Pa 23 May 2023, katswiri wa za umoyo ku United States anachenjeza anthu za mavuto amene achinyamata ambiri akukumana nawo akamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.
Magazini ina inati: “Ngakhale kuti ana komanso achinyamata ena akhoza kupeza zinthu zothandiza pamalo ochezera a pa intaneti, pali maumboni ambiri osonyeza kuti malowa angathe kuwononga maganizo komanso thanzi lawo.”—Social Media and Youth Mental Health: The U.S. Surgeon General’s Advisory, 2023.
Achinyamata oyambira zaka 12 mpaka 15 “amene amakhala pamalo ochezera a pa intaneti kwa maola oposa atatu pa tsiku, amakhala pa chiopsezo chodwala matenda amaganizo kuwirikiza kawiri kuphatikizapo kusonyeza zizindikiro za matendawa.”
Achinyamata azaka 14 “amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, amalephera kugona, sasangalala ndi mmene amaonekera, amachitiridwa nkhanza za pa intaneti, amadzikayikira komanso amasonyeza zizindikiro zambiri za matenda amaganizo ndipo zimenezi zimachitikira kwambiri atsikana kuposa anyamata.”
Ndiye makolo angateteze bwanji ana awo kuti asakumane ndi mavuto amenewa? Baibulo limapereka malangizo othandiza pa nkhaniyi.
Zomwe makolo angachite
Muzichitapo kanthu. Makolo, ganizirani kuopsa kogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kenako mungasankhe kuti mwana wanu azigwiritsa ntchito malowa kapena ayi.
Mfundo ya m’Baibulo: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.”—Miyambo 22:6.