Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANIBE MASO!

Vuto la Othaŵa Kwawo—Mamiliyoni Akuthaŵa m’Dziko la Ukraine

Vuto la Othaŵa Kwawo—Mamiliyoni Akuthaŵa m’Dziko la Ukraine

 Dziko la Russia linayamba nkhondo yofuna kulanda dziko la Ukraine pa February 24, 2022. Izi zinayambitsa mavuto oopsa pamene anthu anayamba kuthaŵa nkhondoyo. a

 “Mabomba anali kuphulitsidwa pali ponse. Sinidziŵa kuti ningafotokoze bwanji kuopsa kwake. Titamva kuti panali masitima opulumutsa anthu, tinaganiza zocoka m’dzikomo. Pa katundu wako wonse, tinali kunyamula cola cimodzi basi. Tinali kungoponyamo zikalata zofunikila, mankhwala, madzi akumwa, komanso tuzakudya twam’njila. Tinasiya ciliconse n’kuthamangila ku sitesheni ya sitima, apo n’kuti mabomba akuphulika.”—Nataliia, wa ku Kharkiv, ku Ukraine.

 “Sitinali kukhulupilila kuti nkhondo ingacitikedi. Koma tsiku lina n’nangodzidzimuka kumva kuphulika kogonthetsa m’khutu, kwina kwake mu mzinda wathu, apo mawindo ali gwede-gwede. N’nati basi nicoka, ndipo n’nalongeza zinthu zofunikila zokhazo. M’maŵa mwake pa 08:00 hrs, n’nakakwela sitima yopita ku mzinda wa Lviv, kenako n’nakwela basi yopita ku Poland.”—Nadija, wa ku Kharkiv, ku Ukraine.

Za m’nkhani ino

 Kodi zenizeni zoyambitsa vutoli la othaŵa kwawo n’zotani?

 Vuto la othaŵa kwawo m’dziko la Ukraine linayambika cifukwa ca nkhondo ya Russia yofuna kulanda dzikolo. Ngakhale n’telo, Baibo imaunikila zifukwa zazikulu zobisika zimene zimayambitsa mavuto a othaŵa kwawo kulikonse:

  •   Maboma a anthu pankhope yonse ya dziko lapansi alephela kuusamalila mtundu wa anthu. Olamulila amagwilitsa nchito ulamulilo wa boma kupondeleza anthu anzawo.—Mlaliki 4:1; 8:9.

  •   Satana Mdyelekezi, “wolamulila wa dzikoli” woipayo, ali na mphamvu kwambili pa anthu. N’cifukwa cake Baibo imakamba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.

  •   Pamwamba pa mavuto amene anthufe tasautsika nawo kwa zaka mazana-mazana, tsopano tikukhala m’nyengo imene Baibo inanenelatu kuti: “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Masiku amenewa, kunali kudzakhalanso nkhondo, matsoka azacilengedwe, njala, na milili ya matenda. Izi ndiye zimakakamiza anthu kuthaŵa.—Luka 21:10, 11.

 Kodi othaŵa kwawo angacipeze kuti ciyembekezo ceniceni?

 Baibo imaonetsa kuti Mlengi wathu Yehova, b ni Mulungu amene ali na cikondi komanso cifundo kwa anthu othaŵa kwawo, pamodzi na aja osiya nyumba zawo cifukwa ca nkhondo. (Deuteronomo 10:18) Iye akulonjeza kuti boma lake lakumwamba lidzathetsa vuto la othaŵa kwawo. Bomalo limachedwa Ufumu wa Mulungu, ndipo Ufumuwo udzatenga malo a maboma onse a anthu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Ufumu wake umenewo, ni umene Yehova adzagwilitse nchito kum’cotsapo Satana Mdyelekezi. (Aroma 16:20) Ndipo Ufumuwo udzakhala boma lokuta dziko lonse lapansi. Izi zitanthauza kuti malile onse ogaŵa maiko adzacoka. Anthu onse padziko lapansi adzakhala banja limodzi logwilizana. Palibe amene adzathaŵe n’kusiya nyumba yake. Tikutelo cifukwa Baibo imalonjeza kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa, pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.”—Mika 4:4.

 Ufumu wa Mulungu ndiwo wokha umene udzathetseletu mavuto a othaŵa kwawo amene tikuwaonawa. Mavuto onse amene akupangitsa anthu kuthaŵa kwawo, Yehova adzawafafaniza pogwilitsa nchito Ufumu wake. Nazi zitsanzo zina:

 Kodi Baibo ingapeleke thandizo kwa othaŵa kwawo masiku ano?

 Inde ikhozadi kutelo. Baibo imapatsa othaŵa kwawo ciyembekezo cotsimikizika. Kuwonjezela apo, ingawathandizenso pa mavuto amene akukumana nawo pali pano.

 Mfundo ya m’Baibo: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mawu alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.”—Miyambo 14:15.

 Tanthauzo lake: Ganizilani zoopsa zimene zingakucitikileni, komanso mmene mungadzitetezele. Cenjelani na acifwamba amene amafuna kubela othaŵa kwawo podziŵa kuti alibe citetezo komanso sadziŵa zinthu kumalo acilendo.

 Mfundo ya m’Baibo: “Pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

 Tanthauzo lake: Pewani kuika kwambili maganizo anu pa zinthu zakuthupi. Mukakhala wokhutila na zofunikila kwenikweni zokha, mudzakhalako na cimwemwe ndithu.

 Mfundo ya m’Baibo: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”—Mateyu 7:12.

 Tanthauzo lake: Khalani woleza mtima komanso wacifundo. Makhalidwe amenewa adzakupezetsani ulemu, ndipo anthu adzakulandilani bwino kumene mukukhalako.

 Mfundo ya m’Baibo: “Musabwezele coipa pa coipa.”—Aroma 12:17.

 Tanthauzo lake: Akakucitani zankhanza, musabwezele cifukwa ca mkwiyo. Mukabwezela, zinthu zidzangoipila-ipila.

 Mfundo ya m’Baibo: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

 Tanthauzo lake: Ikani Mulungu pamalo ofunika mu umoyo wanu, komanso zipemphelani kwa iye. Mukatelo, adzakupatsani mphamvu kuti mupilile.

 Mfundo ya m’Baibo: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.

 Tanthauzo lake: Ngakhale zinthu zivute bwanji kwa inu, pemphani Mulungu kuti akupatseni mtendele wa mumtima na m’maganizo. Onani nkhani yakuti “Afilipi 4:6, 7—‘Musamade Nkhawa Ndi Kanthu Kalikonse.’”

a Nkhondo itayamba ku Ukraine, tsiku lotsatila nthambi ya United Nations yosamalila othaŵa kwawo (UNHCR), inakhala cile pankhani yopeleka cithandizo pa vutolo. M’masiku 12 cabe, anthu opitilila 2 miliyoni anathaŵa m’dziko la Ukraine kupita ku maiko oyandikana nalo. Ndipo enanso 1 miliyoni anabalalitsidwa m’dziko mwawo momwemo.

b Mulungu dzina lake lenileni ni Yehova. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?