Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

WEBUSAITI YA JW.ORG—Ikuchitira “Umboni ku Mitundu Yonse”

WEBUSAITI YA JW.ORG—Ikuchitira “Umboni ku Mitundu Yonse”

Yesu ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Webusaiti ya jw.org ikuthandiza kwambiri kuti anthu a “mitundu yonse” amve uthenga wabwino pa nthawi yochepa imene yatsalayi mapeto asanafike.

Pamene m’bale wina ndi mkazi wake, omwe ndi amishonale ku Solomon Islands, ankalalikira m’mbali mwa nyanja m’mudzi wina, anakumana ndi amuna 4 achikulire. Amishonalewa anaona kuti amunawa anali ndi mafoni a m’manja, choncho anawafunsa ngati amadziwa kugwiritsa ntchito Intaneti. Iwo anayankha kuti amadziwa. Kenako amishonalewo anasonyeza anthuwo mmene angatsegulire  webusaiti ya jw.org, mmene angapezere chinenero chawo, mmene angakopere magazini ndi Baibulo, komanso mmene angapezere nkhani zothandiza mabanja ndi ana. Amishonalewa akapita kukalalikira, amakonda kusonkhanitsa ana n’kuwaonetsa vidiyo yakuti Muzipemphera Nthawi Iliyonse. Ana ena atamaliza kuonerera vidiyoyi, anathamangira m’tchire akuimba nyimbo ya mu vidiyoyi mosangalala kwambiri.

Ulaanbaatar, Mongolia

M’munsimu muli ena mwa makalata ambirimbiri oyamikira amene abale kulikulu lathu ku New York analandira:

“Ine ndi mwamuna wanga tinasamukira ku Mexico kuno, ndipo tikuphunzira Chisipanishi kuti tizitha kulalikira. Nthawi iliyonse ndikatsegula webusaiti ya jw.org, ndimathokoza Yehova chifukwa yandithandiza kuti ndizimvetsera zinthu zosiyanasiyana ndi kuphunzira. Pawebusaitiyi pali zinthu zambiri monga magazini, mabuku, nyimbo ndi masewero m’zinenero zambiri. Ndikukuthokozani ndipo ndimakukondani chifukwa mukugwira ntchito yaikulu.”—D.H., Mexico.

“Ine sindiona kwenikweni, ndipo ndimakonda kwambiri webusaiti yanu chifukwa chakuti pali zinthu zambiri zomvetsera. Ndalemba kalatayi n’cholinga chokulimbikitsani kuti mupitirize kuika pawebusaitiyi ma MP3 a mabuku ndi zinthu zina zimene mumasindikiza chifukwa ndimakonda kumvetsera zinthu zimenezi tsiku lonse.”—K.G., United States.

“Webusaiti ya jw.org ndimaikonda kwambiri. Ndi yosavuta kugwiritsa ntchito ndipo yandilimbikitsa kwambiri kuti ndiziphunzira Baibulo pandekha ndiponso kulalikira. Panopa ndili ndi zaka 72, ndinabatizidwa zaka 47 zapitazo, ndachita upainiya kwa zaka zoposa 30, ndine mayi wa ana 9 omwenso ndi obatizidwa, ndili ndi zidzukulu 16 ndipo ana  a zidzukuluzo alipo atatu. Tsopano m’banja lathu muli mibadwo 4 ya apainiya. Ndikuthokoza Yehova potipatsa chakudya chauzimu chimenechi pa nthawi yake.”—M.T., United States.

“Ndikulemba kalatayi nthawi ili 4 koloko m’mawa. Nthawi zambiri sindigona usiku chifukwa chakuti ndikudwala matenda ofoola ziwalo ndi matenda ena, ngati mmene zilili ndi abale ndi alongo athu ambiri padziko lonse. Yehova akupitiriza kutisamalira mwauzimu. Choncho ndikufuna kukuthokozani. Zithunzi zimandithandiza kwambiri pophunzira, n’chifukwa chake ndimakonda mmene webusaitiyi munaipangira. Mavidiyo, zithunzi komanso zinthu zina n’zogwirizana ndi ndemanga zake zomveka bwino ndipo ndikuyamikira kwambiri zimenezi.”—B.B., New Zealand.

“Ndalemba kalatayi pofuna kukuthokozani. Ndine dokotala ndipo ndimagwirira ntchito yanga kumidzi m’dziko la Sri Lanka, kumene sikufika magazini a chinenero changa. Koma chifukwa cha webusaiti yanuyi, ndimatha kukopera magaziniwa n’kumawerenga m’chinenero changa. Webusaiti  yanuyi ndi imodzi mwa mphatso zimene Yehova wapereka kwa anthu ngati ine.”—N.F., Sri Lanka.

“Ndalemba kalatayi pofuna kukuthokozani chifukwa cha ntchito yaikulu imene mukugwira pothandiza anthu kuti aphunzire za Yehova. Chonde pitirizani kuika mavidiyo pa webusaiti ya jw.org. Mavidiyo amenewa athandiza kwambiri banja lathu. Vidiyo imene inandithandiza kwambiri ndi yakuti Beat a Bully Without Using Your Fists. Ndikubwerezanso kuthokoza kuti zikomo kwambiri chifukwa cha ntchito yaikulu imene mukugwira.”—Y.S., wa zaka 9, United States.

“Ndikufuna kukuthokozani komanso kuthokoza Yehova chifukwa chotipatsa chakudya chauzimu.Webusaiti ya jw.org yandithandiza kwambiri, makamaka nkhani zimene zimakhala pakamutu kakuti ‘Achinyamata.’ Ndimasangalalanso ndi nkhani zakuti Khalani Bwenzi la Yehova. Ndili ndi ang’ono anga atatu aakazi, ndipo ndikuona kuti nkhani zimenezi zikuwathandiza zedi. Ngakhale kuti tili kutali ndi inu, ndife abale ogwirizana kwambiri chifukwa chakuti tonse timakonda Yehova. Zikomo.”—A.B., Peru.