Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

E+/taseffski/via Getty Images (Stock photo. Posed by model.)

KHALANI MASO!

Ciŵelengelo ca Acinyamata Odwala Matenda a Maganizo Cikuculuka—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Ciŵelengelo ca Acinyamata Odwala Matenda a Maganizo Cikuculuka—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Pa Mande, February 13, 2023, bungwe loona za umoyo lochedwa Centers for Disease Control and Prevention (CDC) ku United States linatulutsa lipoti la ciŵelengelo ca acinyamata odwala matenda amaganizo mu U.S. Lipotilo linati ana oposa 40 pelesenti kusukulu ya sekondale amakhala okhumudwa komanso opanda ciyembekezo.

 Dr. Kathleen Ethier, amene ni mtsogoleli wa nthambi ya bungwe la CDC yochedwa Division of Adolescent and School Health (DASH) anati: “Takhala tikuona kuculuka kwa acinyamata amene amadwala matenda a maganizo m’zaka 10 zapitazi. Koma ciŵelengelo ca atsikana odwala matenda amaganizo, komanso amene amafuna kudzipha cawonjezeka kwambili kuposa kale lonse.”

 Lipotilo linati:

  •   Pafupifupi atsikana aŵili pa 10 aliwonse (14 pelesenti) amagonedwa mwacikakamizo. Dr. Ethier ananena kuti: “Pa atsikana 10 alionse amene udziŵa, mtsikana mmodzi ngakhale kuposapo, amakhala kuti anagwililidwapo. Zimenezi n’zomvetsa cisoni kwambili.”

  •   Pafupifupi mtsikana mmodzi pa atsikana atatu alionse (30 pelesenti) anakhalapo na maganizo ofuna kudzipha.

  •   Pafupifupi atsikana atatu pa 5 alionse (57 pelesenti) anapsinjikako maganizo kapena kutaya mtima.

 Ziŵelengelo zimenezi n’zomvetsa cisoni kwambili. Unyamata ni nthawi imene munthu amafunika kukhala wosangalala. N’ciyani cingathandize acinyamata kuthana na nkhawa masiku ano? Kodi Baibo ikutipo ciyani?

Baibo ili na malangizo othandiza kwa acinyamata

 Baibo imakamba mosapita mbali za nthawi yovuta imene tikukhalamo. Imati ni “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1-5) Komabe, imapeleka malangizo amene amathandiza acinyamata mamiliyoni padziko lonse kulimbana na mavuto amene amakumana nawo. Ŵelengani nkhani zotsatilazi zokhala na malangizo a m’Baibo.

 Mfundo zothandiza acinyamata amene ali na maganizo ofuna kudzipha

 Mfundo zothandiza acinyamata kulimbana na matenda amaganizo, kukhumudwa kapena maganizo olefula

 Mfundo zothandiza acinyamata akamavutitsidwa ndi anzawo

 Mfundo zothandiza acinyamata amene akulimbana na nkhanza zokhudza kugonana

Baibo imapeleka malangizo othandiza kwa makolo

 Baibo imapelekanso malangizo abwino amene makolo angagwilitse nchito pothandiza ana awo kulimbana na nkhawa za pa umoyo. Ŵelengani nkhani zotsatilazi zokhala na malangizo a m’Baibo.