Kuona Malo ku Beteli
Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.
Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.
Malawi
Alendo Ndiponso Kuona Malo
Zimene Timachita
Timamasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’Chichewa, Chitonga, Chitumbuka, Chiyao ndiponso Chinenero Chamanja cha ku Malawi. Timayang’aniranso ntchito imene mipingo ya Mboni za Yehova ikugwira m’Malawi.
Adiresi ndi Nambala za foni