimboyo komanso kuthandiza omvetsera kuti aloweze mawu ake. Chitsanzo ndi mawu opezeka pa Salimo 115:9-11, pomwe amati: “Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.” Kodi mwaona mmene kubwereza mawuwa kukanathandizira oimbawo, kuti mfundo zamtengo wapatali zachoonadizi zikhazikike m’mitima mwawo?

Kuti atsindike mfundo zofunika. Nthawi zina olemba Baibulo ankabwereza mawu ofunika. Mwachitsanzo, Yehova atalamula Aisiraeli kuti asamadye magazi, anauza Mose kuti abwereze chifukwa chake kwa maulendo angapo. Mulungu ankafuna kutsindika kuti moyo wa chamoyo chilichonse uli m’magazi, kapena kuti magazi amaimira moyo. (Lev. 17:11, 14) Pambuyo pake, pamene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu ankatchula zinthu zoyenera kupewa kuti munthu asangalatse Mulungu, anabwerezanso kufunika kopewa magazi.​—Mac. 15:20, 29.

Sikuti Yehova amafuna kuti tikhale ndi chizolowezi chomangobwerezabwereza mawu a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ukamapemphera, usamanene mawu omweomwewo mobwerezabwereza.” (Mat. 6:7) Kenako anatchula zinthu zomwe tiyenera kupempherera, zomwe ndi zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Mat. 6:9-13) Koma ngakhale kuti sitiyenera kubwerezabwereza mawu m’mapemphero athu, n’zololeka kupempherera nkhani ina yake mobwerezabwereza.​—Mat. 7:7-11.

Pa chifukwa chabwino, Mulungu analola kuti mawu kapena ziganizo zinazake m’Baibulo zibwerezedwe. Imeneyi ndi njira imodzi imene Mlangizi wathu wamkulu amatiphunzitsira kuti zinthu zizitiyendera bwino.​—Yes. 48:17, 18.