ZOTI NDIPHUNZIRE

Anthu Okonda Yehova Amasankha Zinthu Mwanzeru

Anthu Okonda Yehova Amasankha Zinthu Mwanzeru

Werengani Genesis 25:29-34 kuti muone ngati Esau ndi Yakobo anasankha zinthu mwanzeru.

Fufuzani mozama nkhani yake. Kodi n’chiyani chinachitika poyamba? (Gen. 25:20-28) Nanga n’chiyani chinachitika pambuyo pake?​—Gen. 27:1-46.

Fufuzani mozama mfundo zake. Kodi pa nthawiyo mwana woyamba ankakhala ndi ufulu komanso udindo uti?​—Gen. 18:18, 19; lfb 12:3.

  • Kodi nthawi zonse kukhala mwana woyamba kunkaphatikizapo kukhala kholo la Mesiya? (w17.12 14-15)

Onani zimene mukuphunzirapo, ndipo muzizitsatira. Mosiyana ndi Esau, n’chifukwa chiyani Yakobo ankaona kuti kukhala mwana woyamba n’kofunika kwambiri? (Aheb. 12:16, 17; lfb 12) Kodi Yehova ankawaona bwanji anthu awiriwa, nanga n’chifukwa chiyani? (Mal. 1:2, 3) Kodi Esau ankafunika kuchita chiyani kuti asankhe zinthu mwanzeru?

  • Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimayamikira zinthu zauzimu mlungu uliwonse, mwachitsanzo poonetsetsa kuti tikuchita kulambira kwa pabanja?’