Mmene zinalembedwera. Mabuku ena m’Baibulo analembedwa ngati nyimbo, mwachitsanzo buku la Masalimo, Nyimbo ya Solomo komanso la Maliro. Nthawi zina mawu a nyimbo ankabwerezedwa pofuna kutsindika mutu wa nyimboyo komanso kuthandiza omvetsera kuti aloweze mawu ake. Chitsanzo ndi mawu opezeka pa Salimo 115:9-11, pomwe amati: “Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.” Kodi mwaona mmene kubwereza mawuwa kukanathandizira oimbawo, kuti mfundo zamtengo wapatali zachoonadizi zikhazikike m’mitima mwawo?