Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Asia ndi Middle East

Asia ndi Middle East
  • MAYIKO 47

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 4,282,178,221

  • OFALITSA 674,011

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 672,318

Anathandiza Munthu Yemwe Ndi Wosaona, Wosamva Komanso Wosalankhula

Mu 1999, mpingo wina wa chinenero chamanja wa mumzinda wa Kobe ku Japan, unamva za munthu wina yemwe ndi wosamva, dzina lake Hirofumi. M’bale wina anapita kangapo konse kuti akaonane ndi munthuyu koma mayi ake anakaniza. Tsiku lina m’baleyu atapitakonso n’kuwachonderera mayiwo, anatulutsa Hirofumi kuti m’baleyu  aonane naye. Tsitsi ndi ndevu za Hirofumi zinali zazitali komanso zanyankhalala. Nkhope yake inkaoneka momvetsa chisoni ngati munthu amene wakhala m’chipululu kwa zaka zambiri. Koma iye analinso wosaona. M’baleyo anadzidzimuka kwambiri atamuona, komabe anagwira manja ake n’kumamusisita monga njira yolankhulirana naye. Koma Hirofumi sanachite chilichonse. Pa nthawiyi n’kuti patadutsa zaka 10 kuchokera pamene Hirofumi anasiya kuona. Izi zinachitika ali ndi zaka 31, ndipo pa zaka 10 zonsezi Hirofumi ankatsekeredwa m’nyumba moti sankalankhula ndi aliyense.

Patatha masiku awiri, m’bale uja anapitanso kukaona Hirofumi. Mayi a Hirofumi anadabwa kwambiri chifukwa ankaganiza kuti m’bale uja sabweranso chifukwa cha mmene mwana wawoyo ankaonekera. M’baleyu anachonderera mayi a Hirofumi kuti aonane ndi Hirofumi ndipo mayiwo anavomera. M’bale uja anapita kwa Hirofumi kwa mwezi wathunthu, koma Hirofumi sankaonetsa chidwi chilichonse moti mayi ake anauza m’baleyo kuti asavutike kudzabweranso. Komabe m’baleyo sanataye mtima. Iye ankam’pititsira makeke komanso kuchita zinthu zosonyeza kumuganizira. Koma patatha miyezi inanso iwiri Hirofumi sankaonetsabe chidwi chilichonse moti m’baleyo anayamba kuganiza zongosiya kupitako.

M’baleyo anaganiza zopitako komaliza. Koma asanapite anapemphera kwa Yehova. Anapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa ngati akufunikirabe kupitiriza kumapita kwa Hirofumi. M’baleyu atafika kwa Hirofumi anagwiranso manja ake n’kumuuza n’chinenero chamanja kuti, kuli Mulungu, dzina lake Yehova, amene amaona mavuto ake ndipo amamvetsa mmene iye akumvera kuposa wina aliyense.  Anamuuzanso kuti Yehova amamukonda ndipo akufuna kudzamuthetsera mavuto ake. N’chifukwa chake m’baleyu anafika pakhomo pawo. Poyamba Hirofumi sanachite chilichonse, koma kenako anagwira mwamphamvu dzanja la m’baleyu ndipo misozi inayamba kutuluka m’maso mwake. M’baleyu anakhudzidwa kwambiri ndi zimenezi moti nayenso analira. Kenako anayamba kuphunzira naye Baibulo.

Ataphunzira naye kwa zaka 11, Hirofumi anasiya kumapita kumpingo wa chinenero chamanja womwe uli kutali ndi derali, ndipo anayamba kusonkhana ndi abale a mumpingo wapafupi. Poyamba palibe aliyense wa mpingo umenewu amene ankadziwa chinenero chamanja, koma patatha miyezi 18 abale ndi alongo okwana 22 anaphunzira chinenero chamanja n’cholinga choti athe kuthandiza Hirofumi. Mu January 2012, Hirofumi anakamba nkhani yake yoyamba  m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndipo wina ankamasulira. Mu October m’chaka chomwechi, anakhala wofalitsa wosabatizidwa.

Amaphunzira Baibulo ndi Alonda

M’bale wina dzina lake Floren, yemwe ndi mpainiya ndipo amakhala ku Philippines, amachititsa maphunziro a Baibulo okwana 25, ndipo ambiri mwa anthu amenewa amagwira ntchito yaulonda. Nthawi zambiri anthuwa amagwira ntchito yawo madzulo ndipo ena amagwira usiku wonse. Kuti azitha kuphunzira nawo, Floren anafunika kusintha zina ndi zina. Amaonetsetsa kuti asamawasokoneze pa ntchito yawo choncho amaphunzira nawo pa nthawi yopuma kapena pamene ali ndi mpata. Ena amaphunzira nawo kuyambira 7 koloko mpaka 11 madzulo, ndipo ena amaphunzira nawo kuyambira 5 koloko mpaka 9 koloko m’mawa. Nthawi zina amapita kukaphunzira nawo pa nthawi imene atsala pang’ono kusinthana. Izi zimathandiza kuti aphunzire ndi mlonda amene watsala pang’ono kuyamba ntchito, kenako n’kuphunziranso ndi amene waweruka. Floren ananena kuti: “Kukhala ndi maphunziro ambiri kwandithandiza kuti ndizisangalala kwambiri pa moyo wanga.” Ena mwa anthu amenewa anayamba kusonkhana. Wina anabatizidwa ndipo pano ndi mpainiya wokhazikika.

Philippines: Floren akuchititsa phunziro la Baibulo m’mawa kwambiri

Anayesetsa Kuti Adziwe Zoona

Tsiku lina, lomwenso kunkagwa mvula, alongo awiri a ku Armenia, ankalalikira ndipo anakumana ndi mayi wina ndi mwana wake wamkazi, n’kuwagawira kapepala. Mayiyu dzina lake ndi Marusya, ndipo mtsikanayo dzina lake ndi Yeva. Alongowo anadabwa kwambiri kumva kuti, ngakhale kuti kunali kukugwa mvula, mayi ndi mwana wakeyu anali atakhala kwa maola pafupifupi awiri akuyembekeza kuti akumane ndi a Mboni za Yehova. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mchimwene wake wa Marusya anali ataphunzira choonadi pa nthawi yomwe anali kundende ndipo  anachiphunzira kuchokera kwa abale amene anali kundendeko chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Marusya ankaganiza kuti mchimwene wakeyo akatuluka kundende, akhala wachiwawa kwambiri koposa poyamba. Koma atatuluka anaona kuti wasintha ndipo ndi munthu wabwino. Komanso atayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova, mchimwene wakeyu anapitirizabe kusintha. Komabe, Marusya ndi Yeva analibe chidwi kwenikweni ndi zimenezi chifukwa cha zinthu zoipa zomwe anthu ankalemba komanso kuulutsa pa TV zokhudza Mboni za Yehova. Koma kenako Yeva anayamba kuganiza kuti: ‘Ndikuona kuti amalumewa asintha kwambiri panopa. Nanga n’chifukwa chiyani anthu amalankhula zinthu zoipa zokhudza a Mboni za Yehova?’ Chifukwa choti ankafunitsitsa kudziwa zoona pa nkhaniyi, anauza mayi ake kuti: “Sitingadziwe zolondola, pokhapokha titayesetsa kuti tikumane nawo anthu amenewa. Tiyeni tiyesetse kuti tikumane nawo kuti tidziwe zenizeni zokhudza Mboni za Yehova.” Iwo anachitadi zimenezi ndipo n’zimene zinachititsa kuti akumane ndi alongo aja. Patangotha masiku awiri, Marusya ndi Yeva anayamba kuphunzira Baibulo. Kenako anayambanso kupezeka pa misonkhano ndipo panopa ndi ofalitsa osabatizidwa.

Ana Anaika Magazini Pakhomo la Nyumba Yake

Istanbul, Turkey: M’bale akulalikira pogwiritsa ntchito kabuku ka Uthenga Wabwino

Mumzinda wa Adana, ku Turkey, mayi wina amene ankafuna kudzipha chifukwa cha mavuto a m’banja komanso mavuto ena, anapeza magazini awiri pakhomo la nyumba yake. Zikuoneka kuti ana ena a m’deralo anatola magaziniwa n’kuwaika pakhomo la mayiyu poganiza kuti ndi ake. Mayiyu anachita chidwi kwambiri ndi nkhani zofotokoza mbiri ya moyo wa anthu ena zimene zinali m’magaziniwo. Iye ankafuna moyo wake utasintha ngati mmene anthu a m’nkhanizo anachitira. Mayiyu anagwiritsa ntchito nambala yomwe inalembedwa pa magaziniwo ndipo anaimbira foni mpainiya wina amene ankakhala m’dera lomwelo.  Kenako anayamba kuphunzira Baibulo. Mayiyu anasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira ndipo ananena kuti akufuna kumapita nawo ku misonkhano. Mwamwayi, nyumba yake inali pafupi ndi Nyumba ya Ufumu. Nthawi yomweyo anayamba kupezeka pa misonkhano ndipo akupitirizabe mpaka pano.

Anakhala M’ndende Masiku 10 Koma Sanasinthe Maganizo

Bambo wina wa ku Nepal, dzina lake Bam, anali wapolisi komanso ankakonda kupita kutchalitchi. Tsiku lina akugwira ntchito, anakumana ndi munthu wina ndi mkazi wake, omwe ndi apainiya apadera. Bam anachita chidwi kwambiri chifukwa anthuwa anayankha mafunso ake onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndipo pasanapite nthawi anayamba kusonkhana. Pamene ankapitiriza kuphunzira, chikumbumtima chake chinayamba kumuvutitsa chifukwa cha ntchito yakeyi. Choncho anapempha mabwana ake kuti azigwira ntchito ya mu ofesi n’cholinga choti asamanyamule mfuti. Mabwanawa anavomera. Koma atapezeka pa msonkhano wachigawo, Bam anayambanso kuvutika chikumbumtima ndi ntchito yakeyi. Choncho anaganiza zongosiya ntchitoyo.

Mkazi wa Bam sanasangalale ndi zimenezi chifukwa ankaona kuti ntchitoyi inali ya ndalama zambiri komanso inkachititsa kuti anthu aziwalemekeza. Pofuna kumunyengerera kuti asasiye ntchitoyi, anamuuza kuti: “Mukapanda kusiya ntchito imeneyi, ndiyamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni.” Zitalephereka, mayiyu ananyengerera mkulu wa apolisi kuti atsekere Bam m’ndende kuti mwina asintha maganizo. Atakhala masiku 10 m’ndende, Bam anatulutsidwa koma sanasinthe maganizo ndipo anayamba kufufuza ntchito ina. Iye anayamba bizinezi yonyamula anthu panjinga za hayala ngakhale kuti izi zinachititsa kuti azigwira ntchito maola ambiri pa dzuwa. Ngakhale zinali choncho, iye ankasangalala kwambiri. Anapitiriza kupita patsogolo mwauzimu ndipo  anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Patapita nthawi, mkazi wake uja anasiya kum’tsutsa. Chifukwa cha chikondi chimene abale ndi alongo ankamusonyeza, nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Bam amakwanitsabe kusamalira bwino banja lake chifukwa ntchito yakeyi imamuthandiza kupeza ndalama zambiri kuposa zimene ankalandira ali wapolisi. Bam anabatizidwa pa msonkhano umene unachitika mu February 2013. Panopa mkazi uja komanso mwana wawo wamwamuna amapezeka pa misonkhano.

Nepal: Bam atasiya ntchito imene ankagwira, iye ndi banja lake anayamba kupita patsogolo mwauzimu

Ankafuna Kuchita Upainiya Wothandiza

Mlongo wina wa ku Korea, dzina lake Myeong-hee, amavutika ndi mwendo wake chifukwa cha matenda ofa ziwalo amene anadwala ali ndi zaka ziwiri. Iye sachedwa kutopa komanso nthawi zina amagwa poyenda. Kuwonjezera apo, amakhala ndi nkhawa yaikulu, amadwala chifukwa cha mankhwala amene amamwa ndiponso amavutika kupuma. Ngakhale kuti ali ndi mavuto onsewa, mlongoyu ankafuna atachita upainiya wothandiza ndipo wakhala akuchitadi upainiyawu zaka ziwiri zapitazi. Mlongoyu amathokoza Yehova chifukwa chomuthandiza kukwanitsa kuchita upainiya.

“Ndakhala Ndikulifunafuna kwa Zaka 30”

Agnes yemwe ndi mmishonale ku Indonesia, ankakonda kulalikira mayi wina yemwe anali woyembekezera. Mayiyu ankagulitsa masamba mumsika winawake ndipo ankakonda kuwerenga magazini athu komanso kukambirana mfundo za m’Baibulo ndi Agnes akakhala kuti si wotanganidwa. Tsiku lina Agnes atapita kuti akaonane ndi mayiyu, anam’peza kulibe. Mwamuna wake anauza Agnes kuti mayiyu ali ndi mwana ndipo Agnes anaganiza zokamuona. Anamutengera  Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kuti akam’patse monga mphatso. Mayiyu anasangalala ataona kuti Agnes wabwera kudzaona mwana wake. Koma anasangalalanso kwambiri Agnes atamupatsa mphatsoyo. Atamasula mphatsoyo anapeza kuti ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndipo anadabwa kwambiri moti anati: “Mwalitenga kuti buku limeneli? Ndakhala ndikulifunafuna kwa zaka 30. Ndayenda m’malo ogulitsira mabuku ambiri koma osalipeza. Aliyense ankandiuza kuti sakulidziwa ndipo sanalionepo. Pa mabuku onse amene ndinapeza, panalibe buku labwino ngati limeneli.” Mayiyu ali mwana, amalume ake anali ndi bukuli ndipo iye ankakonda kwambiri kuliwerenga. Choncho anasangalala kwambiri pamene mlongoyu anam’bweretsera bukuli ndipo mwana wake wamkulu amakondanso kuliwerenga. Mayiyu ndi mwana wakeyo anayamba kuphunzira Baibulo.

Indonesia: Agnes ali ndi buku limene anapatsa mayi wina ngati mphatso