KHALANI MASO

Anthu Ambirimbiri Athawa Nkhondo M’dziko la Ukraine

Anthu Ambirimbiri Athawa Nkhondo M’dziko la Ukraine

 Asilikali a dziko la Russia analowa m’dziko la Ukraine pa 24 February, 2022. Nkhondoyi a inayambitsa mavuto aakulu komanso inachititsa kuti anthu ambiri athawe m’dzikolo.

 Mabomba ankangophulitsidwa paliponse. Zinali zoopsa kwambiri moti sindingakwanitse kufotokoza mmene zinalili. Titangomva zoti kuli sitima yotenga anthu othawa nkhondo, tinaganiza zonyamuka nthawi yomweyo. Tinkafunika kusiya chilichonse chifukwa aliyense ankangololedwa kutenga chikwama chimodzi chaching’ono. Tinangotenga zikalata zofunika, mankhwala, madzi akumwa ndi zakudya zochepa basi. Tinasiya chilichonse n’kuthamangira kusiteshoni yasitima kwinaku mabomba akuphulika.”​—Nataliia, wa ku Kharkiv, Ukraine.

 “Sitinkalotako n’komwe kuti kungachitike nkhondo. Ndinayamba kumva kuphulika kwa maboma m’madera ena a mzinda wathu ndipo mawindo a nyumba yathu ankangogwedezeka. Ndinayamba kuthawa nditatenga zinthu zofunika zokha. Ndinanyamuka 8 koloko m’mawa ndipo ndinakwera sitima yopita ku Lviv. Nditafika ku Lviv, ndinakwera basi yopita ku Poland.”​—Nadija, wa ku Kharkiv, Ukraine.

Zimene zili munkhaniyi

 N’chiyani kwenikweni chimene chachititsa vutoli?

 Anthu anathawa m’dziko la Ukraine chifukwa cha nkhondo yomwe inayamba asilikali a dziko la Russia atalowa m’dzikolo. Komabe, Baibulo limafotokoza zifukwa zinanso zikuluzikulu zomwe zimachititsa kuti anthu azithawa kwawo:

  •   Maboma a anthu alephera kupatsa anthu zimene amafunikira. Nthawi zambiri olamulira amagwiritsa ntchito mphamvu zawo popondereza anthu.​—Mlaliki 4:1; 8:9.

  •   Satana Mdyerekezi, amene ndi “wolamulira wa dziko,” amalimbikitsa anthu kuti azichita zoipa. Baibulo limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”​—Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.

  •   Kuwonjezera pa mavuto omwe anthu akhala akulimbana nawo kwa zaka zambiri, panopo tikukhala munthawi imene Baibulo linaneneratu kuti ndi “masiku otsiriza.” Linatinso masikuwa, “adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Baibulo linaneneratunso kuti munthawi imeneyo kudzakhala nkhondo, ngozi zam’chilengedwe, njala komanso miliri, zomwe zimachititsa kuti anthu athawe kwawo.​—Luka 21:10, 11.

 Kodi anthu othawa kwawo angapeze kuti thandizo?

 Baibulo limanena kuti Yehova, b amene ndi Mlengi wathu, amakonda komanso kuchitira chifundo anthu omwe athawa kwawo komanso omwe akakamizika kuchoka m’nyumba zawo chifukwa cha mavuto ena. (Deuteronomo 10:18) Iye akulonjeza kuti adzathetsa mavuto onse a anthu othawa kwawo pogwiritsa ntchito boma lake lakumwamba lotchedwa Ufumu wa Mulungu. Bomali lidzalowa m’malo mwa maboma a anthu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Yehova adzagwiritsanso ntchito Ufumu umenewu pochotsa Satana Mdyerekezi (Aroma 16:20) Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi ndipo zimenezi zidzathetsa mavuto amene amabwera chifukwa chosiyana mayiko. Anthu onse adzakhala banja limodzi logwirizana. Sikudzapezekanso munthu wothawa kwawo chifukwa Baibulo likulonjeza kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa, pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.”​—Mika 4:4.

 Ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetseretu vuto la anthu othawa kwawo. Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pochotsa mavuto onse omwe amachititsa kuti anthu athawe kwawo. Mwachitsanzo, taonani zomwe adzachite:

  •   Nkhondo. Yehova adzathetsa nkhondo. (Salimo 46:9) Kuti mudziwe mmene Mulungu adzachitire zimenezi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Zidzatheka Bwanji Kuti Padziko Lonse Lapansi Padzakhale Mtendere?

  •   Kuponderezana komanso zachiwawa. “Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.” (Salimo 72:14) Kuti mumvetse mmene anthu adzasinthire maganizo aliwonse achidani, werengani nkhani zakuti “Kodi N’zotheka Kuthetsa Chidani?

  •   Umphawi. “Adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo.” (Salimo 72:12) Kuti mudziwe mmene Mulungu adzathetsere umphawi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?

  •   Njala. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.” (Salimo 72:16) Kuti mudziwe zomwe Mulungu adzachite poonetsetsa kuti aliyense ali ndi chakudya chokwanira, werengani nkhani yakuti, “Kodi Njala Idzatha Padziko Pano?

 Kodi Baibulo lingathandize anthu omwe akuthawa kwawo masiku ano?

 Inde. Ngakhale Baibulo limalonjeza kuti vuto la anthu othawa kwawo lidzatha m’tsogolo muno, lilinso ndi mfundo zomwe zingathandize anthu amene akhudzidwa ndi vutoli panopa.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”​—Miyambo 14:15.

 Tanthauzo lake: Muyenera kudziwa mavuto omwe mungakumane nawo komanso zomwe mungachite kuti mukhale otetezeka. Muzisamala ndi anthu oipa omwe amapezerera anthu othawa kwawo chifukwa amadziwa kuti anthuwa amakhala amantha komanso sadziwa zambiri zokhudza kumene athawirako.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”​—1 Timoteyo 6:8.

 Tanthauzo lake: Muzipewa kuganizira kwambiri za katundu. Kukhala okhutira ndi zimene muli nazo kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”​—Mateyu 7:12.

 Tanthauzo lake: Muzileza mtima komanso kukomera mtima anthu ena. Makhalidwewa angakuthandizeni kuti anthu azikupatsani ulemu komanso kuti muzikhala bwino ndi anthu am’dera lomwe mwafikira.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Musabwezere choipa pa choipa.”​—Aroma 12:17.

 Tanthauzo lake: Musalole kuti zinthu zopanda chilungamo zimene ena akuchitirani, zikukwiyitseni mpaka kufika pobwezera. Kuchita zimenezi kukhoza kungokulitsa vutolo.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afilipi 4:13.

 Tanthauzo lake: Muzidalira kwambiri Mulungu ndiponso muzipemphera kwa iye. Mukatero, iye adzakuthandizani kuti mupeze mphamvu zomwe zingakuthandizeni kupirira.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”​—Afilipi 4:6, 7.

 Tanthauzo lake: Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni kukhala ndi mtendere wamumtima. Werengani nkhani yakuti, “Afilipi 4:6, 7 ‘Musamade Nkhawa Ndi Kanthu Kalikonse.’”

a Asilikali a dziko la Russia atangolowa m’dziko la Ukraine, tsiku lotsatira, nthambi ya bungwe la United Nations yoona za anthu othawa kwawo (UNHCR), inanena kuti zomwe zachitikazi ndi vuto lalikulu kwambiri. M’masiku 12 okha asilikaliwa atalowa m’dzikolo, anthu oposa 2 miliyoni anathawa m’dziko la Ukraine n’kupita kumayiko ena apafupi. Pomwe anthu enanso okwana 1 miliyoni anathawa m’nyumba zawo n’kusamukira kumadera ena m’dziko lomwelo.

b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?