NKHANI YOPHUNZIRA 25

NYIMBO NA. 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

Muzikumbukira Yehova Yemwe ndi “Mulungu Wamoyo”

Muzikumbukira Yehova Yemwe ndi “Mulungu Wamoyo”

“Yehova ndi wamoyo.”​—SAL. 18:46.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kuona kuti timapindula chifukwa chodziwa kuti amene timamulambira ndi “Mulungu wamoyo.”

1. Kodi n’chiyani chimathandiza anthu a Yehova kuti azipitirizabe kumulambira ngakhale kuti amakumana ndi mavuto?

 BAIBULO limanena kuti nthawi tikukhalayi ndi “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Kuwonjezera pa mavuto amene aliyense amakumana nawo m’dzikoli, anthu a Yehova amatsutsidwa komanso kuzunzidwa. N’chiyani chingatithandize kuti tizitumikirabe Yehova ngakhale pamene tikukumana ndi mavutowa? Chinthu chimodzi chimene chimatithandiza ndi kudziwa kuti Yehova ndi “Mulungu wamoyo.”​—Yer. 10:10; 2 Tim. 1:12.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo?

2 Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo ndipo nthawi zonse amafunitsitsa kutithandiza. (2 Mbiri 16:9; Sal. 23:4) Kukumbukira kuti Mulungu ndi wamoyo kungatithandize kulimbana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. Tiyeni tione mmene kudziwa zimenezi kunathandizira Mfumu Davide.

3. Kodi Davide ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “Yehova ndi wamoyo”?

3 Davide ankadziwa Yehova ndipo ankamudalira. Pamene Mfumu Sauli komanso adani ake ankafuna kumupha, Davide anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. (Sal. 18:6) Mulungu atayankha pemphero lake n’kumupulumutsa, Davide ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Polankhula mawu amenewa, Davide sankatanthauza kuti ankangodziwa kuti Mulungu aliko. Buku lina linanena kuti Davide ankakhulupirira kuti Yehova “ndi Mulungu wamoyo yemwe nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Zimene zinachitika pa moyo wa Davide zinamutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo zinamulimbikitsa kuti apitirize kumutumikira komanso kumutamanda.​—Sal. 18:28, 29, 49.

4. Kodi kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo kumatithandiza bwanji?

4 Kukhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo kungatithandize kuti tizimutumikira ndi mtima wonse. Tidzapeza mphamvu kuti tizipirira mayesero komanso tizichita zambiri pomutumikira. Tidzakhalanso ofunitsitsa kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi.

MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHAMVU

5. N’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima tikamakumana ndi mavuto? (Afilipi 4:13)

5 Tingathe kupirira mayesero alionse kaya aakulu kapena aang’ono ngati timakumbukira kuti Yehova ndi wamoyo ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Ndipotu palibe vuto limene lingamukanike kulithetsa. Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo akhoza kutipatsa mphamvu kuti tipirire. (Werengani Afilipi 4:13.) Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti tingathe kupirira vuto lililonse. Tikaona Yehova akutithandiza pa mavuto ang’onoang’ono, sitikayikira kuti adzatithandizanso pa mavuto aakulu.

6. Kodi Davide ali wamng’ono anakumana ndi zotani zomwe zinachititsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova?

6 Taganizirani zimene zinachitika pa moyo wa Davide, zomwe zinachititsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Ali wamng’ono, chimbalangondo komanso mkango zinagwira nkhosa za bambo ake zomwe ankaweta. Pa nthawi zonsezi, Davide analimba mtima n’kuthamangitsa zilombozo ndipo anapulumutsa nkhosazo. Koma Davide sanaganize kuti wachita zimenezi ndi mphamvu zake. Ankadziwa kuti Yehova ndi amene wamuthandiza. (1 Sam. 17:34-37) Nthawi zonse Davide ankakumbukira zimene zinachitikazi. Kuganizira zimenezi kunamuthandiza kukhulupirira kuti Mulungu wamoyo adzamuthandizanso m’tsogolo.

7. Kodi kuona zinthu moyenera kunathandiza bwanji Davide kuti amenyane ndi Goliyati?

7 Patapita nthawi, Davide ali wachinyamata anapita kumsasa wa Aisiraeli. Iye anapeza asilikaliwo akuchita mantha chifukwa msilikali wamphamvu wa Afilisiti dzina lake Goliyati ‘ankanyoza asilikali a Isiraeli.’ (1 Sam. 17:10, 11) Asilikaliwo ankachita mantha chifukwa ankaganizira kwambiri za maonekedwe a munthuyo komanso mawu onyoza omwe ankalankhula. (1 Sam. 17:24, 25) Koma Davide ankaona zinthu mosiyana. Iye ankaona kuti Goliyati sankangonyoza asilikali a Aisiraeli koma ‘ankanyoza asilikali a Mulungu wamoyo.’ (1 Sam. 17:26) Davide ankaganizira kwambiri za Yehova. Iye ankakhulupirira kuti Mulungu amene anamuthandiza pamene ankaweta ziweto angamuthandizenso pa nthawiyi. Popeza ankakhulupirira kuti Mulungu amuthandiza, anapita kukamenyana ndi Goliyati ndipo anapambana.​—1 Sam. 17:45-51.

8. N’chiyani chingatithandize kuti tisamakayikire kuti Yehova atithandiza tikakumana ndi mavuto? (Onaninso chithunzi.)

8 Ifenso tingathe kupirira mayesero ngati timakumbukira kuti Mulungu wamoyo ndi wokonzeka kutithandiza. (Sal. 118:6) Tingamakhulupirire kwambiri zimenezi tikaganizira zimene anachitapo kale. Muziwerenga nkhani za m’Baibulo zosonyeza mmene anapulumutsira atumiki ake. (Yes. 37:17, 33-37) Komanso muziwerenga ndi kuonera malipoti a pa jw.org osonyeza mmene Yehova akuthandizira abale ndi alongo athu masiku ano. Kuwonjezera pamenepo, muziganiziranso mmene anakuthandizirani inuyo. Zilibe kanthu kuti simungatchule mavuto akuluakulu monga ngati kumenyana ndi mkango kapena chimbalangondo. Tikutero chifukwa Yehova wakhala akukuchitirani zambiri pa moyo wanu. Anakukokani kuti mukhale naye pa ubwenzi. (Yoh. 6:44) Ndipotu panopa, ndi iyeyo amene amakuthandizani kuti mupitirizebe kukhala m’choonadi. Choncho mungachite bwino kumupempha kuti akukumbutseni nthawi imene anayankha mapemphero anu, kukuthandizani pa nthawi yoyenera komanso kukusamalirani pa nthawi yovuta. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri kuti Yehova adzapitiriza kukuthandizani.

Zomwe timachita tikakumana ndi mayesero zimakhudza Yehova (Onani ndime 8-9)


9. Kodi tiziwaona bwanji mavuto amene timakumana nawo? (Miyambo 27:11)

9 Kukhulupirira kuti Yehova alikodi kungatithandize kuti tiziona moyenera mayesero amene timakumana nawo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timayamba kuona mavuto amene tikukumana nawo monga mbali ya nkhani yaikulu yomwe ilipo pakati pa Yehova ndi Satana. Mdyerekezi amanena kuti tikakumana ndi mavuto tingasiye kutumikira Yehova. (Yobu 1:10, 11; werengani Miyambo 27:11.) Koma tikakwanitsa kupirira mavutowo, timasonyeza kuti timakonda Yehova ndipo timatsutsa bodza la Mdyerekezi. Kodi inuyo mukutsutsidwa ndi akuluakulu a boma, mukukumana ndi mavuto a zachuma, anthu sakumvetsera uthenga wabwino kapena mukukumana ndi mayesero ena? Muzikumbukira kuti zimene mukukumana nazo zingakupatseni mwayi woti musangalatse mtima wa Yehova. Muzikumbukiranso kuti Mulungu sadzalola kuti muyesedwe mpaka kufika poti simungathe kupirira. (1 Akor. 10:13) Iye adzakupatsani mphamvu kuti mupirire.

MULUNGU WAMOYO ADZAKUPATSANI MPHOTO

10. Kodi Mulungu wamoyo adzawachitira chiyani anthu amene amamulambira?

10 Yehova amapereka mphoto kwa amene amamulambira. (Aheb. 11:6) Panopa iye amatipatsa mtendere komanso amatithandiza kukhala osangalala ndipo adzatipatsa moyo wosatha m’tsogolo. Timakhulupirira kwambiri kuti iye amafunitsitsa kutipatsa mphoto ndipo ali ndi mphamvu yochitira zimenezo. Tikamamukhulupirira kwambiri, timapitiriza kumutumikira ndi mtima wonse ngati mmene atumiki ake akale ankachitira. Izi ndi zimenenso Timoteyo anachita.​—Aheb. 6:10-12.

11. Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Timoteyo kuti azigwira ntchito mwakhama mumpingo? (1 Timoteyo 4:10)

11 Werengani 1 Timoteyo 4:10. Timoteyo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu wamoyo adzamupatsa mphoto. N’chifukwa chake iye ankachita khama potumikira Mulungu. Kodi iye ankachita bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo anamulimbikitsa kuti ayesetse kukhala mphunzitsi wabwino pa ntchito yolalikira komanso mumpingo. Iye ankafunikanso kukhala chitsanzo chabwino kwa Akhristu anzake, achinyamata ndi achikulire omwe. Anapatsidwanso ntchito yovuta yomwe inkaphatikizapo kupereka malangizo amphamvu koma achikondi kwa anthu omwe angafunikire malangizowo. (1 Tim. 4:11-16; 2 Tim. 4:1-5) Ngakhale kuti nthawi zina ena sankaona kapena kuyamikira zimene ankachita, Timoteyo sankakayikira kuti Yehova adzamupatsa mphoto.​—Aroma 2:6, 7.

12. Kodi n’chiyani chingalimbikitse akulu kuti azigwira ntchito zawo mwakhama? (Onaninso chithunzi.)

12 Masiku anonso akulu amadziwa kuti Yehova amaona komanso kuyamikira ntchito yabwino imene amagwira. Kuwonjezera pa kusamalira nkhosa za Mulungu, kuphunzitsa komanso kulalikira, akulu ambiri amathandizanso pantchito monga zomangamanga ndiponso kupereka thandizo pakachitika ngozi. Akulu enanso ali m’Magulu Oyendera Odwala kapena Makomiti Olankhulana ndi Achipatala. Akulu amene amadzipereka kugwira ntchito zimenezi amadziwa kuti Yehova ndiye mwiniwake wa mpingo osati munthu. Pachifukwa chimenechi, iwo amagwira ntchito zawo modzipereka ndipo amakhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzawapatsa mphoto chifukwa cha zimene amachita.​—Akol. 3:23, 24.

Mulungu wamoyo adzakupatsani mphoto mukamayesetsa kuchita zambiri mumpingo (Onani ndime 12-13)


13. Kodi Yehova amamva bwanji chifukwa cha zimene timachita pomutumikira mwakhama?

13 N’zosatheka kuti aliyense akhale mkulu. Koma tonsefe tingathe kumupatsa chinachake Yehova. Mulungu wathu amayamikira tikamayesetsa kumutumikira mwakhama. Iye amaona tikamapereka zinthu zathu pothandiza pa ntchito yapadziko lonse, ngakhale zitakhala zochepa. Amasangalala tikayesetsa kukweza mkono kuti tiyankhe pamisonkhano ngakhale kuti ndife amanyazi. Ndiponso amasangalala tikamanyalanyaza zolakwa za ena n’kuwakhululukira. Ngakhale mutamaona kuti simukuchita zambiri pomutumikira, dziwani kuti Yehova amayamikira zimene mumachita. Amakukondani chifukwa cha zimene mumachitazo ndipo adzakupatsani mphoto.​—Luka 21:1-4.

PITIRIZANI KUKHALA PA UBWENZI NDI MULUNGU WAMOYO

14. Kodi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kungatithandize bwanji kuti tikhale okhulupirika? (Onaninso chithunzi.)

14 Tikamakhulupirira kuti Yehova alikodi, zingakhale zosavuta kuti tikhale okhulupirika kwa iye. Umu ndi mmenenso zinalili ndi Yosefe. Iye anakanitsitsa kuchita zachiwerewere chifukwa ankadziwa kuti zochita zake zimakhudza Mulungu ndipo sankafuna kumukhumudwitsa. (Gen. 39:9) Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova tiyenera kumapemphera komanso kuphunzira Mawu ake. Tikamachita zimenezi, ubwenzi wathu ndi iye udzakhala wolimba kwambiri. Choncho mofanana ndi Yosefe, tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, sitidzachita chilichonse chomwe chingamukhumudwitse.​—Yak. 4:8.

Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu wamoyo kungakuthandizeni kuti mupitirize kukhala okhulupirika (Onani ndime 14-15)


15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli anachita ali m’chipululu? (Aheberi 3:12)

15 Munthu akaiwala kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo zimakhala zosavuta kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa iye. Chitsanzo ndi zimene anachita Aisiraeli m’chipululu. Iwo ankadziwa kuti Yehova alipo koma anayamba kukayikira ngati iye angawasamaliredi. Anafika mpaka pofunsa kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?” (Eks. 17:2, 7) Zotsatira zake n’zakuti iwo anasiya kumvera Mulungu. N’zodziwikiratu kuti sitingafune kutengera chitsanzo chawo choipachi.​—Werengani Aheberi 3:12.

16. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingayese chikhulupiriro chathu?

16 M’dzikoli, kupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova si kophweka. Anthu ambiri savomereza kuti Mulungu aliko. Ndipo nthawi zambiri anthu amene satsatira mfundo za Mulungu amaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Tikamaona zimenezi zikuchitika chikhulupiriro chathu chingayesedwe. Ngakhale kuti sitingafike pokayikira kuti Mulungu alikodi, tingayambe kukayikira ngati angatithandize. Amene analemba Salimo 73 anayambanso kukayikira zimenezi. Ankaona kuti anthu amene ankanyalanyaza malamulo a Mulungu zinthu zinkawayendera bwino. Choncho anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kuli ndi phindu lililonse.​—Sal. 73:11-13.

17. N’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova?

17 Kodi n’chiyani chinathandiza wolemba masalimo kuti ayambenso kuona zinthu moyenera? Iye anaganizira zimene zingachitikire anthu amene aiwala Yehova. (Sal. 73:18, 19, 27) Anaganiziranso madalitso omwe anthu amene akutumikira Mulungu amapeza. (Sal. 73:24) Ifenso tingamaganizire madalitso amene Yehova watipatsa. Tiziganizira mmene moyo wathu ukanakhalira zikanakhala kuti sitikutumikira Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhalebe okhulupirika n’kunena ngati mmene wolemba masalimo ananenera kuti: “Kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”​—Sal. 73:28.

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa zimene zichitike m’tsogolomu?

18 Tingathe kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’masiku otsiriza ano chifukwa ‘timatumikira Mulungu wamoyo ndi woona.’ (1 Ates. 1:9) Mulungu wathu amatikonda ndipo nthawi zonse azitithandiza. Iye anathandiza atumiki ake m’mbuyomu ndipo azitithandizanso masiku ano. Posachedwapa tikuyembekezera kuti padzikoli pachitika chisautso chachikulu. Koma sitidzakhala tokhatokha. (Yes. 41:10) Choncho tiyeni tonse “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.’”​—Aheb. 13:5, 6.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani