Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Ana Akusangalala ndi Mavidiyo a Makatuni

Ana Akusangalala ndi Mavidiyo a Makatuni

Kalebe, yemwe akupezeka m’mavidiyo a pa webusaiti ya jw.org a mutu wakuti Khalani Bwenzi la Yehova, tsopano ndi mwana wotchuka padziko lonse. Vidiyo yoyamba ya mwana ameneyu yamasuliridwa kale m’zinenero zoposa 130, ndipo talandira makalata ambiri okhudza mavidiyo amenewa.

Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka 11 ndi mng’ono wake wa zaka 8 analemba kuti: “Tatumiza zopereka kuti zithandize pa ntchito yolalikira padziko lonse. Tinapeza ndalamayi titagulitsa ng’ombe ziwiri zimene tinkaweta. Mayina a ng’ombezi anali Big Red ndi Earl. Tikupereka ndalamazi chifukwa taona kuti zingakuthandizeni kupanga mavidiyo ena akuti Khalani Bwenzi la Yehova. Tikuganiza  kuti zingakhale bwino ngati makolo a Kalebe atabereka mwana wina wamkazi kuti Kalebe akhale ndi mchemwali wake. Tikufuna tidzaone ngati Kalebe azidzachita nsanje kuti kwabwera mwana wina. Vidiyo ya Kalebe timaikonda kwambiri.”

Ana ambiri analoweza mawu a muvidiyo yonseyi, kuphatikizapo nyimbo ndi mawu a wofotokozera. Mlongo wina analemba kuti mumpingo wawo wa ofalitsa 100, muli ana 40. Ambiri mwa ana amenewa sanakwanitse zaka 10. Ndiyeno tsiku lina kumapeto kwa misonkhano, anaimba nyimbo nambala 120. Mlongoyu anagwetsa misozi atamva ana onse akuimba “nyimbo yawoyi” monyadira kwambiri.

Mlongo wina ananena kuti mdzukulu wawo ataonerera vidiyoyi kawiri, ananena kuti: “Ndikufuna ndikakonze kuchipinda kwanga kuti zidole zanga zisagwetse anthu chifukwa angavulale.” Anatsimikizadi kuchita zimenezi moti sanalole kuti adye chakudya mpaka atamaliza kuyeretsako.

Kumudzi wina m’dziko la South Africa, tsiku lililonse ana ambirimbiri ankapita kunyumba ya banja lina la Mboni. Ena ankaganiza kuti anawa ankakonda kupita kunyumbako chifukwa choti banjali linkagulitsa maswiti. Koma ayi, chifukwa chake sichinali chimenechi. Chifukwa chake chinali choti ana ena ankaitana ana anzawo a m’mudzimo kuti akaonerere vidiyo yakuti Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso m’chinenero chawo cha Chikhosa. Tsiku lina kunabwera ana 11 ndipo onse anali ataloweza nyimbo ya mu vidiyoyi.

Ku Ecuador, kuli ana ena awiri olankhula Chikichuwa, omwe si Mboni. Wamkulu dzina lake ndi Isaac ndipo ali ndi zaka 8, pamene mng’ono wake ndi Saul yemwe ali ndi zaka 5. Anawa ankati akawapatsa ndalama kuti akadyere,  iwo ankasunga pang’onopang’ono n’kumagula zidole za mfuti, malupanga ndi asilikali. Tsiku lina amayi awo anawauza kuti ayeretse m’chipinda chawo n’kuika zidole zawo zonse m’katoni pansi pa bedi. Patapita nthawi anawa anapatsidwa mphatso ya DVD yakuti Khalani Bwenzi la Yehova, ndipo anaionerera limodzi. Patapita mlungu umodzi, amayi awo akuyeretsa m’nyumbamo anapeza kuti zidole zina zimene zinali m’katoni zija mulibemo, ndipo mwangotsala za magalimoto zokha. Ndiyeno anafunsa anawo kuti, “Zidole zija zili kuti?” Anawo anayankha kuti, “Tinakazitaya kudzala chifukwa Yehova amadana ndi zidole zimenezo.” Ndiye ana anzawo akamasewera ndi zidole zokhudzana ndi zachiwawa, Isaac amawauza kuti: “Musaseweretse zimenezo. Yehova amadana nazo.”

Croatia: Ana athu amasangalala ndi nyimbo za Ufumu