Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE AND GUINEA

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 2)

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 2)

Kuthandiza Anthu Osamva

Ochita kafukufuku ena anapeza kuti ku Sierra Leone kuli anthu pakati pa 3,000 ndi 5,000 omwe ndi ogontha ndipo ena ambiri amapezekanso ku Guinea. Poti Yehova akufuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke,” kodi anthu amenewa angathandizidwe bwanji kudziwa uthenga wabwino?—1 Tim. 2:4.

Mmishonale wina yemwe anapita ku Sierra Leone m’chaka cha 1998, dzina lake Michelle Washington, ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga Kevin, tinatumizidwa ku mpingo womwe unali ndi anthu 4 osamva. Poti ndinkatha chinenero chamanja cha ku America, ndinkafuna kuwathandiza. Ofesi ya nthambi inandipempha kuti ndizimasulira misonkhano yampingo komanso ikuluikulu m’chinenero chamanja. Inadziwitsanso mipingo ina yapafupi za dongosolo limeneli. Ofesi ya nthambi inakonzanso zoti pakhale makalasi ophunzitsa ofalitsa ena chinenero chamanja. Tinayamba kufufuza anthu  osamva ndipo tikawapeza tinkaphunzira nawo Baibulo. Poona zimene tikuyesetsa kuchita kuti tithandize gulu la anthu amenewa, anthu a m’deralo anatiyamikira kwambiri. Komabe, sikuti aliyense ankasangalala ndi ntchito yathuyi. M’busa wina yemwe ankalalikira anthu osamva ankatinena kuti ndife aneneri onyenga. Iye anauza anthuwa ndi mabanja awo kuti azitipewa. Ankawauzanso kuti akamamvetsera uthenga wathu, asiya kuwapatsa thandizo la ndalama limene ankapereka. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale magulu awiri. Gulu loyamba linali ku mbali ya m’busayo chifukwa linali lisanamvepo uthenga wathu. Gulu lachiwiri linali loti tinalilalikira ndipo linali ku mbali yathu. Ena omwe anali ku mbali yathu anapitirizabe kuphunzira mpaka anabatizidwa.”

Mwachitsanzo, Femi anabadwa ndi vuto losamva moti ankagwiritsa ntchito manja polankhula ndi anthu. Iye ankangokayikira aliyense, makamaka anthu amene amalankhula, ndipo ankaona kuti palibe amene amamukonda. Zimenezi zinkachititsa kuti azikhala wosasangalala. Kenako Femi anayamba kuphunzira Baibulo ndi abale ena omwe anali m’kagulu ka chinenero chamanja. Anayamba kufika pa misonkhano nthawi zonse komanso ankaphunzira yekha chinenero chamanja. Femi anabatizidwa ndipo panopa amasangalala kuphunzitsanso Baibulo anthu ena osamva.

Femi (chakumanjako) akuimba nyimbo ya Ufumu m’chinenero chamanja

Mu July 2010, kagulu ka chinenero chamanja ku Freetown kanakula n’kukhala mpingo. Panopa, ku Bo komanso ku Conakry kuli timagulu ta chinenero chamanja.

Osauka Koma “Olemera M’chikhulupiriro”

Baibulo limasonyeza kuti m’nthawi ya atumwi, Akhristu ambiri anali osauka. Yakobo analemba kuti: “Mulungu anasankha anthu amene ali osauka m’dzikoli kuti akhale olemera m’chikhulupiriro.” (Yak. 2:5) Ofalitsa ambiri m’mayiko a Sierra Leone ndi Guinea amakhulupirira kuti Yehova awathandiza ndipo zimenezi zachititsa kuti azikhala ndi chiyembekezo komanso asamade nkhawa.

 Chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro cholimba, mabanja ambiri a Mboni omwe ndi osauka, amayamba kusunga ndalama kudakali miyezi yambiri kuti adzapite ku msonkhano wachigawo. Ena amalima mbewu kuti adzagulitse n’kupeza ndalama zopitira ku msonkhanowo. Ena amakhala m’magulu a anthu 20 mpaka 30 ndipo amathithikana m’kagalimoto kakang’ono popita ku msonkhano. Ulendowu umakhala wovuta kwambiri chifukwa amayenda maola oposa 20 m’misewu ya mabampu, kukutentha komanso kwa fumbi. Anthu ena amayenda wapansi ulendo wautali kuti akapezeke pa msonkhano. M’bale wina ananena kuti: “Tinkayenda ulendo wa makilomita 80 titanyamula nthochi zambiri. Zina tinkazigulitsa m’njira kuti tipepukidwe komanso kuti tipeze ndalama zokwerera galimoto kuti timalizitse ulendo wotsalawo.”

Abale ndi alongo akupita ku msonkhano wachigawo pagalimoto

Chifukwanso chokhala ndi chikhulupiriro cholimba, ofalitsa ambiri asankha kuti asasamukire kumayiko ena kuti  akapeze ndalama kapena ntchito yabwino. M’bale wina amene anapitako ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira, dzina lake Emmanuel Patton, ananena kuti: “Timakhulupirira kuti Yehova atithandiza kupeza zofunikira pa moyo wathu. Popeza timakhala m’dziko loti muli olalikira za Ufumu ochepa timaona kuti utumiki wathu ndi wofunika kwambiri.” (Mat. 6:33) Panopa Emmanuel akutumikira monga mkulu ndipo iye pamodzi ndi mkazi wake, Eunice, akuyesetsa kuchita zambiri potumikira Yehova. Abale ena omwe ndi mitu ya mabanja, safuna kupita kudziko lina. Iwo amafuna kuti banja lawo likhalebe logwirizana komanso kuti azichitira limodzi zinthu zauzimu. M’bale wina yemwe anali mpainiya wapadera komanso woyang’anira dera wogwirizira, dzina lake Timothy Nyuma, ananena kuti: “Ndinkakana kuyamba  ntchito yoti izindichititsa kusiya banja langa kwa nthawi yaitali. Komanso ine ndi mkazi wanga, Florence, tinasankha kuti ana athu aphunzire konkuno. Sitinafune kuti akaleredwe ndi anthu ena n’cholinga choti akaphunzire m’masukulu abwino.”

Abale ndi alongo ambiri amasonyezanso kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba popirira mavuto osiyanasiyana amene akukumana nawo pochita utumiki. Kevin Washington yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Abale ambiri amalalikira komanso kuchita zinthu zina pampingo ngakhale kuti akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mavutowo ndi aakulu moti akhoza kuwachititsa kuti asamasangalale komanso kuti azingokhala kunyumba. Mwachitsanzo, abale ena akudwala matenda oti sangachire ndipo alibe mwayi wolandira mankhwala kapena kupita kuchipatala. Ena satha kuwerenga ndipo akuyesetsa kuchita khama kuti aphunzire kuwerenga ndi kulemba. Ngati m’bale wina sanakambe bwino nkhani yake kapena ngati sanachite bwino mbali yake, ndimadzifunsa kuti: ‘Kodi ndikanakhala kuti ndimagwira ntchito yolembedwa, ndili ndi matenda enaake aakulu, ndilibe magalasi a maso, ndilibe magetsi komanso ndili ndi mabuku ochepa ofufuzira nkhani, ndikanakamba bwino nkhaniyi kuposa mmene m’baleyo wakambira?’”

Zimene abale ndi alongo akuchitazi zimalemekezetsa Yehova. Iwo amakhala ngati Akhristu a m’nthawi ya atumwi omwe ankasonyeza kuti ndi atumiki a Mulungu “mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, . . . ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri, ngati opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.”—2 Akor. 6:4, 10.

Kuyembekezera Zinthu Zabwino M’tsogolo

Zaka 90 m’mbuyomo, m’bale Alfred Joseph ndi Leonard Blackman ananena kuti m’munda wa ku Sierra Leone “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Patadutsa zaka 35 atanena mawu amenewa, Manuel Diogo ali ku Guinea ananena kuti, “Kuno kuli anthu ambiri achidwi.” Masiku ano,  atumiki a Yehova m’mayiko awiriwa akukhulupirira kuti kutsogoloku anthu ambiri amvetsera uthenga wabwino.

M’chaka cha 2012, anthu 3,479 anapita ku Chikumbutso ku Guinea. Chiwerengero chimenechi n’chapamwamba kwambiri chifukwa kuli ofalitsa pafupifupi 800. Ku Sierra Leone kuli ofalitsa 2,030 koma anthu 7,854 ndi amene anapezeka pamwambo wa Chikumbutso. Mlongo wina wazaka 93 anali nawo pamwambo umenewu. Mlongoyu anali mpainiya wapadera ndipo dzina lake ndi Winifred Remmie. Iyeyu ndi mwamuna wake, Lichfield, anafika kuti Sierra Leone mu 1963. Winifred anachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 60 ndipo pa zaka zonsezi ankatumikira monga mpainiya wapadera.  Winifred ananena kuti: “Palibe amene ankalota kuti ku Sierra Leone kudzakhala abale ndi alongo olimba mwauzimu chonchi. Ngakhale kuti panopa ndakalamba, ndikufuna kuti ndigwire nawo ntchito yosangalatsa yothandiza anthuyi.” *

Mboni za Yehova za ku Sierra Leone ndi ku Guinea zimaona ntchito yolalikira mmene Winifred ankaionera. Ngati mitengo yokhala ndi madzi nthawi zonse, Akhristuwa akufunitsitsa kupitiriza kubala zipatso pofuna kulemekeza Yehova. (Sal. 1:3) Ndipo Yehova aziwapatsa mphamvu zoti apitirize kuthandiza anthu kudziwa za ufulu umene tikuyembekezera, womwe ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.

Abale a m’Komiti ya Nthambi, kuchokera kumanzere: Collin Attick, Alfred Gunn, Tamba Josiah ndi Delroy Williamson

^ ndime 16 Winifred Remmie anamwalira pamene nkhaniyi inkakonzedwa.