Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

N’cifukwa ciyani Baibo imabweleza mawu?

NTHAWI zina, olemba Baibo anali kubweleza ciganizo cimodzi-modzi potsatila liwu na liwu. Ganizilani zifukwa zitatu izi zimene ziyenela kuti zinawapangitsa kucita zimenezi:

Nthawi pomwe inalembedwa. Ku Isiraeli wakale, anthu ambili analibe makope awo-awo a Cilamulo. Kambili, anali kumva Cilamulo cikamaŵelengedwa ku cihema ngati mtundu wonse wasonkhana pamodzi. (Deut. 31:​10-12) Mwacionekele, panali zosokoneza pomwe anali kumvetsela ataimilila pagulu la anthu ambili kwa maola angapo. (Neh. 8:​2, 3, 7) Pa zocitika ngati zimenezi, kubweleza ziganizo zofunika kunathandiza anthu kukumbukila Malemba na kuwaseŵenzetsa. Kubweleza mawu ena kunawathandizanso maka-maka kukumbukila mfundo za m’Cilamulo ca Mulungu, komanso zigamulo zake.—Lev. 18:​4-22; Deut. 5:1.

Kalembedwe kake. Pafupifupi 10 pelesenti ya Baibo, inalembedwa monga nyimbo. Citsanzo ni bulu la Masalimo, Nyimbo ya Solomo, komanso Maliro. Nyimbo zina zinali kubweleza mawu. Zinali kugogomeza mfundo yaikulu ya nyimboyo, komanso kuthandiza oimba kuiika pa mtima. Mwacitsanzo, onani mawu opezeka pa Salimo 115:​9-11 omwe amati: “Iwe Isiraeli, khulupilila Yehova. Iye ndiye thandizo lako ndi cishango cako. Inu nyumba ya Aroni, khulupililani Yehova. Iye ndiye thandizo lanu ndi cishango canu. Inu oopa Yehova, khulupililani Yehova. Iye ndiye thandizo lanu ndi cishango canu.” N’zoonekelatu kuti kubweleza mawu amenewa kunathandiza oimba kuloŵeza pa mtima mfundo za coonadi zimenezi!

Kugogomeza mfundo zofunika kwambili. Nthawi zina olemba Baibo anali kubweleza ziganizo zofunika kwambili. Mwacitsanzo, pomwe Yehova analamula Aisiraeli kuti asamadye magazi, anacititsa Mose kubweleza zifukwa zake nthawi zambili. Yehova anafuna kugogomeza mfundo yakuti moyo wa nyama uli m’magazi, kutanthauza kuti magazi amaimila moyo. (Lev. 17:​11, 14) Patapita nthawi pamene atumwi na akulu ku Yerusalemu anachula zomwe tiyenela kupewa kuti tisakhumudwitse Mulungu, anachulanso kufunika kopewa magazi.—Mac. 15:​20, 29.

Ngakhale kuti Baibo imabweleza mawu, izi sizitanthauza kuti Yehova afuna kuti tikhale na cizolowezi cobweleza ziganizo za m’Baibo. Mwacitsanzo, Yesu ananena kuti: “Iwe popemphela, usanene zinthu mobwelezabweleza.” (Mat. 6:7) Ndiyeno anapitiliza kuchula zinthu zomwe tingapemphelele zogwilizana na cifunilo ca Mulungu. (Mat. 6:​9-13) Conco, ngakhale kuti tiyenela kupewa kubweleza mawu amodzimodzi m’mapemphelo athu, ndife omasuka kubwelezanso mapemphelo amenewo nthawi ina.—Mat. 7:​7-11.

Pa zifukwa zabwino, mawu ouzilidwa a Mulungu amabweleza mawu ena na ziganizo zina. Iyi ni imodzi mwanjila zambili zomwe Mlangizi wathu Wamkulu amatiphunzitsila kuti tipindule.—Yes. 48:​17, 18.