Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mzimu Umacitila Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu

Mzimu Umacitila Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu

“Mzimuwo umacitila umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.”—AROMA 8:16.

NYIMBO: 109, 108

1-3. Ndi zinthu ziti zimene zinapangitsa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. kukhala lapadela? Nanga zimenezo zinakwanilitsa bwanji ulosi wa m’Malemba? (Onani cithunzi pamwambapa.)

TSIKU lina pa Sondo m’maŵa mu 33 C.E., ku Yerusalemu kunacitika zinthu zapadela komanso zosangalatsa. Anthu anali pa cikondwelelo ca Pentekosite, cimene cinali kucitika kuciyambi kwa nyengo yokolola. M’maŵa patsikulo, mkulu wa ansembe anapeleka nsembe pa kacisi monga mwa nthawi zonse. Ndiyeno, ca m’ma 09:00hrs, anapeleka nsembe ya mikate iŵili ya cofufumitsa. Mikateyo inali yopangidwa ndi tiligu woyambilila, kapena kuti zipatso zoyambilila za m’nyengo yokolola. Mkulu wa ansembeyo anaweyula mikateyo ndi kuipeleka monga nsembe kwa Yehova.—Levitiko 23:15-20.

2 Kwa zaka zambili, mkulu wa ansembe anali kupeleka nsembe yoweyula caka ciliconse. Zimenezi zinali kugwilizana kwambili ndi cocitika cofunika kwambili cimene cinacitika pa Pentekosite mu 33 C.E. Cocitika cimeneco cinacitikila ophunzila a Yesu okwana 120 amene anali kupemphela m’cipinda capamwamba ku Yerusalemu. (Machitidwe 1:13-15) Mneneli Yoweli anali atalembelatu za cocitikaco kukali zaka 800 kuti cicitike. (Yoweli 2:28-32; Machitidwe 2:16-21) Kodi n’ciani cimene cinacitika?

3 Ŵelengani Machitidwe 2:2-4. Pa Pentekosite mu 33 C.E., Mulungu anadzoza ophunzilawo ndi mzimu woyela. (Machitidwe 1:8) Kenako, anthu ambili anayamba kusonkhana pamene panali Akristuwo, ndipo ophunzila a Yesu anayamba kulankhula zinthu zodabwitsa zimene anamva ndi kuziona. Mtumwi Petulo anafotokoza tanthauzo la zimene zinacitikazo ndiponso cifukwa cake zinali zofunika kwambili. Kenako, anauza khamulo kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu kuti macimo anu akhululukidwe. Mukatelo mudzalandila mphatso yaulele ya mzimu woyela.” Pa tsikulo, anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa, ndipo naonso analandila mzimu woyela.—Machitidwe 2:37, 38, 41.

4. (a) Kodi zimene zinacitika pa Pentekosite zimatikhudza bwanji? (b) Ndi cocitika citi cimene ciyenela kuti cinacitika zaka zambili m’mbuyomo pa tsiku lofanana ndi la Pentekosite? (Onani mau akumapeto.)

4 Kodi mkulu wa ansembe ndiponso nsembe zimene anali kupeleka pa Pentekosite zinali kuimila ciani? Mkulu wa ansembe anali kuimila Yesu. Nsembe ya mikate inali kuimila ophunzila a Yesu amene anadzozedwa. Ophunzilawo anasankhidwa pakati pa anthu opanda ungwilo, ndipo amachedwa “zipatso zoyambilila.” (Yakobo 1:18) Mulungu anawasankha kuti akhale ana ake ndi kuti adzalamulile pamodzi ndi Yesu kumwamba mu Ufumu wa Mulungu. (1 Petulo 2:9) Yehova adzadalitsa anthu onse omvela kudzela mu Ufumu wake umenewu. Conco, kaya tidzakhala kumwamba pamodzi ndi Yesu kapena tidzakhala m’paladaiso pano padziko lapansi, zimene zinacitika pa Pentekosite mu 33 C.E., zimatikhudza. [1] —Onani mau akumapeto.

N’CIANI CIMACITIKA MUNTHU AKADZOZEDWA?

5. Timadziŵa bwanji kuti Akristu sadzozedwa m’njila yofanana ndendende?

5 Ophunzila a Yesu amene anali m’cipinda capamwamba sanaiŵale zimene zinacitika patsikulo. Aliyense wa io anali ndi cizindikilo cokhala ngati laŵi la moto pamutu pake. Yehova anawapatsa mphamvu yolankhula zinenelo zacilendo. Iwo sanakaikile kuti adzozedwa ndi mzimu woyela. (Machitidwe 2:6-12) Koma zocitika zodabwitsa zotele sizicitikila Mkristu aliyense amene wadzozedwa. Mwacitsanzo, Baibulo silikamba kuti zizindikilo zokhala ngati malaŵi a moto zinaonekelanso pa mitu ya anthu ambilimbili, amene anadzozedwa pambuyo pake ku Yerusalemu. Iwo anadzozedwa pamene anali kubatizidwa. (Machitidwe 2:38) Komanso, si Akristu onse amene amadzozedwa panthawi imene akubatizidwa. Asamariya anadzozedwa patapita nthawi kucokela pamene anabatizidwa. (Machitidwe 8:14-17) Ndipo Koneliyo ndi a m’banja lake anadzozedwa asanabatizidwe n’komwe.—Machitidwe 10:44-48.

6. Kodi Akristu onse odzozedwa amalandila ciani? Nanga cimene amalandilaco cimawathandiza kudziŵa ciani?

6 Mwacionekele, Akristu amadziŵa m’njila zosiyanasiyana kuti ndi odzozedwa. Ena amadziŵa mwamsanga kuti Yehova wawadzoza. Ena amadziŵa patapita nthawi kucokela pamene anadzozedwa. Koma mtumwi Paulo anafotokoza zimene zimacitika kwa munthu aliyense amene wadzozedwa. Iye anati: “Mutakhulupilila munaikidwa cidindo ca mzimu woyela wolonjezedwawo, umene ndi cikole ca colowa cathu cam’tsogolo.” (Aefeso 1:13, 14) Cotelo, pogwilitsila nchito mzimu woyela, Yehova amathandiza Akristu amenewa kudziŵa kuti anasankhidwa kuti adzapite kumwamba. Iwo sakaikila zimenezi ngakhale pang’ono. Mwa njila imeneyi, mzimu woyela umakhala ‘cikole ca colowa cao cam’tsogolo,’ kapena kuti citsimikizo cakuti adzakhala kumwamba osati pano padziko lapansi.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:21, 22; 5:5.

Mkristu aliyense wodzozedwa sayenela kulola cinthu ciliconse kumulepheletsa kutumikila Yehova

7. Kodi Mkristu aliyense wodzozedwa ayenela kucita ciani kuti adzalandile colowa cake?

7 Ngati Mkristu wadzozedwa, kodi zikutanthauza kuti basi adzapita kumwamba? Iyai. Iye amakhala wotsimikiza ndi mtima wonse kuti wasankhidwa kuti adzapite kumwamba. Koma kuti adzalandile colowa cake, afunika kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Petulo anafotokoza kuti: “Pa cifukwa cimeneci abale, citani ciliconse cotheka kuti mukhalebe okhulupilika, n’colinga coti mupitilizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiliza kucita zinthu zimenezi simudzalephela ngakhale pang’ono. Ndipo mukatelo, adzakutsegulilani khomo kuti mulowe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu.” (2 Petulo 1:10, 11) Cotelo, Mkristu aliyense wodzozedwa sayenela kulola cinthu ciliconse kumulepheletsa kutumikila Yehova. Ngakhale kuti anaitanidwa kapena kusankhidwa kuti adzapite kumwamba, sadzalandila colowa cake ngati alephela kukhala wokhulupilika kwa Mulungu.—Aheberi 3:1; Chivumbulutso 2:10.

KODI MUNTHU AMADZIŴA BWANJI KUTI WADZOZEDWA?

8, 9. (a) N’cifukwa ciani ambili amalephela kumvetsa zimene zimacitika munthu akadzozedwa? (b) Kodi munthu amadziŵa bwanji kuti wasankhidwa kuti adzapita kumwamba?

8 Atumiki ambili a Mulungu masiku ano amalephela kumvetsetsa zimene zimacitika munthu akadzozedwa. Zimenezi n’zosadabwitsa cifukwa cakuti io si odzozedwa. Mulungu analenga anthu kuti azikhala padziko lapansi, osati kumwamba. (Genesis 1:28; Salimo 37:29) Koma Yehova amasankha anthu ena kuti adzakhale mafumu ndi ansembe kumwamba. Conco munthu akadzozedwa, ciyembekezo cake ndiponso mmene amaganizila zimasintha moti amayamba kuyembekezela moyo wakumwamba.—Ŵelengani Aefeso 1:18.

9 Nanga munthu amadziŵa bwanji kuti wasankhidwa kuti adzapite kumwamba? Onani zimene Paulo anauza Akristu odzozedwa a ku Roma, amene ‘anaitanidwa kukhala oyela.’ Iye anati: “Simunalandile mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandila mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nao kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo umacitila umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 1:7; 8:15, 16) Pogwilitsila nchito mzimu woyela, Mulungu amathandiza munthu amene wadzozedwa kudziŵa popanda kukaikila kulikonse kuti wasankhidwa kuti adzalamulile monga mfumu kumwamba pamodzi ndi Yesu.—1 Atesalonika 2:12.

10. Kodi lemba la 1 Yohane 2:27 limatanthauza ciani pamene limati Mkristu wodzozedwa sakufunikila wina aliyense kuti azimuphunzitsa?

10 Akristu amene asankhidwa ndi Mulungu kuti adzapite kumwamba safunika kuuzidwa ndi munthu wina kuti adzozedwa. Yehova amawathandiza kutsimikizila ndi mtima wonse kuti anadzozedwa. Mtumwi Yohane anauza Akristu odzozedwa kuti: “Inu munadzozedwa ndi woyelayo, ndipo nonsenu ndinu odziŵa coonadi.” Kenako anakambanso kuti: “Inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Cotelo simukufunikila wina aliyense kuti azikuphunzitsani, koma popeza kuti munadzozedwadi moona osati monama, cifukwa ca kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse. Monga mmene mwaphunzitsidwila, pitilizani kukhala ogwilizana naye.” (1 Yohane 2:20, 27) Mofanana ndi tonsefe, Akristu odzozedwa amafunika kuphunzitsidwa ndi Yehova. Koma safunika kuuzidwa ndi munthu wina kuti atsimikizile kuti ndi odzozedwa. Kudzela mwa mzimu woyela, umene ndi mphamvu yoposa cina ciliconse, Yehova amathandiza Akristuwo kukhulupilila kuti anadzozedwadi, ndipo sakaikila zimenezi ngakhale pang’ono.

‘AMABADWANSO’

11, 12. Kodi Mkristu wodzozedwa angakhale ndi maganizo otani? Nanga n’ciani cimene sakaikila?

11 Akristu akadzozedwa ndi mzimu woyela, amasintha kwambili. Yesu anakamba kuti ‘amabadwanso.’ (Yohane 3:3, 5) Kenako Yesu anati: “Usadabwe cifukwa ndakuuza kuti, anthu inu muyenela kubadwanso. Mphepo imawombela kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziŵa kumene ikucokela ndi kumene ikupita. N’cimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.” (Yohane 3:7, 8) Conco, Mkristu wodzozedwa sangathe kufotokoza momveka bwino mmene amamvelela kwa munthu amene si wodzozedwa. [2]—Onani mau akumapeto.

Mkristu wodzozedwa sakaikila kuti Yehova anamusankha

12 Munthu amene wadzozedwa angadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova wasankha ine osati munthu wina?’ Iye angaganize kuti si woyenela kukhala ndi mwai umenewu. Ngakhale n’conco, sakaikila kuti Yehova wamusankha. Koma amakhala woyamikila ndiponso wacimwemwe kwambili cifukwa ca mphatso imeneyi. Akristu odzozedwa amamva ngati mmene Petulo anamvela pamene anati: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, pakuti mwacifundo cake cacikulu, anatibeleka mwatsopano kuti tikhale ndi ciyembekezo ca moyo mwa kuukitsidwa kwa Yesu Kristu. Anatibeleka kuti tikhale ndi colowa cosawonongeka, cosadetsedwa ndiponso cosasuluka. Colowa cimeneci anasungila inuyo kumwamba.” (1 Petulo 1:3, 4) Pamene wodzozedwa akuŵelenga mau amenewa, amadziŵa popanda kukaikila kulikonse kuti Atate wake akukamba naye.

13. Kodi kaganizidwe ka odzozedwa kamasintha bwanji akadzozedwa? Nanga n’ciani cimacititsa zimenezi?

13 Akristu amenewa asanasankhidwe ndi Yehova kuti adzapita kumwamba, anali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Anali kuyembekezela nthawi imene Yehova adzathetsa zoipa zonse ndi kupanga dzikoli kukhala paladaiso. Mwina anali kuyembekezela mwacidwi nthawi imene adzalandila abale ao kapena mabwenzi ao amene adzaukitsidwa. Ndiponso anali kuyembekezela kudzamanga nyumba ndi kukhalamo kapena kudzalima minda ndi kudya zipatso zake. (Yesaya 65:21-23) Nanga n’ciani cinacititsa kuti asinthe ndi kuyamba kuganiza zokakhala kumwamba? Kodi anasintha cifukwa ca nkhawa kapena cifukwa cakuti anakumana ndi mavuto ena aakulu? Kodi anangosintha mwadzidzidzi cifukwa coganiza kuti moyo wosatha pano padziko lapansi sudzakhala wosangalatsa? Kapena amangofuna kukalawa umoyo wakumwamba? Iyai. Mulungu ndi amene anawasankha kuti akakhale kumwamba. Pamene anawasankha, anacititsa kuti asinthe kaganizidwe kao ndi ciyembekezo cao. Iye anacita zimenezi pogwilitsila nchito mzimu wake woyela.

14. Kodi odzozedwa amamva bwanji pamene ali ndi moyo pano padziko lapansi?

14 Kodi zimenezi zionetsa kuti odzozedwa amafuna kufa? Paulo anafotokoza mmene odzozedwa amamvelela. Iye anayelekezela thupi lao laumunthu ndi ‘msasa,’ ndipo anati: “Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula cifukwa colemedwa. Kwenikweni si cifukwa cofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo, kuti cokhoza kufaci cilowedwe m’malo ndi moyo.” (2 Akorinto 5:4) Akristu odzozedwa safuna kufa. Iwo amasangalala kukhala ndi moyo ndipo amafuna kutumikila Yehova pamodzi ndi banja lao ndiponso mabwenzi ao. Koma nthawi zonse pa umoyo wao amakumbukila cimene Mulungu anawalonjeza.—1 Akorinto 15:53; 2 Petulo 1:4; 1 Yohane 3:2, 3; Chivumbulutso 20:6.

KODI YEHOVA ANAKUSANKHANI?

15. Ndi zinthu ziti zimene sizipeleka umboni wakuti munthu anadzozedwa ndi mzimu woyela?

15 Mwina nthawi zina mumaganiza kuti Yehova anakusankhani kuti mudzapite kumwamba. Ngati mumaganiza conco, yankhani mafunso awa: Kodi mumaona kuti ndinu wacangu pa nchito yolalikila? Kodi mumakonda kuphunzila Baibulo ndiponso “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akorinto 2:10) Kodi muona kuti Yehova wakudalitsani pa nchito yolalikila? Kodi mumafuna kucita cifunilo ca Yehova kuposa cinthu cina ciliconse? Kodi mumakonda kwambili anthu ena ndipo mumafunitsitsa kuwathandiza kutumikila Yehova? Kodi mwaona umboni wosonyeza kuti Yehova wakuthandizani m’njila zosiyanasiyana pa umoyo wanu? Ngati yankho lanu ndi lakuti inde pa mafunso onsewa, kodi ndiye kuti munasankhidwa kuti mudzapita kumwamba? Ai, sizitanthauza zimenezo. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti atumiki onse a Mulungu akhoza kumva mwanjila imeneyi, kaya ndi odzozedwa kapena ai. Ndipo pogwilitsila nchito mzimu woyela, Yehova angapeleke mphamvu yofanana kwa mtumiki wake aliyense, mosasamala kanthu za ciyembekezo cimene ali naco. Ndiponso ngati sindinu wotsimikiza kuti mudzapita kumwamba, ndiye kuti simunadzozedwe. Akristu amene anadzozedwa sakaikila ngakhale pang’ono kuti anasankhidwa. Iwo amadziŵa ndithu.

16. Timadziŵa bwanji kuti ena amene analandila mzimu wa Mulungu sanapite kumwamba?

16 M’Baibulo muli zitsanzo zambili za atumiki a Mulungu okhulupilika amene analandila mzimu woyela wa Yehova, koma sanapite kumwamba. Mmodzi wa anthu amenewa ndi Yohane M’batizi. Yesu anakamba kuti Yohane anali wamkulu kuposa anthu onse, koma pambuyo pake anakambanso kuti Yohane sadzalamulila monga mfumu kumwamba. (Mateyu 11:10, 11) Nayenso Davide anali kutsogoleledwa ndi mzimu woyela. (1 Samueli 16:13) Mzimu woyela unamuthandiza kumvetsa zinthu zozama zokhudza Yehova ndiponso unamutsogolela polemba Mau a Mulungu. (Maliko 12:36) Ngakhale zinali conco, mtumwi Petulo anakamba kuti Davide “sanakwele kumwamba.” (Machitidwe 2:34) Yehova anapatsa atumiki ake amenewa mzimu woyela kuti acite zinthu zazikulu. Koma sanawadzoze ndi mzimuwo kuti adzapite kumwamba. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu amenewa sanali okhulupilika kwambili kapena sanali oyenelela kukalamulila kumwamba? Iyai. Zimangotanthauza kuti Yehova adzawaukitsa m’Paladaiso pano padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

17, 18. (a) Ndi ciyembekezo cotani cimene atumiki ambili a Mulungu ali naco? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani yotsatila?

17 Atumiki ambili a Mulungu masiku ano sadzapita kumwamba. Mofanana ndi Abulahamu, Davide, Yohane M’batizi, ndi anthu ena akale, io ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi pamene Boma la Mulungu lidzalamulila dzikoli. (Aheberi 11:10) Anthu 144,000 ndi amene adzalamulila ndi Yesu kumwamba. Koma Baibulo limanena kuti pali ‘otsalila’ odzozedwa amene akali padziko lapansi m’nthawi ya mapeto ino. (Chivumbulutso 12:17) Conco, ambili mwa Akristu a 144,000 anafa kale ndipo ali kumwamba.

18 Ngati Mkristu wanena kuti ndi wodzozedwa, kodi ena amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi ayenela kucita ciani? Kodi Mkristu wina mumpingo mwanu akayamba kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso, muyenela kumuona bwanji? Nanga muyenela kumva bwanji mukaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya pa Cikumbutso cikukwela? Kodi muyenela kuda nkhawa? Tidzayankha mafunso amenewa m’nkhani yotsatila.

^ [1] (ndime 4) Cikondwelelo ca Pentekosite ciyenela kuti cinali kucitika pa nthawi yofanana ndi nthawi imene Mose anapatsidwa Cilamulo pa Phiri la Sinai. (Ekisodo 19:1) Cotelo, zikuoneka kuti Mose analoŵetsa mtundu wa Isiraeli m’pangano la Cilamulo pa tsiku lofanana ndi limene Yesu analoŵetsa odzozedwa m’pangano latsopano.

^ [2] (ndime 11) Kuti mudziŵe zambili pankhani ya kubadwanso, onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2009, tsamba 3 mpaka 11.