Pitani ku nkhani yake

Kodi Mkhristu Angalandire Chithandizo cha Mankhwala Akadwala?

Kodi Mkhristu Angalandire Chithandizo cha Mankhwala Akadwala?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Yesu anasonyeza kuti otsatira ake akhoza kulandira chithandizo cha mankhwala pamene anati: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” (Mateyu 9:12) N’zoona kuti Baibulo si buku lofotokoza za mankhwala koma lili ndi mfundo zimene zingathandize munthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu posankha chithandizo cha mankhwala.

Dzifunseni kuti

 1. Kodi ndikumvetsa zonse zokhudza chithandizo chimene akufuna kundipatsa? Baibulo limanena kuti tisamangokhulupirira “mawu alionse” koma tizifufuza bwinobwino.—Miyambo 14:15.

 2. Kodi ndifunse maganizo madokotala ena ndisanalandire chithandizochi? Kumva maganizo a anthu ambiri kukhoza kukuthandizani kusankha bwino, makamaka ngati matenda anuwo ndi aakulu.—Miyambo 15:22.

 3. Kodi chithandizochi chichititsa kuti ndiphwanye lamulo la m’Baibulo lakuti ‘tipewe magazi’?—Machitidwe 15:20.

 4. Kodi chithandizocho chikukhudza zamizimu? Pajatu Baibulo limati tiyenera kupewa “kuchita zamizimu.” (Agalatiya 5:19-21) Kuti mudziwe ngati chithandizocho chikukhudza zamizimu, dzifunseni kuti:

  •   Kodi woperekayo amachita zamizimu?

  •   Kodi woperekayo akuganiza kuti matendawo anayamba chifukwa choti mizimu yakwiya kapena ndalodzedwa?

  •   Kodi pokonza kapena pogwiritsa ntchito mankhwalawo amapereka nsembe mwinanso kuchita miyambo inayake yokhudza kukhulupirira mizimu?

 5. Kodi ine ndimangokhalira kuganizira za thanzi langa? Baibulo limatiuza kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Kukhala wololera, kapena kuti woganiza bwino, kudzakuthandizani kuti muziganizira “zinthu zofunika kwambiri,” monga kutumikira Mulungu.—Afilipi 1:10; Mateyu 5:3.