Kulalikira ndi Kuphunzitsa Padziko Lonse
PADZIKO LONSE
MAYIKO 239
OFALITSA 7,965,954
MAOLA ONSE AMENE TINATHERA MU UTUMIKI WAKUMUNDA 1,841,180,235
MAPHUNZIRO A BAIBULO 9,254,963
M'CHIGAWO ICHI
Africa
Anthu ambiri ku Africa akuphunzira Baibulo ndipo akusintha kwambiri makhalidwe awo. Werengani za munthu amene anasiya kumwa mowa mwauchidakwa komanso kusuta ndudu 60 patsiku.
North ndi South America
Nkhanizi zikusonyeza kuti ntchito yolalikira imayenda bwino ngati timathandiza ena komanso timalalikira ngakhale kuti timatsutsidwa.
Asia ndi Middle East
Khama limene abale akusonyeza pa ntchito yolalikira likubala zipatso. Werengani nkhaniyi kuti muone zimene munthu wina anachita kuti athandize munthu yemwe ndi wosamva, wosaona komanso wosalankhula, kuti adziwe zoti Mulungu amamukonda.
Europe
Anthu amadana ndi Mboni chifukwa cha zabodza zomwe anauzidwa. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene pulogalamu ya pawailesi inathandizira anthu kuti asiye kudana ndi Mboni za Yehova.
Oceania
Kulemba makalata ndi njira ina yomwe choonadi cha m’Baibulo chikufalitsidwira mumzinda wa Christchurch ku New Zealand. N’chifukwa chiyani ena amatchula makalatawa kuti “Makalata Ochokera kwa Mulungu?”