Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Apolisi Anathandiza Kutsitsa Njerwa

Kwa zaka 13, mumzinda wa Kutaisi m’dziko la Republic of Georgia, misonkhano ikuluikulu inkachitikira m’chinyumba china chakutha, chomwe poyamba ankapangiramo vinyo. Pakakhala msonkhano, abale ankamanga mapepala apulasitiki kudenga kuti asanyowe ndi mvula. Koma panopa abale ali ndi malo abwino kwambiri opangira misonkhano. Iwo anamanga Nyumba ya Ufumu yopanda makoma a m’mbali komanso yotheka kuiwonjezera, kuti apangiremo misonkhano ikuluikulu. Nthawi ina ntchito yomangayi ili mkati, abale okwana 50 ankatsitsa njerwa za simenti m’galimoto ina yaikulu. Ndiyeno panafika apolisi kuti adzaone zomwe zinkachitika. Apolisiwa anachita chidwi kwambiri ataona mmene abalewo  ankagwirira ntchito mwakhama komanso mwachimwemwe. Iwo anayamikira abalewo ndipo kenako anayamba kuwathandiza kutsitsa njerwazo. Apolisiwa anauza abalewa kuti ngati wina atabwera kudzawavutitsa adzawaitane. Analonjezanso kuti adzabwera pa msonkhano woyamba umene udzachitike pa Nyumba ya Msonkhano yatsopanoyi.

Anagulitsa Njinga Yake

Malachi, yemwe ndi mkulu m’dziko la Burundi, ankagwira ntchito yolima komanso ankanyamula katundu pa njinga yake kuti azipeza zofunika pa moyo wake. Nyumba ya Ufumu yawo itayamba kumangidwa anaganiza kuti tsiku lililonse azikathandiza ntchitoyo. Koma kuti akwanitse zimenezi, ankafunika kuti apeze ndalama zothandizira banja lake kwa miyezi iwiri imene adzakhale akuthandiza nawo ntchitoyi. Choncho anagulitsa njinga yake ndipo anatengako zina mwa ndalamazo n’kupatsa mkazi wake ndipo zotsalazo anakaziponya m’bokosi la zopereka kuti zithandize pa ntchito yomangayo. Chifukwa cha khama lakeli anaphunzitsidwa bwino ntchito yomanga ndi atumiki omanga Nyumba za Ufumu. Nyumba ya Ufumuyo itatha, Malachi anapeza ntchito ina yomanga chifukwa chakuti anthu anaona kuti ali ndi luso lomanga nyumba. Panopa Malachi anagulanso njinga ina.

Anadzipereka Kuti Athandize

M’dziko la Malawi, kumanga Nyumba za Ufumu kumadera a kumudzi kumakhala kovuta. M’chaka cha utumiki chathachi, Nyumba ya Ufumu ina inamangidwa kumalo amene misewu yake ndi yoipa kwambiri. Choncho kuti akafike kumalowo, abale ochokera ku ofesi ya nthambi ankanyamula katundu wawo m’magalimoto amphamvu otha kuyenda m’misewu yovuta. Abale a kumeneko ananena kuti anthu ambiri a m’deralo ankachita chidwi ndi ntchitoyi. Ambiri omwe si Mboni anadzipereka kuthandiza ntchito yotsitsa mchenga, miyala, matumba a simenti ndi malata ndipo anagwira ntchitoyi mpaka usiku. Ndipotu nthawi zina anthu ongodzipereka omwe sanali Mboni ankakhala ambiri kuposa Mboni. Anthuwa anadzipereka kwambiri chonchi chifukwa choona khama la Mboni za  Yehova pomanga malo olambiriramo abwino kumadera ovuta kufikako ngati amenewa.

Ana Ankagulitsa Tofi

Banja lina lomwe likuchita upainiya wapadera m’dziko la Côte d’Ivoire limaphunzira Baibulo ndi banja lina la ana 10. Iwo amaphunzira ndi banjali m’chinenero cha Chibete, chomwe chimalankhulidwa m’dera lina m’dzikolo. M’mwezi wa May 2013 kunachitika msonkhano woyamba m’Chibete m’tauni ya Daloa, ndipo banja lonse linkafunitsitsa kupitako. Komabe munthu aliyense m’banjamo ankafunika ndalama zoyendera zokwana 800 franc (kapena kuti madola 1.60 a ku United States). Koma bambo a m’nyumbamo sakanakwanitsa kupeza ndalama zokwanira banja lonse. Koma popeza kuti ankafunitsitsa kupita ku msonkhanoko, bambowo anaganiza zopatsa mwana wawo wamkazi ndalama zokwana 300 franc (kapena kuti masenti 60 a ku United States), kuti ayambe bizinezi ya tofi. Iye anachitadi zomwezo ndipo anapeza phindu moti ndalama zoyendera popita ku msonkhano zinapezeka. Bambowo anachitanso chimodzimodzi ndi ana ena onse. Anapatsa aliyense ndalama zokwana masenti 60 kuti achitire bizinezi yogulitsa tofi kuti apeze ndalama zolipirira thiransipoti yopitira ku misonkhano. Pamapeto pake onse anapeza ndalamazo ndipo limodzi ndi ena anapita ku msonkhanowo. Banja lonse linasangalala kwambiri kumvetsera msonkhanowo m’chinenero chawo.