Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 19

NYIMBO 22 Ufumu Ulamulila—Ubwele!

Kodi Tidziŵapo Ciyani za Mmene Yehova Adzaweluzile Anthu M’tsogolo?

Kodi Tidziŵapo Ciyani za Mmene Yehova Adzaweluzile Anthu M’tsogolo?

“Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.”2 PET. 3:9.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Sitikayika ngakhale pang’ono kuti ziweluzo za Yehova za m’tsogolo zidzakhala zolungama.

1. N’cifukwa ciyani tinganene kuti tikukhala m’nthawi yapadela?

 TIKUKHALA m’nthawi yapadela kwambili! Tsiku lililonse, timaona kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo. Mwa citsanzo, timaona “mfumu yakum’mwela” na “mfumu yakumpoto” akukankhana polimbilana ulamulilo wa dziko lonse. (Dan. 11:​40, mawu a m’munsi.) Tikuonanso uthenga wabwino ukulalikidwa pa mlingo waukulu ndipo anthu mamiliyoni akuulandila. (Yes. 60:22; Mat. 24:14) Ndipo timalandila cakudya cauzimu coculuka “pa nthawi yoyenela.”—Mat. 24:​45-47.

2. Ndife otsimikiza za ciyani? Ndipo tiyenela kuzindikila ciyani?

2 Yehova akutithandiza kumvetsa bwino zinthu zazikulu zimene zidzacitika posacedwa. (Miy. 4:18; Dan. 2:28) Ndife otsimikiza kuti cisautso cacikulu cisanayambe, tidzakhala titadziŵa zonse zofunikila kuti tipilile mokhulupilika, na kupambana panthawi yovuta imeneyo. Komabe, tiyenela kuzindikila kuti pali zinthu zina zimene sitidziŵa zimene zidzacitika posacedwa. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tasintha kamvedwe kathu pa zinthu zomwe tinanena kumbuyoku zokhudza zimene zidzacitike kutsogoloku. Tikambilanenso zimene tidziŵa za kutsogolo, komanso mmene Atate wathu wa kumwamba adzacitile zinthu.

ZIMENE SITIDZIŴA

3. Kodi kumbuyoku tinali kunena ciyani za kutsekedwa kwa mwayi wowolokela kumbali ya Yehova? Ndipo n’ciyani cinatifikitsa pa mfundo imeneyi?

3 Kumbuyoku tinali kunena kuti cisautso cacikulu cikadzangoyamba, palibe osakhulupilila amene adzakhalenso na mwayi wokhala kumbali ya Yehova na kupulumuka Aramagedo. Tinafika pa mfundo imeneyi cifukwa kamvedwe kathu pa nthawiyo kanali kakuti nkhani ya Cigumula inali kuphiphilitsila zinthu za kutsogolo. Mwa citsanzo, Yehova “anatseka citseko” ca cingalawa Cigumula cisanayambe. Conco, tinali kuona kuti kuciyambi kwa cisautso cacikulu Yehova adzatsekanso mwayi kwa anthu a m’dzikoli wowolokela kumbali yake kuti apulumuke.—Mat. 24:​37-39.

4. N’cifukwa ciyani sitinenanso kuti Cigumula cinacitila mthunzi za m’tsogolo?

4 Kodi tiyenela kuona kuti zimene zinacitika pa Cigumula zinali mthunzi wa zinthu za kutsogolo? Ayi. Cifukwa ciyani? Cifukwa Baibo siinena zimenezo mwachuchuchu. a N’zoona kuti Yesu anayelekezela “masiku a Nowa” na nthawi ya kukhalapo kwake. Koma iye sanakambe kuti Cigumula cinali mthunzi wa zocitika za kutsogolo, kutanthauza kuti munthu aliyense, kapena cocitika ciliconse, ngakhale kutsekedwa kwa citseko zinaphiphilitsila za kutsogolo ayi. Koma sindiye kuti sitingatengepo phunzilo lililonse pa Cigumula ca m’nthawi ya Nowa.

5. (a) Kodi Nowa anacita ciyani Cigumula cisanayambe? (Aheberi 11:7; 1 Petulo 3:20) (b) Kodi pali kufanana kotani pakati pa ife na Nowa pogwila nchito yolalikila?

5 Nowa atalandila uthenga wocenjeza wa Yehova anaonetsa kuti anali na cikhulupililo mwa kukhoma Cingalawa. (Ŵelengani Aheberi 11:7; 1 Petulo 3:20.) Mofananamo, anthu amene amamvetsela uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ayenela kucitapo kanthu pa zimene amvazo. (Mac. 3:​17-20) Petulo anacha Nowa “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5) Komabe, monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, sitidziŵa ngati Nowa anapanga kampeni yakuti mpaka afikile munthu aliyense pa dziko lonse lapansi kuti amulalikile Cigumula cisanacitike. Masiku ano, timayesetsa kulalikila kwa anthu onse padziko lonse lapansi. Ndipo timacita zimenezi mokangalika kwambili. Komabe, ngakhale titayesetsa bwanji, sitingakwanitse kufikila munthu aliyense kuti timulalikile uthenga wabwino mapeto asanafike. Cifukwa ciyani?

6-7. Kodi tidzakwanitsa kulalikila uthenga wabwino kwa munthu aliyense padzikoli mapeto asanafike? Fotokozani.

6 Ganizilani zimene Yesu ananena za kukula kwa nchito yathu yolalikila. Iye ananenelatu kuti uthenga wabwino uyenela kulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse.” (Mat. 24:14) Ulosi umenewu ukukwanilitsidwa pa mlingo waukulu zedi masiku ano kuposa n’kale lonse. Uthenga wa Ufumu ukufalitsidwa m’zinenelo zoposa 1,000. Ndipo anthu ambili pa dziko lonse akuulandila mosavuta kudzela pa webusaiti ya jw.org.

7 Yesu anauzanso ophunzila ake kuti sadzamaliza “kuzungulila mizinda yonse,” kapena kuti kulalikila munthu aliyense iye asanabwele. (Mat. 10:23; 25:​31-33) Mawu a Yesu amenewa akukwanilitsidwanso masiku ano. Anthu ofika m’mamiliyoni amakhala m’madela amene nchito yathu ni yoletsedwa kwambili. Kuwonjezela apo, ana mahandiledi amabadwa mphindi iliyonse. Ngakhale timacita zonse zotheka kuti tilalikile uthenga wabwino kwa anthu a “kudziko lililonse, fuko lililonse, cilankhulo ciliconse ndi mtundu uliwonse,” zoona zake n’zakuti sitingakwanitse kulalikila munthu aliyense pa dziko lapansi.—Chiv. 14:6.

8. Kodi pangabwele funso lanji za mmene Yehova adzaweluzila anthu m’tsogolo? (Onaninso zithunzi)

8 Izi zimautsa funso lina lakuti: N’ciyani cidzacitikile anthu amene alibe mwayi womvetsela uthenga wabwino cisautso cacikulu cisanayambe? Kodi Yehova na Mwana wake, amene wamusankha kuti adzaweluze anthu, adzawaweluza motani? (Yoh. 5:​19, 22, 27; Mac. 17:31) Lemba lomwe pacokela mfundo yaikulu ya nkhani ino imati, “Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.” M’malo mwake, iye afuna kuti “anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9; 1 Tim. 2:4) Ngakhale kuti tidziŵa mfundo imeneyi, iye akalibe kutiululila mmene adzaweluzile anthuwo. Ndi iko komwe, iye safunikila kutiuza zilizonse za zimene anacitapo kumbuyo kapena zimene adzacita m’tsogolo.

Kodi Yehova adzawaweluza motani anthu amene sanakhalepo na mwayi womvetsela uthenga wabwino cisautso cacikulu cisanafike? (Onani ndime 8) c


9. Kodi Yehova watiululilako zotani kudzela m’Baibo?

9 Kupitila m’Mawu ake, Yehova watiululilako zina zimene adzacite kutsogolo. Mwa citsanzo, Baibo imatiuza kuti Yehova adzaukitsa anthu “osalungama” amene sanakhalepo na mwayi womvetsela uthenga wabwino na kusintha njila zawo. (Mac. 24:15; Luka 23:​42, 43) Izi zimautsanso mafunso ena ofunika.

10. Ni mafunso ena ati amene angakhalepo?

10 Kodi onse amene adzafa pa cisautso cacikulu adzakhala alibe ciyembekezo codzaukitsidwa? Malemba amakamba momveka bwino kuti anthu amene amatsutsa Yehova adzawonongedwa na magulu ake a nkhondo pa Aramagedo, ndipo sadzaukitsidwa. (2 Ates. 1:​6-10) Nanga n’ciyani cidzacitikile anthu amene adzafa panthawiyo cifukwa ca ukalamba, matenda, ngozi, kapena kuphedwa na anthu ena? (Mlal. 9:11; Zek. 14:13) Kodi n’kutheka kuti angadzakhale pakati pa anthu “osalungama” amene adzaukitsidwa m’dziko latsopano? Sitidziŵa.

ZIMENE TIDZIŴA

11. Kodi anthu adzaweluzidwa pa maziko ati pa Aramagedo?

11 Tidziŵa zinthu zingapo pa zimene zidzacitika m’tsogolo. Mwa citsanzo, tidziŵa kuti pa Aramagedo anthu adzaweluzidwa mogwilizana na zimene anacitila abale ake a Khristu. (Mat. 25:40) Amene adzaweluzidwe kukhala nkhosa, ni amene anali kucilikiza odzozedwa komanso Khristu. Tidziŵanso kuti ena mwa abale a Khristu adzakhalabe pa dziko lapansi cisautso cacikulu cikadzayamba, koma adzatengeledwa kumwamba Aramagedo itatsala pang’ono kubuka. Malinga ngati abale a Khristu ali pa dziko lapansi, n’kutheka kuti anthu ena oona mtima nawonso adzakhala na mwayi wocilikiza abale a Khristu pa nchito yawo. (Mat. 25:​31, 32; Chiv. 12:17) N’cifukwa ciyani mfundo zimenezi n’zofunika kwambili?

12-13. Kodi ena angadzacite ciyani pambuyo poona kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu”? (Onaninso zithunzi)

12 Ngakhale cisautso cacikulu citayamba kale, n’kutheka kuti anthu amene adzaona kugwa kwa “Babulo Wamkulu” adzakumbukila kuti Mboni za Yehova zinali kunena za cocitika cimeneci kwa zaka zambili. Kodi amene adzaone zocitika zimenezi angadzasinthe maganizo awo?—Chiv. 17:5; Ezek. 33:33.

13 Ngati anthuwo angadzasinthe maganizo awo, zingakhale monga zinacitikila ku Iguputo m’nthawi ya Mose. Kumbukilani kuti “gulu la anthu a mitundu yosiyana-siyana” linatsagana nawo Aisiraeli potuluka mu Iguputo. Ena mwa anthuwo cikhulupililo cawo cinayamba kukula ataona kuti Milili 10 imene Mose anacenjeza inacitikadi. (Eks. 12:38) Ngati zotelozi zingadzacitike pambuyo pakuti Babulo Wamkulu wawonongedwa, kodi tingadzakhumudwe poona kuti anthu ena awolokela kumbali yathu mapeto atatsala pang’ono kufika? Kutalitali! Tifuna kutengela umunthu wa Atate wathu wa kumwamba yemwe ni, “Mulungu wacifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wacikondi cokhulupilika coculuka komanso coonadi.” bEks. 34:6.

Ena amene adzaona kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu,” adzakumbukila kuti Mboni za Yehova zinali kunenapo za cocitika cimeneci kwa zaka (Onani ndime 12-13) d


14-15. Kuti munthu akakhale na moyo wosatha, kodi zidalila kuti anamwalila liti, ndiponso kumene akukhala? Fotokozani. (Salimo 33:​4, 5)

14 Nthawi zina timamva ena akunena kuti, “Zingakhale bwino wacibale wanga atamwalila cisautso cacikulu cisanayambe, kuti mwina angakhale na mwayi wodzaukitsidwa.” Iwo amakamba zimenezi na zolinga zabwino. Koma kuti munthu akakhale na moyo wosatha sizidalila kuti anamwalila liti. Yehova ni woweluza wangwilo—amaweluza mwacilungamo. (Ŵelengani Salimo 33:​4, 5.) Ndife otsimikiza kuti “Woweluza wa dziko lonse lapansi” adzacita zoyenela.—Gen. 18:25.

15 Komanso, kuti munthu akakhale na moyo wosatha sizidalila kumene akukhala. Yehova sangaweluze anthu ofika m’mamiliyoni kuti ni “mbuzi” cabe cifukwa akukhala kumene analibe mwayi wolandila uthenga wa Ufumu kuti asinthe umoyo wawo. (Mat. 25:46) Woweluza wa dziko lonse wolungama amawadela nkhawa anthu amenewo kuposa mmene ife tingacitile. Sitidziŵa mmene Yehova adzayendetsele zinthu pa cisautso cacikulu. Mwina ena mwa anthu amenewo adzakhala na mwayi wophunzila za Yehova, kumukhulupilila, na kuwolokela ku mbali yake pamene iye adzapangitsa anthu onse padziko kuti am’dziŵe.—Ezek. 38:16.

Cisautso cacikulu cikadzayamba, . . . kodi pali ena amene adzasintha maganizo awo akadzaona zocitika zimenezi?

16. Kodi tafika podziŵa zotani ponena za Yehova? (Onaninso cithunzi)

16 Kuphunzila Baibo mwakhama kwatithandiza kudziŵa kuti Yehova amaona moyo wa munthu kukhala wa mtengo wapatali. Anapeleka moyo wa Mwana wake kuti tonsefe tipeze mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. (Yoh. 3:16) Ndipo tonsefe tikuona cikondi cake pa ife. (Yes. 49:15) Iye amatidziŵa bwino kwambili ngakhalenso maina athu. Amatidziŵadi bwino lomwe, aliyense payekha-payekha, moti ngakhale titafa akhoza kulenganso mbali iliyonse ya umunthu wathu na kubwezeletsa maganizo athu onse! (Mat. 10:​29-31) Kunena zoona, sitikaikila zakuti Yehova adzaweluza munthu aliyense mwacilungamo cifukwa ni wanzelu, wolungama, komanso wacifundo.—Yak. 2:13.

Sitikayikila kuti Yehova adzaweluza munthu aliyense mwacilungamo cifukwa ni wanzelu, wolungama, komanso wacifundo (Onani ndime 16)


17. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

17 Kamvedwe katsopano kameneka katithandiza kuona kuti nchito yolalikila iyenela kugwilidwa mwacangu kuposa n’kale lonse. Tikutelo cifukwa ciyani? Ndipo n’ciyani cimatikolezela kuti tipitilize kulalikilabe uthenga wabwino mwakhama? Tidzakambilana bwino lomwe mayankho a mafunso amenewa m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 76 Kodi Mumamvela Bwanji?

a Kuti mudziŵe cifukwa cake pakhala masinthidwe amenewa, onani nkhani yakuti “Munavomeleza Kuti Zimenezi Zicitike” mu Nsanja ya Mlonda ya March 15, 2015, masamba 7-11.

b Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, atumiki onse a Yehova adzayesedwa pamene Gogi wa Magogi adzawaukila. Aliyense amene adzakhale kumbali ya anthu a Mulungu, pambuyo pa kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, nayenso adzayesedwa.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Zifukwa zitatu zoonetsa kuti n’zosatheka kufikila munthu aliyense pa nchito yathu yolalikila: (1) Mzimayi akukhala ku dziko kumene kulalikila n’koopsa cifukwa ca cipembedzo ca kumeneko, (2) banja likukhala m’dziko limene boma linaletsa nchito yathu yolalikila, (3) munthu akukhala ku malo akutali kwambili komanso ovuta kufikako.

d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mtsikana amene analeka kutumikila Yehova wakumbukila zimene anaphunzila za kugwa kwa “Babulo Wamkulu.” Cotelo akuyambilanso kutumikila Yehova ndipo akubwelelanso kwa makolo ake a Cikhristu. Ngati zotelezi zingadzacitike, tiyenela kutengela Atate wathu wa kumwamba amene ni wacifundo komanso wacikondi, na kusangalala kuti wocimwa wabwelela kwa iye.