Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Munthu Amene Sadziŵa Zinthu Amakhulupilila Mau Alionse”

“Munthu Amene Sadziŵa Zinthu Amakhulupilila Mau Alionse”

“Wopusa ndi munthu amene saŵelenga nyuzipepala. Ndipo wopusa kwambili ndi munthu amene amakhulupilila zimene waŵelenga cifukwa cakuti zalembedwa m’nyuzipepala.”—Anatelo August von Schlözer, wolemba mabuku ndi mbili yakale wa ku Germany (1735-1809).

ZAKA zoposa 200 zapitazo, anthu sanali kukhulupilila zonse zimene zalembedwa m’manyuzipepala. Masiku ano, sitingakhulupilile zonse zimene taŵelenga kapena kuona pa Intaneti. Pa Intaneti pamapezeka nkhani zambili, ndipo zipangizo zamakono zimacititsa kuti kukhale kosavuta kuŵelenga nkhanizo. Nkhani zambili zimakhala zoona, zothandiza, ndiponso zabwino. Koma zambilinso zimakhala zabodza, zacabecabe, ndi zoipa. Ndiye cifukwa cake, tiyenela kusamala kwambili posankha zinthu zoti tiŵelenge. Ena akayamba kugwilitsila nchito Intaneti, angaganize kuti uthenga umene ulipo ndi woona cifukwa cakuti uli pa Intaneti, kapena cifukwa cakuti mnzao wawatumila pa imelo. Iwo angakhulupilile nkhaniyo ngakhale kuti ndi yacilendo. Komabe, Baibulo limaticenjeza kuti: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mau alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.”—Miyambo 14:15.

Kukhala wocenjela kumasiyana ndi kukhulupilila zonse zimene tamvela. Tikakhala wocenjela, timasamala kwambili ndipo timakhulupilila nkhani imene ndi yoona. Tidzapewa kunamizidwa kuti tikhulupilile nkhani yabodza imene taŵelenga pa Intaneti, ngakhale kuti nkhaniyo ndi yofala kwambili. N’ciani cingakuthandizeni kukhala wocenjela? Coyamba, muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi nkhani imeneyi yacokela pa webusaiti yodalilika? Kodi yacokela pa webusaiti imene aliyense amalembapo maganizo ake, kapena yacokela pa webusaiti yosadziŵika bwino? Kodi webusaiti yodalilika ikutipo ciani pa nkhaniyo?’ * (Onani mau a munsi.) Ndiyeno, citani zinthu ‘mwanzelu.’ (Miyambo 7:7) Ngati mwaona kuti nkhani inayake ndi yovuta kukhulupilila, ndiye kuti mwina nkhaniyo ndi yabodza. Ndiponso, mukaŵelenga nkhani zoipa zokhudza ena, ganizilani amene angapindule ngati nkhaniyo yafalikila. Ganizilaninso cifukwa cake wina angafune kufalitsa nkhaniyo.

KODI MUMAKONDA KUTUMILA ENA MAUTHENGA?

Ena angatumile anzao nkhani popanda kuona kuti nkhaniyo ndi yoona kapena ai, kapena popanda kuganizila zotsatilapo zake akatuma nkhaniyo. Mwina amacita zimenezi cifukwa afuna kuti anthu aziwatamanda, ndi kuti akhale oyamba kufalitsa nkhaniyo. (2 Samueli 13:28-33) Koma munthu wocenjela coyamba amaganizila za mavuto amene angabwele. Mwacitsanzo, zikhoza kuononga mbili yabwino ya munthu, kapena ya gulu linalake.

Munthu amene afuna kutumila ena nkhani angalephele kuona kaya nkhaniyo ndi yoona kapena ai, cifukwa kucita zimenezo kumafuna nthawi ndi khama. Iye amangotuma poganiza kuti amene adzalandila uthengawo adzacita zimenezo paokha. Koma naonso amene alandila uthengawo amaona kuti nthawi ndi ya mtengo wapatali. (Aefeso 5:15, 16) Conco, m’malo motumila ena zinthu zimene sitinatsimikize kuti n’zoona, zingakhale bwino kuganizila mwakuya kuti: “Ngati ndikaikila, ndiye kuti ndiyenela kupewa kutumizila ena zinthu zimenezi.”

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonda kutumila ena mauthenga? Kodi panthawi ina ndinapepesa kwa anzanga cifukwa cowatumila zinthu zolakwika kapena zabodza? Kodi pali aliyense amene anandiuzapo kuti ndisiye kum’tumila mauthenga?’ Kumbukilani kuti ngati anzanu ali ndi imelo adilesi, naonso amagwilitsila nchito Intaneti ndipo akhoza kufufuza zinthu zimene zingawakondweletse, m’malo moyembekezela inu. Iwo sangakonde kulandila mauthenga ambilimbili okhudza nkhani zoseketsa, mavidiyo, ndi zithunzi. Ndiponso, si canzelu kutumila ena nkhani zimene mwajambula, kapena mfundo zonse zimene mwalemba zokhudza nkhani za Baibulo. * (Onani mau a munsi.) Kumbukilaninso kuti ngati munthu afufuza payekha malemba m’Baibulo, kapena kukonzekela zimene adzayankha pa misonkhano, iye adzapindula kwambili kuposa mmene angapindulile ngati mwam’tumila zinthu zimenezi.

Kodi nditumileko winawake uthenga umenewu?

N’ciani cimene muyenela kucita ngati mwaona nkhani inayake pa Intaneti imene ionetsa mabodza amkunkhuniza okhudza gulu la Yehova? Muyenela kuwapewa mwamsanga! Musakhulupilile zimenezo. Si canzelu kutumila ena zimene mwaŵelenga, ndi kupempha kuti mumve maganizo ao. Kucita zimenezo kungapangitse kuti nkhani yoipa imeneyo ifalikile kwambili. Ngati mwaona cinacake pa Intaneti cimene cakudetsani nkhawa, pemphani Yehova kuti akupatseni nzelu. Ndiyeno, kambilanani nkhaniyo ndi abale ofikapo kuuzimu. (Yakobo 1:5, 6; Yuda 22, 23) Sitiyenela kudabwa ngati anthu amatinenela mabodza. Anthu anali kukamba zabodza ponena za Yesu. Ndipo iye anauza ophunzila ake kuti adani ao adzawazunza ndi ‘kuwanamizila zoipa zilizonse.’ (Mateyu 5:11; 11:19; Yohane 10:19-21) Motelo, ngati mukhala anzelu ndiponso osamala, mudzatha kuzindikila mabodza amene wina akukamba n’colinga cakuti asoceletse ena.—Miyambo 2:10-16.

MUZILEMEKEZA ENA

Tiyenelanso kukhala osamala kwambili pankhani yotumila ena nkhani yokhudza abale athu, kapena zocitika zina zimene tamvela. Nthawi zina, si bwino kufalitsa nkhani ngakhale kuti ndi yoona. (Mateyu 7:12) Mwacitsanzo, si cikondi kutumila ena nkhani zoipa zokhudza anthu ena. (2 Atesalonika 3:11; 1 Timoteyo 5:13) Nkhani zina zimakhala zacisinsi. Anthuwo angafune kufalitsa nkhani imeneyo panthawi ina, kapena mwa njila inayake. N’cifukwa cake, tiyenela kulemekeza ufulu wao wosankha nthawi yakuti afalitse nkhaniyo, ndi mmene angaifalitsile. Ngati tiuza ena za nkhaniyo kukali nthawi, zingabweletse mavuto osaneneka.

Masiku ano, nkhani zimafalikila mwamsanga, kaya nkhaniyo ndi yoona kapena ai, yothandiza kapena yacabecabe, yabwino kapena yoipa. Ngakhale kuti mwatumila munthu mmodzi uthenga winawake, munthuyo angathe kutumila anthu padziko lonse m’masekondi ocepa cabe. Conco, pewani kutumila mwamsanga uthenga kwa aliyense amene mumadziŵa. Ngakhale kuti cikondi “cimakhulupilila zinthu zonse,” ndipo sicikaikila ena, tiyenela kupewa kukhulupilila nkhani iliyonse yatsopano ndi yokondweletsa. (1 Akorinto 13:7) Ndipo sitiyenela kukhulupilila mabodza kapena zinthu zoipa zimene ena amakamba ponena za gulu la Yehova, komanso abale athu amene timakonda. Kumbukilani kuti anthu amene amayambitsa ndi kufalitsa mabodza amenewa amakondweletsa Satana Mdyelekezi, “tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Motelo, tiyeni tikhale ocenjela ndi osamala kwambili ndi nkhani zambili zimene timalandila ndi kuona tsiku lililonse. Baibulo limakamba kuti “anthu osadziŵa zinthu, ndithu adzakhala opusa, koma kwa ocenjela, kudziŵa zinthu kudzakhala ngati covala ca kumutu.”—Miyambo 14:18.

^ par. 4 Nkhani ina ingafalitsidwenso ngakhale kuti poyamba inadziŵika kuti ndi yabodza. Angasinthe zinthu zina kuti nkhaniyo ioneke kukhala yoona.

^ par. 8 Onani Utumiki Wathu wa Ufumu, wacingelezi wa April 2010, “Bokosi la Mafunso.”