Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 24

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

Khalani Mlendo m’Tenti ya Yehova Kwamuyaya!

Khalani Mlendo m’Tenti ya Yehova Kwamuyaya!

“Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?”SAL. 15:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuphunzila zimene tiyenela kucita kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino na Yehova, komanso mmene tiyenela kucitila zinthu na mabwenzi ake.

1. Kodi kukambilana Salimo 15:​1-5 kungatipindulile motani?

 M’NKHANI yapita, tinaphunzila kuti atumiki a Yehova odzipatulila angakhale alendo m’tenti yake yophiphilitsa mwa kukhala naye pa ubale wolimba. Koma kodi tiyenela kutani kuti tikhale naye pa ubale wotelo? Salimo 15 imafotokoza zimene tiyenela kucita. (Ŵelengani Salimo 15:​1-5.) Salimo limeneli, limachula zinthu zimene zingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu.

2. Kodi n’ciyani ciyenela kuti cinasonkhezela Davide kuchula tenti ya Yehova?

2 Salimo 15 imayamba na mawu akuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale mʼphili lanu lopatulika?” (Sal. 15:1) Pokamba mawu akuti “tenti” ya Yehova, wamasalimo Davide ayenela kuti anali kuganizila za cihema comwe cinali mu mzinda wa Gibiyoni kwa kanthawi. Pochula “phili” lopatulika la Mulungu, Davide ayenela kuti anali kunena za phili la Ziyoni lomwe linali ku Yerusalemu. Phili limenelo linali pa mtunda wa makilomita angapo ca kum’mwela kwa mzinda wa Gibiyoni. Pa phililo, Davide anamangapo tenti yoikamo likasa la pangano, ndipo linakhala kumeneko mpaka kacisi atamangidwa —2 Sam. 6:17.

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kucita cidwi na Salimo 15? (Onaninso cithunzi.)

3 Aisiraeli ambili sanali kuloledwa kutumikila pa cihema, ndipo ni Aisiraeli ocepa cabe amene anali kuloledwa kuloŵa mkati mwa tentiyo, momwe anali kusungilamo likasa la pangano. Ngakhale zinali conco, atumiki onse okhulupilika a Yehova anali na mwayi wokhala alendo m’tenti yake mwa kukhala mabwenzi ake na kupitiliza kutelo. Ndipo izi n’zimene tonsefe timalakalaka. Salimo 15, limachula ena mwa makhalidwe amene tiyenela kukhala nawo kuti tikhalebe mabwenzi a Yehova.

Aisiraeli a m’nthawi ya Davide anali kutha kuona m’maganizo mwawo zimene kukhala mlendo m’tenti ya Yehova kumatanthauza (Onani ndime 3)


MUZIYENDA MOSALAKWISA ZINTHU NDIPO MUZICITA ZABWINO

4. Tidziŵa bwanji kuti ubatizo paokha si wokwanila kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu? (Yesaya 48:1)

4 Pa Salimo 15:2 pamanena kuti bwenzi la Mulungu ni munthu “amene akuyenda mosalakwitsa zinthu, amene amacita zinthu zabwino.” Mawu akuti “akuyenda,” komanso “amacita,” aonetsa kuti munthu sayenela kuleka kucita zimenezi. Koma kodi n’zotheka ‘kuyenda mosalakwisa zinthu’? Inde. N’zoona kuti kulibe munthu wangwilo, koma Yehova amationa kuti ‘tikuyenda mosalakwitsa zinthu’ tikamayesetsa kumumvela. Kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika ni ciyambi cabe ca ulendo wathu na iye. Kumbukilani kuti m’nthawi zochulidwa m’Baibo, kungokhala mu mtundu wa Isiraeli sikunali kuyeneleza munthu kukhala mlendo wa Yehova. Aisiraeli ena anali kuitanila pa iye koma osati “m’coonadi kapena m’cilungamo.” (Ŵelengani Yesaya 48:1.) Komabe, Aisiraeli oona mtima anali kuphunzila malamulo a Yehova na kuwatsatila. Mofananamo, kubatizika na kugwilizana na mpingo wa Cikhristu, si zokwanila kuti tikhale mabwenzi a Mulungu. Koma tiyenela kupitiliza ‘kucita zinthu zabwino.’ Kodi izi zitanthauza ciyani?

5. Kodi kumvela Yehova mu zonse kuphatikizapo ciyani?

5 Kwa Yehova, ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu,’ komanso ‘kucita zinthu zabwino,” kumaphatikizapo zambili kuposa kungosonkhana mokhazikika pa Nyumba ya Ufumu. (1 Sam. 15:22) Tiyenela kuyesetsa kumvela Mulungu m’zocita zathu zonse, ngakhale pamene tili kwatokha. (Miy. 3:6; Mlal. 12:​13, 14) M’pofunika kwambili kuyesetsa kumvela Yehova, ngakhale pa nkhani zing’ono-zing’ono. Kucita zimenezi kumaonetsa kuti timam’konda ngako. Zotsatila zake n’zakuti iyenso amayamba kutikonda ngako.—Yoh. 14:23; 1 Yoh. 5:3.

6. Malinga na Aheberi 6:​10-12, n’ciyani cofunika kwambili kuposa nchito za cikhulupililo zimene tinacita kumbuyoko?

6 Yehova amayamikila ngako zinthu zimene tinacita kumbuyoko pom’tumikila. Komabe, nchito za cikhulupililo zimenezo pa zokha si zokwanila kuti tikhalebe alendo m’tenti ya Yehova. Mfundo imeneyi inamveketsedwa bwino pa Aheberi 6:​10-12. (Ŵelengani.) Yehova saiŵala zinthu zabwino zimene tinacita. Koma amafuna kuti tipitilize kumulambila na mtima wonse “mpaka mapeto.” Tidzakhala mabwenzi ake kwamuyaya “tikapanda kutopa.”—Agal. 6:9.

MUZILANKHULA ZOONA MUMTIMA MWANU

7. Kodi kulankhula zoona mumtima mwathu kumaphatikizapo ciyani?

7 Munthu amene afuna kukhala mlendo m’tenti ya Yehova ayenela “kulankhula zoona mumtima mwake.” (Sal. 15:2) Izi sizitanthauza kungopewa kunama. Yehova amafuna kuti tikhale oona mtima m’zokamba na zocita zathu zonse. (Aheb. 13:18) Kukhala woona mtima n’kofunika “cifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu waciphamaso. Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.”—Miy. 3:32.

8. Ni khalidwe liti limene tiyenela kupewa?

8 Anthu amene ‘amalankhula zoona mumtima mwawo’ sadzionetsa ngati omvela pamaso pa anthu, koma n’kumaphwanya malamulo a Mulungu akakhala kwaokha. (Yes. 29:13) Amapewa kucita zinthu mwacinyengo. Munthu wacinyengo angayambe kuona kuti ena mwa malamulo a Yehova ni osathandiza. (Yak. 1:​5-8) Iye angamaphwanye malamulowo pa nkhani zimene aona kuti n’zazing’ono. Ndipo akaona kuti kucita zimenezi sikunamubweletsele vuto lililonse, angakhale na cizolowezi cophwanya malamulo a Mulungu. Zotsatila zake, Yehova sangalandile kulambila kwake. (Mlal. 8:11) Koma ife sitiyenela kukhala otelo, tifunika kukhala oona mtima m’zinthu zonse.

9. Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitika Yesu atakumana koyamba na Natanayeli? (Onaninso cithunzi.)

9 Tingaphunzile zambili za kufunika kokhala oona mtima tikaganizila zimene zinacitika Yesu atakumana koyamba na Natanayeli. Pomwe Filipo anatenga mnzake Natanayeli kuti akaone Yesu, panacitika cinacake cocititsa cidwi. Yesu anali asanakumanepo na Natanayeli. Koma atamuona, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.” (Yoh. 1:47) N’zoona kuti ophunzila onse a Yesu anali oona mtima, koma iye anaona kuti Natanayeli anali woona mtima mwapadela. Nayenso Natanayeli anali wopanda ungwilo ngati ife, Koma sanali kucita zacinyengo mwa njila ina iliyonse. Yesu anamunyadila Natanayeli na kumuyamikila cifukwa ca zimenezi. Ungakhale mwayi wapadela zedi nafenso Yesu atationa mwa njila imeneyi!

Filipo anapita kwa Yesu pamodzi na Natanayeli, munthu wopanda cinyengo. Kodi inunso mumadziŵika kuti ndinu munthu wopanda cinyengo? (Onani ndime 9)


10. N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kuseŵenzetsa mphatso ya kulankhula molakwika? (Yakobo 1:26)

10 Zambili mwa zinthu zochulidwa mu Salimo 15 zikhudza mmene timacitila zinthu na ena. Pa Salimo 15:3 pamati mlendo m’tenti ya Yehova “sanena misece ndi lilime lake, sacitila mnzake coipa ciliconse, ndipo sanyoza anzake.” Kuseŵenzetsa molakwika mphatso ya kulankhula mwa njila imeneyi kungakhumudwitse ena, ndipo kungatilepheletse kukhala m’tenti ya Yehova.—Ŵelengani Yakobo 1:26.

11. Kodi misece n’ciyani? Nanga n’ciyani cimacitika kwa anthu a misece osalapa?

11 Pa Salimo 15:​3, wamasalimo anachulapo misece. Kodi misece n’ciyani? Ni mawu oipa komanso abodza amene angawononge mbili ya munthu. Anthu onse a misece osalapa, amacotsedwa mu mpingo wa Cikhristu.—Yer. 17:10.

12-13. Ni pa zocitika ziti pamene mosazindikila tingapezeke na mlandu wotonza anzathu? (Onaninso cithunzi.)

12 Salimo 15:3 imatikumbutsanso kuti mlendo wa Yehova sacitila mnzake coipa ciliconse, ndipo samutonza kapena kuti kumuipitsila mbili. Kodi tingaipitse bwanji mbili ya mnzathu?

13 Tingamuipitsile mbili munthu mosadziŵa mwa kufalitsa nkhani yabodza yokhudza iye. Mwa citsanzo, ganizilani zocitika izi: (1) Mlongo waleka kutumikila monga mpainiya wa nthawi zonse, (2) banja linalake lacoka pa Beteli cifukwa utumiki wawo watha, kapena (3) m’bale sakutumikilanso monga mkulu kapena mtumiki wothandiza. Kungakhale kulakwa kuuza anthu ena kuti abale na alongo amenewa analakwitsa zinazake, ndiye cifukwa cake mautumiki awo anatha. Tikutelo cifukwa pangakhale zifukwa zambili zimene sitidziŵa zomwe zingapangitse masinthidwe amenewa. Kuwonjezela apo, mlendo m’tenti ya Yehova “sacitila mnzake coipa, ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.”

N’capafupi kunenela ena misece (Onani ndime 12-13)


MUZILEMEKEZA ANTHU AMENE AMAOPA YEHOVA

14. Fotokozani mmene alendo a Yehova amapewela kugwilizana na “munthu aliyense wonyansa.”

14 Lemba la Salimo 15:4 limanena kuti mabwenzi a Yehova “sagwilizana ndi munthu aliyense wonyansa.” Kodi tingamudziŵe bwanji munthu wonyansa? Pokhala anthu opanda ungwilo, sindife oyenelela kuweluza munthu winawake kuti ni wonyansa. Cifukwa ciyani? Mwacibadwa, tingakopeke na anthu ena cifukwa ca makhalidwe awo, koma ena sitingawakonde kwenikweni cifukwa sitisangalala na mmene amacitila zinthu. Conco, tiyenela kupewa anthu okhawo amene Yehova amawaona kuti ni ‘onyansa.’ (1 Akor. 5:11) Anthu amenewa aphatikizapo amene amacita zinthu zoipa mosalapa, amene amanyoza cikhulupililo cathu, kapena amene amafuna kuwononga ubale wathu na Yehova.—Miy. 13:20.

15. Kodi njila imodzi imene tingalemekezele “anthu amene amaopa Yehova” ni iti?

15 Mbali yotsatila ya Salimo 15:4 imati tiyenela kulemekeza “anthu amene amaopa Yehova.” Tiyenela kufuna-funa njila zoonetsela kukoma mtima komanso ulemu kwa mabwenzi a Yehova. (Aroma 12:10) Tingacite bwanji zimenezi? Njila imodzi imene mlendo m’tenti ya Yehova angacitile zimenezi yachulidwa pa Salimo 15:​4, pamene pamati mlendo wa Yehova “sasintha zimene walonjeza ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.” Kusasunga malonjezo athu kumakhumudwitsa anthu ena. (Mat. 5:37) Mwa citsanzo, Yehova amafuna kuti alendo ake azisunga malumbilo awo a ukwati. Amakondwelanso ngati makolo amayesetsa kukwanilitsa zimene alonjeza kwa ana awo. Cifukwa cakuti timakonda Mulungu komanso anthu, timacita zonse zotheka kuti tikwanilitse malonjezo athu.

16. Ni njila ina iti imene tingalemekezele mabwenzi a Yehova?

16 Njila ina imene tingalemekezele mabwenzi a Mulungu ni mwa kukhala oceleza komanso oolowa manja. (Aroma 12:13) Kupatula nthawi yoceza na abale na alongo athu kumatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu na iwo, komanso na Yehova. Ndipo tikamakhala oceleza, timatengela citsanzo ca Yehova.

MUSAMAKONDE NDALAMA

17. N’cifukwa ciyani Salimo 15 imakamba za ndalama?

17 Timaŵelenganso kuti mlendo wa Yehova “sakongoza ndalama zake kuti alandile ciwongoladzanja, ndipo salandila ciphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.” (Sal. 15:5) N’cifukwa ciyani Salimoli likukamba za ndalama? Cifukwa ngati sitiona ndalama moyenela tikhoza kucita zinthu zimene zingapweteke ena, ndipo tingawononge ubwenzi wathu na Mulungu. (1 Tim. 6:10) M’nthawi za m’Baibo, anthu ena anali kudyela masuku pamutu abale awo osauka mwa kuwaikila ciwongoladzanja cacikulu pa ndalama zimene anali kuwakongoza. Ndipo oweluza ena anali kulandila ziphuphu, komanso anali kuweluza anthu osalakwa mopanda cilungamo. Yehova amanyansidwa na makhalidwe amenewa.—Ezek. 22:12.

18. Tingadzifunse mafunso ati kuti tidziŵe mmene timaonela ndalama? (Aheberi 13:5)

18 Tingacite bwino kudzisanthula kuti tidziŵe mmene timaonela ndalama. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zambili nimaganizila za ndalama komanso zimene ningagule na ndalamazo? Nikakongola ndalama, kodi nimacedwa kuibweza poganiza kuti mwiniwake sakuifuna? Kodi kukhala na ndalama kumanipangitsa kudziona wofunika ngako kuposa ena? Kodi ndine wowolowa manja na ndalama zanga? Kodi nimaweluza abale na alongo anga kuti amakonda zakuthupi cabe cifukwa cakuti ali na ndalama? Kodi nimapanga ubwenzi na anthu olemela na kupewa anthu osauka?’ Tili na mwayi wapadela wokhala alendo a Yehova. Kuti tikhalebe mabwenzi a Mulungu, tiyenela kupewa mzimu wokonda ndalama. Ndipo tikatelo, Yehova sadzatisiya!—Ŵelengani Aheberi 13:5.

YEHOVA AMAKONDA MABWENZI AKE

19. N’cifukwa ciyani Yehova amatipatsa malamulo?

19 Salimo 15 limamaliza na lonjezo lakuti: “Munthu aliyense amene amacita zimenezi, sadzagwedezeka.” (Sal. 15:5) Salimo imeneyi ifotokoza colinga cimene Mulungu amatiikila malamulo. Amafuna kuti tikhale osangalala. Ndiye cifukwa cake amatipatsa malamulo amene tikawatsatila, timapeza madalitso na kukhala otetezeka.—Yes. 48:17.

20. Kodi alendo a Yehova ali na tsogolo lotani?

20 Alendo a Yehova ali na tsogolo lowala. Akhristu odzozedwa okhulupilika akakhala kumwamba kumene Yesu anapita kukawakonzela “malo ambili okhalamo.” (Yoh. 14:2) Akhristu amene ali na ciyembekezo codzakhala pa dziko lapansi akuyembekezela kukwanilitsidwa kwa malonjezo a pa Chivumbulutso 21:3. Kunena zoona, tonsefe timauona kukhala mwayi waukulu kulandila ciitano capadela ca Yehova cokhala mabwenzi ake—inde kukhala alendo m’tenti yake kwamuyaya!

NYIMBO 39 Tipange Dzina Labwino na Mulungu