KHALANI MASO
Achinyamata Ambiri Akuvutika Ndi Matenda Amaganizo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Lolemba pa 13 February 2023, bungwe loona za umoyo la ku United States (Centers for Disease Control and Prevention, CDC) linatulutsa lipoti lokhudza achinyamata am’dzikoli omwe ali ndi vuto la matenda amaganizo. Zikuoneka kuti 40 peresenti ya ana a kusekondale amakhala okhumudwa komanso opanda chiyembekezo.
Dr. Kathleen Ethier yemwe ndi mkulu wa bungwe la CDC ndi Division of Adolescent and School Health (DASH), ananena kuti: “Tapeza kuti vuto la matenda amaganizo pakati pa achinyamata lawonjezereka kwambiri pa zaka 10 zapitazo. Koma kuposa kale lonse, vutoli lakula kwambiri pakati pa atsikana ndipo pali atsikana ambiri amene akumaganiza zodzipha kapena kuyesa kudzipha.”
Lipoti la pa 13 February 2023, linanena kuti:
Atsikana oposa 14 pa 100 aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, amakakamizidwa kuchita chiwerewere. Dr. Ethier ananena kuti: “Zimenezi n’zokhumudwitsa chifukwa pa atsikana 10 aliwonse, mmodzi kapena kuposa pamenepo anagwiriridwapo.”
Pafupifupi mtsikana mmodzi pa atatu aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, anaganizirapo kwambiri zofuna kudzipha.
Pafupifupi atsikana atatu pa 5 aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, amangokhala okhumudwa kapena opanda chiyembekezo.
Malipotiwa ndi okhudza mtima kwambiri. Nthawi imene munthu ali wachinyamata amafunika azisangalala. Ndiyeno n’chiyani chomwe chingathandize achinyamata kuti azitha kupirira mavuto amenewa? Kodi Baibulo limanena zotani?
M’Baibulo muli malangizo othandiza achinyamata
Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti tizikumana ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa. Ndipo linanena kuti, ‘tidzakhala m’nthawi yapadera komanso yovuta.’ (2 Timoteyo 3:1-5) Komabe, Baibulo limapereka malangizo othandiza achinyamata mamiliyoni padziko lonse kulimbana ndi mavuto amene akukumana nawo. Taonani nkhani zotsatirazi zochokera m’Baibulo.
Mfundo zothandiza achinyamata omwe ali ndi maganizo ofuna kudzipha
Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?
Mfundo zothandiza achinyamata kulimbana ndi matenda amaganizo, kukhumudwa kapena maganizo olakwika
Mfundo zothandiza achinyamata akamavutitsidwa ndi anzawo
Mfundo zothandiza achinyamata omwe akukumana ndi nkhanza zokhudza kugonana
Baibulo limapereka malangizo othandiza kwa makolo
Baibulo limaperekanso malangizo kwa makolo kuti azithandiza ana awo kupirira mavuto omwe akukumana nawo. Taonani nkhani zotsatirazi zochokera m’Baibulo.
N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?
Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo
Kodi Ndingatani Ngati Nditamva Kuti Mwana Wanga Amavutitsidwa ndi Anzake?
Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala
Ana ndi Mafoni—Mbali Yoyamba: Kodi Mwana Wanga Akhale ndi Foni?
Ana ndi Mafoni—Mbali Yachiwiri: Phunzitsani Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Foni Mosamala
Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
NSANJA YA OLONDA
Matenda Ovutika Maganizo Ndi Vuto la Padziko Lonse
Matenda ovutika maganizo akhoza kukhudza munthu wina aliyense posatengera msinkhu kapena kochokera. Onani mmene malangizo a m’Baibulo angakuthandizireni ngati muli ndi matendawa.
ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS
N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi.
ZOKHUDZA IFEYO
Pemphani Kuti Tidzakuyendereni
Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.