Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ntchito Yomanga Ikuyenda Bwino Kwambiri ku Wallkill ndi ku Warwick

Ntchito Yomanga Ikuyenda Bwino Kwambiri ku Wallkill ndi ku Warwick

Ntchito yaikulu yomanga nyumba ndi maofesi atsopano a Mboni za Yehova ku United States ikuyenda bwino kwambiri. Ntchitoyi ikuchitika m’malo awiri ndipo anthu ongodzipereka, ochokera m’dziko lomweli, ndi amene akugwira ntchitoyi.

Ku Wallkill m’dera la New York: Uku kumakhala anthu a Mboni oposa 1,600 ndipo ndi kumene kuli makina osindikizira mabuku a Mboni za Yehova m’dziko la United States. Popeza ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill ikukula, kumalowa kwayambika ntchito yowonjezera nyumba zina. Anthu ambiri amene akugwira ntchito yomangayi ndi ongodzipereka ndipo akumanga nyumba yosanja katatu yomwe mukhale maofesi. Kuwonjezera pamenepa, akumanganso malo oimika magalimoto komanso nyumba yogona yomwe ndi yosanja katatu. Pomafika m’chaka cha 2012, anthu omwe akugwira ntchitoyi anali atamaliza kumanga nyumba yosungiramo zipangizo zosiyanasiyana komanso anali atakulitsa chipinda chodyera kuti m’chipindacho muzitha kukhala anthu 200.

A Mboni za Yehova ali ndi maofesi ena m’mayiko osiyanasiyana monga ku Brazil, Germany ndi ku Mexico ndipo maofesi amenewa amawatchula kuti maofesi a nthambi. Ku United States, a Mboni za Yehova alinso ndi malo ku Patterson m’dera la New York, komwe kuli masukulu osiyanasiyana ophunzitsa Baibulo komanso ali ndi maofesi ku Brooklyn, m’chigawo chomwecho cha New York. Ntchito yomangayi ikatha, ndiye kuti ku Wallkill n’komwe kukhale nyumba zambiri komanso zikuluzikulu kuposa maofesi ndi nyumba zina za Mboni za Yehova zimene zili m’madera ena padziko lonse.

Ku Warwick m’dera la New York: Kumalo amenewa n’komwe kudzakhale likulu la Mboni za Yehova padziko lonse. Nyumba zopanda anthu zomwe zinali pamalowa zinagwetsedwa. A Mboni apeza malo ena ku Tuxedo, m’dera lomweli la New York, omwe ali pa mtunda wamakilomita 10 kuchokera ku Warwick. Kumalo amenewa n’kumene akusungirako zipangizo zawo zimene akugwiritsa ntchito pa ntchito yomanga ku Warwick. Panopa, akuluakulu oona zachilengedwe avomereza kuti ntchitoyi ipitirire chifukwa aona kuti siwononga zachilengedwe. Pulani ya maofesiwo ikangovomerezedwa, a Mboni za Yehova alemba chikalata ku boma chopempha chilolezo choti ntchito yomangayo ipitirire. Padakali pano, likulu la Mboni za Yehova lidakali ku Brooklyn, mumzinda wa New York.