Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mwambo Wopereka Nthambi

Mwambo Wopereka Nthambi

Pa October 20, 2012, Mboni za Yehova m’dziko la Korea zinasangalala kwambiri kuchita mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi yomwe anali ataiwonjezera ndi kukonzanso nyumba zake. Mboni za Yehova m’dzikoli zinkaona kuti mwambowu ndi wapadera kwambiri zikaganizira mmene zakhalira zokhulupirika kwa zaka 100. Chosangalatsanso n’choti m’chaka cha 2012, kwa nthawi yoyamba, chiwerengero cha ofalitsa chinapitirira 100,000. Abale ndi alongo 1,200 a m’dzikoli komanso ena 239 ochokera m’mayiko 9 anadzipereka kumanga nawo nyumba zina zatsopano za ofesi ya nthambiyi. Nyumbazi zikuphatikiza nyumba yogona, nyumba yosindikizira mabuku, nyumba yojambulira mawu ndi mavidiyo komanso nyumba yokonzera magalimoto. Kuwonjezera pamenepo, nyumba zambiri zomwe zinalipo kale zinakonzedwanso n’kukhala zatsopano.

M’bale Anthony Morris, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yolimbikitsa yotsegulira ofesi ya nthambiyo ndipo pa  mwambowu panali abale ndi alongo okwana 3,037. Tsiku lotsatira, panachitikanso msonkhano wapadera m’holo ina yaikulu. Abale ndi alongo m’mipingo yoposa 1,300 ya m’dziko la Korea, anamvetsera pulogalamuyo kudzera pa Intaneti. Mboni za Yehova komanso anthu amene akuphunzira Baibulo anasangalala kwambiri ndi pulogalamu yauzimu imeneyi. Onsewa pamodzi analipo okwana 115,782.

Tsiku la March 9, 2013 silidzaiwalika m’mbiri ya anthu olambira Yehova m’dziko la Liberia. Pa tsikuli alendo ochokera m’mayiko 11 anasonkhana pa mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi yomwe anali ataiwonjezera ndi kukonzanso nyumba zake. Anthu onse omwe anabwera pa mwambowu analimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani yotsegulira ofesiyi, yomwe inakambidwa ndi M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira. Kwa zaka zoposa 10, ntchito yomanga ofesiyi inaima kaye chifukwa cha nkhondo yapachiweniweni yomwe inkachitika m’dzikoli. Koma nkhondoyo itatha, abale anayambiranso kugwira ntchito yowonjezera ofesi ya nthambi. Pochita zimenezi iwo anagwiritsanso ntchito malo omwe pa nthawi ya nkhondoyi kunkabisala zigawenga, komanso omwe kunkakhala anthu othawa nkhondo. Abale ndi alongo 51 otumikira pa Beteli, akusangalala kwambiri kugwiritsa  ntchito nyumba yatsopano yogona yokhala ndi zipinda 35, maofesi okonzedwanso, nyumba yatsopano yosungiramo mabuku, nyumba yatsopano ya dipatimenti yokonza zinthu, khitchini yatsopano komanso malo odyera atsopano.

Dziko la Republic of Georgia ndi la anthu ochezeka komanso okonda kwambiri kupembedza. Dzikoli litachoka mu mgwirizano wa Soviet Union, anthu ambiri anayamba kuphunzira choonadi ndipo zinthu zinayamba kuyenda bwino kwambiri. Komabe patadutsa kanthawi kochepa, abale anayamba kuzunzidwa koopsa. Panopa zinthu zasintha ndipo abale sakuzunzidwa kwambiri ngati kale. Tsiku losaiwalika m’mbiri ya Mboni za Yehova m’dziko la Georgia linali Loweruka pa April 6, 2013. Pa tsikuli panali mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi imene anaiwonjezera n’kukonzanso zinthu zina. Anakonzanso Nyumba ya Msonkhano n’kumanga makalasi a sukulu zosiyanasiyana monga Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ndiponso Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda ndi Akazi Awo. M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani yotsegulira nyumbazi. Anthu okwana 338 ochokera m’mayiko 24 anabwera kudzamvera pulogalamuyi limodzi ndi Mboni zoposa 800 za m’dziko la Georgia.

Georgia

Tsiku lotsatira, abale ndi alongo okwana 15,200 m’dziko lonseli anamvetsera nkhani yapadera ya M’bale Splane pa masikirini ali kumipingo yawo. Anthu analimbikitsidwa kwambiri ndi mwambo wapaderawu. Mwachitsanzo, m’bale wina wachinyamata ananena kuti, “Panopa ndadziwa mmene zinthu zidzakhalire m’dziko latsopano.”

Pa June 29, 2013 panachitikanso mwambo wotsegulira maofesi okhala ndi nsanjika zitatu, ku Beteli ya ku Yangon m’dziko la Myanmar. M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yotsegulira maofesiwa. Pa mwambowu panali abale ndi alongo okwana 1,013 kuphatikizapo alendo ochokera m’mayiko 11. Abale ndi alongo ena a ku Myanmar anapemphedwa kuti akalandire alendo ochokera kumayiko ena kubwalo la ndege la ku Yangon. Ndiye bambo wina wochokera kudziko limene ntchito ya Mboni za Yehova ndi yoletsedwa anafika pamene panali abalewa. Bamboyu anaona zikwangwani zolembedwa kuti, “Takulandirani a Mboni za Yehova” zomwe abale ndi alongowa  ananyamula ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mboni zimene mukulandira apazi n’zoti zikachitire umboni pa mlandu m’khoti?” Abalewa anamuyankha kuti, “Ayi, tikulandira anzathu.” Kenako anawafunsanso kuti, “Ndiye kodi Yehova amene mukunena apayu ndani?” Zimenezi zinawapatsa abale ndi alongowa mwayi wokambirana naye mfundo za m’Baibulo. Pulogalamu yotsegulira maofesi itachitika, tsiku lotsatira kunalinso msonkhano wapadera womwe unachitikira kuholo ina ku Myanmar. Pa msonkhanowu, M’bale Pierce anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Tumikirani Yehova ndi Mtima Wozindikira.” Abale ena omwe anasonkhana m’madera 6 osiyanasiyana m’dziko la Myanmar anamvetsera pulogalamuyi kudzera pa telefoni. Zimenezi zinachititsa kuti chiwerengero cha abale ndi alongo okwana 2,963 amvetsere uthenga wa panthawi yakewu. Bambo wina amene ankayendetsa basi yonyamula abale ndi alongo opita ku msonkhano wapaderawu ku Yangon ananena kuti: “Ndaona kuti ndinu anthu osiyana kwambiri ndi anthu a zipembedzo zina. Muli ndi makhalidwe abwino, mumavala mwaulemu komanso ndinu anthu okoma mtima. Kwa zaka zambiri ndakhala ndikuyendetsa magulu osiyanasiyana a anthu, koma sindinaonepo anthu abwino ngati inuyo.”

Myanmar: Ofalitsa a m’dzikoli akulandira alendo obwera ku mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi

 Lachitatu pa July 3, 2013, atumiki okhulupirika a Yehova m’dziko la Moldova anasangalala kwambiri ndi mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi imene anaiwonjezera. M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani pa mwambowu. Pamalowa anamangapo nyumba ya nsanjika zitatu mmene muli malo osungiramo mabuku ndi zipinda 10 zogona. Palinso Nyumba ya Ufumu ya nsanjika ziwiri ndipo ikugwiritsidwa ntchito ndi mipingo 7. Abale ndi alongo 33 omwe akutumikira pa Beteli anasangalala kwambiri kulandira alendo ochokera ku Germany, Ireland, Netherlands, Romania, Russia, Ukraine ndi ku United States. Komanso pa anthu amene anasonkhana pa mwambowu panali abale ndi alongo omwe atumikira Yehova mokhulupirika pa nthawi imene ntchito yolalikira inali yoletsedwa m’dzikoli. Ena a iwo ankathandiza kukopera ndi kutumiza mabuku kumadera osiyanasiyana. Panalinso abale ndi alongo omwe anathamangitsidwa limodzi ndi makolo awo n’kupita kudziko la Siberia pa nthawi imene boma la Soviet Union linkachitira nkhanza Mboni za Yehova. Lamlungu, M’bale Lett anakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri yomwe inamasuliridwa m’Chiromaniya ndi Chirasha. Anthu okwana 14,705 ndi amene anamvetsera nkhaniyi ndipo pa misonkhano yonse imene yachitikapo m’dziko la Moldova, aka kanali koyamba kuti Mboni za Yehova zochuluka chonchi zisonkhane pamodzi.

Pitirizani Kupemphera, Musaleke

Yesu anatsindika kuti tiyenera kupemphera nthawi zonse ndipo sitiyenera kuleka. (Luka 18:1) Tikamalankhula ndi Yehova mochokera pansi pa mtima, zimatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo cholimba. Choncho tiyenera ‘kupemphera mosalekeza’ kapena kuti tiyenera ‘kulimbikira kupemphera.’ (1 Ates. 5:17; Aroma 12:12) Pamene mukuchita zimenezi, “Mulungu wamtendere . . . akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, achite mwa [inu] zimene zili zokondweretsa pamaso pake.”—Aheb. 13:20, 21.