Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Comstock Images/Stockbyte via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Mudzasankha Ndani Kukhala Mtsogoleri Wanu?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mudzasankha Ndani Kukhala Mtsogoleri Wanu?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 M’mawiki akubwerawa, m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse mukhala mukuchitika zisankho, ndipo anthu akuganizira zosankha atsogoleri amene akufuna kuti adzawalamulire.

 Kodi Baibulo limanena zotani?

Utsogoleri wa anthu uli ndi malire

 Baibulo limanena kuti maulamuliro onse a anthu ali ndi malire.

  •   “Musamakhulupirire anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso. Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.”​—Salimo 146:3, 4, mawu a m’munsi.

 Ngakhale olamulira ena amakhala abwino, n’kupita kwa nthawi amafa. Komanso, sangayembekezere kuti anthu amene adzabwere pambuyo pawo adzapitiriza ntchito zabwino zimene iwowo ankachita.​—Mlaliki 2:18, 19.

 Zoona zake n’zakuti Baibulo limanena kuti sizingatheke kuti anthu azidzilamulira okha bwinobwino.

  •   “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23.

 Kodi alipo amene angalamulire anthu bwinobwino masiku ano?

Mtsogoleri wosankhidwa ndi Mulungu

 Baibulo limafotokoza kuti Mulungu wasankha mtsogoleri wabwino kwambiri ndiponso wodalirika, Yesu Khristu. (Salimo 2:6) Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu womwe ndi boma lomwe likulamulira kuchokera kumwamba.​—Mateyu 6:10.

 Kodi musankha Yesu kukhala mtsogoleri wanu? Baibulo limafotokoza chifukwa chake kupeza yankho la funsoli kuli kofunika:

  •   “Psompsonani mwanayo [Yesu Khristu] kuopera kuti Mulungu angakwiye, ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo. Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumira. Odala ndi onse amene akuthawira kwa iye.”​—Salimo 2:12.

 Panopa ndi nthawi yoti musankhe zochita. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti Yesu anayamba kulamulira m’chaka cha 1914 ndipo posachedwapa Ufumu wa Mulungu ulowa m’malo mwa maboma onse a anthu.​—Danieli 2:44.

 Kuti mudziwe zambiri zomwe mungachite kuti mukhale kumbali ya ulamuliro wa Yesu, werengani nkhani yakuti, “Sankhani Kukhala Kumbali ya Ufumu wa Mulungu Panopa.”