Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

“Mufa Chaka Chisanathe”

Zachaeus Martyn

“Mufa Chaka Chisanathe”
  • CHAKA CHOBADWA 1880

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1942

  • MBIRI YAKE Anayamba upainiya ali ndi zaka 72.

PALIBE aliyense amene anaphunzira Baibulo ndi Zachaeus. Iye atangowerenga buku lakuti Zeze wa Mulungu ndi la Salvation, anazindikira kuti wapeza chipembedzo choona.

Lamlungu lina mu 1941, Zachaeus analawirira kuti akapezeke pa msonkhano wake woyamba wa Mboni za Yehova. Msonkhanowu unkachitikira pamalo omwe anali pa mtunda wa makilomita 8 kuchokera komwe ankakhala ndipo ankafunika kutsetsereka phiri. Popeza sankadziwa nthawi yoyambira msonkhanowo, iye anafika mofulumira kwambiri. Choncho Zachaeus anakhala pansi n’kumadikirira kuti abale abwere. Atasonkhana ku Nyumba ya Ufumu kwa milungu itatu, anauza atsogoleri a mpingo wa Anglican kuti afufute dzina lake kumpingowo.

Mnzake yemwe ankapemphera naye limodzi ku Anglican kuja, anamunyoza kuti: “Madala, mukapitiriza kumayenda mtunda wa makilomita 8 kukwera phirili kuti muzikasonkhana ndi amene aja, mufa chaka chisanathe.” Zachaeus anapitiriza kupita kumeneko kawiri pa mlungu ndipo pamene zinkatha zaka 5, mnzakeyu ndi amene anamwalira. Zachaeus anakwanitsa kuchitabe zimenezi kwa zaka zina 25.

Zachaeus anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira ali ndi zaka 97.