Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

NYIMBO 64 Timasangalala Kuthandiza pa Nchito Yokolola

Mmene Tingaonjezele Cimwemwe Cathu mu Ulaliki

Mmene Tingaonjezele Cimwemwe Cathu mu Ulaliki

“Tumikilani Yehova mokondwela.”SAL. 100:2.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nkhani ino itithandiza kuona zimene tingacite kuti tiwonjezele cimwemwe cathu pogwila nchito yolalikila.

1. Kodi ofalitsa ena amamva bwanji kufikila anthu ena mu ulaliki? (Onaninso cithunzi.)

 IFE ANTHU a Yehova, timalalikila kwa ena cifukwa cokonda Atate wathu wa kumwamba, komanso cifukwa cofuna kuthandiza anthu ena kuti am’dziŵe. Ofalitsa ambili amasangalala kugwila nchito yolalikila. Koma ena cimaŵavuta kupeza cimwemwe pa nchito imeneyi. Cifukwa ciyani? Ofalitsa ena ni amanyazi komanso amantha. Ena cimaŵavuta kupita ku nyumba za anthu cosaitanidwa. Ndipo ena amaopa kuti mwininyumba sadzaŵalandila bwino. Komanso, ena anaphunzitsidwa kupewa kukhumudwitsa anthu ena. Ngakhale kuti abale na alongo athu amenewo amamukonda ngako Yehova, zimaŵavuta kufikila munthu amene samudziŵa kuti amulalikile. Ngakhale n’telo, iwo amadziŵa kuti nchitoyi ni yofunika, ndipo amaigwila mokhazikika. Izi zimam’kondweletsa ngako Yehova!

Kodi mumasangalala pogwila nchito yolalikila? (Onani ndime 1)


2. Ngati cimakuvutani kupeza cimwemwe pa nchito yolalikila, n’cifukwa ciyani simuyenela kutaya mtima?

2 Kodi inunso zimene tachula pamwambapa zimakulepheletsani kupeza cimwemwe polalikila? Ngati n’telo, musataye mtima. Izi zimaonetsa kuti ndinu wodzicepetsa, komanso sim’madzifunila ulemu. Cina, zimaonetsanso kuti simufuna kukangana na ena. Palibe munthu amene amafuna kukanidwa maka-maka ngati akuyesetsa kucitila ena zabwino. Atate wathu wa kumwamba amadziŵa bwino zopinga zimene mumakuna nazo polalikila, ndipo amafuna kukupatsani thandizo lofunikila. (Yes. 41:13) M’nkhani ino, tikambilane malingalilo 5 amene angatithandize kugonjetsa zopingazo, komanso kuwonjezela cimwemwe cathu pa nchito yolalikila.

LOLANI MAWU A MULUNGU KUKULIMBIKITSANI

3. N’ciyani cinam’thandiza mneneli Yeremiya kulalikila kwa ena?

3 Kucokela m’nthawi ya makedzana, uthenga wa Mulungu wakhala ukulimbikitsa atumiki ake akafuna kugwila nchito yovuta. Ganizilani citsanzo ca mneneli Yeremiya. Iye anadodoma Yehova atamuuza kuti akalalikile. Iye anati: “Ine sinditha kulankhula cifukwa ndine mwana.” (Yer. 1:6) N’ciyani cinamuthandiza kugonjetsa manthawo? Anapeza cilimbikitso pa mawu amene Mulungu anamuuza. Yeremiya anati: “Mawu ake anali ngati moto woyaka umene watsekeledwa mʼmafupa anga, ndipo ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule.” (Yer. 20:​8, 9) Ngakhale kuti Yeremiya anali na gawo louma, uthenga umene anauzidwa kulengeza unam’patsa mphamvu zofunikila kuti agwile nchitoyo.

4. N’ciyani cimacitika tikamaŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha? (Akolose 1:​9, 10)

4 Uthenga wa m’Mawu a Mulungu umawalimbikitsa Akhristu. M’kalata imene mtumwi Paulo analembela mpingo wa ku Kolose, anawafotokozela cifukwa cokhalila na cidziŵitso colondola. Iye anawauza kuti cidziŵitso cidzawalimbikitsa kuti ‘akhale ndi khalidwe logwilizana ndi zimene Yehova amafuna . . . pamene akupitiliza kubala zipatso pa nchito iliyonse yabwino.’ (Ŵelengani Akolose 1:​9, 10.) Nchito iliyonse yabwino imeneyi, imaphatikizapo kulalikila uthenga wabwino. Conco, pamene tiŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha, cikhulupililo cathu mwa Yehova cimalimba, ndipo timamvetsa kufunika kogaŵilako ena uthenga wa Ufumu.

5. Tingacite ciyani kuti tizipindula nako kuŵelenga Baibo?

5 Kuti tipindule kwambili na Mawu a Mulungu, tiyenela kupewa kuthamanga powaŵelenga, komanso powasinkhasinkha. Mukapeza lemba limene lakuvutani kulimvetsa, musalilumphe n’kupita pena. M’malo mwake, seŵenzetsani Watch Tower Publications Index kapena Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, kuti mudziŵe tanthauzo la lembalo. Ngati muŵelenga modekha, mudzakulitsa cidalilo canu cakuti Mawu a Mulungu amakamba zoona. (1 Ates. 5:21) Cidalilo canu cikakula kwambili, mudzakhala osangalala kuuzako ena zimene mumaŵelenga.

KONZEKELANI MOKWANILA MUSANAPITE MU ULALIKI

6. N’cifukwa ciyani tiyenela kukonzekela mokwanila tisanapite mu ulaliki?

6 Mukaukonzekela mokwanila ulaliki wanu, simudzakhala na mantha kwambili pokamba na anthu. Yesu anakonzekeletsa ophunzila ake asanawatumize mu ulaliki. (Luka 10:​1-11) Cifukwa coseŵenzetsa zimene Yesu anawaphunzitsa, ophunzilawo anapeza cimwemwe pa zimene anakwanitsa kucita.—Luka 10:17.

7. Kodi tingaukonzekele motani ulaliki? (Onaninso cithunzi.)

7 Kodi tingaukonzekele motani ulaliki? Tiyenela kuganizila mmene tingafotokozele coonadi mogwila mtima kwa ena m’mawu athu-athu. Zimakhalanso bwino kuganizila njila ziŵili kapena zitatu za mmene anthu angalandilile uthenga wathu. Kenaka tiziona mmene tingayankhile. Ndipo tikafikila munthu tizikhala odekha, tizimwetulila na kukhala waubwenzi.

Konzekelani bwino musanapite mu ulaliki (Onani ndime 7)


8. Kodi Akhristu ali ngati ziwiya za dothi zimene Paulo anachula m’lingalilo lotani?

8 Mtumwi Paulo anauza abale na alongo ake kuti: “Tili ndi cuma cimeneci mu ziwiya zadothi.” (2 Akor. 4:7) Kodi cuma cimeneci n’ciyani? Ni nchito yolalikila uthenga wa Ufumu, imene imapulumutsa miyoyo. (2 Akor. 4:1) Nanga ziwiya za dothi n’ciyani? Ni atumiki a Mulungu, amene amagaŵilako ena uthenga wabwino. M’nthawi ya Paulo, a zamalonda anali kuseŵenzetsa ziwiya za dothi ponyamula zinthu za mtengo wapatali monga cakudya, vinyo, na ndalama. Mofananamo, Yehova watipatsa uthenga wabwino wa mtengo wapatali. Na thandizo lake, timakhala na mphamvu zofunikila kuti tilalikile uthenga wabwino mokhulupilika.

PEMPHELANI KUTI MUKHALE WOLIMBA MTIMA

9. N’ciyani cingatithandize kuleka kuopa anthu, komanso kuopa kuti uthenga wathu udzakanidwa? (Onaninso cithunzi.)

9 Nthawi zina, tingamaope anthu kapena kuopa kutsutsidwa. Nanga tingagonjetse bwanji mantha amenewa? Ganizilani pemphelo limene atumwi anapeleka atalamulidwa kuti aleke kulalikila. M’malo mocita mantha, iwo anapempha Yehova kuti ‘apitilize kulankhula mawu ake molimba mtima.’ Yehova anayankha pemphelo lawo nthawi yomweyo. (Mac. 4:​18, 29, 31) Ngati nthawi zina nafenso timacita mantha, tizipemphela kwa Yehova kuti atithandize. M’pempheni kuti akuthandizeni kukulitsa cikondi canu pa anthu kuti muleke kuopa kuwauzako uthenga wabwino.

Pemphelani kuti mukhale wolimba mtima (Onani ndime 9)


10. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kukwanilitsa udindo wathu monga Mboni zake? (Yesaya 43:​10-12)

10 Yehova anatisankha kuti tikhale Mboni zake, ndipo analonjeza kuti adzatithandiza kukhala olimba mtima. (Ŵelengani Yesaya 43:​10-12.) Nazi njila zinayi mwa njila zambili zimene amacitila zimenezi. Yoyamba, Yesu amakhala nafe nthawi zonse tikamalalikila uthenga wabwino. (Mat. 28:​18-20) Yaciŵili, Yehova anasankha angelo kuti azitithandiza. (Chiv. 14:6) Yacitatu, Yehova watipatsa mzimu woyela umene umatithandiza kukumbukila zinthu zimene tinaphunzila. (Yoh. 14:​25, 26) Yacinayi, Yehova watipatsa abale na alongo athu amene amakhala nafe polalikila. Na thandizo la Yehova komanso la apaubale wathu, tili na zonse zimene tifunikila kuti tikhale opambana pa nchitoyi.

NKHALANI OKONZEKA KUSINTHA NDIPO KHALANI NA MAGANIZO OYENELA

11. Kodi mungatani kuti muzipeza anthu ambili mu ulaliki? (Onaninso cithunzi.)

11 Kodi mumagwa ulesi ngati anthu ambili sapezeka pa nyumba? Mungadzifunse kuti: ‘Kodi anthu a m’gawo langa amapita kuti pa nthawi ino?’ (Mac. 16:13) ‘Kodi ali ku nchito kapena apita kugula zinthu ku msika?’ Ngati n’telo, kodi mungapeze anthu ambili mwa kulalikila m’misewu kapena m’misika? M’bale wina dzina lake Joshua anati: “Nimapeza mipata yambili yolalikila mwa kupita m’misika, komanso m’malo ena amene kumapezeka anthu ambili.” Iye na mkazi wake, Bridget, amapeza anthu ambili pa nyumba akapita m’gawo lawo m’madzulo, komanso masana pa Sondo.—Aef. 5:​15, 16.

Sinthani ndandanda yanu (Onani ndime 11)


12. Tingadziŵe bwanji zimene anthu amakhulupilila kapena zimene zimawadetsa nkhawa?

12 Ngati anthu saonetsa cidwi pa uthenga wanu, yesani kudziŵa zimene amakhulupilila kapena zimene zimawadetsa nkhawa. M’bale Joshua na mkazi wake Bridget, amaseŵenzetsa funso la patsamba loyamba la kathilakiti poyambitsa makambilano. Mwa citsanzo, poseŵenzetsa kathilakiti kakuti Kodi Baibo Mumaiona Bwanji? iwo amati: “Anthu ena amakhulupilila kuti Baibo ni buku locokela kwa Mulungu, koma ena sakhulupilila zimenezi. Nanga inu muganiza bwanji?” Nthawi zambili izi zimawathandiza kuyambitsa makambilano.

13. N’ciyani cingatipangitse kuona kuti tapeza cipambano, ngakhale pamene anthu sanalandile uthenga wathu? (Miyambo 27:11)

13 Cipambano cathu mu ulaliki sicidalila mmene anthu akulabadilila uthenga wathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa tacita zimene Yehova na Mwana wake amafuna kuti ticite—kupeleka umboni. (Mac. 10:42) Ngakhale pamene sitinapeze aliyense wokamba naye, kapena pamene uthenga wathu wakanidwa, timakhala na cisangalalo podziŵa kuti takondweletsa Atate wathu wa kumwamba.—Ŵelengani Miyambo 27:11.

14. N’cifukwa ciyani timasangalala wofalitsa wina akapeza munthu wacidwi m’gawo?

14 Timasangalala wofalitsa wina akapeza munthu wacidwi m’gawo. Nsanja ya Mlonda ina inayelekezela nchito yathu na nchito yosakila mwana amene wasoŵa. Ambili angathandizile kufuna-funa mwanayo, mwa kupita ku malo osiyana-siyana kukamufuna-funa. Mwanayo akapezeka—aliyense amene wagwilako nchitoyo amasangalala—osati cabe amene wamupeza. Mofananamo, nchito yopanga ophunzila ni khama la anthu ambili. Ofalitsa onse amapita kukalalikila m’gawo, ndipo onse amakondwela wacatsopano akayamba kupezeka ku misonkhano.

IKANI MAGANIZO ANU PA KUKONDA YEHOVA NA ANTHU

15. Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa Mateyu 22:​37-39 kungatithandize bwanji kuwonjezela cimwemwe cathu pa nchito yolalikila? (Onaninso cithunzi ca pacikuto.)

15 Tingakulitse cimwemwe cathu pa nchito yolalikila ngati timakonda kwambili Yehova, komanso anzathu. (Ŵelengani Mateyu 22:​37-39.) Tangoganizilani cimwemwe cimene Yehova amakhala naco akationa tikugwila nchitoyi, komanso cimwemwe cimene anthu amakhala naco akayamba kuphunzila Baibo! Ganizilaninso cipulumutso cimene anthu amene amalandila uthenga wathu adzakhala naco.—Yoh. 6:40; 1 Tim. 4:16.

Kukonda kwambili Yehova, komanso anzathu kudzawonjezela cimwemwe cathu pa nchito yolalikila (Onani ndime 15)


16. Tingatani kuti tipeze cimwemwe panchito yolalikila ngakhale kuti siticoka pa nyumba? Fotokozani zitsanzo.

16 Kodi simumakwanitsa kucoka pa nyumba pa cifukwa cina cake? Ngati n’telo, ikani maganizo anu pa mmene mungaonetsele cikondi canu kwa Yehova, komanso anthu ena. Pa mlili wa COVID-19, m’bale Samuel na mlongo Dania sanali kucoka pa nyumba. Panthawi yonseyi yovuta, iwo anali kucita ulaliki wa pafoni, wa m’makalata, komanso kutsogoza maphunzilo pa Zoom. M’bale Samuel anali kulalikila anthu amene anali kuwapeza ku cipatala, kumene anali kulandila cithandizo pa matenda ake a khansa. Iye anati: “Mavuto amatilefula m’maganizo, mwakuthupi, komanso mwauzimu. Koma tifunikila kupeza cimwemwe potumikila Yehova.” Mkati mwa zocitika zimenezi, mlongo Dania anagwa ndipo anakhala cigonele pa bedi kwa miyezi itatu. Ndiyeno anaseŵenzetsa njinga ya olemala kwa miyezi 6. Iye anati: “Ninayesetsa kucita zimene nikanatha pa nchito yolalikila. N’nali kulalikila nesi amene anali kubwela kunisamalila. Ndipo n’nali kukamba na anthu amene anali kubweletsa zinthu zimene tinali kugula. N’nali kukhalanso na makambilano abwino pafoni na mzimayi wina amene anali kugwila nchito zacipatala.” Zimene zinacitikila m’bale Samuel na mlongo Dania zinawalepheletsa kucita zambili pa nchito yolalikila. Komabe, iwo anacita zimene akanatha pa nchitoyi, ndipo anali kusangalala pocita zimenezi.

17. Mungacite ciyani kuti mupindule mokwanila na mfundo zimene zafotokozedwa mu nkhani ino?

17 Mfundo 5 zimene zafotokozedwa m’nkhani ino, zimagwila bwino nchito ngati zaseŵenzetsedwa pamodzi. Mfundo iliyonse ili ngati cokometsela cakudya. Tikaziika zonse mu cakudya, cakudyaco cimakoma. Tikaseŵenzetsa mfundo zonse, tidzakhala okonzeka kuthana na maganizo alionse olefula, ndipo tidzakhala na cimwemwe pa nchito yolalikila.

KODI KUCITA ZOTSATILAZI KUNGAKUTHANDIZENI BWANJI KUPEZA CIMWEMWE PA NCHITO YOLALIKILA?

  • Kupatula nthawi yokonzekela bwino

  • Kupemphela kuti mukhale olimba mtima

  • Kukonda Yehova komanso anzathu

NYIMBO 80 “Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino”