Pitani ku nkhani yake

Nsanja ya Olonda—Magazini Oposa Magazini Ena Onse

Nsanja ya Olonda—Magazini Oposa Magazini Ena Onse

Magazini a Nsanja ya Olonda amafalitsidwa ochuluka kwambiri kuposa magazini ena onse padziko lonse lapansi. Magaziniyi imatuluka kawiri pa mwezi ndipo magazini iliyonse imasindikizidwa makope oposa 42 miliyoni. Magazini yotsatira ndi ya Galamukani! ndipo imatuluka mwezi uliwonse. Magazini ya mwezi uliwonse imasindikizidwa makope 41 miliyoni. Magazini onsewa akufalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo amagawidwa m’mayiko 236.

Nanga bwanji ponena za magazini ena amene safalitsidwa ndi Mboni za Yehova? Malinga ndi bungwe lina loyang’anira makampani ofalitsa magazini, (The Association of Magazine Media), magazini ogulitsidwa a ku America omwe amafalitsidwa kwambiri, ndi a bungwe linalake lotchedwa AARP. Nkhani za m’magaziniwa zimakhala zokhudza kwambiri anthu a zaka zoposa 50. Magazini imeneyi imasindikizidwa makope oposa 22.4 miliyoni. Magazini yotsatira ndi ya ku Germany (ADAC Motorwelt) yomwe imasindikizidwa makope pafupifupi 14 miliyoni. Magazini yachitatu ndi ya ku China (Gushi Hui [Nkhani]) yomwe imasindikizidwa makope 5.4 miliyoni.

Pa nkhani ya manyuzipepala, yoyamba ndi ya ku Japan (Yomiuri Shimbun). Nyuzipepalayi imasindikizidwa makope oposa 10 miliyoni.

Mabuku a Mboni za Yehova akuposanso mabuku ena onse pa nkhani yomasuliridwa m’zinenero zina. Magazini ya Nsanja ya Olonda imamasuliridwa m’zinenero zoposa 190 ndipo magazini ya Galamukani! imamasuliridwa m’zinenero zoposa 80. Pamene magazini a Reader’s Digest amafalitsidwa m’zinenero 21 ndipo nkhani zake zimakhala zosiyana malinga ndi dziko limene yafalitsidwako.

Mosiyana ndi magazini ena onse amene atchulidwa m’nkhaniyi, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani amafalitsidwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Komanso salengezedwa pamalo oitanira malonda ndiponso alibe mtengo.

Cholinga cha Nsanja ya Olonda n’kufotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa, makamaka zokhudza Ufumu wa Mulungu. Kuyambira mu 1879, magaziniyi yakhala ikufalitsidwa mosadukiza mpaka pano. Magazini ya Galamukani! imafotokoza nkhani zosiyanasiyana, monga zokhudza chilengedwe ndiponso sayansi, n’cholinga chotithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mlengi. Imafotokozanso mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire pa moyo wathu.