Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Pezani Cuma Cauzimu Comwe Mungaseŵenzetse

Pezani Cuma Cauzimu Comwe Mungaseŵenzetse

Tikamaŵelenga Baibo, timapeza cuma cauzimu mwa kufufuza mfundo zothandiza. Koma kodi tingatani kuti tizipindula mofikapo?

Kumbani mozamilapo kuti muimvetse bwino nkhani ya m’Baibo. Mwacitsanzo, pezani mayankho pa mafunso akuti, kodi ndani analemba nkhaniyi? Analembela ndani? Nanga anailemba liti? Kodi zinthu zinali bwanji pomwe anali kuilemba? Nanga n’ciyani cinacitika pambuyo pake?

Dziŵani phunzilo limene lilipo mwa kupeza mayankho pa mafunso monga akuti: ‘Kodi okhudzidwa na nkhaniyi anamva bwanji? Kodi anaonetsa makhalidwe otani? N’cifukwa ciyani niyenela kutengela makhalidwe awo kapena kuwapewa?’

Gwilitsani nchito phunzilo lake, mwina mu utumiki kapena pocita zinthu na anthu ena. Potelo, mudzaonetsa nzelu ya umulungu, monga Baibo imakambila kuti: “Wanzelu ndani? Iye aona zimenezi.”—Sal. 107:43.

  • Mfundo yothandiza: Onani mmene zofalitsa zomwe zimaikidwa pa mbali yakuti Cuma Copezeka m’Mawu a Mulungu pa msonkhano wamkati mwa mlungu zimatithandizila kuona mmene tingaseŵenzetsele zimene tiphunzilapo. Mbali imeneyi imakhala na mafunso amene tingadzifunse, mfundo zimene tingasinkhesinkhepo, komanso zitsanzo zimene tingakambilane.